Television Islam Malawi

Television Islam Malawi Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Television Islam Malawi, TV Channel, Raynor Avenue, Blantyre.
(4)

 As Malawi is going to celebrate 60 years of independence on 6th July 2024 the grouping calling itself concerned citizen...
26/06/2024



As Malawi is going to celebrate 60 years of independence on 6th July 2024 the grouping calling itself concerned citizens has said that they will be on the street mourning for problems they are facing.

Speaking in an interview with Television Islam Chairperson for concerned citizens Edward Kambanje, says that the grouping is planning a national wide demonstrations which they are calling national wide shutdown demonstrations schedules for 10th July 2024.

Kambanje further says this time around demos will be different as authorities will be celebrating 60 years of independence Malawians will be mourning problems that this country is facing.

(Reported by: Hameeda kananji, Blantyre; 26/06/2024)

!

26/06/2024



Chipatala cha Bwaila chikupitilira kulandila anthu ochuluka odwala nthenda ya kadzamkozo kapena kuti Fistula pamene anthu ena ochokera maiko oyandikana nawo ngati Mozambique akumapita kukalandila nthandizo.

Lucia Bendulo wa zaka 42 ochokera mdziko la Mozambique yemwe wapita kukalandila thandizo la nthendayo pa Chipatala cha Bwaila wati ali ndi chikhulupiliro kuti achira ku nthenda ya kadzamkozo poona mmene amzake omwe anali ndi nthendayi akuonekera.

Malingana ndi Dokotala oona za nthendayi Annette Chipungu wati pafupifupi 10 percent ya omwe amalandila thandizo la nthendayi amachokera ku dziko la Mozambique zomwe zikupeleka chithumzithumzi chokuti ku Mozambique nakonso kuli vuto la nthendayi ngati ku Malawi kuno.

Wolemba: Fareedah Muheya, Lilongwe.

25/06/2024



Bungwe lowona za mipikisano pamalonda la Competition and Fair Trading Commision CFTC lapempha anthu omwe amagwilitsa ntchito mafuta a Dark and Lovery moisture plus komanso Dark and Lovery Anti breakage omwe amapangidwa mdziko la South Africa kuti asiye kugwilitsa ntchito kamba koti muli tizilombo toyambitsa matenda apa khungu komanso tsitsi totchedwa bacteria.

Muchikalata chomwe watsindikiza wamkulu wa bungweli a Lloyds Vincent Nkhoma wati omwe amapanga mafutawa atsimikiza kuti mafutawa akhoza kuyambisa kuthothoka kwa tsitsi komanso matenda ena.

Bungweli lati kwa omwe amagulitsa katunduyi akuyenera kusiya kugulisa komanso kukabweza komwe anakawoda ndikubwezeledwa ndalama yawo.

Wolemba: Victor M'mana, Blantyre.

.

 Chipani cha People's Development Party-PDP chalengeza kuti chichititsa msonkhano wake waukulu pa 13 mpaka pa 14 Septemb...
25/06/2024



Chipani cha People's Development Party-PDP chalengeza kuti chichititsa msonkhano wake waukulu pa 13 mpaka pa 14 September chaka chino mu mzinda wa Blantyre.

Chipani cha PDP ndi chipani chomwe changokhazikitsidwa kumene ndipo mtsogoleri wake ndi Kondwani Nankhumwa.

Malingana ndi chikalata chomwe chasainidwa ndi yemwe akugwilizila udindo wa mlembi wamkulu wa chipanichi Rhodes Msonkho, ku msonkhano waukuluwu, ma membala achipani adzapasidwa mwayi odzapikisana pa mpando wina uliwonse omwe akufuna mu chipanichi.

Wolemba: Fareedah Muheya; Lilongwe

 .Khansala Esther Sagawa wa Dera la Chimutu ndi yemwe wasankhidwa kukhala mfumu ya mzinda wa Lilongwe atapeza ma voti 21...
25/06/2024

.

Khansala Esther Sagawa wa Dera la Chimutu ndi yemwe wasankhidwa kukhala mfumu ya mzinda wa Lilongwe atapeza ma voti 21 ndipo yemwe amapikisana naye Felix Tsokonombwe wa dera la biwi anapeza ma voti 9.

