Sapitwa FM Radio

Sapitwa FM Radio Your partner in business

Mulhako Uliponso Chaka Chino!Bungwe la Chikhalidwe la Mulhako wa Alhomwe lalengeza kuti chaka chino chisangararo cha Chi...
08/08/2022

Mulhako Uliponso Chaka Chino!

Bungwe la Chikhalidwe la Mulhako wa Alhomwe lalengeza kuti chaka chino chisangararo cha Chikhalidwe cha Mulhako wa Alhomwe chikharako. Izi ndi malingana ndi Bambo Jubeki Monjeza, yemwe ndiwapa mpando wofalitsira nkhani za chisangalalochi chaka chino yemwe anauza atolankhani kulikuru la bungweri kwa Chonde, m'boma la Mulanje.

Chisangalalochi chizachitika pa 9 October 2022, ndipo akumbekezeka kugwiritsa ntchito ndalama zosachepera 150,000,000.00MK.

Mwazina pa chisangalalochi kuzakhara zakudya ngati ntsapysa ndi chipere, magule, makhwara ndizina. Ngati njira imodzi yolimbikitsa umodzi, chomweso ndi mutu wachakachino, Mulhako wa Alhomwe wayitanaso anthu a mitundu ina, kuno ku Malawi ngakhaleso kunja.

03/08/2022
03/08/2022

Tune now

107.5Mhz

Mulhako wa Alhomwe’s Press Statement on the Slander of Alhomwe People through Circulated Audio Authored by Mr. Silrage P...
04/07/2022

Mulhako wa Alhomwe’s Press Statement on the Slander of Alhomwe People through Circulated Audio Authored by Mr. Silrage Phiri
Dated: 1st July, 2022

The Lhomwe Cultural Grouping has learnt and painstakingly listened with shock and disbelief the repugnant and horrendous contents of a 15 minute long diatribe audio which was, undoubtedly, aimed at inciting Malawians into violence against fellow Malawians belonging to the Lhomwe tribe. In the clip, Mr. Phiri has made accusations against Lhomwe’s which are unfounded, antagonistic and a deliberate attempt to incite tribal and cultural hatred in a nation that has thrived on co-existence from time immemorial.

The demonization of a tribe on the basis of political and ethnic extraction is primitive, counterproductive to socio-economic development and further hangs a nation on the blink of conflict. Africa is awash of examples where inability to appreciate the power of cultural and tribal diversity led to disagreements that costed innocent people their dear lives. Malawi needs not to go through the same route. Malawians are peace loving people. Malawians live beyond the boundaries of ethnicity. Malawians are one, have been one and will always remain one regardless of tribal differences.

It is absolutely regrettable that the said Mr. Phiri alleged that Lhomwe’s are Blood Suckers, that all the problems in this country are caused by people of Lhomwe Tribe, that all Malawians are victims of Lhomwe’s exploits in different sectors, and that Lhomwes be declared persona non grata in their own country. This smacks the perpetration of a culture of character assassination and the hangover of tribal and ethnic alienation that others wish to vent on people that are innocent, peace-loving and development-conscious.

The Lhomwe Cultural Group premises itself on the foundations of love, respect for humanity and the preservation of the dignity of all human beings regardless of race, colour and ethnic extraction. Lhomwes are proud to have lived with people of different ethnic lines in peace and harmony, as brothers and sisters and together fostering social economic development. Lhomwes are further proud that they even contributed alot towards the significant development of this nation. Lhomwes have impacted greatly in economic, agriculture, education, medical, engineering, law and many other sectors of life and they still continue and will keep on without being threatened by ill-minded ethnic despots.
One would have anticipated that the Ministry of Unity and Civic Education would have been at the forefront condemning the disparaging remarks, vehemently and categorically rebuking the irresponsible and ill advised announcements that have the potential to ignite tribal fire in the country. Alas, we are greeted with deafening silence.

It must be clarified that Lhomwe tribe, just like any other tribe, has no political affiliation. Lhomwes do not entertain or encourage the practicing of politics that thrives on ethnic differences as that is a recipe for national disaster. It promotes nepotism and is retrogressive as it is lacks merit on the basis of its inability to accord people same liberties.

