Eye of an Eagle Malawi

Eye of an Eagle Malawi 0 881 673 119

03/12/2023

Mphunzitsi wa Sliver Strikers wapasidwa card yofiila after k*tafunira fourth official.

Pakadalipano tilinaye ku ma stand
BB 1_ 1 Sliver

03/12/2023

Sliver equalises through Patrick Macheso
BB 1_1 Sliver

03/12/2023

Substitution
Sliver Strikers
IN
Stain Davie
Out
Mphatso Kamanga

Bullets.

In
Kondowe
Out
Phodo

03/12/2023

Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yapeza chigoli kuzera mwa Patrick Mwaunguru otchinga kumbuyo kwa ma Bankers atalekelera mpira omwe unabwera mu box.

Pakadalipano mapale ak*tsogoka ndi chigoli chimodzi kwachilowere.

03/12/2023

Pa Kamuzu stadium chigawo choyamba chatha opanda mphatso yachigoli kumbali zonse ziwiri.

Chigawo choyambachi anthu aonera masewero apamwamba poti matimu onse anasewera bwino.

Pakadalipano oyimba Zeze alim'bwalo kusangalasa anthu ndi nyimbo zake ndipo pakadalupano nyimbo yomwe akuyimba ndi yotchedwa kusangalala.

Anthu ochuluka ayima ndipo akusatizira nyimboyi.

#

03/12/2023

Masewero pa Kamuzu afika pa mwana wakana phala pomwe matimu onse ak*tha kupeza mwayi wazigoli ngakhale k*t sitinalandirebe mphatso yachigoli.
#

03/12/2023

Tilipa Kamuzu stadium pomwe tikhale tikukupatsirani tsatanetsatane wa masewero a mpira wa myendo pakati pa FCB Nyasa Big Bullets komaso Sliver Strikers.

Pakadalipano matimu onse awiri alowa mbwalo k*ti chigawo yoyamba chiyambike.

Asanalowe m'bwalo matimuwa oyimba otchedwa Zeze anasangalatsa anthu ndi mayimbidwe uku akudumpha mwamba tsitsi lake lili losapesa monga muja amachitira nthawi zonse..
#

29/11/2023

Unduna wa zaumoyo mogwilizana ndi bungwe la Unicef lero anakonza maphunziro kwa olemba nkhani komaso anthu omwe amafalitsa uthenga pa internet pa momwe angalembere nkhani komaso kufalisa uthenga okhuza malingaliro angwiro.

Maphunzirowa omwe anachitikira mu mzinda wa Blantyre anakhazikika pa Udindo wa olemba nkhani pochepetsa mchitidwe wozipha komaso kusalana pankhani za malingaliro angwiro mdziko muno .

Pa maphunziro amenewa zaziwikanso k*ti ndizolakwika kufotokoza njira komaso zipangizo zomwe munthu wozipha anagwiritsa ntchito ponena k*ti izi zimakolezera ena kuchitanso mchitidwewu pogwiritsa ntchito njirazi.

Poyankhula atatha maphunzirowa mkulu ona za matenda osapasilana komaso malingaliro angwiro mu unduna wa zaumoyo Dr Jonathan Chiwanda anati pakhala pali vuto lalikulu pakalembedwe ka nkhani za malingaliro angwiro komaso kuzipha kotero anachiona chanzeru kubweretsa maphunzirowa.

"Chomwe tikuyembekeza ndichak*ti tiona kusintha pakalembedwe ka nkhani zokhuza malingaliro angwiro ndipo pak*tero tithandiza kuchepetsa nkhani zozipha", anatero Dr Chiwanda.

Maphunzirowa anayambira ku Lilongwe ndipo akuyembekezelekaso kupita kuchigawo chakumpoto.

#

Mkulu wa Eye of an Eagle Malawi, Happy Makhalira yemwe ndi mtolankhani komaso presenter wa CFC radio wapangidwa nominate...
21/10/2023

Mkulu wa Eye of an Eagle Malawi, Happy Makhalira yemwe ndi mtolankhani komaso presenter wa CFC radio wapangidwa nominate mu ma award a Uzimu vibes pa category ya Best radio personality of the year.

