Mzati Radio & Tv

Mzati Radio & Tv To Entertain, Educate and Inform .. Mzati Limited Company- is registered and licensed with the Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA).
(1)

The station broadcasts social and developmental programs on the following frequencies: 94.0Mhz & 94.2 MHz
MZATI TV-GO TV CHANNEL 811 & MDBNL 810 ZUKU CHANNEL 75

Radio online: Getmeradio.com, A2Z Malawi App, radio box & radio garden

15/01/2025




Mtsogoleri wa dziko la South Korea Yoon Suk Yeol wamangidwa pomuganizira kuti ankafuna kubweletsa lamulo loti asilikali ayendetse kaye dzikolo, lomwe limatchedwa Martial Law.

Pakhala pali mpungwepungwe mu dzikolo pomwe apolisi ndi asilikali oteteza mtsogoleriyu akhala akukaniza kuti apolisi komanso akuluakulu a bungwe lofufuza katangale wokhudza akuluakulu a m'boma, amumange.

Malingana ndi BBC, mtsogoleriyu yemwe ali ndi zaka 64 wati iye wavomeleza zakumangidwaku pofuna kuti m'dzikolo musakhale chisokonezo ndipo wanenetsa kuti kumangidwaku nkosatsata lamulo.

Achitetezo opitilira 1,000 ndiomwe akwanitsa kumanga mtsogoleriyu podula ma wire achitetezo komanso kudumba mpanda.

Bwalo la milandu lidapereka chilolezo kuti a Yun amangidwe pakafukufuku yemwe akuwaganizira kuti ankafuna abweretse lamulo lochedwa Martial Law ati kaamba kokwiya kuti aphungu otsutsa, omwe alipo ochuluka, ankakana kuvomereza mfundo zake zina m'nyumba ya Malamulo.

Pa 14 December chaka chatha aphungu anyumba yamalamulo adavota kuti a Yoon achoke pampando wa utsogoleri, (impeachment) ndipo akungodikila kuti bwalo la milandu lalilikulu livomereze kuchotsedwa kwa mtsogoleriyo.

Wolemba: Bernike Gomani

15/01/2025



Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera komanso mkazi wawo Monica Chakwera afika ku likulu la mpingo wa Providence Industrial Mission(PIM) m'boma la Chiradzulu.

Iwo alandilidwa ndi nduna yoona za maboma ang'ono, umodzi ndi chikhalidwe Richard Chimwendo Banda ndi akuluakulu ena a boma.

Mwazina mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera atsogolera mwambo oyala nkhata pa chipilala cha Chikumbutso cha malemu Rev John Chilembwe komanso mapemphero.

Wolemba:Akim Malindi-Chiradzulu

  Mtsogoleri wa chipani cha People's Development (PDP) Dr Kondwani Nankhumwa akhala nawo pa mwambo  okumbukira m'busa oy...
15/01/2025



Mtsogoleri wa chipani cha People's Development (PDP) Dr Kondwani Nankhumwa akhala nawo pa mwambo okumbukira m'busa oyamba wa mpingo wa Providence Industrial Mission(PIM) Rev John Chilembwe.

Mwambowu uchitika ku likulu la mpingowu m'boma la Chiradzulu.

Mwambowu umabweletsa pamodzi anthu osiyanasiyana monga akhilisitu a mipingo yosiyanasiyana komanso akuluakulu a ndale.

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus zarus Chakwera ndiyemwe atsogolere mwambowu.

Pakadali pano anthu ayamba kusonkhana ku mwambowu.

Wolemba:Akim Malindi-Chiradzulu

 Unduna woona za mayendedwe wati system yopanga ziphaso zoyendesera galimoto ku Directorate of Road Traffic and Safety S...
15/01/2025



Unduna woona za mayendedwe wati system yopanga ziphaso zoyendesera galimoto ku Directorate of Road Traffic and Safety Services, yomwe inawonongeka pa 6 January chaka chino itha kuyambiranso kugwira ntchito sabata ino.