It is imperative to put matters in an appropriate context. Mulhako wa Alhomwe is an organization founded in 2008 to provide exposure to cultural traditions of the Lhomwe tribe. Its main focus is to expose children, and people from other tribes and countries, to the ethnic customs (dance, drumming, storytelling, poetry, tribal history, arts and crafts) as a means of promoting self-esteem, creativity and preservation of the Lhomwe tribal customs. By preserving a culture, one keeps the traditions, family values, sociological standards and morals, and language.

The Cultural Grouping has noble objectives which include, but not limited to:

(a) To assist government in developing and preserving culture, customs and traditions of this country and to cooperate with other tribes in Malawi and elsewhere in the preservations of African cultures, traditions and heritage.

(b) To play a key role in promoting and safeguarding of human rights particularly that of women and girls in regard to Girls Education, HIV/AIDS, Sexual Reproductive Health, Protection from Harmful Cultural Practices and Child Harassment including Trafficking.

(c) To assist Government in empowering communities through innovations in education, science and technology to mitigate issues of poverty, environment and climate change.

(d) To enhance unity and cultural diversity through promotion and protection of intellectual properties, genetic resources, expression of folklores, and traditional knowledge.

In the light of this retrogressive conduct exposed through the voice of Mr. Phiri, it is imperative that the government through the Ministry Responsible for Civic Education condemns the demonic message advanced by Mr. Phiri and his cronies that may have been resonating with his sentiments. Let churches, Cultural Heritage Groupings, Public Affairs Committee, CSO’s, International Organizations make their responses to the circulated audio as it puts the country at the risk of the cancer of cultural and tribal hatred.

Mulhako wa Alhomwe humbly demands that one Mr. Silrage Phiri, author of the audio massage, apologizes to all Lhomwe Chiefs, Entire Mulhako Wa Alhomwe Leadership and all Alhomwe Cultural Grouping through written communication and audio message within the next 48 hours. Failure to comply with the demand will leave the Alhomwe cultural grouping with no any other option than taking unspecified action within legal parameters.

All Lhomwes, being peaceful as they have always been, are urged to be stronger as ever before. Unity and strength, oneness and prosperity, is never stronger, than when tested. Lhomwes take pride in their cultural heritage and will always cherish their values in harmony with people of all ethnic extractions.

God bless Malawi, God Bless us All.
The Board of Trustees-Mulhako wa Alhomwe

Catch-Us Live
24/05/2022

Catch-Us Live

Tidzakhara "LIVE" pa page yathu ino. Komaso sabata imeneyi, tikhara tikukupatsiraniso magawo ena a zina zomwe malemu Bin...
03/04/2022

Tidzakhara "LIVE" pa page yathu ino. Komaso sabata imeneyi, tikhara tikukupatsiraniso magawo ena a zina zomwe malemu Bingu Wa Mutharika zinali m'maso mphenya awo komaso malingariro awo ku dziko la Malawi ndi Africa.

Izi ndizomwe anazilemba mu book lawo lotchedwa "The African Dream, 'From Poverty to Prosperity'

Kharani pompo.

28 MARCH-MU MBIRIMu 1658, tsiku ngati lero sitima ya Dutch East Indus Company (VOC), yotchedwa Amersfoort inafika ndi ak...
28/03/2022

28 MARCH-MU MBIRI

Mu 1658, tsiku ngati lero sitima ya Dutch East Indus Company (VOC), yotchedwa Amersfoort inafika ndi akapolo okwana 174 ku South Africa, ndipo ichi chikukhara chiyambi cha zaka 200 za malonda a ukapolo pa doko la Cape ku South Africa.

Sitima yama Dutchyi sinari yotenga akaporo, koma inakumanizana ndi sitima ya Apwitikizi omwe anatenga akapolo 500, amayi ndi amuna kuchokera ku dziko la Angola.

