Mzati Radio & Tv

Mzati Radio & Tv To Entertain, Educate and Inform .. Mzati Limited Company- is registered and licensed with the Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA).

The station broadcasts social and developmental programs on the following frequencies: 94.0Mhz & 94.2 MHz
MZATI TV-GO TV CHANNEL 811 & MDBNL 810 ZUKU CHANNEL 75

Radio online: Getmeradio.com, A2Z Malawi App, radio box & radio garden

21/12/2024



Bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno la MEC lati liwonjezera masiku ochitira kalembera wa zisankho za chaka cha mawa.

Malinga ndi kalata yomwe bungweli latulutsa,ganizoli labwera kutsatira mkumano omwe bungweli linali nawo lolemba lapitali.

Bungweli lati lichita izi ngati mbali imodzi yofuna kulemekeza chigamulo cha bwalo la milandu.

Pakadali pano bungweli lati lilengeza posachedwapa masiku omwe kalemberayu achitike.

Wolemba: Modester Muyaya-Blantyre

20/12/2024

.

A Milward Tobias ati akazasankhidwa kukhala mtsogoleri wa dziko lino azapanga ulimi kukhala wamakono osati odalira Khasu.

Iwo ati azalimbikitsa ulimi wa nthilira komanso oweta ziweto.

Kupititsa ulimi wa maluwa ati uzakhalanso pa mtima pawo akazasankhidwa pa udindowu.

Wolemba: Austin Katunga - Lilongwe.

20/12/2024



A Tobias ati Boma lawo lizathetsa ndale za chipani zomwe kwa nthawi yaitali zakhala zikuthandizira kusakaza chuma cha dziko lino.

Ku mbali ya za chuma, a Tobias ati ngati mtsogoleri oyima payekha azayesesa kupanga chuma cha dziko lino kupita patsogolo ndikuchepetsa ngongole za dziko lino.

Iwo atinso azachotsa ma alawansi ena omwe amapelekedwa kwa mtsogoleri wa dziko lino komanso wachiwiri wake.

Wolemba: Austin Katunga - Lilongwe.

 A Milward Tobias omwe ndi m'modzi mwa anthu omwe akufuna kuzapikitsana nawo pa udindo wa mtsogoleri wa dziko lino pa ch...
20/12/2024



A Milward Tobias omwe ndi m'modzi mwa anthu omwe akufuna kuzapikitsana nawo pa udindo wa mtsogoleri wa dziko lino pa chisankho cha chaka cha mawa, lero akukhazikitsa mfundo zomwe azachite ngati atasankhidwa pa udindowu.

Mwambowu ukuchitikira ku hotela ya Crossroads munzinda wa Lilongwe.

A Tobias omwe abwera okha pa mwambowu ndipo avala Suti yawo ya mtundu wakuda (Black), ayamba kuyankhula podzudzula boma la mgwirizano wa Tonse ati kaamba kosayendetsa bwino dziko lino zinthu zomwe ati zakhudza chuma cha dziko lino mwa zina.

Wolemba: Austin Katunga - Lilongwe.

Phungu wadera la Blantyre city south east Sameer  Sulemani wapempha sipikila wa nyumba yamalamulo a Catherine Gotani Har...
20/12/2024

Phungu wadera la Blantyre city south east Sameer Sulemani wapempha sipikila wa nyumba yamalamulo a Catherine Gotani Hara kuti awonetsetse kuti phunguyu akhale ndi chitetezo chokwanila akamatuluka mnyumbayi.

Sulemani wapeleka pemphori mnyumba yamalamulo ponena kuti achinyamata achipani cha Malawi Congress (MCP) akufuna kumupanga chiwembu panja pa chipata cha nyumba yamalamulo ndipo ali ndi maina omwe anyamata akufuna ndi phunguyi wati ndimmodzi mwanthu ofunidwawo.

Apa a Hara atsimikizila a Sulemani kuti asadandaule ali ndi chitetezo chokwanila ndipo palibe aliyense angawachite chiwembu.

Wolemba : John Makondetsa - Lilongwe.

