Ntunda Osema News Online

Ntunda Osema News Online Follow this page and you get more news (NTUNDA OSEMA NEWS ONLINE)

Oops!Bus ya company ya Sososo yachita ngozi mu nkhalango ya Chikangawa m'boma la Mzimba after the driver failed to negot...
27/12/2024

Oops!
Bus ya company ya Sososo yachita ngozi mu nkhalango ya Chikangawa m'boma la Mzimba after the driver failed to negotiate a corner. Will keep you updated.

25/12/2024

HAPPY MERRY CHRISTMAS DAY TO YOU ALL 🎄🎅🧑‍🎄

An Immigration Officer, Constable Francisco Kavina, has died while five prison officers and their spouses have escaped w...
21/12/2024

An Immigration Officer, Constable Francisco Kavina, has died while five prison officers and their spouses have escaped with various degrees of injuries after a vehicle they were travelling in overturned in Chikwawa escarpment today.

"Kavina, aged 31, an Immigration Officer at Nsanje office was driving a service vehicle registration number MG 696AL with 10 passengers on board.

"Upon arrival at Chimbuto village, the driver failed to negotiate a corner, the vehicle swerved to the extreme offside of the road where it overturned," explained Sergeant Dickson Matemba, Chikwawa police spokesperson.

According to Sergeant Matemba the passengers were rushed to Chikwawa District hospital for medication but the driver was pronounced dead whilst receiving medical treatment.

Meanwhile Sergeant Matemba says one of the passengers Inspector Nowa Saulos 54, of Therere village under Traditional Authority Malemia in Nsanje is still receiving treatment at the facility, while eight others have been treated as out patients.

(by Alfred Guta-Nsanje:12/21/24)

Anthu osachepera khumi ndi anayi afa komanso ena 255 avulala pa zilumba za Mayotte m’nyanja ya mchere ya Indian chifukwa...
15/12/2024

Anthu osachepera khumi ndi anayi afa komanso ena 255 avulala pa zilumba za Mayotte m’nyanja ya mchere ya Indian chifukwa cha namondwe wa Chido.

Namondweyu akugwetsa mvula yochuluka ndi mphepo yamphamvu imene ikuwomba pa liwiro loposa makilomita 220 pa ola limodzi.

Mtundawu ndi chimodzimodzi kuchoka ku Blantyre kukafika ku Dedza.

Zilumba za Mayotte ziri pakati pa mayiko a Mozambique ndi Madagascar ndipo ndi za dziko la France.

Nduna ya za m’dziko ku France, a Bruno Retailleau, yawuza France24 kuti zitenga masiku kuti chiwerengero chenicheni cha anthu okhudzidwa chidziwike.

Ndunayi yati chiwerengerochi chikhala chokwera chifukwa chakuti nyumba zambiri zagwa ndipo anthu ochuluka sakudziwika kumene ali.

Namondweyu wazulanso ndi kugwetsa mitengo, mwakuti nyumba zoposa 15,000 ziribe magetsi.

Padakali pano namondweyu ali m’dziko la Mozambique kumene wayambanso kale kuwononga.

Pali chiyembekezo chakuti madzulo ano ndi mawa namondweyu afikanso m’mayiko a Malawi ndi Zimbabwe.

Wolemba Ronald Mpaso
Chithunzi cha France24

CHENJEZO LOKHUDZA NAMONDWE WAMPHANVU CHIDOTsiku ndi nthawi yosindikizira: Lachisanu pa 13 December, 2024; 15:00pm.Kusind...
13/12/2024

CHENJEZO LOKHUDZA NAMONDWE WAMPHANVU CHIDO

Tsiku ndi nthawi yosindikizira: Lachisanu pa 13 December, 2024; 15:00pm.Kusindikiza kwa nambala : TC2024/25-05

