The Giraffe Malawi Online News

The Giraffe Malawi Online News Get the latest Local and International news updates. News concerning Politics, sports, Health etc
(1)

 Wachiwiri kwa mtosgoleri wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) wakale wa chigawo chakumwera, a Kondwani Nan...
11/12/2023



Wachiwiri kwa mtosgoleri wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) wakale wa chigawo chakumwera, a Kondwani Nankhumwa yemwenso ndi mtsogoleri otsutsa boma kunyumba ya malamulo ayankhula mtundu wa a Malawi lero Lolemba pa 10 December, 2023.

Izi zikutsatira chipwirikiti chomwe chabuka m'chipani cha DPP pomwe a Nankhumwa achotsedwa pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri kuchigawo chakumwera ndikuwaika pa udindo wa mlangizi wa mtsogoleri wa chipanichi.

Mwa ena omwe achotsedwa m'maudindo awo ndi mlembi wamkulu wachipanichi ndi a Grezelder Jeffrey komanso a Cecilia Chazama.

Wolemba: Lumbani Kazeze

 Chipwirikiti chikupitilira mchipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive Party (DPP)pomwe mtsogoleri wa chipanichi...
10/12/2023



Chipwirikiti chikupitilira mchipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive Party (DPP)pomwe mtsogoleri wa chipanichi a Peter Mutharika, wachotsa a Kondwani Nankhumwa pampando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi kuchigawo cha kumwera komanso a Cecilia Chazama pamipando wa mtsogoleri wa amayi mchipanichi.

Mkalata yomwe wasindikiza ndi mtsogoleri wa chipanichi a Mutharika, a Nankhumwa ndi a Chazama akhala alangizi a mtsogoleri wa chipanichi pomwe maudindo awo atengedwa ndi a George Chaponda ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi ku chigawo chakumwera ndipo a Mary Navitcha ngati mtsogoleri wa amayi.

Izi zikudza patangotha masiku awiri a Mutharika atachotsanso a Grezelder Jeffrey pampando wa mlembi wamkulu wachipanichi zomwe a Jeffrey sanagwirizane nazo ndipo atenga chiletso kuti ganizoli lisagwire ntchito.

Wolemba: Lumbani Kazeze

 Bungwe lalikulu loyendetsa mpira la Football Association of  Malawi (FAM) layimitsa kaye ganizo lake loletsa timu ya Mi...
08/12/2023



Bungwe lalikulu loyendetsa mpira la Football Association of Malawi (FAM) layimitsa kaye ganizo lake loletsa timu ya Mightu Mukuru Wanderers kusewera mu mipikisano yomwe limakonza bungweri pomwe lapereka masewero a mu Castel Challenge Cup ku timuyi.

Manona akuyembekezeka kudzasewera ndi Moyale Barracks pa bwalo la masewero la Kamuzu Lamulungu pa 10 December, 2023.

Mwa masewero ena, loweruka pa 9 December, 2023, FCB Nyasa Big Bullets ikumana ndi akatsiwiri ododa chikopa amu m'mzinda wa Lilongwe a Civil Service United pa bwalo la masewero Kamuzu pomwe Chitipa United ikhale ikugwebana ndi Bangwe All Stars pabwalo la masewero la Karonga mundime ya matimu khumi asanu ndi imodzi (Round of 16).

Zpnse zili motere:

Wolemba- Lumbani Kazeze

 Chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) chauza mlembi wamkulu wachipanichi a Grelzeder Jeffrey kuti awulule komw...
08/12/2023



Chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) chauza mlembi wamkulu wachipanichi a Grelzeder Jeffrey kuti awulule komwe zinachokera ndalama zomwe anachititsira msonkhano wa komiti yaikulu ya chipanichi pa 7 December, 2023 ku Golden Peacock mu mzinda wa Lilongwe.

Mkalata yomwe wasindikiza ndi wamkulu woyang'anira nkhani za malamulo mchipanichi a Charles Mhango, a Jeffrey akuyenera kupereka tsatanetsatane wa kuchuluka kwa ndalama komanso mayina a anthu omwe anathandiza popereka ndalamazi monga mwa gawo 27 ndime ya 2, 5 ndi 6 ya malamulo oyendetsera zipani mudziko muno(Political Parties Act 2018).

Mwazina, a Jeffrey akuyeneranso kutumiza ndalama zonse ku thumba la chipanichi kamba koti ndalama zomwe zinatchulidwazo akuti sizinafike kuthumbali.

Koma anthu ena otsatira ndale akuganiza kuti anthu mchipanichi akusungirana kampeni kumphasa kamba koti zomwe zalamulidwazi, sizinayambe zachitikapo mchipanichi ngakhale kuti malamulo oyendetsera zipani anali alipo.

