26/07/2022
TINABWELA KUDZAGWILA NTCHITO YOWATEZA KOMA AKUTIPANGASO CHIPONGWE.
Asilikali ammaiko osiyanasiya kuphatikizako adziko lino omwe adapita kukasungitsa bata pansi pa bungwe la United nations adandaula kamba kazomtopola zomwe akupanga anthuwa kudela lina kumeneko.
Dzulo anthu amdelali anapanga zionetselo pofuna kukakamiza bungwe la United Nations k*t lichotse asilikali ake kudelali ndipo adzipitakwapo ponena k*ti sakuwafunaso pazifukwa zodziwa okha, anthu okwiyawa agwetsa mpanda wamalo ena komwe kumakhala asilikaliwo ndipo alanda zinthu monga makama matilesi ndikuotcha zipangizo zina za united nations pazionetselo zomwe anachit dzulo ndipo podziteteza asilikaliwa apha anthu okwana 4.
Kuchakwalelo anthuwa anapitilila kuchitabe zamtopola ndipo tikunena pano asilikaliwa athawa ndipo Ali pa malo ena Ku bwalo landege lamudzikoli lotchedwa goma komwe akudikila chiganizo chomwe apange abungweli chobwelela mmakwawo kapena kupitilila kukhala mudzikolo.