Monga banja la Eye of an Eagle Malawi tikumufunira zabwino zonse pomwe akupikisana ndi ma presenter Ena okwana 5 pa mpikitsanowu.

Kotero tikukupemphani k*ti mu mumuvototele mkuluyi pogwiritsa ntchito link ili m'musimu.

Kumbukiran k*ti kuvota ndi daily mpaka pa 17 November Chaka chino.
https://l.facebook.com/l.php?u=https%3A%2F%2Fuzimuvibes.weebly.com%2F2023-uzimu-vibes-awards---vote-now.html%3Ffbclid%3DIwAR1LknV0pN2MHVPwLg67WDvpfndJW8BoKeChi7nC2KhNzfG0cTyQz_KCb7g&h=AT2QVHueyNKpWnC3LsxlAmN4_YbKJI0JDZk98k1RRT3rkAidDuvHeq5IG-ir4g3lsBWQwihztNl5pnHRI8JC9gJepU2t68AhWtSMyhQla5-AT4HXuaJgbdb1cAOl88jnPr0aIniLzQ

Ma lipoti osatsimikizika ak*ti katswiri odziwika bwino pankhani yamaimbidwe mdziko muno Athoti Manje wamwalira.Malipotiw...
08/10/2023

Ma lipoti osatsimikizika ak*ti katswiri odziwika bwino pankhani yamaimbidwe mdziko muno Athoti Manje wamwalira.

Malipotiwa ak*t katswiriyu dzulo amayimba ku sukulu ya ukachenjede ya Livingstonia ndipo atamaliza kuimba anayamba kusanva bwino zomwe zinamupangitsa k*ti apite akapume mu galimoto panja.

Kenako zikunveka k*ti anthu anamupeza atakomoka ndipo atamutengera ku chipatala anauzidwa k*ti katswiriyu anali atamwalira kale.

Pakadalipano akubanja sanayankhulepo pa malipoti akunvekawa.

Athoti Manje yemwe zinalake lenileni ndi Elias Missi amaziwika bwino ndi nyimbo monga Patuma, phone ya bebi, zilibwino ndi Zina zambiri ndipo watulutsatso nyimbo ina posachedwapa yomwe mutu wake ndi "Nchape".

#

07/10/2023

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wasankha a Simplex Chithyola omwe anali nduna ya zamalonda ndi mafakitale kukhala nduna ya zachuma ndipo omwe anali pa unduna wazachuma a Sosten Gwengwe tsopano ndi nduna ya zamalonda ndi Mafakitale.

Kusinthaku kukuza pomwe dziko lino likupitilira kukumana ndi mavuto azachuma kuphatikizapo kusowa kwa ndalama zakunja.

Malamulo adziko lino gawo 94(1) imapeleka mphanvu kwa mtsogoleri wa dziko kusankha nduna mu cabinet yake.

#

20/09/2023
Bungwe lomenyera ufulu wa atolankhani m'dziko muno MISA Malawi ladzudzula mchitidwe wankhaza omwe ophunzira ena a kusuku...
16/09/2023

Bungwe lomenyera ufulu wa atolankhani m'dziko muno MISA Malawi ladzudzula mchitidwe wankhaza omwe ophunzira ena a kusukulu ya ukachenjede ya Mzuni achitira mtolankhani wa Nation Publications Limited dzulo pomwe ophunzirawa amachita zionetsero zosakondwa ndi kukwera kwa school fees.

Malinga ndi chikalata chomwe bungweri latulutsa ndipo chasainilidwa ndi wa pampando wa bungweri a Golden Matonga zomwe anachita ophunzirawa ndikuphwanya ufulu wa olemba nkhani.

A Matonga ati atolankhani ali ndi ufulu wolemba komaso kujambula chilichonse chomwe ndichokhuza dziko lino.

Iwo atiso zomwe achita ophunzirawa ndizokhumudwitsa ponena k*ti amayenera kuchita zinthu mozindikira.

A Matonga apempha apolisi k*ti malamulo agwire ntchito kwa aliyense amene akukhuzidwa ndi zaupanduzi.