Pa mpando wa wachiwiri kwa mfumu ya mzindawu wapambana ndi Ruth Chingwalu wa Dera la Mtandire atapeza ma voti 16.

Mmau ake mfumu yatsopanoyi wati akagwira ntchito limodzi ndi ma khansala anzake ndi cholinga chofuna kukwanilisa masomphenya a khonsolo ya Lilongwe.

Wolemba: Fareedah Muheya, Lilongwe.

 .Kuvota tsopano kwayamba ku ma ofesi a Lilongwe City council.Amene akupikisana pa mpando wa mfumu ya mzinda wa Lilongwe...
25/06/2024

.

Kuvota tsopano kwayamba ku ma ofesi a Lilongwe City council.

Amene akupikisana pa mpando wa mfumu ya mzinda wa Lilongwe ndi a Esther Sakala komanso Felix Sokonombwe.

Pa mpando wa wachiwili kwa mfumu ya mzinda akupikisana ndi khansala Ruth Chingwalu, William Ngulube komanso Lynod Chaziya.

Anthu omwe afika kuzaponya voti alipo 30.

Wolemba: Fareedah Muheya, Lilongwe.

 .Chinachilichonse chili mchimake pamene anthu a mumzinda wa Lilongwe lero akuyembekezera kusankha mfumu ina ya mzindawu...
25/06/2024

.

Chinachilichonse chili mchimake pamene anthu a mumzinda wa Lilongwe lero akuyembekezera kusankha mfumu ina ya mzindawu.

Zisankhozi zikuchitikila ku ma ofesi a khonsoloyi ndipo aphungu komanso ma khansala a bomali afika kale.

Mlendo olemekezeka Nancy Tembo yemwe ndi nduna yoona maubale adziko lino ndi maiko ena akufika kumene.

Wolemba: Fareedah Muheya, Lilongwe.
.
.

 Magulu osiyanasiyana omenyera ufulu wa anthu akupitilirabe kudzudzula za kumangidwa kwa Bon Kalindo komanso Kamlepo Kal...
24/06/2024



Magulu osiyanasiyana omenyera ufulu wa anthu akupitilirabe kudzudzula za kumangidwa kwa Bon Kalindo komanso Kamlepo Kaluwa omwe anamangidwa sabata yatha.

Malingana ndi apolisi, awiriwa anamangidwa atapeleka maganizo awo mmasamba a mchezo pa nkhani ya ngozi ya Ndege yomwe inadzetsa imfa ya yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino malemu Dr. Saulos Chilima ndi ena asanu ndi atatu.

Malingana ndi Chikalata chomwe bungwe la Human Rights Defenders Coalition- HRDC, kukhala chete kwa mtsogoleri wadziko lino Dr. Lazarus Chakwera ndi kodabwitsa chifukwa zinthu ngati zomwezo anazidzudzulapo mu chaka cha 2019.

Kotero bungweli lalamula kuti chilungamo chioneke ndipo malamulo ena akuyenera aunikidwe.

Ena mwa mabungwe omwe adzudzula pa kumangidwaku ndi Center for Human Rights Rehabilitation-CHRR komanso gulu lomenyera ufulu wa anthu la Concerned Citizens.

(Wolemba: Fareedah Muheya, Lilongwe; 24/06/2024)

!

24/06/2024

24/06/2024

highlights

 .Achinyamata omwe achita mphumi pa mpikisano wa aqeeda  quiz competition awalangiza kuti  agwilitse ntchito maphunziro ...
23/06/2024

.

Achinyamata omwe achita mphumi pa mpikisano wa aqeeda quiz competition awalangiza kuti agwilitse ntchito maphunziro omwe aphunzira pa mpikisanowu ndicholinga chotukula chipembezo chawo.

Izi zanenedwa ndi Siraj Hussein yemwe ndi Ustaz amayendetsa mpikisanowu wa quiz.

Iye analakhula izi pa mwambo opeleka mphoto kwa anyamata ndi atsikana omwe achita phumi pa mpikisano omwe unachitika pa 8 komanso 9 June 2024.

Hussein anati achinyamata alingati mlantho omwe ungamawaolotsele anthu kuntchito zoipa kupita kuzabwino, koma izi zimatheka ngati achinyamata angakhale ndi chidwi chosakasaka maphunziro achipembezo.