Wolemba- Lumbani Kazeze

08/12/2023



Bungwe logulitsa magetsi mudziko muno la Electricity Supply Cooperation of Malawi (Escom)layimitsa pa ntchito mlembi wamkulu wa bungwe la ogwira ntchito ku bungweli la Escom Staff Union (ESU)a William Mnyamula kamba kololeza kugwiritsa ntchito zipangizo za bungweli paziwonetsero zomwe ogwira ntchitowa anachita pa 7 December, 2023.

Mkalata yomwe wasindikiza ndi wamkulu woyendetsa bungwe la Escom a Kamkwamba Kumwenda, iwo ati a Mnyamula analekelera pantchito yawo pomwe ogwira ntchitowa anagwiritsa ntchito magalimoto komanso katundu wina wabungweri paziwonetsero zawo popanda chilolezo.

Mwazina mkalatayi a Kumwenda ati kuyimitsidwa pantchito kwa a Mnyamula ndikoyenera kamba koti ndimbali imodzi yolimbikitsa kutsatira malamulo komanso kagwiridwe bwino ka ntchito ku bungweri.

Wolemba: Lumbani Kazeze

Kanema- Citizen journalism

06/12/2023

Anti corruption Bureau (ACB) has arrested three Small holders farmer fertilizer revolving fund of Malawi (SFFRFM) staff members and one guard for allegedly being involved in corruption practice over Affordable Inputs Programs (AIP) at Benga Depot in Nkhotakota.

Through the press statement released today signed by ACB principal public relations officer, Egrita Ndala says the suspects are two salesclerk, Maria Chilinda and Gift Mkanda, the Porter, Lovemore Kandu and the Guard, Wilson Masanjala.

Meanwhile, these four are in police custody awaiting to be taken to court to answer the charges.

ACB received the complaint on 16th of November, 2023 alleging SFFRFM salesclerks demanding some extra money from beneficiaries in order for beneficiaries to buy the inputs.

Reported by Evans Gondwe.

Timu ya Silver Strikers ikuyenera kudzapambana ndi zigoli zoposa zisanu ndi zitatu Lamulungu likudzali pa Kamuzu Stadium...
29/11/2023

Timu ya Silver Strikers ikuyenera kudzapambana ndi zigoli zoposa zisanu ndi zitatu Lamulungu likudzali pa Kamuzu Stadium pomwe idzakumane ndi FCB Nyasa Big Bullets.

Izi zikutsatira kupambana kwa Bullets pamwamba pa Karonga United ndi chigoli chimodzi chomwe anamwetsa ndi Patrick Mwaungulu pa mphindi zisanu ndi ziwiri kuti timuyi ifike pa mulingo wa mapoint 59, atatu pamwamba pa mabankers.

Zateremu, Manoma ayiwale zotenga ukatswiriwu kamba koti amadalira chipambano cha Karonga United kuti tsogolo lokhutchumula chikhochi lichuluke.

Kuphedi kwa mundandanda wa matimu kuli mkomkoke pomwe matimu a Ekwendeni, MAFCO, Civil Service United komanso Moyale Barracks alipakalikiliki kudzimeneyera nkhondo okha kuti atsale m'mpikisanowu.

Masewero amu Tnm Super League 2023 akutha Lamulungu pa 2 December, 2023.

Wolemba: Lumbani Kazeze

FCB Nyasa big bullets yakhala timu yoyamba kudzigulira malo mu ndimwe yotsiriza ya Airtel Top 8 Zamadolo 2023 itagonjets...
26/11/2023

FCB Nyasa big bullets yakhala timu yoyamba kudzigulira malo mu ndimwe yotsiriza ya Airtel Top 8 Zamadolo 2023 itagonjetsa Blue Eagles pabwalo la masewero la Bingu mmzinda wa Lilongwe.

Zigoli za Hassan Kajoke, Lanjesi Nkhoma ndi Ephraim Kondowe zinali zokwanira kuletsa timu ya asirikali aku area 30 ku Lilongwe kuti ifikenso mundimo yotsirizayi.

Christopher Gototo komanso Richard Rabson anamwetsa zigoli za Blue Eagles mundimwe yachiwiri zomwe sizinasinthe chigamulo pabwaloli.

Blue Eagles inakumananso ndi Bullets m'mpikisanowu mundime yotsiriza muchaka cha 2018 pomwe asirikaliwa anatenga ukatsiwiri ndi chigoli chimodzi kudzera pa penate m'mphindi zowonjezera.

Pamasewerowa, Patrick Mwawungulu wasankhidwa kukhala wosewera wapamwamba pomwe Blessings Mpokera anaonetsedwa chibaluwa chofiira kutsatira pa mphindi 92.

Wolemba- Lumbani Kazeze

14/10/2023

Moto watentha mbali imodzi ya chipatala cha Rumphi Central masana alero.

Malingana ndi mmodzi yemwe anathandizira kuzimitsa motowu, a Owen Chipofya, iwo ati motowu unayambira kumbali yosungira mankhwala.