 Pamene dziko lino likupita ku chisankho chaka cha mawa, bungwe la Tournons LA Page Malawi lati likufuna kuphunzitsa nzi...
19/12/2024



Pamene dziko lino likupita ku chisankho chaka cha mawa, bungwe la Tournons LA Page Malawi lati likufuna kuphunzitsa nzika udindo omwe zili nawo pokaponya voti komanso udindo wa zipani za ndale kuuza nzika mfundo zomwe akufuna kuzachita zikavoteredwa.

M'lembi wa mkulu wa bungweli M'busa Donnex Mateyu Ngalande wanena izi pomwe wati dziko lino silikuchita bwino pa nkhani za maufulu komanso demokalase popereka chitsanzo cha kukanizidwa kwa mabungwe kuchititsa zionetsero komanso kukanizidwa kwa zipani zina kuchita misonkhano momasuka ku madera ena mdziko muno.

Ndipo pofuna kuti ntchito yophunzitsa nzika za ufulu ndi demokalase iyende bwino, mlembiyu wati aphunzitsa adindo a mabungwe okwana 17 omwe ali pansi pa bungwe la TLP Malawi.

M'modzi mwa adindowa ndi Gloria Sabudu kuchokera ku Umodzi Youth, bungwe la achinyamata kuchokera ku tawuni ya Mbayani, wati kudzera ku upangira omwe bungwe la TLP Malawi lawapatsa, azindikira mwakuya nkhani za demokalase komanso ufulu.

Wolemba-Evance Matola Blantyre

19/12/2024



Apolisi ku Mponela m'boma la Dowa, atsimikiza zakumangidwa kwa bambo wazaka 30 Nemeri Mpanda, pomuganizira kuti amagonana ndi mwana wazaka zisanu.

M'neneri wa apolisi m'bomali Macpatson Msadala ndiye watsimikiza za nkhaniyi pomwe wati bamboyu anachita izi pa 14 December chaka chino mmudzi mwa Chinkhwiri.

Msadala wati kutsatira zomwe apolisi ya Chinkhwiri apeza, mwanayo amasewera limodzi ndi anzake anayi pafupi ndi mtsinje wa M'gona ndipo atamaliza kusewera anzakewo anachoka pamalowo ndikumusiya nzawoyo ndipo akuti Mpanda anapezelapo mwayi ndikugwililira mwanayo.

Iye wati makolo atadabwa kuti mwana wawo amachedwa kufika pakhomo, Iwo ati adayamba kumulondora ndipo adafunsa anzake omwe amasewera naye omwe adawawuza kuti amusiya akusewera ku mtsinje wa M'gona koma posakhalitaa mwanayo anafika pakhomopo akulira.

M'neneri wa polisiyi wati mwanayo anafotokoza zomwe zinamuchitikila kwa makolo ake ndipo anawandandaulira kuti akumva kupweteka kumalo ake obisika.

Makolowatu anakanena ku polisi ya Chinkhwiri za nkhaniyi ndipo zotsatira zachipatala zidaonetsa kuti mwanayu wagwililidwa.

Pakadali pano apolisi amanga bamboyu ndipo ati akaonekela kubwalo lamilandu posachedwapa kukayankha mulandu ogwililira.

Wolemba: Maureen Kanyundo.

 Anthu okhala m'dera la mfumu yayikulu ndanga komanso madera ena ozungulirila m`boma la mulanje awalangiza kusamalila ch...
19/12/2024



Anthu okhala m'dera la mfumu yayikulu ndanga komanso madera ena ozungulirila m`boma la mulanje awalangiza kusamalila chitukuko cha madzi ammipopi omwe ayikidwa mderali.

Langizoli laperekedwa ndi m'modzi mwa akuluakulu ku nthambi yowona za ngozi zogwa mwadzidzi ya DODMA a Reverend Moses Chimphepo pomwe amayendera m'mene ntchito ya madzi oyendera mphavu ya dzuwa ikuyendela mbomali.

