![Sukulu ya ukachenjede ya UNIMA yatulutsa bukhu lomwe yalemba pankhani yokhudza ufulu wa aphunzitsi komanso ophunzira pa ...](https://img5.medioq.com/164/832/1005176621648322.jpg)
21/12/2024
Sukulu ya ukachenjede ya UNIMA yatulutsa bukhu lomwe yalemba pankhani yokhudza ufulu wa aphunzitsi komanso ophunzira pa mutu oti "Academic Freedom in Africa; The Struggle Rages On" mchingerezi.
Mwazina bukhuli likuunikira mavuto omwe sukulu ya UNIMA yomwe panthawiyo inkatchedwa Chancellor College, inakumana nawo pomwe boma kudzera mwa apolisi, linkafuna kulamulira ndi kulowerela pa kaphunzitsidwe kapasukuluyi zaka zoposa khumi zapitazo.
Poyankhula pa mwambo okhazikitsa bukhuli, mmodzi mwa aphunzitsi omwe analipo panthawi yomwe izi zinkachitika ndipo atsogolera polemba bukhuli, Dr. Garton Kamchedzera, ati silikungobweletsa poyera zovuta zomwe anakumana nazo, komanso likufuna kulimbikitsa ufulu wa aphunzitsi ndi ophunzira a msukulu za ukachenjede kudzera mo zomwe zinachitikazo.
Kumbali yake, mtsogoleri wa aphunzitsi apasukulu ya UNIMA, Dr. Foster Gondwe ati potengera kuti omwe atenga gawo polemba bukhuli si aphunzitsi aku Malawi kokha komanso amaiko ena kuphatikizapo ku Asia, zithandiza aphunzitsi ndi ophunzira amsukulu za ukachenjede kuligwiritsa ntchito maka pankhani za kafukufuku.
Wolemba: Chimwemwe Mikwala.