Zimbabwe Chewa Nyanja News

Zimbabwe Chewa Nyanja News Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Zimbabwe Chewa Nyanja News, Media/News Company, Bulawayo.

29/05/2024

This version of Facebook uses less data and works in all network conditions.

12/04/2024



Chiwerengero cha asungwana ndi amayi a zaka za pakati pa 15 ndi 24 amene akutenga HIV chikukwera kaamba ka abambo achikulire omwe amakonda kugona ndi a misinkhu imeneyi, latero bungwe lolimbana ndi matenda a Aids la NAC.

Mkulu woona zopewa kachirombo ka HIV/Aids ku bungwelo a Francis Mabedi ati mwa anthu 100 alionse amene akutenga kachirombo koyambitsa Aids, 22 ndi asungwana ndi amayiwo.

Iwo atinso ambiri mwa amene akutenga kachiromboka m'mizinda ya Blantyre, Lilongwe, Zomba ndi Mzuzu ndi ophunzira m'sukulu za ukachenjede. A Mabedi ati izi zili chomwechi pomwe ophunzirawo akugona m'magowero ndipo amadzisakira okha.

Wolemba: Jonathan Pasungwi

11/04/2024

World Bank yalengeza kuthi dziko laZimbabwe ndilomwe liri ndizakudya zodula kuposa maiko onse apansi pano

11/04/2024

Papa Francisco wati ndi wokhudzidwa ndi ngozi ya kusefukira kwa madzi yomwe yachitika m'dziko la Kazakhstan.

Iye wayankhula izi mu uthenga wake wopepesa momwenso wapempha mapemphero opemphelera anthu onse omwe akhudzidwa ndi ngoziyi ndipo athawa m'nyumba zao.

Mtsogoleri wa Mpingo wa a Katolika'yu wati ndi pemphero lake kuti pa nthawi yovutayi anthuwa azilimbikitsidwa ndi chimwemwe chomwe akhristu akugawana padakali pano cha Yesu Khristu wouka kwa akufa.

Malipoti akuti anthu oposa 110,000 athawa m'nyumba zao potsatira kusungunuka kwa madzi owundana zomwe zachititsa kuti mitsinje yambiri ilandire madzi ochuluka ndikuyamba kusefukira kupita m'madera omwe anthu amakhala.

11/04/2024

#

AGAMULIDWA ZAKA KHUMI KU NDENDE CHIFUKWA CHOTUKWANA.

Bwalo la milandu la first grade Magistrate ku M'chinji lero lagamula a George Milanzi azaka 33 ndi a Yamikani Banda azaka 30 kukagwila ndende ya kalavula gaga kwazaka khumi aliyese chifukwa chotukwana m'zimai wina m'mudzi wa Chinkhota m'bomalo.

Bwaloli kudzela kwa mboni ya boma a Linda Kwinda linamvetsedwa kuti ogamulidwawa akhala akutukwana maiyu kwa nthawi yaitali,kamba koti otukwanidwayo amafalitsa bodza kuti ndiwo anaba mtengo wa m'mkulu wina m'delari.

A Kamwinda anati pambali potukwana maiyu paguru la anthu, abambo awiriwa akhalaso akugenda nyumba yake pa nthawi ya usiku.

Ndipo mayi otukwanidwayo atakasiya nkhaniyi ku polisi, abambo awiriwa akhala akuyenda mothawa kufikila atamangidwa pa 6 February chaka chino.

Ataonekera m'bwalo la milandu abambo awiriwa, anakana mulanduwu ndipo mboni ya boma inabweletsa mboni ziwiri m'mbwalori ndipo kenako awiriwa anavomela mulanduwu.

Ozenga mulanduwu, Yohane Nkhata analamula awiriwa kukakhala kundende zaka makumi awiri aliyese.

Malingana ndi ndime yachitatu la gawo loyamba la lamuro 88 pa malamulo ozengera milandu yotchedwa pinal code, kutukwana ndi mulandu.

A George Milanzi ndi a Yamikani Banda amachokera m'mudzi wa Chimimba mfumu yaikulu Zulu.

Wolemba: Patrick Nditi Nyirenda-Mchinji.

Mutsogoleri wakhale wadziko laSouth Africa aJacob Zuma, awa lola kuthi akale nawo pazisankho zimene ziza chitika mudziko...
10/04/2024

Mutsogoleri wakhale wadziko laSouth Africa aJacob Zuma, awa lola kuthi akale nawo pazisankho zimene ziza chitika mudzikolo. AZuma omwe anali mtsogoleri muchaka cha2009 mphaka 2018, analetsedwa kukhala nawo pazisankho ndibungwe la Electoral Commission koma bwalo lamulandu, lathi iwo ndiwo loledwa malinga ndiConstitution yadziko laSouth Africa..Ponuani maganizo anu pankhani iyi..

Nzika yaZimbabwe yokala ku dziko laSouth Africa, Yaombera akazi ake ndikudziomberanso iyeyo.  Malingana ndimaripoti, mka...
10/04/2024

Nzika yaZimbabwe yokala ku dziko laSouth Africa, Yaombera akazi ake ndikudziomberanso iyeyo. Malingana ndimaripoti, mkazi uyu anafuna kuthetsa banja ndimwamuna wakhe. Mwamuna ana khwiya kwambiri mpakana khupa mkazi wakhe. Anaombelanso twin sister wamkazi ndikumu vulaza. Amafuna aombere apongozi ake koma mfuthi ina lephera...

10/04/2024

Madzuka bwanji kuHarare, Bulawayo, Gweru, Masvingo, Shurigwi, Mutare, Kwekwe, Kadoma....

Dziko laZimbabwe latulutsa ndalama yatsopano yochedwa ZIG. Ndondomeko yandalamazi alonjeza ndi aGoverner aReserve Bank O...
10/04/2024

Dziko laZimbabwe latulutsa ndalama yatsopano yochedwa ZIG. Ndondomeko yandalamazi alonjeza ndi aGoverner aReserve Bank Of Zimbabwe.

Address

Bulawayo

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Zimbabwe Chewa Nyanja News posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share