Zina mwa mphoto zomwe ochita bwino alandila ndi ma t-shirt, ndalama ndi zina.

Wolemba: Hameeda Kananji, Lilongwe.

.

 Mwambo opereka mphoto kwa achinyamata omwe achita mphumi pa mpikisano wa aqeeda quiz competition omwe  anachititsa a bu...
23/06/2024



Mwambo opereka mphoto kwa achinyamata omwe achita mphumi pa mpikisano wa aqeeda quiz competition omwe anachititsa a bungwe la Muslim Youth Development Initiative MYDI mothandizidwa ndi a Rashie fashion uli mkati Ku Malawi College of Health Sciences mu mzinda wa Lilongwe.

Tikupatsilani zambili zamwambowu.

Wolemba: Hameeda Kananji, Lilongwe.

 Mkulu oyendetsa sukulu ya atsikana ya Maksab wapempha ophunzira pa sukuluyi amene akuyembekezereka kulemba mayeso a MSC...
22/06/2024



Mkulu oyendetsa sukulu ya atsikana ya Maksab wapempha ophunzira pa sukuluyi amene akuyembekezereka kulemba mayeso a MSCE kuti akadzisunge pamene akhale akupita ku tchuthi.

Poyankhula loweluka pa mwambo otsanzikana, Jack Matemba wati, nkofunika atsikanawa kuti akasunge mwambo omwe sukuluyi imawaphunzitsa.

Matemba anatinso ophunzirawa sakuyenera kukatengeka ndi anyamata ponena kuti kulemba mayeso a MSCE simapeto a maphunziro.

Iye wapemphanso ophunzirawa kuti pamene kwatsala masiku ochepa kuti alemba mayesowa akuyenera kukhala odekha komanso kuwelenga zomwe amaphunzira.

Mmodzi mwa ophunzira pa sukuluyi, Maryam Waliwali, wati iye ngati ophunzira akatsata miyambo yomwe amaphunzira pa sukuluyi.

Ena mwa omwe anabwera pa nkhani ya msangulutso pa mwambowu ndi monga Kazembe wa sukuluyi Aqeel Masinja, Abdul-Hakeem Muhamaad, Yusuf Bhamusi ndi ena.

Sukulu ya Maksab Girls Academy imapezeka ku Mpondas m'boma la Mangochi.

(Wolemba: Hameeda Kananji, Mangochi; 22/06/2024)

!

22/06/2024



Mpologalamu ya Pambalambanda lero pa 22 June, 2024 kuyambira 10:00 koloko m’mawa, tikambirana za kusankhidwa kwa a Michael Usi kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino ndi a Annabel Mtalimanja kukhala wapampando wa bungwe la MEC.

Tikhala ndi a Osman Kennedy (Katswiri waza malamulo) ndi a Humphreys Mvula (Woyankhulapo pa nkhani zosiyanasiyana).

Perekani ndemanga ndi mafunso poimba foni, SMS kapena WhatsApp ku 0999 345 786 kapenanso pa Facebook, Television Islam Malawi.


21/06/2024

_Madrassah

 Mtsogoleri wadziko lino wasakha a Michael Usi ngati Wachiwiri wawo.Kusakhidwa kwa a Usi kwasimikizidwa ndi kalata yotsi...
20/06/2024



Mtsogoleri wadziko lino wasakha a Michael Usi ngati Wachiwiri wawo.

Kusakhidwa kwa a Usi kwasimikizidwa ndi kalata yotsindikizidwa ndi Mlembi mu ofesi yamtsogoleri ndi nduna Colleen Zamba.

Kusakhidwa kwa a Usi kwabwera pambuyo pa imfa ya yemwe anali Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino malemu Dr Saulosi Chilima amene anafa pangozi yandege sabata yatha, ndipo a Usi alowa mmalo mwawo.


 Olemba nkhani alimbikitsidwa kuti adzifalitsa uthenga okhudza za nyengo moyenera.Izi zanenedwa ndi katswiri wa za nyeng...
20/06/2024



Olemba nkhani alimbikitsidwa kuti adzifalitsa uthenga okhudza za nyengo moyenera.