Mlembi mu undunawu Engineer David Mzandu wanena izi mu kalata yomwe atulutsa lero pomwe ati pa nthawiyi nthambiyi sikukwanitsa kupanga ziphaso kapena mapepala aliwonse oyendera pa nsewu.

Undunawu wati pakadali pano ukukonza vutoli ndipo walangiza adindo onse okhudzidwa kukhwimitsa malamulo apanseu.

Wolemba- Modester Muyaya Blantyre.

 .Katswiri osunga ndi kufotokoza mbiri John Gunde waonetsa kukhumudwa kuti dziko lino likusalira pokwanilitsa zinthu zom...
15/01/2025

.

Katswiri osunga ndi kufotokoza mbiri John Gunde waonetsa kukhumudwa kuti dziko lino likusalira pokwanilitsa zinthu zomwe anthu omwe anamenyera ufulu wa dziko lino amafuna kuti zizichitika.

Gunde wayankhula izi pomwe lero dziko lino likukumbukira malemu m'busa John Chilembwe yemwe anamenyana ndi asamunda achizungu pofuna kuti anthu achikuda a m'dziko muno akhale ndi ufulu ozilamulira okha.

Gunde wafotokoza m'busa John Chilembwe kuti anali olimba mtima ndipo ndi amene anapangitsa atsogoleri ena monga mtsogoleri oyamba wa dziko lino malemu Dr Hastings Kamuzu Banda kukhala nyonga zolimbana ndi azungu pofuna ufulu.

Komabe Gunde wati dziko lino silikukwanilitsa moyenera zinthu zomwe Chilembwe amafuna monga kukhala ndi dziko la anthu osapondelezana, pomwe nawo umphawi komanso njala zikupitilira kukhudza dziko lino.

Apa Gunde wapempha Boma kuganizila zokweza malo a PIM ku Chiradzulu potengera kuti malowa ndi a mbiri yofunikira.

Malingana ndi mbiri yomwe ilipo, m'busa John Chilembwe anabadwa m'chaka cha 1871 ndipo anaphedwa akumenya nkhondo yolimbana ndi asamunda m'chaka cha 1915.

Wolemba: Austin Katunga - Lilongwe.

  Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wafika munzinda wa Blantyre kuchokera ku Lilongwe, kudzera pa bwalo la nd...
14/01/2025



Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wafika munzinda wa Blantyre kuchokera ku Lilongwe, kudzera pa bwalo la ndege ya Chileka.

Dr Chakwera omwe afika ndi mkazi wawo Monica alandiridwa ndi nduna yazofalitsa nkhani Moses Kunkuyu ndi akuluakulu ena achipani cha Malawi Congress (MCP).

Iwo akuyembekezeka kukatsogolera mwambo wa chikumbutso cha malemu m'busa John Chilembwe mawa ku Providence Industrial Mission
( PIM)m'boma la Chiradzulu.

Wolemba: Evance Matola-Blantyre.

14/01/2025



Bungwe logawa madzi m'chigawo cha pakati la Central Region Water Board (CRWB) lati likugwira bwino ntchito yake yogawa madzi m'chigawochi ngakhale pali mavuto ena omwe akukumana nawo.

Mkulu wabungweli a John Makwenda ayankhula izi pamene kwatsala chaka kuti bungweli limazitse ntchito zomwe linayelekeza kuti lipanga muzaka zisanu zomwe ndi kuyambira m'chaka cha 2021 kufikira 2026.

Poyankhula ndi Mzati a Makwenda ati ndiokondwa kuti bungwe lawo lakwanitsa kugwila ntchito zikulu zikulu zomwe bungwe lawo linali nazo kuyambira mchaka cha 2021 monga kumanga malo osungila madzi m'boma la Dowa, ku Nkholongo komaso Damu lalikulu m'boma la Kasungu zomwe zithandizile kuchepetsa vuto lakusowa kwa madzi mchigawo chapakati.

