16/11/2024
"Koma ngati Mulungu aveka chotero udzu wa kuthengo, [Umene] ukhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto, nanga si inu kopambana ndithu, inu akukhulupirira pang'ono?" _ Mateu 6:30.
Tikamaona chilengedwe, mmene Mulungu anapangira zinthu zonse, inde anapanga zinthu zokongola kwambiri, anthu, maudzu akutchile, zinyama, ndi zina zambiri. Zinthuzi anakonza mopatsa chidwi kwambiri, and zinthu zimenezi zimakhala ndi moyo mu njira zosiyanasiyana. Yesu ankafotokoza za nkhawa za moyo uno, ndipo amalankhula kuti musamadere nkhawa m'moyo wanu, kuti mudzadya and kuti mudzabvala chani. Taonani maudzu akutchile, taonani maluwa, m'mene amakhalira okongola, inde Ngakhale Solomo mu ulamuliro wake sanavalepo chinthu chokongola ngati duwa ili. Tsono ngati Mulungu amatha kuveka, kukongoletsa maluwa akutchile chotere, chili bwanji inu amene mumampembedza?
Chimene ndikufuna kunena ndi chakuti, Mulungu asamalira za ife, ndipo iye ndiye potsamira pathu, zili ndi ife kuika chikhulupiriro chathu pa iye kapena ayi. Koma Mulungu ngati amadyetsa mbalame, inde Akhoza kukudyetsani koposa inu, ngati amamveka maluwa, akhoza kukuvekani koposa inu, pakuti inu muposa maluwawo. Akuti mutulireni Mulungu nkhawa zanu zonse pakuti iye akuderani nkhawa. Koma ndi pemphero ndi pembedzero lonse zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Amen.