16/11/2023
TIYENI TIWACHENJERERE
Kuti nkhaniyi timvetsetse bwino choyamba tiyeni tidziwe tathauzo la mau ak*ti Kuchenjerera.
"KUCHENJERERA ndiko kupanga pulani mwachinsisi ndicholinga chak*ti umulepheretse mzako kupeza zithu zabwino zimene amayenera kulandira ngati mphatso kapena madalitso ake"
๐ Exodus 1:9-10 "Ndipo ananena ndi anthu ace, Taonani, anthu, ndiwo ana a Israyeli, achuluka natiposa mphamvu"
10 "Tiyeni tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani anthu ikafika nkhondo, ndikulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo"
Pa ๐ Exodus 1:9-10 tikupeza nkhani yomwe ana a Israyeli idawachitikira ali mudziko la Igupto. Baibulo lik*tiuza k*ti ana a Israyeli ali mu dziko la Igupto mfumu Faraoh panthawiyo idazindikira k*ti ana a Israyeli achuluka kwambiri komaso anali amphamvu kwambiri kuposa eni dziko Aigupto.
Tsono mfumu Farao poona mphavu komaso kuchuluka kwa ana a Israyeli anafika pochita mantha, poganizira k*ti mwina ana a Israyeli chifukwa cha mphavu komaso kuchuluka kwawo tsiku lina adzathira nkhondo m'dziko la Igupto ndikuligonjetsa.
๐ Exodus 1:13 "Ndipo Aigupto anawagwilitsa ana a Israyeli nchito yosautsa"
Faraoh pofuna k*ti mtundu wa Israyeli usakhaleso chiopsezo ku dziko lawo, Iye adaganiza zowachenjerera ana Israyeli, powasandutsa akapolo.
Faraoh pakusundutsa ana a Israyeli kukhala akapolo, kumeneku kunali kuwachenjerera koopsa kumene kunapangitsa ana Israyeli ngakhale kusiya kudalira Yehova Mulungu wawo amene amawapatsa madalitso komaso mphavu zogonjetsera adani awo.
Abale ndi Alongo, tamvetserani Faraoh tikumukambayu akuimila Satana ndipo ana a Israyeliyo ndi Iweo ndi Ine.
Abale mukuenera kuzindikira k*ti, Satana akauchenjerera moyo wa munthu, Iye amakhala wawona madalitso ochuluka omwe Mulungu adamupatsa munthuyo
๐ Yohane 8:34 "Yense wakuchita tchimo ali kapolo wa tchimolo"
Abale Satana akauchenjerera moyo wamuthu, munthuo amafika posandutsidwa kapolo wa tchimo.
Komatu choopsa ndichak*ti, Satana akangokwanitsa kumupanga muth