Pomwe amachita zionetsero zosakondwa ndi kukwera kwa school fees dzulo, ophunzirawa anamenya mtolankhani wa The Nation ndikumufufutisa zithunzi zomwe iye anajambula.

Malamulo akulu adziko lino pa section 36, amapeleka ufulu kwa olemba nkhani popanda kuopsezedwa.

Wolemba Happy Makhalira
#

Omenyera ufulu wa anthu a Bon Kalindo amangidwa lero mu nzinda wa Lilongwe  pomwe amakaonekera ku bwalo la milandu.A Kal...
15/09/2023

Omenyera ufulu wa anthu a Bon Kalindo amangidwa lero mu nzinda wa Lilongwe pomwe amakaonekera ku bwalo la milandu.

A Kalindo anali ku bwalo la milandu komwe amakaonekera pa mulandu umene anamangidwira sabata yatha pankhani yophwanya malamulo a belo yawo pa mulandu olumikiza magetsi mwachinyengo.

Iwowa pomwe amatuluka mu bwaloli mk*ti apolisi akuwadikilira panja ndipo pakadali pano sizikuziwika k*ti ndichifukwa chani apolisiwa amanga a Kalindo.

A #

Chipani Cha Democratic Progressive DPP chachotsa a Nicolas Dausi muchipanichi ati mkamba kosowa mwambo.Izi zili mukalata...
04/09/2023

Chipani Cha Democratic Progressive DPP chachotsa a Nicolas Dausi muchipanichi ati mkamba kosowa mwambo.

Izi zili mukalata yomwe chipanichi chatulutsa ndipo yasainilidwa ndi m'neneri wa chipanichi a Shadreck Namalomba.

Pakadalipano a Dausi ati sanalandire chikalata chochotsedwa muchipa Cha DPP ndipo iwo ati ayankhulapo akalandira kalatayi.

Kangapo konse a Dausi akhala akuonedwa ndi akulu akulu a chipani cha Malawi Congress ndipo iwo anali nawoso pa msonkhano omwe chipani cha MCP chinachitisa m'boma la Mwanza komwe Iwo anali m'modzi mwa anthu olemekezeka omwe anafika pansonkhanowo.

24/08/2023

Bungwe la anthu achi albino la APAM mogwirizana ndi bungwe la UNESCO lakonza mamphuziro a wolemba nkhani a mchigawo Cha kumwera pansi pa bungwe la MISA Malawi powasula mmene angalembere nkhani zokhuza anthu akhungu la chi albino.

Mtsogoleri wa bungweri Young Muhamba ndi wa chiwiri kwa wapampando wa bungwe la MISA Malawi Chisomo Ngulube ndi ena omwe afika pa maphunziro wa

09/08/2023

Anthu ku Robin's park kuyimba nyimbo zolemekeza Mulungu.

09/08/2023

Bishop Dr. A Gulupira ati mantha komaso nkhawa ndi Zina zomwe zimaonesa k*ti munthu sunamasulidwe.

Iwo ati munthu yemwe anamasulidwa ndi mwazi wa Yesu samakhala odandula Kapena wankhawa kamba koti amadziwa k*ti Yesu alinaye.

A Gulupira anena izi ku Robin's park komwe mpingo wa Cavalry International ukuchita msonkhano wake wa ukulu.

Mtumikiyi wati mfiti siyoopsa ngat munthu unamasulidwa ndi mphanvu za Mulungu.

Iwo apitiliza kunena k*ti ino sinthawi yomadana ndi mfiti koma kukonda mfitizi ponena k*ti mphanvu ya mfiti singapambàne mphanu za Mulungu.

"Kumawapasa moni afitiwo muona akuyankha monyasidwa. Inuyo osakwiya zimakhala k*ti mwa alepheresa plan yawo yokulozani utsiku umenewo", atero a Gulupira.
#

Mpingo wa Cavalry International  walowa mu tsiku la chiwiri  pa msonkhano wake wa ukulu omwe uk*tchulidwa k*ti Internati...
09/08/2023

Mpingo wa Cavalry International walowa mu tsiku la chiwiri pa msonkhano wake wa ukulu omwe uk*tchulidwa k*ti International Gathering of Kings and priests.