Iwo ati akuganiza zokambilana ndi unduna wazachuma komanso unduna owona za madzi kuti athandize bungweri kumagawo azachuma kuti likwanitse masomphenya othana ndivuto lakuvuta kwa madzi m'maboma amchigawo chapakati.

Mchaka cha 2021 bungwe la Central Region Water Board linakhadzikitsa ndandanda wantchito za mzakazisanu zomwe cholinga chake ndikuthana vuto lakuvuta kwa madzi m'maboma amchigawo chapakati pofika chaka cha 2026.

Wolemba : John Makondetsa - Lilongwe.

14/01/2025

Mtsogoleri wa dziko ino Dr Lazarous Chakwera amupempha kuunikila mozama Mfundo zomwe bungwe la atsogoleri amipingo la Public Affairs Committee (PAC) apeleka pofuna kuwonetsetsa kuti zolakwikwa zomwe bungweli lanena zofuna kukonzedwa zikonzedwe nsanga.

Izi ndi malingana ndi katswiri olankhulapo pa nkhani zandale m'dziko muno George Phiri yemwe wati mtsogoleriyu akuyenera kukhala pansi pamodzi ndi anthu omwe anawasankha kukhala alangizi ake ndikuunikila bwino magawo onse omwe akuyenera kukonzedwa zinthu zisanafike poipa.

Phiri wati aka sikoyamba kuti atsogoleli abungweri akumane ndi mtsogoleriyi koma mfundo zomwe bungweli limapeleka kwa mtsogoleriyu sizimaphula kanthu kaamba koti palibe chomwe mtsogoleriyu amatolapo pamikumano yoteleyi zomwe zili zinthu zodandalitsa kwambiri.

Iye wati Ali ndichikhulupiliro kuti pakadali pano mtsogoleri wa dziko linoyu akhala pansi ndikupeza zina mwanjira zothanilana ndumavuto ochuluka omwe akhudza dziko lino monga vuto la njala komanso kusowa kwamafuta a galimoto.

Zina mwa mfundo zomwe bungweli lapempha mtsogoleriyu kuti akonze ndimonga kumangidwa kwa atsogoleri osiyanasiyana azipani zotsutaa boma komanso bungweli lapempha mtsogoleriyu kuti akhale pansi ndi nduna zake kuti zichepetse maulendo akunja zomwe zikupitiliza kusakazika kwa chuma chaboma pambali poti dziko ino likukumananso kale ndumavuto azachuma.

Wolemba: Maureen Kanyundo

14/01/2025



Apolisi m'boma la Thyolo amanga anthu asanu ndi atatu kaamba kowaganizira kuti akukhudzidwa ndikusowa kwamatumba a Cement okwana 70 andalama zokwana 3 million kwacha omwe anasowa pa sukulu ya pulaimale ya Ntawa m'bomali.

M'neneri wa apolisi m'bomali Rabecca Kashoti wati pa 30 December chaka chatha a Kingsly sitiya omwe ndi M'phunzitsi wankulu pasukulu ya Ntawa analandila uthenga kuchokela kwa wachiwiri wake kuti matumbawa akusowa kunyumba imene amasungilako katundu pasukuluyi.

Izi zinapangitsa Sitiya kuitanitsa nkumano wadzidzidzi komwe zinadziwika kuti ena mwa akuluakulu apasukuluyi akukhudzidwa ndi kusowa kwa matumbawa ndipo nkhaniyi idakatulidwa ku polisi ya Thyolo ndipo apolisi atayendela pamalowa anapeza kuti nyumba yosungila katunduyi siinaonongedwe kapena kuthyoledwa.