Izi zanenedwa ndi katswiri wa za nyengo ku nthambi yoona za nyengo ya Department of Climate change and meteorological services Alick Chipanthuwa pa maphunziro a masiku atatu omwe anthambiyi ikuchititsa kwa atolankhani olemba nkhani za nyengo.

Mmau ake Chipanthuwa wati olemba ankhani akuyenera kumafalitsa uthenga okhudza zanyengo mu chiyankhulo chokuti anthu omwe akufuna kuwafikila amvetsetse mosavuta mopanda kusintha matanthauzo a uthenga omwe apatsidwa.

Mmau ake wapampando wa bungwe la olemba ankhani za nyengo la Network of climate journalists, Deitrich Frederich wayamikira nthambiyi pochititsa maphunzirowa kwa olemba nkhaniwa ndipo wati ali ndi chikhulupiliro kuti maphunzirowa akatha olemba nkhani azikwanitsa kumvetsetsa komanso kulemba nkhani za nyengo molondola.

Maphunzirowa omwe ndi amasiku asanu akuthandiza ndi a world Bank pansi pa pulojekiti ya Malawi Resilience and Risk Management.

(Wolemba: Fareedah Muheya, Zomba; 20/06/2024)

!

 Bungwe loyendetsa chisakho la Malawi Electoral Commission MEC lalengeza kuti mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwer...
20/06/2024



Bungwe loyendetsa chisakho la Malawi Electoral Commission MEC lalengeza kuti mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera wasakha wapampando watsopano wabungweri kukhala Justice Annabel Mtalimanja pamodzi ndi makomishonala awiri amene ndi Rev Philip Kambulire komanso Dr Limbikani Kamlongera.

Mukalata imene wasindikiza Ofalitsa nkhani zabungweri Sangwani Mwafulirwa, kusakhidwa kwa atatuwa kwachitika motsatira gawo 75 lamalamulo adziko lino komanso gawo 4 lamalamulo abungwe loyendetsa chisakholi.

Kalatayi yatinso ganizo losakha wapampando watsopanoli pamodzi ndi makomishonala awiriwa ladza pambuyo pofika kumapeto nthawi yokhala mu ofesi ya yemwe anali wapampando wabungweri Dr Chifundo Kachale, komanso makomishonala Dr Antony John Makumbwa ndi Olivia Mchaju Liwewe pa 06 June chaka chino.

Amene asakhidwawa nthawi yawo yoyambira kugwira ntchito malinga ndi kalatayi ndipa 7 June chaka chino.

Wolemba: Hanis Ogrieve Ntapasha, Blantyre.
.
.

 Mwambo wotsegulira nzikiti wa Sonjera omwe uli m’mudzi wa Sonjera, uli nkati mdera la mfumu yaikulu Sitola m’boma la Ma...
19/06/2024



Mwambo wotsegulira nzikiti wa Sonjera omwe uli m’mudzi wa Sonjera, uli nkati mdera la mfumu yaikulu Sitola m’boma la Machinga,

Mzikitiwu wamangidwa ndi a Jibu Jauma a m’mudzi wa Sonjera, ndi ndalama zokwana R350, 000 zomwe ndi pafupifupi K41 m.

Ena mwa akuluakulu omwe ali nawo pa mwambowu ndi mfumu yaikulu Sitola, a gulupu a Sifa, Leonard, Chabwera ndi a Saiti, M***i Jafali a mderali, M***i Abdul Karim Kamwendo, a Shaibu Masasa ndi Professor Saidi Hassan Zambia.

Malinga ndi mfumu yaikulu Sitola, nzikitiwu udzipindulira anthu opitilira 1,000 ochokera m’mudzi wa Sonjera ndi midzi ina yoyandikira yomwe anthu ake amapita ku mzikiti wakutali kuti akapemphere.



19/06/2024



National Registration Bureau says they are wiping out the registration exercise of citizens that have not owned their national identity cards in all districts in a phase that will run up to August 2024.

In a statement signed by principal Secretary of NRB, Mark Sambo has emphasized his concern following the video that has been circulating on social media claiming that citizens are not getting enough help when issuing national IDs due to shortage of people who exercise national registration.