Msonkhanowu ukuchitikira ku Robin's park mu nzinda wa wa Blantyre.

Mkumanowu wabweretsa pa modzi atumiki a Mulungu kuchokera maiko akunja kwa dziko lino monga Bishop Dr. A Gulupira, Bishop Nwaka ndi ena.

Wolemba Happy Makhalira- Robin's park, Blantyre.
#

BANKERS ON TOPSilver strikers football club is now leading the log table in TNM super league  after beating Blue Eagles ...
06/08/2023

BANKERS ON TOP
Silver strikers football club is now leading the log table in TNM super league after beating Blue Eagles 2:1 at Bingu National Stadium.

The central Bankers got its first goal at 32 minutes through Chinsisi Maonga and Stain Dave doubled the lead at 72 minutes.

Ranken Mwale scored a consolation goal at 74 minutes.

As it stands now, goal difference is separating the Bankers and Chitipa United as both teams have 32 points.

As Silver was facing Blue Eagles at Bingu, Chitipa United was hammering Karonga United at Karonga stadium on Sunday.

Ramadan Ntafu scored the first goal at 10 minutes before China Chirwa doubles the lead at 75 minutes to make it 2:0 in favour of Chitipa United.

Karonga United was awarded a penalty but Josaya Duwa chose to miss.

#

06/08/2023

A polisi awiri a pansewu pa police station ya Thyolo avulala galimoto ina itawaomba pomwe Iwo amagwira ntchito yawo.

Galimoto yomwe imachokera ku Limbe inawomba apolisiwa pomwe amayesera kuiimisa ndipo pakadalipano sizikuziwika k*ti ndichifukwa chani oyendetsa galimotoyi anagunda apolisiwa.

Modzi mwa polisiwa, wavulala kwambiri ndipo watengeredwa kuchipatala Cha Queen Elizabeth pamene wina akulandira thandizo pa chipatala Cha Thyolo.

Akulu akulu aku polisiyi sanayankhulepo zambiri ndipo ati kafukufuku wokhuza ngoziyi alimkati.

Ma lipoti akuonesa k*ti oyendetsa galimoto yomwe inagunda apolisiwa Ali m'manja mwa a polisi.

#

Katswiri wotchinga pakati komaso katswiri osewera kusogolo ku timu ya mpira wa manja ya dziko lino the Malawi Queens ati...
06/08/2023

Katswiri wotchinga pakati komaso katswiri osewera kusogolo ku timu ya mpira wa manja ya dziko lino the Malawi Queens ati asiya kusewerela timuyi pofuna kupereka mwayi kwa atsungwana achisodzera.

Akatswiriwa Mwawi Kumwenda komaso Takondwa Lwazi anena izi pok*tha kwa masewero ozigulira malo a pa number 7 ku mpikitsano wa Netball world cup mdziko la South Africa.

Atafusidwa ndi olemba nkhani ngati tizamuonetso Mwawi Kumwenda ku Netball world cup inayo, iye anati mbali yake wachita ndipo pakufunika ena atumikire timu ya Malawi Queens.

"Nthawi yakwana tsopano k*ti ndipume k*tumikira national team, magazi atsopano akuyenera abwere nawo atumikire dziko lino", watero Kumwenda.

Naye Takondwa Lwazi wati ntchito wagwira ndipo akuyenera k*ti apume.
Iye wayamikira a Malawi mkamba kokhala mbali yake munthawi yomwe wakhala ak*tumikira timu ya Queens.

Kumpikitsano wa world cup wa Chaka chino akatswiriwa anaonetsa ukadaulo wao posewera mwa pamwamba ndipo anasankhidwapo kukhala akatswiri osewera bwino kapena k*ti player of the match.

Timu ya Malawi Queens yatsiliza pa number 7 itagonjetsa timu ya Tonga.