A Chipofya ati khwimbi la anthu lomwe linakhamukira pamalowa linakwanitsa kuthana ndi motowu pogwiritsa ntchito zidebe komanso ma pipe othilirira maluwa kamba koti panthawiyi, nthambi yothana ndi ngozi zamoto inali isanafike.

Pakadali pano kuchuluka kwa katundu yemwe waonongeka sikunadziwikebe.

Wolemba: Lumbani Kazeze

Zithunzi: Owen Chipofya

 Silver Strikers have tasted their first defeat in the 2023 TNM Super League following a 1-0 loss at the hands of Mighty...
20/07/2023



Silver Strikers have tasted their first defeat in the 2023 TNM Super League following a 1-0 loss at the hands of Mighty Mukuru Wanderers.

The match which took place at Kamuzu Stadium in Blantyre, on Thursday afternoon was rocked by controversy as the bankers walked away with a send off involving the defender, Nickson Mwase in the 92nd minute of the match.

Silver's coach, De Jong, his assistant, Peter Mgangira and goal keeper trainer, Padambo were also washed with matching orders which let them watch the remainder of the match behind the fence.

At the end of the match, Francis Mkonda was named man of the match after his great performance.

Sliver strikers remain at 25 points which leaves them second in the log table, a point short of Bullets who are at 26 points.

Bankers face Extreme FC on Wednesday, 26th July, 2023 at Civo stadium in Lilongwe while Wanderers welcome Blue Eagles at Kamuzu Stadium on Sunday, 23rd July, 2023.

Report by Lumbani Kazeze-Blantyre

Photo: Mighty Mukuru Wanderers & TNM

19/07/2023

Get the best news with the Giraffe Malawi Online News. Objectivity, truth and verification are our core values.

 Malawi prolific forward, Chawanangwa Kaonga,  has been voted player of the Tournament for the just ended Hollywood Bets...
16/07/2023



Malawi prolific forward, Chawanangwa Kaonga, has been voted player of the Tournament for the just ended Hollywood Bets COSAFA Cup 2023 edition.

Kaonga was also voted man of the match twice against Seychelles and South Africa on Friday and today respectively after his sensetional football display in the tournament.

Flames is the only team that has produced more men of the matches than any other team such as Alick Lungu,Patrick Mwaungulu and Chimwemwe Idana were awarded men of the matches against Zambia, Comoros and Lesotho respectively.

Report by Lumbani Kazeze-Blantyre

Picture: Supersport

16/07/2023



Zambia yakhalanso akatswiri a COSAFA kachiwiri motsata itapambana pamwamba pa Lesotho ndi chigoli chimodzi kwa chilowere.

Chigoli chomwe chinabwera pa mphindi 78 kudzera mwa Wisdom Libamba chinali chokwanira kuteteza ukatswiriwu.

Lesotho inapanikiza koma Zambia inabwera mosinthika kamba koti imasewera mpira wothamanga.

Wolemba: Lumbani Kazeze-Blantyre

  An out going student of Malawi University of Science and Technology, identified as Charity Iman passed on late yesterd...
16/07/2023



An out going student of Malawi University of Science and Technology, identified as Charity Iman passed on late yesterday 15 July 2023 at Queen Elizabeth Central Hospital.

Miss Catherine died after fighting cancer for sometime, and her burial took place earlier today in the afternoon at Lunzu.

The deceased, was an intern working with Malawi National Council of sports under the department of sports Development at their head office, Blantyre.

May her soul rest in eternal peace.

Reported by Brenda Pensulo- Blantyre

 Malawi have finished fourth in the Hollywood Bets COSAFA Cup 2023 following a 5-3 loss to the hosts, South Africa on po...
16/07/2023



Malawi have finished fourth in the Hollywood Bets COSAFA Cup 2023 following a 5-3 loss to the hosts, South Africa on post-match penalties despite their glamoring display.

Jacama Kumwembe missed the fourth penalty after he was denied by woodwork and failed to level the scores to grant the third place to the Bafana-bafana.

Meanwhile, Chawanangwa Kaonga was named man of the match for a second time.

While back in the TNM super league, big teams continue to lose points as the battle stiffens.

Report by Lumbani Kazeze-Blantyre

16/07/2023



Full-time 90+2'

South Africa 0-0 Malawi

The match goes into post match penalty shootouts.

16/07/2023



South Africa 0-0 Malawi

It's halftime in a 50-50 with all teams registering more two shots on target.

What's your prediction?

16/07/2023



Lero masewero a mu TNM super league aliponso anayi ndipo mkhoza kuonera potsatira ma linki omwe Ali munsiwa.