Blessings Mikeus ndi wapampando wa Ndanga water users association ndipo wati kutsatira namondwe wa aida anthu okhala mderali ndi madera ena ozungulira analibe madzi otetedzeka kamba koti mijigo komanso zitsime zomwe amadalira zinakokoloka ndi madzi

Ntchito yobweretsa madzi yomwe ikuyendera mphavu ya dzuwa ikugwiridwa m'maboma omwe anakhudzidwa ndi namondwe wa aida ndi nthambi yowona ngozi zogwa mwadzidzidzi ndipo inayamba mchaka cha 2023 ndi thandizo la ndalama kuchokera ku African Development Bank .

Wolemba Grace Lingani

 Bungwe la National Economic Empowerment Fund Limited (NEEF),  Zomba Jali branch,  lapeleka Feteleza wangongole wa mtund...
19/12/2024



Bungwe la National Economic Empowerment Fund Limited (NEEF), Zomba Jali branch, lapeleka Feteleza wangongole wa mtundu wa NPK matumba okwana 340 kwa alimi 66 okhala kwa Jali ku Zomba.

Poyankhula pa mwambowu, mkulu woyendetsa ntchito za NEEF kudelari Flonny Kapsese wati alimi ambiri alibe kuthekera kopeza feteleza pawokha, choncho fetelezayi athandizira kuchepetsa nkhawa zomwe alimi ambiri ali nazo makamaka kudelari.
" Tiwonetsetsa kuti feteleza ameneyi walowadi mmunda ndipo tikhala tikulondoloza kuti alimiwa akubweza ngongoleyi akakolora mbewu zawo, "-Kapsese.

Kumbari yakusintha kwanyengo, Kapsese wati, alimiwa anakonzekelesedwa kulowa mabungwe a insurance omwe angathandizire kubweza ngongole zawo ngati zokolora zawo zingakhuzidwe ndikusintha kwanyengo.

Wapampando wa gulu la ulimi la amayi lotchedwa "Lonjezo" a Magret Justen ati, pali zovuta zambiri zomwe alimi akukumana nazo monga kusowa kwa zipangizo zaulimi choncho kubwera kwa ngongole ya fetelezayi kuwathandizira kuchepesa zovutazi ndikuwapasa mphamvu zoyika chidwi paulimi kuti azapindule ndikuchepesa vuto lakusowa kwachakudya mmadera lawo.

Wolemba: Laston Ingolo.

 # MzatiOnlineBungwe la Future Vision Ministry lapeleka mphoto ya ulemu kwa m'khalakale pa masewero othamanga Tereza Mas...
19/12/2024

# MzatiOnline

Bungwe la Future Vision Ministry lapeleka mphoto ya ulemu kwa m'khalakale pa masewero othamanga Tereza Master wa m'boma la Mulanje.

Poyankhula popeleka mphotoyi mkulu wa bungweli Newton Sindo wati achita izi pofuna kupeleka ulemu kwa katswiriyu pozipeleka pa luso lake komanso kwa nthawi yayitali wakhala akuimilira dziko lino ku mipikitsano ya kunja.

Sindo walimbikitsa achinyamata m'dziko muno kuti asaziyang'anile pansi pa luso lawo ndipo akhale osunga mwambo pofuna kupitisa patsogolo miyoyo yawo.

M'mau ake mkulu oyang'anira ntchito za masewero m'boma la Mulanje Sherrif Malunga wati ngati khonsolo aonetsesa kuti akupeleka chisamaliro kwa anthu luso losiyanasiyana pofuna kuti akwanilitse masomphenya awo.

Naye Tereza Master wayamikila bungweli kaamba ka mphotoyi komanso wapempha boma kuti likonze mavuto omwe anthu a luso lothamanga akukumana nawo m'dziko muno.

Bungwe la Future Vision Ministry lapeleka chikho komanso ndalama kwa katswiriyu.

Wolemba:Akim Malindi

  online  Kugwilitsa ntchito luso la wochita zisudzo komanso oyimba nyimbo ati zingathandize kuthana ndi mchitidwe wochi...
18/12/2024

online


Kugwilitsa ntchito luso la wochita zisudzo komanso oyimba nyimbo ati zingathandize kuthana ndi mchitidwe wochitilana nkhanza pakati pa anthu mdziko muno.