#

NDINTHAWI YOTI ANA APUMEUnduna wa zamaphuniziro wachenjeza sukulu k*ti zitsatire bwino calendar ya maphunziro achaka Cha...
31/07/2023

NDINTHAWI YOTI ANA APUME

Unduna wa zamaphuniziro wachenjeza sukulu k*ti zitsatire bwino calendar ya maphunziro achaka Cha 2023-2024 potsegulira sukuluzi.

Mneneri mu undunawu Mphatso Mkuonera wanena izi pomwe Sukulu Zina zikupelekabe maphunziro ndipo zina zikuyembekezeleka k*tsegulira mwansanga kwa ophunzira okhawo omwe azipereka ndalama yapadera ngakhale k*ti sukuluzi zili patchuti.

Amkuonera ati mchitidwewu ndi wa sankho ponena k*ti ophunzira omwe alibe ndalama sakuloredwa zomwe iwo ati ndi chiphinjo kwa anthu osaoka.

"Unduna umapereka nthawi k*ti mwana aphunzire komaso umapereka nthawi yoti mwana apume kotero kumupanikiza k*ti aphunzire Chaka chonse ndikulakwa", atero a Mkuonera.

Undunawu wati sukulu zomwe zikuchita mchitidwewu zilekeretu ndipo ngat satero malamulo agwira ntchito.

Undunawu wapitiliza kukumbutsa anthu mdziko muno k*ti telemu yamawa itseguliridwa pa 11 September osati pakadalipano.

#

Katswiri yemwe anayimba nyimbo yotchedwa mpanipani  Tremour wamwalira lero. Katswiriyu yemwe dzina lake leni leni ndi Vi...
30/07/2023

Katswiri yemwe anayimba nyimbo yotchedwa mpanipani Tremour wamwalira lero.

Katswiriyu yemwe dzina lake leni leni ndi Victor Mwangobola anachita ngozi lamulungu sabata yatha pomwe njinga yakabaza yomwe anakwera akuchokera ku studio inaombana ndi galimoto.

Tremour adavulara kwambiri mutu ndipo anatengeledwa ku chipatala Cha Kamuzu Central.

Malemuyu anaziwika kwambiri ndi nyimbo yotchedwa mpanipani yomwe imalimbikisa anthu k*ti asamataye nthawi ndikundaula mkamba kamavuto m'moyo uno, m'malo mwake azilimbikira kugwira ntchito.

Pakadalipano dongosolo la mwambo wa maliro silidaziwike.

Mzimu wa Tremour uwuse mu mtendere.

Wolemba: Happy Makhalira (Blantyre)
#

Moyo ndi wakanthawi kochepa tiyen tilape poti mawa sitikuziwa k*ti libwera ndizotan.

28/07/2023

Nduna ya za mziko a Ken Zikhale Ng'oma yati boma lachotsa tsiku lok*tha kwa chiphatso chaunzika.

Izi zik*tanthauza k*ti ziphatsozi sizimapanga expire monga mmene zinaliri mbuyomu.

Ndunayi yanena izi lachisanu kunyumba ya malamulo.

A Ng'oma atiso unduna wawo walamula a polisi k*ti asiye k*tolera ndalama yomwe amalandira k*ti alembe police report maka pomwe muthu akufuna kubwezeretsa chiphatso chake cha unzika chikasowa.

#

20/07/2023

BOLA NDILOWERE KWINA- De Jongh

Mphunzitsi wamkulu watimu ya Sliver strikers Peter De Jongh wati akulingalira zochoka mdziko muno ndikupita kukayamba kuphunzitsa mayiko ena ponena k*ti oyimbira mdziko muno akumuda.

Iye wanena izi lachinayi pak*tha pa masewero apakati pa timu ya Sliver strikers ndi Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo laza masewero la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.

Pa masewerowa mphunzitsi ochomera ku Netherlands yu anapatsidwa red card pamodzi ndiomuthandizira ake awiri komaso otchinga kumbuyo kwatimuyi.

De Jongh wati palibe chomwe iye analakwitsa pa masewerowa k*ti mpaka referee Mayamiko Kanjere apeleke red card.

Iye wati oyimbira akuda naye kukhosi popanda chifukwa chenicheni.

