
25/06/2025
Bungwe lowona za zisankho la Civil Society Elections Integrity Forum (CSEIF) lati likhazikitsa ndondomeko yobweretsa poyera maina a zipani zandale komanso atsogoleri ake omwe akhale akulimbikitsa m'chitidwe wa ziwawa pa ndale panthawi ya misonkhano yokopa anthu pofuna kuti anthuwa adzipatsidwa zilango zokhwima.
Izi zikudza pomwe kwangotsara sabata ziwiri kuti bungwe loyendetsa zisankho la MEC litsegulire nyengo ya misonkhano yokopa anthuyi.
Wapampando wa bungweli Benedicto Kondowe wati kudzera ku ndondomekoyi bungweli lizichita kafukufuku wokhudza nkhanizi ndi kutulutsa malipoti ake.
Katswiri pankhani zandale Dr. George Chaima wati pakadali pano zipani zina zikukhudzidwa ndi m'chitidwe wa ziwawa pa ndale ndipo wati akuyembekezeka kuti ndondomekoyi ithandiza kuchepetsa izi panthawiyi.
Wolemba: Billy Amos