M'modzi wa akuluakulu a MUVI Creations Studios,Lex Masikito wati anthu a luso amagwilitsa ntchito luso lawo pofalitsa uthenga olimbikitsa chikondi, bata ndi mtendere pakati pa anthu zomwe ndizofunika pa ntchito za chitukuko cha dziko.

Masikito wati atulutsa kanema yemwe mutu wake ndi "Mtima wa nzako" yemwe akuphunzitsa anthu makhalidwe abwino ndikulimbikitsa chikhalidwe cha dziko lino.

"Tipemphe anthu azikonda kuonela kanema komanso nyimbo zomwe zimathandiza kuthana ndi mchitidwe wozipha pakati pa anthu" watelo Masikito.

Posachedwapa dziko lino limachita nawo masiku khumi akuyipa kochitilana khanza pakati pa amayi ndi abambo pa mutu woti"Tigwilane manja pothetsa nkhanza kwa amayi ndi atsikana pomwe tikuyandikira pangano la zaka 30 laku Beijing".

Wolemba Austin Muliyekha.

18/12/2024

A Malawi palibe kupuma, kutuluka CHIDO kulowa kutentha konyanyira.

Nthambi yoona za nyengo ndikusintha kwa nyengo yati anthu ayembekezere nyengo yotentha modetsa nkhawa m'madera osiyanasiyana a dziko lino kuyambira pa 19 mpaka 23 December chaka chino.

Kalata ya nthambiyi yati madera a m'chigwa cha mtsinje wa Shire mulingo wakatenthedwe ufika pa 43 digiri celcius komwe ndikutentha koposa katenthedwe koyenera ndi madigiri 6.

Madera a mphepete mwa nyanja mulingo wotentha upitilira madigiri 36 pamene madera okwera akummwera mulingo wotentha ufika pa 34 ndipo chigawo chapakati mulingo ufika pa 32.

Padakali pano nthambiyi yapereka malangizo awa: tikumbukire kumwa madzi pafupipafupi, kuvala zovala zopepuka komanso zopita mphepo komanso kupewe kugwira ntchito zolemetsa padzuwa makamaka nthawi ya pakati pa 11 and 3 koloko.

Wolemba:Evance Matola-Blantyre

18/12/2024



Mtsogoleri wazipani zotsutsa boma kunyumba yamalamulo a George Chaponda ati ndiokhumudwa kamba mtsogoleri wadziko lino sanayankhe fuso lokhudza njala yomwe yokhudza dziko lino.

A Chaponda ayankhula izi pamene mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera anatuluka mchipinda chazokambilana za aphungu akunyumba yamalamulo osayankha fuso limodzi lomwe ndilokhudza vuto la njala lomwe ndifuso lofunikila kwambiri kamba koti mdziko muno muli vuto lanjala lomwe likupangitsa anthu m'maboma ena kudya Chitedze.

Iwo ati amayembekezela kuti a Chakwera ayankha mafunso onse amene amayenela kuyankha komatu izi sizidatheke kamba mtsogoleri wazokambilana mnyumba yamalamulo a Richard Chimwendo Banda sanaonjezele nthawi kuti mtsogoleri wadziko linoyu amalizitse kuyankha mafuso onse ochokela kwa aphungu.

A Chaponda atinso sanakhutile ndimomwe anayankhila funso lomwe anafusa kuti mtsogoleri wadziko lino akuyenera kuchepetsa maulendo ake opita kunja kwa dziko lino komanso maulendo kamba maulendowa akuononga ndalama zomwe zitha kugwilitsidwa ntchito zina mdziko muno.

Wolemba : John Makondetsa - Lilongwe.

Apolisi ku Blantyre ati chipatala cha gulupu chikusunga bambo wina yemwe wakhala akulandira thandizo ndipo wachira koma ...
18/12/2024

Apolisi ku Blantyre ati chipatala cha gulupu chikusunga bambo wina yemwe wakhala akulandira thandizo ndipo wachira koma sakudziwika kwawo.

