30/12/2024
ZINA MWAZIFUKWA ZIMENE NDINASIYIRA KUIKA NKHANI ZA MAGANYU NDI MWAYI WA NTCHITO.
Mmiyezi ya July , August ndi September mabwana ambiri anali kufuna anthu oti aziwathandidza ntchito mmakomo, mmashop ndi mminda yawo , ena amapanga business, ena amalima January to December, ena alinso ndi zochita zawo zimene zimafunika thandizo ndi MPHAMVU za anthu ena.
Mmiyezi yokhayi ndinakwanitsa kulumikizisa anthu 19 ku mabwana 7 ndipo sindimaiwala kuti mmodzi mwa Iwo anali Mnyamata wa zaka 25 amene anandipempha kuti ndimusakire ntchito. Pa anthu amenewa anthu 9 anandilowetsa mmilandu yosiyanasiyana. Ena anabako kumene ndinawalumikizisako ndipo mnyamata amene amati anavutika kwambiri anayambanso za dama ndi mkazi waabwana ake mwezi woyamba womwewo. Zonse zikamachitika mabwanawo amabwera Kwa ine kuti ndinalakwitsa kuwapatsa anthu osalongosoka. Ena mpaka kundilipiritsa katundu amene anaberedwa.
Ena kutukwana. Kuchokera pompo chidwi mwa ine chinachoka.
Panopa ndimaponya za ntchito mwa apo ndi apo ndipo basi sindiikaponso mtima ngati kale paja. Ntchito zimene ndimaponya zimakhala zoti munthuyo safunika ineyo kuti ndimuimire ngati mboni.
Mwina mtsogolomu titha kudzayambiranso komano mu njira ina osati ineyo kukhala mkhalapakati.