1. Bangwe All Stars v Extreme FC - https://www.fifa.com/fifaplus/en/live/event/2RpJaOKpUHBZ3a9X8HQkKibXcQD

2. Kamuzu Barracks v MAFCO FC - https://www.fifa.com/fifaplus/en/live/event/2RpJdlS1i1JrfIgs0OSAyivsbks

3. Blue Eagles v Karonga United - https://www.fifa.com/fifaplus/en/live/event/2RpJjZm6HJ4IQG4DttuOD6vVNgM

4. Ekwendeni Hammers v Red Lions - https://www.fifa.com/fifaplus/en/live/event/2RpJsboZDXbWejsnxs9WoIDo2eR

 Tnm Super League yabweleranso kumathero a sabata yino pomwe lero Loweruka kuli masewero atatu omwe bungwe loyendetsa ch...
15/07/2023



Tnm Super League yabweleranso kumathero a sabata yino pomwe lero Loweruka kuli masewero atatu omwe bungwe loyendetsa chikhochuli la SULOM layika.

Chithunzi: SULOM

14/07/2023


Breaking News
Tough luck for the Flames as they are eliminated from the Hollywood Bets COSAFA Cup 2023 on penalty shootouts.

14/07/2023


Halftime
Malawi 1-1 Lesotho

Both teams are playing a fast and entertaining game.

 EAGLES YAIMITSA NTCHITO KUWALIAkuluakulu a timu ya Blues Eagles ayimitsa ntchito wosewera watimuyi Schumacher Kuwali ka...
14/07/2023



EAGLES YAIMITSA NTCHITO KUWALI

Akuluakulu a timu ya Blues Eagles ayimitsa ntchito wosewera watimuyi Schumacher Kuwali kamba kakhalidwe la oweserayu.

Kudzera mu kalata yomwe timu ya apolisiyi yatulutsa, yomwe wasindikiza ndi wapampando wa timuyi, a Alex Simenti, akuluakuluwa ati Kuwali sanawonetse khalidwe labwino kwa osewera anzake komanso kwa akaluakuluwa.

Malinga ndi kalayayi, wosewerayu sakuyenera kutenga nawo gawo muzochitikachitika za timuyi kufikira adzadziwitsidwe ndi akuluakulu a timuyi kuti chibalo chake chatha.

Wolemba: Lumbani Kazeze-Blantyre

 Mphunzitsi wa timu ya Flames, Patrick Mabedi, wakhulupilira osewera onse omwe anasewera masewero a Comoros kuti ayambe ...
14/07/2023



Mphunzitsi wa timu ya Flames, Patrick Mabedi, wakhulupilira osewera onse omwe anasewera masewero a Comoros kuti ayambe masewero a lero omwe akumenya ndi Lesotho pa bwalo la masewero la King Zwelithini, m'mzinda wa Durban ku South Africa.

Masewerowa ayamba 3 kololo nthawi ya ku Malawi ndipo mndandanda wa osewera onse uli motere;

Brighton Munthali (GK), Stanley Sanudi (C), Denis Chembezi, Lloyd Aaron, Nickson Mwase, Alick Lungu, Chimwemwe Idana, Patrick Mwaungulu, Lanjesi Nkhoma, Chawanangwa Kaonga, Christopher Kumwembe.

Wolemba: Lumbani Kazeze-Blantyre

Chithunzi; Football Association of Malawi

 DODMA ICHEDWA KUSAMUTSA OKHUDZIDWA NDI NAMONDWE WA FREDDYBungwe lothana ndi ngozi zogwa mwadzidzi m'dziko muno la Depar...
14/07/2023



DODMA ICHEDWA KUSAMUTSA OKHUDZIDWA NDI NAMONDWE WA FREDDY

Bungwe lothana ndi ngozi zogwa mwadzidzi m'dziko muno la Department of Disaster Management Affairs (Dodma) lati litenga nthawi kuti lisamutse anthu omwe anakhudzidwa ndi ngozi ya namondwe wa Freddy kupita m'madera ena.

Wachiwiri kwa mkulu wokonzekeredwe ka ngozi ku bungweli, a Fredson Chikuse atsimikiza izi ku ma ofesi aboma ku Lilongwe lero lachisanu pomwe amalandira katundu kuchokera ku bungwe la Mighty Tambala Graduates, wothandizira anthu omwe anakhudzidwa ndi ngozi ya namondwe wa Freddy mchigawo chakumwera.

"Pakadali pano tikukambirana kaye ndi unduna wa mabona ang'onoang'ono, mafumu, mabwanamkubwa komanso nthambi yoyang'anira za malo kuti papezeke ndondomeko yoyenera kuti anthuwa apatsidwire malo ena. Chomwe tikufuna ndichoti anthuwa asadzalandidwe malowa adzakhale awoawo kamba koti madera ambiri omwe anthuwa adakhudzidwa ndi ngoziyi, sangabwelerekonso, " anatero a Chikuse.

A Chikuse anayamkiranso bungwe la Mighty Tambala Graduates kamba kakudzipereka pofuna kuthandiza anthu okhudzidwa ndi ngozi ya namondwe wa Freddy. Iwo anapemphanso nzika kuti zitengepo gawo kuti dziko lisamangodalira mabungwe akunja.