Kashoti wati omangidwawa ndi Samuel Chibisa, Cecilia Nyowera, Shyreen Moyenda, Christopher Danken, Trouble Makina, Limbaugh Petro, Patrick Makombe, Komanso Enerst Mathiya ndipo akhala akukaonekela kubwalo lamilandu posachedwapa.

Wolemba Maureen Kanyundo

14/01/2025




Vuto lakusowa kwa madzira ankhuku lakhudza misika ina m'dziko la America.

Malingana ndi CNN, vutoli ladza chifukwa cha nthenda ya Influenza yomwe yapha nkhuku za madzira zoposa 17.2 million pakati pa miyezi ya November ndi December 2024 mdzikolo.

Wailesiyi yati mwachitsanzo kampani ya Publix yomwe ili ndi magolosale okwana 1500 inadziwitsa makasitomala ake kuti yakhudzidwa ndi vuto lakusowa kwa madzira.

CNN yati vutoli lachititsa kuti mitengo ya madzira pa dazeni ifike pa 4.33 dollars zomwe ndi K7,577.05, ndalama yakuno ku mudzi.

Wolemba-Evance Matola.

 Bungwe la Wildlife and Environmental Society of Malawi (WESM) lati ligawa mbande zamitengo zoposera 3 thousand mwa ulel...
14/01/2025



Bungwe la Wildlife and Environmental Society of Malawi (WESM) lati ligawa mbande zamitengo zoposera 3 thousand mwa ulele kwa magulu ndi anthu omwe akufuna kubzala mitengo munyengo ya chaka chino m'boma la Mulanje.

Mlangizi wophunzitsa anthu zakasamalidwe ka zachilengedwe kubungweli m'boma la Mulanje a Clement Selenje auza Mzati kuti ntchito yagawa mbandezi akuyigwira molumikizana ndi bungwe la Mulanje Mountain Conservation Trust (MMCT).

Selenje wati pakadali pano bungweli lakwanitsa kugawa mbande zamitengozi kwa ophunzira am'sukulu zosiyanasiyana, makalabu akumudzi komanso anthu ena omwe ali ndi chidwi chobzala mitengo munyengo ino.

Iye watinso ndiwokondwa ndi chiwerengero cha anthu omwe akuzatenga mbandezi zomwe ati zikupereka chilimbikitso kuti mitengo yochuluka ibzalidwa m'bomalo munyengo yobzala mitengo ya chaka chino.

Nyengo yobzala mitengo yachaka chino inayamba pa 15 December 2024 ndipo ikuyembekezeka kuzafika kumapeto pa 15 April chaka chino.

Olemba: Innocent Mutipe.

  Bungwe la Limbe Rotary Club aliyamikira kamba kotengapo gawo lokweza maphunziro m'dziko muno.M'phunzitsi wamkulu pa su...
14/01/2025



Bungwe la Limbe Rotary Club aliyamikira kamba kotengapo gawo lokweza maphunziro m'dziko muno.

M'phunzitsi wamkulu pa sukulu yoyendera ya sekondale ya Addolorata m'boma la Thyolo Esther Chanunkha ndiye wayamikira bungweli pomwe lapereka njinga kwa ophunzira a pa sukuluyi lolemba sabata ino.

Malinga ndi a Chanunkha, njinga zomwe zaperekedwazi zithandiza pankhani ya mayendedwe kwa ophunzira.

Poyankhulapo wa pampando wa komiti yapasukuluyi Damiano Symoni Maloza wati kubwera Kwa njingazi kupangitsa kuti atsikana ambiri akhale ndi chidwi pa maphunziro awo.

M'mawu ake m'modzi mwa ophunzira omwe walandira nawo njinga yemwe ali form 3 Eunice Maliwa wati njinga imuthandiza kuchepetsa ulendo wawutali omwe amayenda zomwe pena zimapangitsa kuti azifika mochedwa ku sukulu.

Njinga zokwana 109 ndizomwe sukulu ya Addolorata yalandira kuchokera mchaka cha 2020.