Sambo has further highlighted that their aim is to make sure that all eligible citizens who missed previous national registration, including those who just turned 16 and those needing replacements for national IDs have been reached in this phase.

(Reported by: Victor M'mana, Blantyre; 19/06/2024)

!

 Maphunziro a masiku atatu a olemba nkhani za nyengo ayamba mu mzinda wa Zomba.Malingana ndi katswiri wa zanyengo kuchok...
19/06/2024



Maphunziro a masiku atatu a olemba nkhani za nyengo ayamba mu mzinda wa Zomba.

Malingana ndi katswiri wa zanyengo kuchokera ku nthambi yoona za nyengo ya Department of Climate change and meteological services Brenda Mdzagada, maphunzirowa kwambiri cholinga chake ndi kufuna kuwaphunzitsa olemba nkhaniwa mmene angalembele nkhani zanyengo kuti anthu amvetsetse komanso kuwauza matanthauzo a mau ena omwe nthambiyi imagwilitsa ntchito.

Wapampando wa bungweri Deitrich Frederich wapempha olemba nkhaniwa kuti aike chidwi pa maphunziro awo.

(Wolemba: Fareedah Muheya, Zomba; 19/06/2024)

!

18/06/2024



Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wati sakakhala nawo pa mwambo olumbilitsa mtsogoleri watsopano wa dziko la South Africa mmalo mwake atuma a Nancy tembo yemwe ndi nduna yoona zamaubale adziko lino ndi maiko ena.

Mneneri wa boma Moses Kunkuyu wanena izi pomwe anaitanitsa mkumano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe.

Mwazina Kunkuyu wati boma pamodzi ndi mtsogoleri wa dziko lino ati akhazikitsa kafukufuku wapadera kuti athandizire kufotokozela mtundu wa amalawi kuti chinachitika ndichani kuti ndege igwe mu nkhalango ya Chikangawa.

A Kunkuyu adawonjezerapo kuti mtsogoleri wa dziko lino akuthokoza azipembezo komanso atolankhani ndi nyumba zowulutsa mawu chifukwa chowatumikila amalawi pamene iwo amafuna kuziwa zokhudza ngoziyi.

(Wolemba: Victor M'mana, Blantyre; 18/06/2024)

!

 Nthambi yowona za masewero mdziko muno ya Malawi National Council of Sports yalengeza kuti tsopano masewero atha kupiti...
18/06/2024



Nthambi yowona za masewero mdziko muno ya Malawi National Council of Sports yalengeza kuti tsopano masewero atha kupitilira.

Bungweli linaimitsa masewerowa sabata latha kutsatira infa ya wachwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino malemu Dr. Saulos Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu.

Malingana ndi chikalata chomwe wasainila ndi nkulu wa bungweli Henry Kamata, ochita masewero akuyenela adzipeleka ulemu kwa malemuwa asanayambe masewelo.

(Wolemba: Victor M'mana, Blantyre; 18/06/2024)

!

 Zomba District Council environmental health officer, Penjani Chunda has advised Malawians to join hands in ensuring the...
17/06/2024



Zomba District Council environmental health officer, Penjani Chunda has advised Malawians to join hands in ensuring there is a good fight against climate change shocks thereby promoting a health population.

Chunda has made the sentiment after Kenya's former prime minister Railla Odinga's remarks calling for concerterd efforts among African countries in fighting climate change challenges.

He has further said Malawi has potential to overcome climate change effects if the citizenry join hands in coming together to enforce various initiatives and strategies implemented by the government to ensure there is no further prevalence of climate change induced diseases likely to affect the growth and development of the country.

(Reported by: Hanis Ogrieve Ntapasha, Zomba; 17/06/2024)

!

 Analysts say President Lazarus Chakwera faces a formidable challenge in appointing a new vice president to fill the voi...
17/06/2024



Analysts say President Lazarus Chakwera faces a formidable challenge in appointing a new vice president to fill the void left by the late Vice President Saulos Chilima although the right candidate for the position is Michael Usi.

The position of Malawi's vice president has fallen vacant following the death of Chilima who died in a plane crash and is expected to be laid to rest today in his home village Nsipe in Ntcheu.

According to section 84 and 88 of the Constitution as read with section 45 of the General Interpretation Act, President Lazarus Chakwera is required to appoint a replacement of the office of the Vice President within 7 days after the death of the Vice President.