" Zalowa kukhumbana tsopano. Aliyese sanaone chomwe ine Ndalakwa, ndinamufusa match assessor komaso forth official chomwe ine ndalakwa onsewo ak*ti sanaone. Ndikuona k*ti ndikoyenera k*ti ndisanzike ndiyese kulowera kwina", watero De Jongh.

Pamasewerowa timu ya Wanderers yathetsa mbiri yosagonja ya Sliver strikers pomwe timuyi yagonjesa ma banker ndi chigoli chimodzi kwa duuu.

Katswiri otchinga pakati ku timu ya Wanderers Francis Mkonda ndiyemwe anamwesa chigoli chokhacho cha masewerowa ndipo pok*tha pa zonse anasankhidwa kukhala osewera yemwe anasewera bwino kuposa aliyense.

#

Timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino ya Flames yafika mundime ya ma semi-final ku mpikisano wa Cosafa itagonjesa  timu...
11/07/2023

Timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino ya Flames yafika mundime ya ma semi-final ku mpikisano wa Cosafa itagonjesa timu ya Comoros zigoli ziwiri kwa duu.

Timu ya Malawi inagolesa kuzera mwa Chawanangwa Kaonga komaso Patrick Mwaungulu.

Malawi yasewera masewero atatu ndipo sinagonjepo komaso sinagolesedwe chigoli chilichonse.

Malawi Energy Regulatory Authority MERA says will continue to engage various stakeholders on ESCOM`s application to adju...
11/07/2023

Malawi Energy Regulatory Authority MERA says will continue to engage various stakeholders on ESCOM`s application to adjust electricity base tariffs with 69.7% in the next four years.

MERA`s chief Executive officer Henry Kachaje made the remarks after the first public hearing meeting held on Monday in Blantyre.

The Chief Operations Manager for ESCOM Engineer Maxwell Kulimakwenda emphasized on the need for tariffs to be increased saying that this will improve their service delivery.

“Yes it is true that as ESCOM we proposed a 69.7 % tariffs adjustment. ESCOM as a single buyer we made this application on behalf of all players in the electricity industry so we combined cost for generators like EGENCO, independent power producers, MERA levies MAREP levy and we also look at ESCOM cost so putting together all in the next four years that is why we are proposing 69.7% tariff increase”, Engineer Kulimakwenda said.

On his part the executive director for Consumers Association of Malawi CAMA John Katipo said it is very unfortunate to hear ESCOM proposing 69.7% tariff adjustment for the next four years yet they have underperformed in the past four years.

Kapito has therefore proposed that tariff increase should not be more than 46 % saying considering the economic hardships Malawians are facing.

“when you read the document they have presented to MERA you find that they are just playing with minds of consumers they are not going to achieve anything”, said Kapito.

During the public hearing held in Blantyre it was revealed that Blantyre Water Board owes ESCOM money amounting to k 35 billion.

Reported by Happy Makhalira.
#

Katswiri oyimba nyimbo za uzimu Shamma Sitola yemwe amaziwika ndi dzina loti Shamma Vocals watsutsa mphekesera zomwe zik...
27/06/2023

Katswiri oyimba nyimbo za uzimu Shamma Sitola yemwe amaziwika ndi dzina loti Shamma Vocals watsutsa mphekesera zomwe zikuyenda m'masamba anchezo k*ti wasiya kuyimba.

Anthu ambiri anali odabwa dzulo ataona uthenga patsamba lake la Facebook onenak*ti sali oyenera kukhala oyimba wa uzimu ndipo pa ichi akhala asakuyimba.

Koma Eye of an Eagle Malawi itamutchaira thenifolo Shamma wati a Malawi asakhulupilire zimenezo ponena k*ti tsamba lake la Facebook linapangidwa hack.

Iye wati pakadalipano akupanga chilichonse chothekera k*ti abwezeletse tsambali.

Shamma vocals amaziwika ndi nyimbo monga no reverse, Kalondo londo, daily ndi Zina zambiri.