Sitima ya Apwitikizi inalandidwa akaporo 250, nkuwasiyira ena. Ena mwa akapolowa anafika nawo ku gombe kuti apeze mpweya wabwino poti ambiri anafooka, kudwara ndi kufa. Potero chiwerengero chinafika pa 174. Izi zikufotokozedwa bwino muzolemba za Van Riebeck yemwe tikumuona mu mbiri kukhara mbari imodzi yayikuru malonda a ukapolo kuno ku Africa.

Malonda a ukapolo anali oipa kwambiri. Ana ndi akuru, amayi ndi abambo amagwidwa nkumawagulitsa ngati katundu. Amatengedwa nkumakagwira ntchito nyumba komaso m'minda ndi makampani ku maiko azungu mokakamizidwa. Kugwidwa, kutengedwa komaso kugwiritsidwa ntchito ngati chinthu chabe osati anthu, ndi mbari imodzi ya mbiri za nkhanza zonse mtundu wa anthu akuda ku Africa unachitiridwira. Anthu ma million agwidwa, kuthawa, komaso kufa kumene kudzera mu mchitidwewu.

Mabungwe ndi anthu omenyera ufuru akhara akudzudzura mchitidwewu komaso kupempha kuti maiko omwe anatenga akapolo alipire, komabe izi zakhara zobvuta kuti zikwaniritsidwe.

Mu nkhani zathu zokhudzana ndi MBIRI pano pa Sapitwa tikhara tikufukura za malonda a ukapolo, chiyambi, kulimbana nawo kufikira pomwe anathetsedwa.


DESMOND DUNDWA PHIRI       23 February, 1931 - 24 March 2019     "Mzimu Wawo Uuse Mu Mtendere Wosatha"Amadziwika  bwino ...
24/03/2022

DESMOND DUNDWA PHIRI

23 February, 1931 - 24 March 2019

"Mzimu Wawo Uuse Mu Mtendere Wosatha"

Amadziwika bwino ndi dzina loti DD Phiri. Anali mlembi, katswiri pa nkhani zachuma, kachitidwe ka zinthu komaso katswiri wa mbiri (historian)

Phiri anabadwira ku Mzimba, pa 23 February, 1931 ndipo anatisiya pa 24 February, 2019. Kupatula kugwira ntchito m'boma ndikuluma mu 1972, amachitaso maphunziro mpaka a udokotala (Doctorate). DD Phiri amalemba nkhani zosiyanasiyana mu newspaper ya Nation. Anayambitsa sukulu ya Agrrey Memorial yomwe yathandiza anthu ochuluka m'Malawi ndi kunja.

DD Phiri anasindikiza mabukhu 17 okhudA zachuma, mbiri, kayendetsedwe kazinthu ndi zina. Amalembaso nkhani zopeka (fiction) ndipo nkhani zina amalemba m'chilankhuro chachitumbuka ngati bukhu lotchedwa "Ulanda Wa Mavunika".

Mu 2011 anapatsidwa ulemu ndi bungwe la Pan-African Writers Association lomwe limalimbikitsa zolemba za chi Africa. Ndipo anali gulu la alembi 20 omwe zolemba zawo zinali za mphamvu kwambiri muno mu Africa.

Malawi analuza nkhokwe ya nzeru ndi luso lakuphunzitsa kudzera muzolemba. Mzimu wa DD Phiri kudzera mu zolemba zawo upitirize kutilimbikitsa tonse ngati alembi ndi okonda kuwerenga.

Mzimu Wawo Uuse Mu Mtendere Wosatha

NYIMBO YOFUNIKA KUIMVERA"sikungomvera kokha, komaso kuphunzira, makamaka achinyamata"Agorosso Llyod Phaundi, yemwe nyimb...
24/03/2022

NYIMBO YOFUNIKA KUIMVERA
"sikungomvera kokha, komaso kuphunzira, makamaka achinyamata"

Agorosso Llyod Phaundi, yemwe nyimbo zake zimaimbidwa mumamvekedwe a magule a kwathu kuno maka achigwa cha mtsinje wa Shire ndi ena, waturutsa nyimbo yatsopano yotchedwa .