Meanwhile, the Malawi Law society has said in computing the 7-day period from the date of death to exclude any Sunday or Public Holiday, Chakwera is expected to have appointed a person to replace Chilima in the constitutional office of a Vice President by and not later than 19th June 2024.

Commenting on the matter, social and political analyst Joe Mayere said Chakwera's decision will have a profound impact on his political legacy in relation to the agreement he had with his late vice president but the right person to be on the position is Michael Usi as he was the vice president to the late Chilima at the UTM party.

In an interview with Joe Mayere says choosing Abida Mia as the name has also popped up, would be a good idea as she has always been loyal to the president but as things are right now the best candidate is Michael Usi although both Mia and Usi would hold the position very well hence has insisted that the president has a tough decision to make.

Mayere further said the president has a tough decision to make in as far as appointing the new VP is concerned and that decision will either make or break his political legacy and also the person has to measure up to the high standards set by Chilima as he was a man of exceptional abilities making the president’s decision more challenging.

(Reported by: Tagamchira Meeklem Chiperesa, Blantyre 17/06/2024)

!

 Mapemphero a Eid pa Uper stadium atha tsopano.Pakadali pano anthu akubalalika kuthamangira mmalo osiyanasiyana komwe ak...
17/06/2024



Mapemphero a Eid pa Uper stadium atha tsopano.

Pakadali pano anthu akubalalika kuthamangira mmalo osiyanasiyana komwe akufuna kukapereka nsembe zozinga zinyama zomwe azikomzekeretsa nazo.

(Wolemba: Amirie Hassanih, Blantyre; 17/06/2024)

!

 Pamene mapemphero akupitilira pa uper stadium mu mzinda wa Blantyre Swalah ya Eid yatsogoleledwa ndi Grand M***i Sheikh...
17/06/2024



Pamene mapemphero akupitilira pa uper stadium mu mzinda wa Blantyre Swalah ya Eid yatsogoleledwa ndi Grand M***i Sheikh Muhammad Uthman.

Pakadalipano Khutubah ilimkati ndipo akuwerenga ndi Sheikh Muhammad Silika ochokera ku Blantyre Islamic Mission(BIM).

(Wolemba: Amirie Hassanih, Blantyre; 17/06/2024)

!

 Swalah ya Eid ikufuna iyime ndipo omwe atsogolele ndi Grand M***i Sheikh Muhammad Uthman.(Wolemba: Amirie Hassanih, Bla...
17/06/2024



Swalah ya Eid ikufuna iyime ndipo omwe atsogolele ndi Grand M***i Sheikh Muhammad Uthman.

(Wolemba: Amirie Hassanih, Blantyre; 17/06/2024)

!

 Mapemphero a Eid Al-adhuha alimkati pa bwalo la masewero la uper stadium mu mzinda wa Blantyre.Pakadalipano ulaliki uku...
17/06/2024



Mapemphero a Eid Al-adhuha alimkati pa bwalo la masewero la uper stadium mu mzinda wa Blantyre.

Pakadalipano ulaliki ukuyambika ndipo omwe akupeleka ulaliki ndi Sheikh Muhammad Silika kuchokera ku Blantyre Islamic Mission.

Mwa ena omwe abwera pa malopa ndi mlembi wamkulu wa Muslim Association of Malawi (MAM), Alhajj Dr. Twaibu Lawe komanso Grand M***i wadziko lino Sheikh Muhammad Uthman.

(Wolemba: Amirie Hassanih, Blantyre; 17/06/2024)

!

16/06/2024



Oyimira bungwe la United Nations, mlembi wa bungweli Rabecca Addah Donto wati bungweli ndilokhudzika ndi imfa ya Chilima.

Iye wati SKC anali munthu wamasophenya yemwe amagwira ntchito modzipereka nthawi zonse.

Donto wati ngati dziko, lataya mtsogoleri yemwe amathandiza kwambiri pachitukuko chadziko.

(Wolemba: Fareedah Muheya, Lilongwe; 16/06/2024)

!

Address

Raynor Avenue
Blantyre

Telephone

+265999345786

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Television Islam Malawi posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Videos

Share

Category