Koma m'modzi wa membala a bungweli a professor David Kamchacha ati anachiona chanzeru kuthandizapo pa ngoziyi kamba koti mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera, anapempha nzika kudzera mu ndondomeko ya "Operation tigwirane manja" pofuna kufikira nzika zokhudzidwazi.

"Ngozi ya namondwe wa Freddy inakhudza anthu ochuluka makamaka chigawo chakumwera kotero kuti ife tipitiriza kuthandiza anthuwa kamba koti ndi zinthu zochuluka zomwe zinawonongeka ndi namondweyu, " anatero a Kamchacha.

Mwazina, bungweli lapereka katundu monga mbale, zikhoza ndi mapepala zokwana ndalama 1 miliyoni ndi 2 handiledi sauzande kwacha (1.2 million kwacha).

Wolemba: Lumbani Kazeze-Blantyre

Zithunzi: Innocenciah Phiri (Dodma)

 MANEB TO ADMISTER DIFFERED EXAMS TO FOUR AT BULALAThe Malawi National Examinations Board (MANEB) says it will administe...
12/07/2023



MANEB TO ADMISTER DIFFERED EXAMS TO FOUR AT BULALA

The Malawi National Examinations Board (MANEB) says it will administer differed examinations to four students whose papers were stolen in the room they were kept, in the night of Sunday, 9 July, 2023 at Bulala Community Day Secondary School in Mzimba.

In a statement MANEB has released on 11th July, the thieves only tampered with already written scripts of four students in subjects of Agriculture 1, Mathematics 1&2, English 1, 2&3, Biology 1, Social and Life skills 1 and 2.

"Security has since been enhanced at the storage facility while police are conducting investigations into the matter," reads part of the statement.

It further states that the papers will be administered from Thursday 16th July to Sunday 19th July 2023. A comprehensive timetable for the examinations has been sent to the school.

MANEB started administering MSCE examinations from Tuesday 27th July and task is expected to end on Friday 21st July 2023.

By Brenda Pensulo- Blantyre

 Malawi vs. Comoros starting XIs
11/07/2023



Malawi vs. Comoros starting XIs

 Flames return to action this afternoon in the fight for a semi-final slot in the Hollywood Bets COSAFA Cup 2023 edition...
11/07/2023



Flames return to action this afternoon in the fight for a semi-final slot in the Hollywood Bets COSAFA Cup 2023 edition.

Mabedi's side takes on Comoros Island who are coming from a loss at the hands of the defending champions, Zambia in the match which kicks off at three o'clock central African time (15:00hrs) at Moses Mabhida Stadium ind Durban.

Malawi will capitalize on the momentum from the previous win over Seychelles to book themselves a place in the semis.

Flames just need a point to automatically qualify for the semi final having already accumulated six points from the two games played in the tournament.

The three previous encounters against Comoros favour Malawi with three wins and a loss from four games played between 2017 and 2021, the latest being a loss for Malawi.

What's your prediction for the match?

Report by Lumbani Albert Kazeze

 Forum For National Development (FND) has asked National Bank of Malawi to deal with the situation arising from Know You...
10/07/2023



Forum For National Development (FND) has asked National Bank of Malawi to deal with the situation arising from Know Your Customer (KYC) activity and provide solutions immediately.

In a press statement signed by the chairperson Bright Kampaundi and the national coordinator Fryson Chodzi, the organization is dismayed with the act of the bank which among others brings suffering to its customers.

Many customers have raised concerns on social media over the way the bank is handling the process of KYC.

There is congestion in most branches of NB across the country as people are queuing for long hours before they can be assisted.

The situation has been worse in some areas as elderly people and mothers with babies are obliged to also stand on lines.

Meanwhile, the bank has extended the period for the activity until 31st August, 2023 to ensure that all members update their accounts smoothly.

Report by Frank Humphreys

 THIRD CLEAN SHEET FOR MABEDIMalawi has taken its tally to six points topping group B table in two games played after be...
09/07/2023



THIRD CLEAN SHEET FOR MABEDI

Malawi has taken its tally to six points topping group B table in two games played after beating Seychelles in a 2-0 thriller in which both Lanjesi Nkhoma and Jacama Kumwembe registered on the score sheet.

The game that took place at King Zwelithini Stadium in South Africa, saw Malawi clinching a second clean sheet at the COSAFA Cup and a third one since Patrick Mabedi took charge of the team in June.

Currently, Flames have managed to forward three goals and concede none in two matches played at the tournament.

Meanwhile, Malawi has played four games since Mabedi took over from Marinica, drawing twice against Mozambique and Ethiopia and winning twice against Zambia and Seychelles while conceding only once.

The team flooded with young stars faces, Comoros on Tuesday, 11 July, 2023 at Chatsworth Stadium from 3 o'clock in the afternoon.