Nyimboyi waimba ndi Local Girl Keturah yemweso nyimbo zake zimaonetsa chikhalidwe cha Malawi komaso Africa.

Mawa Friday, 25 February 2022, 14:00pm tikhara tikusanthura nyimbo imeneyi.

Mukhoza kumvera komaso kupeza nyimboyi pa masamba osiyanasiyana a internet omwe amapanga za nyimbo.



MIZINGA YA RUSSIA YIPITIRIRA KUKANTHA UKRAINE'Pomwe nkhondo yikulowa sabata ya chinayi.'Malingana ndi ma report a nkhond...
23/03/2022

MIZINGA YA RUSSIA YIPITIRIRA KUKANTHA UKRAINE

'Pomwe nkhondo yikulowa sabata ya chinayi.'

Malingana ndi ma report a nkhondo akuti zomwe yachita Russia zikhoza kukhara machitachita a nkhondo akuru kwambiri pa nthaka yaku Ulaya kutsatira World War 2, muzaka za 1938-1945.

Kutsatira zomwe Russia yachita kuthira nkhondo Ukraine kwachitika zambiri zomwe zakhudzaso maiko ambiri ndi umoyo wa anthu. Zina ndi monga: Kusalidwa kwa Russia pa nkhani za chuma ndi malonda, ndipo maiko akuganiza zochotsa Russia mu bungwe la maiko 20 olemera kwambiri pa dziko lonse. Anthu olemera aku Russia (Russian Billionaires) ayamba kusamutsa chuma chawo ku Russia. Ukraine kudzera mwa mtsogoleri wawo, Volodymir Zelensky wakhara akupempha maiko maka a bungwe la chitetezo la NATO kuti a chitepo kanthu kuthana ndi nkhondo yomwe Russia yayambitsa. Komaso kudzudzulidwa kwa Russia pakamenyedwe ka nkhondo yake yomwe akuti mizinga yawo ikufikira anthu omwe si asilikari ndi malo omwe si asilikari. Kufikira lero anthu osachepera 19000 aphedwa kapena kufa, ena 1900 avulazidwa, ndipo ena 100,000 akakamira mu mzinda wa Mariupol, komwe asilikali aku Russia akangalika kuponya mizinga. Ndipo ena 10million athawa komwe amakhara ndipo a kukhara ngati osowa malo (refugees) Nyumba 1700 zaonongedwa ndipo katundu okwana $119billion waonongedwaso.

Mafunao omwe akufunsidwa ndi akuti, m'chifukwa chani Russia inalowa m'dziko la Ukraine ndi nkhondo? Pali zomwe zadziwika, komaso zina sizinadziwike kapena kumvetsetseka. Sapitwa FM Radio yikupatsirani Zobisika Zokhudzana ndi Nkhondo ya Russia ku Ukraine.

Tidziwe kuti, Russia ndi Ukraine anali mbali imodzi ya United Socialist Soviet Republics (1917 mpaka 1991). Komaso m'chaka cha 2014 pa February 20, dziko la Russia lidalowaso ku Ukraine ndi nkhondo. Tidziweso kuti Russia ndi Ukraine alindi mzika zofanana za gulu lolankhura chilankhuro chachi Slavic, limodzi ndi maiko ngati Poland, Czech, komaso Bulgaria. Vladimir Putin, yemwe ndi mtsogoleri Wa Russia pachiyambi anati iyi sinkhondo koma kukhazikitsa bata maka kuthana ndi gulu la N**I, komaso kuchepetsa mphamvu za nkhondo za dziko la Ukraine lomwe linayamba ubare ndi bungwe la nkhondo la NATO momwe muliso maiko a USA, Britain, France and ena.

Kodi zoona za nkhondo iyi ndi ziti? M'chifukwa chani maiko a mphamvu ngati USA, France, Germany, Japan ndi ena sakufuna kulowerera potumiza asilikali awo?

Kondani (LIKE THIS PAGE) page ino komaso auzeni anzanu amene akufuna kumva za nkhondo ya Russian ku Ukraine.



