Mzika Voice

Mzika Voice Mzika Voice is a platform where Malawian Citizens can express their concerns in exercising the princi

Anthu ambiri ali ndi mafunso opanda mayankho. Ndichifukwa ninji oyimba ambiri akumwalira modabwitsa? Mzimu wa Athot Manj...
09/10/2023

Anthu ambiri ali ndi mafunso opanda mayankho. Ndichifukwa ninji oyimba ambiri akumwalira modabwitsa? Mzimu wa Athot Manje uwutse mu ntendere!😭🙏

MUTHARIKA AZAIMA NGATI PRESIDENT WA DPP 2025Professor Arthur Peter Mutharika akuzayima pa udindo wa President ku chipani...
09/10/2023

MUTHARIKA AZAIMA NGATI PRESIDENT WA DPP 2025
Professor Arthur Peter Mutharika akuzayima pa udindo wa President ku chipani Cha DPP ku zisankho zosankha mtsogoleri wa dziko zomwe anthu akuyembekeza kuzachita 2025.

Iwo anena izi ku mkumano wa Alhomwe omwe umachitika chaka chirichonse mwezi wa October ku likulu lawo kwa a Chonde m'boma la Mulanje.

Dziko la Malawi likudutsa mu nyengo zowawitsa ngati kukwera kwa zinthu, kusowa kwa chakudya kungotchulapo zochepa.

A Mutharika asimikizira mzika za dziko lino kuti amva kulira kwawo ndipo 2025 akubweranso kuzaliphula dzikoli pamoto ndikulichotsa mmanja mwa anthu oyipa.

Potsindika iwo ati kwa dzaka ziwiri chuma chizakhala kuti chiri mchimake zonse zikuyenda bwino.

Mwazina iwo anakumbutsa anthu onse zomwe anayankhula mchaka cha 2020 kuti "aMalawi sankhani chitukuko osati ndale". Izi zimapereka chithunzithunzi choti palibenso chipani choganizira umoyo wa anthu ngati cha DPP.

Mulhako wa Alhomwe unayamba mchaka cha 2008 mosongozedwa ndi masomphenya a Malemu Professor Bingu Wa Mutharika.

MULHAKO WA ALHOMWE 2023 WAYAMBA BWINOChaka chirichonse Alhomwe amakhala ndi mwambo umene umathandizira kulimbikitsa chik...
07/10/2023

MULHAKO WA ALHOMWE 2023 WAYAMBA BWINO
Chaka chirichonse Alhomwe amakhala ndi mwambo umene umathandizira kulimbikitsa chikhalidwe cha Chilomwe.

Mchaka chino Cha 2023 mwambowu unayamba lachinayi pa 5 October, ndipo unayamba ndi mapemphero.

Mwazina, mfumu yaikulu kaduya omwenso anali mlendo olemekezeka ati chiyambi Cha nzeru ndikuopa Mulungu choncho chofunikira mu zonse ndikusaka chisongozo kwa Iye.

A Kaduya ati pa mwambowu alimbikitsa anthu kufunikira kozala mitengo m'mapiri komanso misinje kuti mavuto osefukira kwa madzi achepe.

Mwambowu unasongozedwa ndi akuluakulu a zipembezo zosiyanasiyana monga chi Silamu komanso chi Khristu.

DZIKO LAFIKA POVUTA. KODI MCP ANTHU ATANI NAYO?
02/10/2023

DZIKO LAFIKA POVUTA. KODI MCP ANTHU ATANI NAYO?

MWAMBO WA MULHAKO WA ALHOMWE UCHITIKA PA 8 OCTOBER, 2023.Zokonzekera zonse zokhuza mwambo wa Mulhako wa Alhomwe omwe uma...
30/09/2023

MWAMBO WA MULHAKO WA ALHOMWE UCHITIKA PA 8 OCTOBER, 2023.
Zokonzekera zonse zokhuza mwambo wa Mulhako wa Alhomwe omwe umachitika chaka chirichonse mwezi wa October zafika kumapeto.

Potsindika ena mwa akuluakulu oyendetsa mwambowu monga a Elvis Todi, Muchanakwaye Mpuluka komanso Pius Mvenya asimikizira Mzika Voice kuti mwambo wa chaka chino ukhala opambana kwambiri kamba koti zokonzekera zonse zayenda bwino ndipo akupempha aliyense kuzafika pa tsikuli.

Mwazina iwo ati kukhala ndi nkumano otere ndikofunikira kwambiri kamba koti zimalimbikitsa umodzi komanso kupititsa patsogolo chikhalidwe cha Chilomwe.

Mulhako wa Alhomwe umachitikira kwa a Chonde m' Boma la Mulanje.