Wolemba Happy Makhalira_ Blantyre

25/06/2023

Mpungwe pungwe sukufuna kuchoka ku banja la chipan Cha Democratic Progressive DPP pomwe kwabukaso kugawanikana k*tsatira chileso chomwe chaimisa mkumano wa akulu akulu achipanichi NGC omwe umayenera kuchitika loweruka pa 24 June Chaka chino

Malinga ndika audio clip komwe kakuyenda mu masamba amchezo, ena mwa akulu akulu achipanichi ndiokwiya ndichiganizo cha a Billy Malata omwe atenga chilesochi.

Muka audio ka munthu wina yemwe sakuziwika anayimbira 4n munthu wina yemwe akuganizilidwa k*ti ndi a Malata kuwauza k*ti nkhondo ayiyambayi sayimaliza.

Iye wati zomwe apanga a Malata ndikuputa mavu pa chitsa.

" Suzimaliza wanva, wak*tumayo akupweteketsa. Waiyambayo ndi nkhondo", watero munthuyo.

Malipoti akuonesa k*ti a Billy Malata anakatenga chilesochi mkamba koti akulu akulu achipanichi anaitana anthu omwe sali mu NGC yachipanichi ndikusiya ma membala ena a NGC osayitanidwa ku msonkhano wa NGC omwe umayenera kuchitika loweruka ku Mangochi.

#

Unduna wa zamphunziro wati ndiozipereka kusula a Mphuntsitsi omwe ndi akadaulo pophunzitsa anthu a ulumali ngati njira i...
22/06/2023

Unduna wa zamphunziro wati ndiozipereka kusula a Mphuntsitsi omwe ndi akadaulo pophunzitsa anthu a ulumali ngati njira imodzi yoonetsetsa k*ti aliyese akulandira maphunziro apamwamba.

Mneneri mu undunawu Mphatso Mkuonera wati anthu okwana 150 omwe anamaliza maphunzirowa mu Mwezi wa March Chaka chino akhala ak*tumizidwa ku sukulu zosiyana siyana za pulayimale mdziko muno komwe akathandize kupititsa patsogolo maphunziro kwa ana omwe ali ndi ulumali.

Iwo ati pakadalipano anthu okwana 360 akuchita maphunziro pa sukulu zosula aphunzitsi awukadaulo pankhani zophunzitsa ana a ulumali za Montfort komaso Machinga.

"Ngati unduna tikuziwa bwino kufunika kwa maphunziro kwa munthu aliyese posatengera chilema ndipo pa ichi aphunzitsi omwe akusulidwawa athandiza kuchepesa mavuto omwe anthu olumala amakumana nawo pofuna kupeza maphunziro oyenera", atero a Mkuonera.

Mumalamulo akulu adziko lino amapereka ufulu wa maphunziro kwa aliyese mdziko muno.

Wolemba Happy Makhalira

#

22/06/2023

Mkulu wa bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo kuchi gawo cha kum'mwera a Raphael Humba alim'manja mwa apolisi ku Lilongwe.

A Humba akuganizilidwa k*ti anagwilitsa ntchito satifiketi ya fulomu 4 yoti siyawo kupezera ntchito.

#

20/06/2023

A polisi amanga nyamata wazaka 26 Innocent Kananji yemwe mu mwezi wa May anathandiza police ya Limbe ndindalama zokwana k100,000 k*ti zithandize kugwira ntchito yoika ma camera ku Limbe.

Kananji akuganizilidwa k*ti amasegula ma account a Facebook mu dzina la mkulu wa apolisi mayi Merlyne Yolamu pomabera anthu k*ti awalemba ntchito ku polisi.

Woganizilidwayo ak*ti anakwanisa kuwabera anthu ndalama pafupifupi k150,000 kuzera munjirayi.

Malinga ndichikalata chomwe apolisi atulutsa, Kananji akaonekera ku bwalo lamilandu posachedwa k*ti akayankhe mulandu wogwilitsa ntchito internet molakwika.

#

Nkhala kale pa nkhani zoyimba a Gides Chalamanda akulandila thandizo pachipatala cha Chiladzuru pomwe katswiri oyimbayu ...
15/06/2023

Nkhala kale pa nkhani zoyimba a Gides Chalamanda akulandila thandizo pachipatala cha Chiladzuru pomwe katswiri oyimbayu sakupeza bwino.

