![```AROMA 8 : 25```Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro.Tikuyembekeza Ulem...](https://img5.medioq.com/575/883/964696835758837.jpg)
30/01/2025
```AROMA 8 : 25```
Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro.
Tikuyembekeza Ulemerero, tikuyembekeza moyo wosatha, tsono pamene tikuyembekeza moyo wosatha umene sitikuuona, ulemerero umene sitikuuona, Tiuyembekeza ndi chipiriro, chifukwa otonza amachuluka, otiseka amachuluka, otinyoza amachuluka, koma ife tichilindirira ndi chipiriro mpakana mapeto a zonse, mpaka kubwera kwa mwina wake Yesu Khristu, ife tichilindirirabe ndi chipiriro, tidafooke tissbwerere m'mbuyo, ndipo tipitirire ulendou, kulalikira mawu, kupemphera, fasting ndi zina zambiri, mpaka kubwera kwa mwina wake. ife tichilindirira ndi chipiriro.
CHOONADI CHAMAMASULA GROUP