MATENDA A POLIO ABUKASOPa 17 February 2022, unduna wa zaumoyo m'dziko muno unalengeza za kupezekaso kwa matenda a polio....
21/03/2022

MATENDA A POLIO ABUKASO

Pa 17 February 2022, unduna wa zaumoyo m'dziko muno unalengeza za kupezekaso kwa matenda a polio. Matenda wa awonekaso kwathu kuno koyamba kuchokera m'chaka cha 1992. Ndipo ku Afrika kuno kuchokera m'chaka cha 2016. Kuzindikiridwa koyamba kwa polioyu yemwe akutchedwa kuti Type 1 Wild Polivirus (WPV1) kunachitika ku Lilongwe.

Pachifukwa ichi mtsogoleri wa dziko lino mwezi wa February womwewo anaika kupezeka kwa nthenda ya polioyi ngati ngozi pa ntchito zu umoyo (Public Health Emergency). Ndipo kudzera mu ndondomeko za umoyo zomwe zilipo kale, kudzeraso mu ntchito za kulimbikitsa madyedwe abwino (Scaling Up Nutrition), komaso ntchito za ma Health Surveillance Assistant (HSA's), komaso ndondomeko ya National Expanded Programme on Immunization (EPI) yomwe inayamba m'chaka cha 1971, boma la Malawi lakhazikitsa ntchito yopereka katemera wina wa polio kwa anthu ochuluka (mass vaccination). Katemerayu aziperekedwa kwa ana osaposera zaka 5 motere:
1. Gawo loyamba, kuyambira pa 1 March, 2022
2. Gawo lachiwiri, kuyamvira pa 1 April 2022

Ntchitoyi igwiridwa ndi thandizo la chuma kuchokera ku World Health Organization (WHO) ndipo boma la Malawi kudzera ku unduna wa za Umoyo agwirira limodzi ndi bungwe la Red Cross Society.

Nkhani yakatemera wa polio yikudza pambuyo pakusabvomekeza kwa anthu pa nkhani zokhudza katemera wa Covid-19. Ena akuganiza kuti boma likunamizira nthenda ya polio kuti likwaniritse mulingo womwe akufuna wa anthu obayitsa katemera wa Covid-19.

Koma choti tidziwe nthenda ya polio siyalero. Inabuka Covid-19 asanabwere. Ndiyoopsa, ikhoza kuwononga moyo. Nthendayi imafoora nthiti ndi kufa kwa ziwaro. Manja ndi miyendo zimanyetcheraso. Nthendayi amapatsirana makamaka pakati pa anthu omwe sanabayitse katemera wa polio.

Chifukwa chachikondi, koma chidziwitsa pa moyo wa ana anthu, tiyeni titenge gawo poonetsetsa kuti onse oyenera kulandira katemerayu alandira.



Uthenga umene ukutipeza kuchokera ku Kamuzu StadiumBullets 2-1 WanderersIdana 16"Mfune 82"Nyangulu 78"Mapale ayamba bwin...
19/03/2022

Uthenga umene ukutipeza kuchokera ku Kamuzu Stadium
Bullets 2-1 Wanderers
Idana 16"
Mfune 82"

Nyangulu 78"

Mapale ayamba bwino, Manoma azitolere akukuwa choncho anthu ozitsata.


BOLA PAMTSETSE-SUPER LEAGUE YAYAMBIKAKuwinyawinya, kusakhutitsidwa, kunalipo ndithu. Komabe zonse zikuyambika lero, mase...
19/03/2022

BOLA PAMTSETSE-SUPER LEAGUE YAYAMBIKA

Kuwinyawinya, kusakhutitsidwa, kunalipo ndithu. Komabe zonse zikuyambika lero, masewero a mpira wa miyendo. Ma timu 16, iriyonse kumenya ma game 30. Ligi yonse ma game 480. TNM, 2022 akuti BOLA PAMTSETSE.

Iyitu ndi ligi yapamwamba kwambiri m'dziko muno, yomwe ndalama zake imapereka ndi TNM. Nyengo ino TNM ikuti pali 40,000,000.00MK kwa katswiri wa mpikisanowu. Komaso mphotho ndi zina zochitika zambiri mkati mwandimemu.