#

KWACHA YAGWANSO KACHINAYI (4) KUYAMBIRA MWEZI WA JANUARY 2023.Reserve Bank of Malawi yalengeza kuti ndalama ya kwacha ya...
29/09/2023

KWACHA YAGWANSO KACHINAYI (4) KUYAMBIRA MWEZI WA JANUARY 2023.
Reserve Bank of Malawi yalengeza kuti ndalama ya kwacha ya dziko lino la Malawi igwa phamvu ndi 4.7 perecent zomwe ndi kuchokera pa K1,126 kufika pa K1,180.29 kuyelekeza ndi ndalama ya dollar ya ku America kuyambila pa 2 October, 2023 mwenzi wa m'mawa.

Vutoli labweretsa chiwopyezo ku ntundu onse kamba koti zinthu zikhala zikukwera mitengo zimenso ziike pamavuto miyoyo yochuluka.

Padakali pano ntengo wa fetereza uli pa 100,000 ndipo thumba lachimanga likugulidwanso ndi ndalama zokwana 50,000 kungotchulapo zochepa.

#

MAPEMPHERO OPEMPHERERA DZIKO LA MALAWIGulu la Pastors Link (Blantyre Chapter) mogwirizana ndi ma Concerned Citizens akon...
29/09/2023

MAPEMPHERO OPEMPHERERA DZIKO LA MALAWI
Gulu la Pastors Link (Blantyre Chapter) mogwirizana ndi ma Concerned Citizens akonza mwambo wa mapemphero omwe uchitike pa Robin's Park.

Mwambowu uzachitika pa 2 okotobala 2023.

Mwazina, cholinga cha mwambowu ndikufuna kupempherera Malawi kumavuto omwe mzika zake zikukumana nawo monga umbava ndi umbanda, zipolowe, kuponderezedwa ku mwayi wa ntchito ndi zina komanso ku infa zophedwa mosaziwika bwino kamba kakusowekera chitetezo cha dziko.

Potsindika, amabugwewa ati akapanda kutetezera dziko Mulungu mwini, onse amene amachita ntchitoyi pawokha amagwira chabe.

#

Kodi zomwe achita a Amalys Hotel kuthamangitsa Thabo Chaka Nyirenda pamaso pa alendo ndizabwino?
28/09/2023

Kodi zomwe achita a Amalys Hotel kuthamangitsa Thabo Chaka Nyirenda pamaso pa alendo ndizabwino?

Dzikoli mene liririmu, njala ponseponse, kusowa kwa ntchito, ndalama sizikupezeka kungotchulapo zochepa. INU AMALAWI MUM...
28/09/2023

Dzikoli mene liririmu, njala ponseponse, kusowa kwa ntchito, ndalama sizikupezeka kungotchulapo zochepa. INU AMALAWI MUMAWAGANIZIRA ZOTANI ANTHU AMENEWA?🤔

Kodi akuluwa amaziwika ndi mbiri zotani? Mowanyadira tazitchuleni! 😁
28/09/2023

Kodi akuluwa amaziwika ndi mbiri zotani? Mowanyadira tazitchuleni! 😁

28/09/2023

Chigawo chapakati tangwirizana kuzavotera Peter Mutharika 2025. Nanga inu aku Mpoto komanso ku Mmwera mukuti bwanji?

Kodi m'mene zateremu mukuonapo bwanji? Kodi nanga nkulakwa kunena zakukhosi kwako munthu?
28/09/2023

Kodi m'mene zateremu mukuonapo bwanji? Kodi nanga nkulakwa kunena zakukhosi kwako munthu?

TIWONA M'MENE ZITHERENduna yowona za chitetezo a Ken Zikhale N'goma awopyeza kuthana ndi mzika za dziko lino kamba koti ...
27/09/2023

TIWONA M'MENE ZITHERE

Nduna yowona za chitetezo a Ken Zikhale N'goma awopyeza kuthana ndi mzika za dziko lino kamba koti zikukamba chilungamo pa mavuto omwe aMalawi akukumana nawo.

Potsatira nkumano omwe anali nawo ndi atolankhani, a Ng'oma ati Pali anthu ena omwe akumafotokoza mbiri ya dziko lino angakhalenso chiyambi Cha zinthu sosiyanasiyana.

Mwazina iwo anapereka chitsanzo cha munthu Yemwe ndi mwini page ya Bakili Muluzi TV kuti zimene iye amakamba zikuzindikiritsa chowonadi anthu ambiri.

Potsindika iwo ati athana ndi mwini page ya Bakili Muluzi TV.

Kuphedwa kwa anthu ochuluka m'mwezi wa September, 2023 komanso Kuwululika kwa zinsisi zina za chipani cha MCP ndikomwe kwausa mapiri pachigwa pa nkhaniyi.

#

Mmene dziko likuyendera pano mungamuuze chani Peter Mutharika?🤔
27/09/2023

Mmene dziko likuyendera pano mungamuuze chani Peter Mutharika?🤔

UTHENGA WACHISONIYemwe anali mtsogoleri wakale wa chipani Cha MCP a John Zenasi Ungapake Tembo amwalira lero atadwala nt...
27/09/2023

UTHENGA WACHISONI

Yemwe anali mtsogoleri wakale wa chipani Cha MCP a John Zenasi Ungapake Tembo amwalira lero atadwala nthenda ya shuga.