Manager wa a Gides Chalamanda Pemphero Mphande watsimikiza za izi polemba pasamba lake lamchezo la Facebook.

Mphande wati pomwe iye amafika kuchipatalako anawapeza a Gide atayamba kupezako bwino kuyelekeza ndim'mene katswiri oyimbayu analili asanayambe kukandira thandizo.

A Gide omwe alindi zaka zakubadwa zoposa makumi asanu ndi anayi 90+ , ndi modzi mwa oyimba omwe amakondedwa kwambiri m'dziko muno.

#

(Picture: Pemphero Mphande)

03/06/2023

Reverend Kyle Martin wati njira yokhayo yoonesa kugonja pa maso pa Mulungu ndikupepha k*ti Mulungu atsuke miyoyo a anthu.

Iwo anena izi pa bwalo lazamasewero la Kamuzu pomwe pakuchitikira mapemphero olapa.

Pakadalipano Reverend Dr Martin apempha anthu omwe afika pa bwalo la Kamuzu k*ti apite ku tsogolo akufuule kwa Mulungu kupenpha k*ti atsukidwe ndi mwazi wa Yesu.
Wolemba Happy Makhalira

Mwambo wa mapemphero omwe cholinga chake ndikumema a Malawi k*ti alape upitilira lero masanawa utayamba zulo pa bwalo la...
03/06/2023

Mwambo wa mapemphero omwe cholinga chake ndikumema a Malawi k*ti alape upitilira lero masanawa utayamba zulo pa bwalo la Kamudzu munzinda wa Blantyre.

Mapempherowa omwe ayamba zulo ndipo akuyembekezereka k*tha Lero anayitanitsa anthu ochuluka kuchokera Madera osiyana siyana m'chigawo chakumwera ndipo afika pachimponda chimera masanawa pomwe mlaliki ochokera m'dziko la America, Reverend Dr Kyle Lance Martin akhale akupitiliza kugawa uthenga wabwino wa Ambuye Yesu.

Kupatula kubweretsa pa modzi a khiristu osiyana siyana, mapempherowa abweletsaso pamodzi atumiki a Mulungu kuchokera mipingo yosiyana siyana.

Mwambowu ukuyembezeleka kuchitikaso ku Balaka, Lilongwe komaso Mzuzu.

Mapemphero olapa akuza k*tsatira vumbulutso lomwe Reverend Dr Kyle Lance Martin analandira kuzera ku maloto k*ti dziko lino likufunika kulapa ndikuyamba kuyenda muchiyero.

Wolemba Happy Makhalira
#

02/06/2023

Dr Kyle Martin ati siiwo amene anasankha k*t mapempherowa achitikire m'dziko muno.

Iwo ati Chaka chatha analota Mtsogoleri wadziko lino atatsogolera anthu m'dziko muno kulapa ndipo loto linapitira kunena k*ti dziko lino likufunika kulapa.

Iwo ati uthengawu sunali ophweka kuufotokoza I k*t dziko lino likufunika kulapa.

02/06/2023

Mlaliki ochokera mdziko la America Kyle Martin wakwera pa pasanja

02/06/2023

Bishop Mankhanamba apempha athu k*ti apempherere dziko lino k*ti anthu ayambe kuyankhula zabwino za dziko lino komaso atsogoleri ake.

Pakadalipano anthu agwirana manja ndipo akupemphera.

Wolemba Happy Makhalira

02/06/2023

Andrew Mankhanamba apempha anthu omwe abwera pano k*ti agwirane manja pofuna kupemphera mtima wansanje pakati pa anthu ponena k*t msanje ikulepheresa dziko lino kupita patsogolo.

Akamaliza Bishop Andrew Mankhanamba Reverend Dr Kyle Martin kuchokera m'dziko la America akwera pa sanja ndikugawa mawu a Mulungu komaso k*tsogolera anthu kulapa.
Wolemba Happy Makhalira

Address

Chimwankhunda
Blantyre

Telephone

+265881673119

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Eye of an Eagle Malawi posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Videos

Share



You may also like