M'neneri wa polisi ya Blantyre Peter Mchiza wati bamboyu yemwe mukumuona mchithuzichi anagwidwa ndi nyesi za magetsi pa transformer ina ku Ginnery corner mwezi wa June chaka chino ndipo wakhala akulandira thandizo pa chipatalachi kufikira pano pomwe wachira.

Mchiza wati mkuluyu sakukwanitsa kutchula dzina lake komanso kwawo ndipo akumuganizira kuti adakumana ndi tsokali kaamba kodwala matenda a muubongo.

Padakali pano iye wapempha anthu akufuna kwabwino kuti ngati akumuzindikira mkuluyu apite ku nthambi ya apolisi ofufuza milandu pa Polisi ya Blantyre komwe akawathandize.

M***a kutchaya lamnya pa manambala awa: 0881025513 kapena 0991402889.

Wolemba-Evance Matola Blantyre.

 .Panachitika zopatsa chidwi mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera atangotuluka kumene m'nyumba yamalamulo komwe ...
18/12/2024

.

Panachitika zopatsa chidwi mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera atangotuluka kumene m'nyumba yamalamulo komwe amayankha mafunso kuchokera kwa aphungu m'nyumbayi!!

Aphungu ena ambali yaboma anawoneka akupita pomwe panakhala phungu wadera la kumpoto kwa boma la Rumphi a Yeremiah Chihana komwe amaoneka kuti amawayankhula mau apaderadera ati kaamba koti sanayimilire pomwe amapatsana moni ndi mtsogoleri wa dziko lino pomwe amatuluka m'nyumbayi.

Koma aphungu ena ambali yotsutsa Boma anaoneka akuteteza a Chihana kwa aphungu ambali yabomayi.

Izi ndi zina mwa zithunzi zomwe nzati inatola panthawiyi.

18/12/2024

.

Mtsogoleri wa zokambilana m'nyumba ya malamulo a Richard Chimwendo Banda alengeza kuti nthawi yomwe mtsogoleri wa dziko lino amayenera kuyankha mafunso yatha ndipo saonjezeranso nthawiyi.

Izitu zachitika ngakhale pepala la zokambilana m'nyumbayi likuonetsa kuti panasala funso limodzi kuchokera kwa phungu wa dera la Machinga East a Esther Jolobala lokhudza njala.

Izitu zakwiyitsa aphungu ena achipani cha DPP monga a Shadreck Namalomba omwe awonetsa kukhumudwa kaamba kakulephera kwa mbali ya Boma kuonjezera nthawi yofunsa mafunso.

Wolemba: Austin Katunga - Lilongwe.

18/12/2024

.

Phungu wadera la Nkhatabay North West a Julius Chione Mwase afunsa funso lomwe linadzetsa phokoso m'nyumba yamalamulo maka ku mbali yaboma.

A Chione afunsa a Chakwera ngati akudziwa kuti pano feteleza akugulidwa pa mtengo wa K105 thousand pa thumba limodzi la 50 kilogalamu kusiyana ndi mtengo wa K4,495 omwe anawalonjeza anthu panthawi yokopa anthu.

Koma poyankhapo a Chakwera ati pano anthu akumatha kugulitsa matumba awiri okha a Chimanga kuti agule Feteleza pomwe mbuyomu anthu amatha kugulitsa matumba asanu achimanga kuti agule thumba limodzi la feteleza.

Wolemba: Austin Katunga - Lilongwe.

Address

P. O. Box 372
Mulanje

Opening Hours

Monday 06:00 - 00:00
Tuesday 06:00 - 00:00
Wednesday 06:00 - 00:00
Thursday 06:00 - 00:00
Friday 06:00 - 00:00
Saturday 06:00 - 00:00
Sunday 06:00 - 00:00

Telephone

+265996492211

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mzati Radio & Tv posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Mzati Radio & Tv:

Videos

Share