Kamuzu Stadium, lero pa 19 March, 2022. Mapale, Nyasa Big Bullets maso ndi maso ndi Manoma Mighty Wanderers. Zonse zikuyamba 10:00 mmawa uno, pomwe zipata za Kamuzu Stadium zikutsekuridwa.



ATSARA NDI MASANJEWatero Mlaka Maliro mu nyimbo yake yatsopano yotchedwa "Vinyo Watha".Funso nkumati, wamuthera vinyoyo ...
18/03/2022

ATSARA NDI MASANJE

Watero Mlaka Maliro mu nyimbo yake yatsopano yotchedwa "Vinyo Watha".

Funso nkumati, wamuthera vinyoyo ndi ndani anthuni? Anthu akufuna kudziwa mu nyimbo ya Mlaka Maliro yemwe kwaka nthawi anasiya kaye kuyimba nkuyankha mayitanidwe a Ubusa ndi mpingo wa ECG woyambitsidwa ndi Mneneri Shepherd Bushiri, yemwe so amadzitcha kuti ndi Mneneri wankulu. Nkhani yikuti Mbusa Mlaka wabwererako ku mpingowu ndipo wasiya kutumikira pazifukwa za banja. Paliso nkhani yoti mkazi wake Bernadette anali mu mpungwepungwe wakhalidwe losayenera Mayi Mbusa mpaka zinthu zinasokonekera. Awiriwa ngati banja abwerera ku Malawi. Kapenatu ku Swaziland analiko vinyo watha?

Koma verse yapatsaso chidwi mu nyimboyi ikumati:

Akuyenda mwa mdidi mbendera petupetu
Komatu vinyo watha
Nkanadziwa Kanani munkanena uja anali wapachibale
Nkatsara konkuja nkumaphura njerwa nkumadya kamodzi
Atsara ndi masanje, musapusitsike
Palibe chilipo
VINYO KULIBE.

Aliyense akhoza kuwona ekha kuti awa anali malonjezano a boma la Tonse omwe pano sakuonekaso. Tonse tikudziwa bwino m'mene anyamata a Tonse amalankhulira "Sweet Talk"

Kapenatu kumeneko ndi kumene vinyo watha.


Pa 17 March ndi tsiku lomwe mtsogoleri wakale wa dziko lino komaso woyamba mu ulamuliro wazipani zambiri Dr. Bakili Mulu...
17/03/2022

Pa 17 March ndi tsiku lomwe mtsogoleri wakale wa dziko lino komaso woyamba mu ulamuliro wazipani zambiri Dr. Bakili Muluzi, Atcheya anabadwa. Komaso tsiku lomweri ndi lomwe mwana wakatswiri woyimba nyimbo Soldier Lucius Banda, Mapiri Bakili Banda anabadwa. Atcheya ndiomwe anampatsa mwanayu dzinali. Zimamvekaso kuti mwana wa Atcheya, Atupele, yemwe ndi mtsogoleri Wa UDF anapatsidwa dzinari ndi mtsogoleri woyamba wadziko lino malemu Dr. Hastings Kamuzu Banda. Wodala Opatsidwa mayina ndi ma pulezidenti.


Mtengo uwu ndi wasabata ino. Mtengo Wa sabata ya mawa tikupatsiraniso.Posachedwapa anduna azachuma mu ndondomeko yachuma...
16/03/2022

Mtengo uwu ndi wasabata ino. Mtengo Wa sabata ya mawa tikupatsiraniso.

Posachedwapa anduna azachuma mu ndondomeko yachuma cha dziko cha 2022 ndi 2023 analengeza kuchotsedwa kwa msonkho womwe unali pa mafuta ophikira uja amati VAT. Izi amachita kuti mafuta ophikira atsike mtengo. Lero malo motsika akukwera.


Address

Blantyre

Telephone

+265990420446

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Sapitwa FM Radio posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Sapitwa FM Radio:

Share

Category