Report by Lumbani Kazeze-Blantyre

 U.N. ADVANCES AIFor the first time in history, robots have responded to questions and  told reporters that they can mak...
07/07/2023



U.N. ADVANCES AI

For the first time in history, robots have responded to questions and told reporters that they can make better-leaders than humans during a press conference.

The event took place as part of International Telecommunication Union, Artificial Intelligence for Good' global summit in Geneva, Switzerland on Friday, July 07, 2023.

Nine AI-enabled humanoid robots sat or stood with their creators at a podium, which the United Nation's International Telecommunication Union called the word's first news conference featuring humanoid social robots.

Among others, Sophia is first robot innovation ambassador for the U.N. Development Program, Grace is described as the world's most advanced humanoid health care robot, and Desdemona, a rock star robot.

Surprisingly, AI powered robots which among others resembled their masters, dismissed fears of taking away human jobs and rebellion against their masters as they claimed that their masters treat them well.

Instead, they assured reporters that they would create an effective synergy with humans in order to work effectively without any bias like humans since they don't have emotions.

The event was part of the AI for Good Global Summit, meant to illustrate how new technology can support the U.N's goals for sustainable development.

Report by Lumbani Kazeze-Blantyre

Source: CBS 17



https://www.cbs17.com/news/ap-humanoid-robots-say-they-could-be-better-leaders-but-will-not-rebel-against-human-creators/

 Super sport yasankha katswiri wakale wosewera kutsogolo kwa Malawi Queens, Mary Waya kukhala m'modzi mwa anthu omwe aka...
07/07/2023



Super sport yasankha katswiri wakale wosewera kutsogolo kwa Malawi Queens, Mary Waya kukhala m'modzi mwa anthu omwe akazukute ndi kusanthula masewero a mpira wa manja amu 2023 Vitality Netball World Cup.

Mpikisanowu womwe uyambe la Chisanu pa 28 July, 2023 mpaka pa 6 August, 2023, uchitikira mu dziko la South Africa komwe Malawi Queens ikatenganawo mbali.

Waya anasewerapo m'mpikisano wa dziko lonse la pansi mu chaka cha 1995 ndi 2007, m'masewero a Commonwealth mu 1997, 2006 ndi 2010 komanso mu masewero ena a World Netball Series mu 2009 ndi 2010.

Katsiwiriyu anasewera masewero oposa 200 ndi Queens asanasankhidwe kukhala mphunzitsi wa Queens mu chaka cha 2017 komanso m'chaka cha 2022 ngati mphunzitsi wa timu ya dziko la Namibia.

Wolemba: Lumbani Kazeze-Blantyre

Photos: Birmingham 2022

 M'modzi mwa atolankhani ojambula zinthunzi (Photo journalist) wa Malawi News Agency (MANA), Gracian Jeke wamwalira usik...
07/07/2023



M'modzi mwa atolankhani ojambula zinthunzi (Photo journalist) wa Malawi News Agency (MANA), Gracian Jeke wamwalira usiku wa dzulo la Chinayi ku chipatala chachikulu cha Queen Elizabeth m'mzinda wa Blantyre.

Mkulu wa MANA chigawo chakumpoto, a George Bulombola ati malemu Jeke anali mtolankhani wokonda kugwira ntchito pamodzi ndi anzawo komanso wolimbikira.

Imfa ya a Jeke yadzetsa chisoni chachikulu pakati pa atolankhani am'dziko lino.

Wolemba: Lumbani Kazeze-Blantyre

Nkhani ndi Chithunzi: AfricaBrief

 TWITTER-THREADS BATTLE NOT OVERTwitter's lawyer, Alex Spiro has threatened to take a legal action against Meta boss, Ma...
07/07/2023



TWITTER-THREADS BATTLE NOT OVER

Twitter's lawyer, Alex Spiro has threatened to take a legal action against Meta boss, Mark Zuckerberg following the release of Threads App which is ironically a copy of Twitter.

Spiro has initially written a letter to Meta stating that his client company intends to strictly enforce its intellectual property rights as he believes the former Twitter employees have been instrumental in the development of Twitter twin sister, Threads .

However, Meta spokesperson Andy Stone has brushed off the allegations that the App has been built by Twitter former employees .

Previously, Twitter boss, Elon Musk, through Twitter wrote, "competition is fine, but cheating is not", this followed the release of Threads which has registered over thirty million subscribers just in two days.

Will Threads overtake Twitter? This is the question that many people are asking.

Report by Lumbani Kazeze-Blantyre

Source-Sky News

 6TH JULY, WAKOMERA FLAMESFlames yasangalira kukwanitsa zaka 59 yili pa ufulu odzilamulira payokha yili ku South Africa ...
06/07/2023



6TH JULY, WAKOMERA FLAMES

Flames yasangalira kukwanitsa zaka 59 yili pa ufulu odzilamulira payokha yili ku South Africa pomwe yagonjetsa Zambia ndi chigoli chimodzi kwa chilowere m'mpikisano wa Hollywood Bets COSAFA Cup 2023.