Wolemba Chrispine Dzimbiri.

 Nduna yazofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu achenjeza alimi omwe alandira zipangizo zaulimi pangongole kuchokera ku bungwe...
14/01/2025



Nduna yazofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu achenjeza alimi omwe alandira zipangizo zaulimi pangongole kuchokera ku bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) kuti apewe mchitidwe ogulitsa zipangizozi kwamavenda ponena kuti izi zimakolezera njala m'dziko.

A Kunkuyu atinso anthu apewe kutenga ngongoleyi ngati chida chopangira ndale ponena kuti aliyense yemwe ali ndikuthekera kotenga ngongoleyi akupindula.

Ndunayi yayankhula izi lero ku Thondwe m'boma la Zomba pa mwambo ogawa Feteleza kwa alimi kuchoka ku bungwe la NEEF.

Mau ake, mkulu wa bungwe la NEEF a Humphrey Mdyetseni ati pofika pano anthu oposa 40,000 apindula kale ndi ngongoleyi yomwe ikuyembekezeka kufikira anthu 400,000.

Iwo atsindikanso kuti m'chaka cha ulimi cha 2025 komanso 2026, ndondomeko yogawa zipangizo zangongoleyi izayamba msanga pofuma kupeleka mwayi kwa alimi kuti azikonzekeletse.

Pakadali pano, mfumu yaikulu Mulumbe yakuderali yapempha onse omwe atenga ngongoleyi kuti azakumbukire kubwenza.

Wolemba: Laston Ingolo.

 Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera mawa pa 15 January 2025 akuyembekezeka kukakhala nawo pa mwambo okumbukira...
14/01/2025



Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera mawa pa 15 January 2025 akuyembekezeka kukakhala nawo pa mwambo okumbukira m'busa John Chilembwe m'boma la Chiradzulu.

Mlembi mu ofesi ya mtsogoleri ndi nduna a Collen Zamba ndiwo atsimikiza izi kudzera m'kalata yomwe atulutsa lero.

Pakadali pano, wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za mpingo wa Providence Industrial Mission (PIM) Davies Kambewa wati zokonzekera zonse za mwambowu zafika kumapeto.

Kambewa wakumbusanso atsogoleri andale komanso owatsatira awo kuti asazavale nsalu zachipani pobwera kumwambowu potengera kuti mwambowu ndi wadziko.

Mwambo okumbukira m'busa John Chilembwe wachaka chino uchitikira pa muti oti "Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu", omwe ndi mau ochokera m'buku la Mateyu 11 vesi 28.

Wolemba: Austin Katunga - Lilongwe.

  Nthambi yoona za nyengo ndikusintha kwa nyengo yati anthu ayembekezere mvula ya mphamvu yomwe iyambe kugwa lero m'made...
14/01/2025



Nthambi yoona za nyengo ndikusintha kwa nyengo yati anthu ayembekezere mvula ya mphamvu yomwe iyambe kugwa lero m'madera ena.

Nthambiyi yanena izi kudzera mu kalata yomwe yatulutsa pomwe yati kawuniwuni wawo akuonetsa kuti chiopsezo ndichochepa kwambiri kuti mdziko muno mufika namondwe otchedwa DIKELEDI.

Kalatayi yomwe yatsindikizidwa lero yati namondweyu yemwe wachepa mphamvu, adakalibe pa nyanja ya mchere yapakati pa Madagascar ndi Mozambique maka chifupi ndi Angoche chifupi ndi Nampula.

Wolemba-Evance Matola-Blantyre.

 Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Michael Usi wanyamuka m'dziko muno kupita ku Mozambique komwe akuyembekezeka ...
14/01/2025



Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Michael Usi wanyamuka m'dziko muno kupita ku Mozambique komwe akuyembekezeka kukakhala nawo pa mwambo olumbilitsa mtsogoleri watsopano wa dzikolo a Daniel Chapo.