A Tembo anali munthu olimbikira ku ndale komanso anathandizira ku ntchito za chitukuko cha dziko lino mu nthawi yomwe iwo anali ndi moyo.

Iwo anabadwa mchaka cha 1932 ndipo amwalira chaka chino cha 2023 ali ndi zaka 91.

Mzimu wa John Zenasi Ungapake Tembo uwuse mumtendere.🙏

#

27/09/2023

ZINTHU ZA CHILENDO ZIKUPITIRIRA KUCHITIKA MDZIKO MUNO

Patangotha sabata imodzi mphekesera zitamveka kuti mdziko muno mwabwera asilikali achilendo ndipo galimoto za nkhondo zodabwitsa zinachokera ku Boarder ya Mozambique; leronso usiku wapa 26 September, 2023 kwadutsa Galimoto zitatu zachilendo za asilikali ndipo zakhota pa Chitakale kumapita nsewu wa Phalombe.

Mphekesera zikumveka kuti a John Ungapake Tembo yemwenso anali mtsogoleri wakale wachipani Cha MCP amwalira. Mzimu wawo ...
27/09/2023

Mphekesera zikumveka kuti a John Ungapake Tembo yemwenso anali mtsogoleri wakale wachipani Cha MCP amwalira.

Mzimu wawo uwuse mumtendere 😭

Chiwerengero cha ana omwe akusiya school chakwera m'maboma ambiri a mdziko muno. Izi ziri chomwechi kamba ka umphawi kom...
27/09/2023

Chiwerengero cha ana omwe akusiya school chakwera m'maboma ambiri a mdziko muno.

Izi ziri chomwechi kamba ka umphawi komanso kusowa kwa ndalama.

Makolo ambiri akulephera kusamalira ana ndipo m'malo mwake akumalimbikitsa kusaka maganyu kuti angopeza chakudya chalero.

#

MAIKO A CHIZUNGU ALI OKHUMUDWA KAMBA KA KUPHEDWA KWA M'BALE WAWO.Kuphedwa kwa anthu m'mizinda ya m'dziko muno monga Blan...
26/09/2023

MAIKO A CHIZUNGU ALI OKHUMUDWA KAMBA KA KUPHEDWA KWA M'BALE WAWO.

Kuphedwa kwa anthu m'mizinda ya m'dziko muno monga Blantyre, Lilongwe, Rumphi kungotchulapo pang'ono zakhumudwitsa komanso kukwiitsa a Zungu kamba ka chipongwe chomwe watchitiridwa munthu wa ntundu wawo.

#

SINDIKUONAPO VUTO PAKUPHEDWA KWA ANTHU M'DZIKO MUNOAwa ndi mawu omwe ayankhula a Ken Zikhale N'goma omwenso ndi nduna yo...
26/09/2023

SINDIKUONAPO VUTO PAKUPHEDWA KWA ANTHU M'DZIKO MUNO

Awa ndi mawu omwe ayankhula a Ken Zikhale N'goma omwenso ndi nduna yowona za chitetezo cha dziko kuchokera ku MCP.

Mzika zambiri zikudandaula komanso kukhala mwa mantha kamba ka imfa za anthu omwe akhala akuphedwa komanso kusowesedwa m'dziko muno.

Poyankhula ndi atola nkhani ndunayi yati zimenezi sizikutanthauza kuti chitetezo palibe komanso kuphedwa kwa anthuwa sizinthu zodetsa nkhawa.

#

26/09/2023

Mwa changuchangu!
Kodi mukuganizira kuti anthu omwe akusokoneza chipani Cha DPP ndi ati? Atchuleleni ndithu kuti aMalawi asazapangenso mistake.

ALANDIDWA NJINGA ZA MOTOApolisi Alanda njinga zamoto zokwana 38 kwa anthu omwe amachita kabaza wa njingazi m'boma la Mzu...
26/09/2023

ALANDIDWA NJINGA ZA MOTO

Apolisi Alanda njinga zamoto zokwana 38 kwa anthu omwe amachita kabaza wa njingazi m'boma la Mzuzu.

Mwazina anthuwa alamuliddwa kuti njinga zawo akazitenga akakwaniritsa ndondomeko zokhomera nsokho.

Padakali pano njingazi zikusungidwa ku bungwe lowona zapa nsewu la Road Traffic m'bomalo.

#

26/09/2023

Kuwina kwa Bambo Finiyasi ngati Khansala wa DPP ku Zomba zikupereka chithunzithunzi choti DPP izawina 2025.

Address

Maselema
Blantyre

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mzika Voice posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Videos

Share


Other Broadcasting & media production in Blantyre

Show All