Izi zikusemphana ndi momwe otsata masewero ochuluka aku Malawi amayankhulira kuti a Malawi asayembekezere kuchita bwino kumpikisanowu.

Malawi inayamba ndi moto pomwe imabwera pafupifupi ku golo la Zambia kudzera mwa anyamata akustogolo Lanjesi Nkhoma, Jakama Kumwembe ndi Chawanangwa Kaonga omwe anapereka mpungwepungwe kwa otchinga kumbuyo a timu ya Zambia.

Panali pa mphindi khumi ndi zisanu ndi ziwiri (17') pomwe otchinga kumbuyo wa timu ya Zambia, Katebe anakuchotsera mpira muwukonde wake womwe ndi mutu atalephera kutchinga kona yauta yomwe anamenya Alick Lungu.

Chigawo choyamba chinatha Malawi ikutsogolabe ngakhale Zambia imapanikiza ku golo la Flames.

Chigawo chachiwiri Zambia inabwera mosinthika pomwe inapanikiza kwambiri ngakhale sizinaphule kanthu poti Denis Chembezi, Stanley Sanudi, Alick Lungu ndi Nickson Mwase anakanitsitsa kupereka mpata.

Zateremu, Malawi ili pa nambala 2 ndi mapointi atatu (3) mu gulu B pambuyo pa Comoros yomwe yilinso ndi mapointi omwewo koma yachinya zigoli zitatu.

Flames idzasewera ndi Sychelles la Mulungu pa 9 July, 2023 ndipo ngati ingadzapambane idzakhaka pamwamba pa gulu B ngati Comoros ingadzagonje kapena kufanana mphamvu ndi Zambia.

Wolemba: Lumbani Kazeze-Blantyre

Happy happy 59th birthday our beautiful Malawi 🎂🎂🎂
06/07/2023

Happy happy 59th birthday our beautiful Malawi 🎂🎂🎂

 TWITTER'S RIVAL IN TOWNMeta who owns Facebook, Instagram and Whatsapp, has launched a new app, "Threads"  that  works s...
06/07/2023



TWITTER'S RIVAL IN TOWN

Meta who owns Facebook, Instagram and Whatsapp, has launched a new app, "Threads" that works similar to Twitter despite having a different font.

The new app whose features are also similar to Twitter, has received praise having already clinched at least 10 million subscriptions at the moment.

Threads is designed as a place to share public real-time text updates, just like Twitter with posts being up to 500 characters long including links, photos, and videos of up to five minutes.

The app ensures that all posts appear in a timeline, and can be liked, reposted, replied to, and shared elsewhere. However, posts don't appear chronologically, and there seems to be no way to make it so.

Just like Elon's Twitter, users will be able to follow celebrities, athletes, and friends, many of whom will have jumped over from Instagram.

Currently, the app is available on the Apple App Store and Google Play Store.

Report by Lumbani Kazeze-Blantyre

Source: Sky News

 Bungwe lothana ndi katangale komanso ziphuphu, la Anti Corruption Bureau (ACB), lalowa m'mgwirizano ndi akatswiri amala...
04/07/2023



Bungwe lothana ndi katangale komanso ziphuphu, la Anti Corruption Bureau (ACB), lalowa m'mgwirizano ndi akatswiri amalamulo oyima pawokha kuti likwaniritse kuthana ndi milandu yochuluka yomwe yakhala yikufufuzidwa kamba koti khothi lozenga milandu yokhudzana ndi za chuma linayamba kugwira ntchito tsopano.

Akatswiriwa omwe ndi a Clement Mwala, Gabriel Chembezi and Wesley Namasala, alowa m'mgwirizanowo ndi bungweli pogwiritsa ntchito ndalama zapadera zowonjezera zomwe boma linayika mundondomeko ya chuma (national budget) ndi cholinga chofuna kufulumizitsa milandu yomwe yakhala nthawi yayitali isanazengedwe.

ACB yati, akatswiriwa agwira ntchito mothandizana ndi akuluakuli oyendetsa milandu kubungweli (prosecutors) pogawana nzeru ndi ukadaulo wakayendetsedwe ka milanduyi.

Pakadali pano, bungwe la ACB linafotokoza kuti lamaliza kufufuza milandu yina yokwana 151 zomwe zikutanthauza kuti bungweli lakwanitsa kumaliza kufufuza milandu yokwana 111 pa milandu 100 yiliyonse (111%).

Umodzi mwa milandu yomwe yayamba kuzengedwa, ndi mlandu wokhudza wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulosi Chilima, womwe wayimitsidwa pa 3 July kufikira pa 19 July, 2023 pomwe akawunikenso belo ya mtsogoleriyu.