A Usi anyamuka kudzera pa bwalo la ndege la Kamuzu munzinda wa Lilongwe lachiwiri sabata ino.

Malingana ndi kalata kuchokera ku unduna woona ubale wa dziko lino ndi mayiko ena, a Usi akuyembekezeka kubwelera m'dziko muno lachinayi sanata ino kudzera pa bwalo la ndege la Chileka munzinda wa Blantyre.

Kwakhala kuli mpungwempungwe m'dziko la Mozambique kuchokera m'mwezi wa October 2024 pomwe anthu anaponya voti, pomwe mtsogoleri otsutsa boma m'dzikolo a Venancio Mondlane akuti sakugwirizana ndi zotsatira zachisankhochi.

Wolemba: Austin Katunga - Lilongwe.

 Phungu wadera la pakati m'boma la Ntcheu Dr. Albert Mbawala tsopano ndi wapampando wakomiti yoona zamalamulo kunyumba y...
14/01/2025



Phungu wadera la pakati m'boma la Ntcheu Dr. Albert Mbawala tsopano ndi wapampando wakomiti yoona zamalamulo kunyumba yamalamulo.

A Mbawala asankhidwa paudindowu kulowa m'malo mwa a Peter Dimba omwe posachedwapa asankhidwa kukhala wachiwiri kwa nduna ya zamtengatenga.

Ndipo a Agnes Nkusankhoma omwe ndi phungu wadera la kumwera kwa Boma la Mchinji asankhidwa kukhala wachiwiri kwa wapampando wakomitiyi.

Wolemba: Austin Katunga - Lilongwe.

 Bungwe la Citizen for Justice and Equity lapempha mlangizi wa boma pa nkhani zamalamulo komanso adindo ena okhudzidwa k...
14/01/2025



Bungwe la Citizen for Justice and Equity lapempha mlangizi wa boma pa nkhani zamalamulo komanso adindo ena okhudzidwa kuchitapo kanthu mwansanga, pofuna kuti ntchito za bungwe la Agricultural Development and Marketing Corporation (Admarc) ziyambilenso kuyenda m'dziko muno.

Izi zikudza pamene posachedwapa bwalo la milandu linalamula kuti makaunti a bungwe la Admarc atsekedwe ndipo kutinso katundu wake wina alandidwe, pofuna kukakamiza bungweli kupeleka ndalama zachipukuta misonzi zokwana K25 billion kwa ogwira ntchito ake osachepera 3000 omwe anachotsedwa ntchito m'chaka cha 2023.

Poyankhula ndi Mzati, mneneli wa bungwe la Citizen for Justice and Equity a Agape Khombe wati kutsekedwa kwa makaunti a bungwe la Admarc kupangitsa kuti ntchito zake zina monga zogulitsa Chimanga m'misika yake ikhudzidwe, zinthu zomwe zingaonjezere njala yomwe ilipo kale m'dziko muno.

Apa Khombe wapempha mlangizi wa Boma pankhani zamalamulo a Thabo Chakaka Nyirenda komanso adindo onse okhudzidwa kuwonetsetsa kuti athana ndi nkhaniyi pofuna kuti ntchito za bungwe la Admarc ziyambilenso kuyenda bwino.

Masiku apitawa, ma Sherifu ochokera ku bwalo la milandu analanda galimoto komanso kutseka ma ofesi ena abungweli pofuna kuwumiliza bungweli kukwanilitsa chigamulochi.

Wolemba: Austin Katunga - Lilongwe.

Address

P. O. Box 372
Mulanje

Opening Hours

Monday 06:00 - 00:00
Tuesday 06:00 - 00:00
Wednesday 06:00 - 00:00
Thursday 06:00 - 00:00
Friday 06:00 - 00:00
Saturday 06:00 - 00:00
Sunday 06:00 - 00:00

Telephone

+265996492211

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mzati Radio & Tv posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Mzati Radio & Tv:

Videos

Share