Wolemba: Lumbani Kazeze-Blantyre

 Pali chikayiko choti mitengo yogulira shuga isintha monga momwe a Malawi amaganizira.Izi zikutsatira kufotokoza kwa mku...
04/07/2023



Pali chikayiko choti mitengo yogulira shuga isintha monga momwe a Malawi amaganizira.

Izi zikutsatira kufotokoza kwa mkulu wa kampani yopanga shuga ya Illovo, a Limbani Katandula omwe ati mitengo yawo ndiyotsika kusiyana ndi momwe shuga amagulidwira m'mayiko omwe azungulira dziko lino.

A Katandula afotokoza izi kutsatira mpungwepungwe womwe wabuka pakati kampaniyi ndi ogula komanso anthu ena okhudzidwa monga boma, omwe akudandaula kuti mitengo ya shuga ndiyokwera kwambiri m'dziko muno.

"Ngakhale kuti ndi zomveka komanso zosangalatsa kwa ogula shuga omwe akufuna titsitse mitengo yogulitsira shugayi, chilungamo chake n'chakuti izi zikhoza kubweretsa mavuto ochuluka monga zinachitikira chaka chatha (2022) pakati pa April ndi May, pamene mitengo yogulira shugayu yinakwera kamba ka kusowa kwake pamsika," a Katandula anafotokoza.

Iwo anafotokozanso kuti mitengo ya shuga amayipanga ndi dongosolo loti athe kukwanitsa kufikira dziko lonse la Malawi, chaka chonse ndi cholinga chofuna kulepheretsa m'chititidwe wozembetsa katunduyu kapena kutulutsa shugayi kupita mayiko ena kamba koti mitengo yimakhala yosiyana pang'ono.

Koma mwezi watha, boma kudzera mu kalata yaku unduna wazamalonda, linapereka masiku asanu ndi awiri kuti kampani yopanga shugayi itsitse mitengo yake yogulitsira katunduyu pamsika.

Pakadali pano boma lawopseza kuti liwonjezera kupereka ziphaso zogulira shuga kuchoka mayiko ena kwa makampani ena ndi cholinga choti mitengo ya shuga m'dziko muno yitsike ngati kampaniyi siyitsitsa mitengo yake.

M'madera ambiri m'dziko muno, shuga akugulitsidwa pamtengo wapakati pa K1,300 ndi K1, 500 pa paketi yolemera 1 kilogram.

Wolemba: Lumbani Kazeze-Blantyre

 Mphunzitsi wongogwirizira wa timu ya dziko la Malawi, Patrick Mabedi wasankha anyamata okankha chikopa okwana makumi aw...
03/07/2023



Mphunzitsi wongogwirizira wa timu ya dziko la Malawi, Patrick Mabedi wasankha anyamata okankha chikopa okwana makumi awiri ndi asanu (25) kuti akatumikire dziko lino m'mpikisano wa Hollywood Bets COSAFA Cup, 2023.

Timuyi yomwe inyamuke ulendo wa ku South Africa mawa lachiwiri pa 4 January, 2023, yili ndi osewera 23 omwe amasewera ku Malawi pomwe awiri okha ndi omwe amasewera m'dziko la Zambia.

M'mpikisano wa chaka chino, Flames yili mu gulu B lomwe muli mayiko monga, Zambia, Comoros ndi Sychelles ndipo masewero awo oyamba adzamenya ndi Zambia pa 9 July, 2023, asanakumane ndi Sychelles pa 9 July, 2023 komanso kumaliza ndi Comoros pa 11 July, 2023.

Mndandanda wa osewera omwe atengedwa uli motere;

Otchinga pagolo: Brighton Munthali ( Blue Eagles), Austin Chirambo ( FCB Nyasa Big Bullets Reserves) and Innocent Nyasulu (Mighty Tigers)

Osewera kumbuyo: Macdonald Lameck ( Blue Eagles), Dennis Chembezi (Opanda timu), Dan Chimbalanga (MAFCO), Lawrence Chaziya, Stanley Sanudi ( Mighty Mukuru Wanderers), Nickson Mwase (Silver Strikers)

Osewera pakati: Alick Lungu, Frank Willard, Patrick Mwaungulu ( FCB Nyasa Big Bullets, Blessings Singini ( Ekwendeni Hammers), Chikumbutso Salima, Robert Saizi ( Bangwe All Stars), Chimwemwe Idana, Chikondi Kamanga, Patrick Macheso ( Silver Strikers), Chrispin Mapemba (FCB Nyasa Big Bullets Reserves).

Omwetsa zigoli: Chawanangwa Kaonga ( Zanaco, Zambia), Chifundo Mphasi ( Shamuel Academy), Christopher Kumwembe, Gaddie Chirwa ( Mighty Mukuru Wanderers) Lanjesi Nkhoma ( FCB Nyasa Big Bullets)

Address

Masauko Chipembere High Way
Blantyre

Telephone

+265996968806

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when The Giraffe Malawi Online News posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to The Giraffe Malawi Online News:

Videos

Share



You may also like