Nthambi Yoona za Nyengo ndi Kusintha kwa Nyengo ikudziwitsa mtundu wa a Malawi kuti Namondwewamphanvu CHIDO yemwe ali m’nyanja ya m’chere ya India kumpoto cha kumvuma kwa chilumba cha Madagascar akupitilira kukula mphamvu ndipo ali pa mlingo wa 960 hPa tsopano akuyenda pa liwilo
la 22km/h. Koma liwilo la mphepo likumatha kufika 250km/h nthawi zina.
Kauniuni wa namondweyu akuonetsa kuti apitilira kukhala wamphanvu m’maola 36 akubwerawa asanafike pafupi ndi doko la Nacala Lamulungu pa 15 December 2024 lomwe lili pa mtunda otalika pafupifupi 500 km kuchokera malire a boma la Mulanje. Pakali pano chiyembekezo choti zotsatira Namondwe CHIDO afika ku Malawi kuno chili pa 70%. Madera omwe akuyembekezereka kukhudzidwa kwambiri ndi awa: Mangochi, Machinga, Phalombe, Balaka, Mulanje, Blantyre,Thyolo, Chiradzulu, Zomba, Mwanza ndi Neno.

 Anthu anayi kuphatikizapo mayi wazaka 65 avulazidwa kutsatira mkangano olimbirana Dambo omwe unabuka pakati pa anthu a ...
09/12/2024



Anthu anayi kuphatikizapo mayi wazaka 65 avulazidwa kutsatira mkangano olimbirana Dambo omwe unabuka pakati pa anthu a mmudzi mwa Namjawa komanso Mopiha kudera la mfumu yaikulu Mtumbwinda ku Machinga.

Mfumu yaikulu Mtumbwinda yatsimikiza za nkhaniyi ponena kuti kusamvetsetsana kunadza pomwe anthu a mmudzi mwa Mopiha anakwiya kaamba koti anthu a mmudzi mwa Namjawa adalowerela malo awo olima.

Malinga ndi a Mtumbwinda mikangano ya malo pakati pa anthu a midzi iwiriyi siikukata pomwe idayamba pakanthawi ngakhale kuti mafumu akhala akulowerelapo.

"Nkhani za mikangano ya malo pakati pa anthu amenewa nzapakanthawi ndipo mmbuyomu nkhaniyi idatengedwera kubwalo la milandu la mfumu yaikulu ya Yao Paramount Chief Kawinga ndipo adagamula kuti malowa ndi a anthu a mmudzi mwa Mopiha koma mkangano ukupitirilabe"Atero a Mtumbwinda.

Wolemba: Blessings Tambala.

Gogo Gumba atisiyaMfumu Gumba ya mu boma la Mchinji yamwalira mmawa wa lachinayi pachipatala cha Kamuzu Central mu mzind...
06/12/2024

Gogo Gumba atisiya

Mfumu Gumba ya mu boma la Mchinji yamwalira mmawa wa lachinayi pachipatala cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe.

Malemu gogo Gumba amwalira atadwala kwakanthawi kochepa.

A gogo Gumba, dzina lenileni Faneli Lemekani, adagonekedwa m’chipatala cha pa boma la Mchinji asanatumizidwe ku chipatala chachikulu cha Kamuzu, komwe amwalira.

Thupi la gogo Gumba lifika ku Mchinji lachisanu pa December 6, ndipo thupi lawo likafikira ku likulu lawo ku Khwazi.

Mwambo oyika mmanda gogo Gumba ukuyembekezeka kuchitika Loweruka pa December 7.

Malinga ndi mmodzi mwa a ku banja, a Kachere Chibweya, gogo Gumba anabadwa pa January, 19, 1971.

Chibweya adati banja lachifumu likugwira ntchito limodzi ndi akuluakulu a khonsolo kuti apereke mwambo wa maliro a mfumu oyenerera.

Malipoti akusonyeza kuti mfumu Gumba adakwezedwa pa udindo wa mfumu yayikulu pa November 8 chaka cha 2022.

Iwo asiya ana 7.

 Mkulu wina mdziko la Nigeria Ismail Usman wadziombera ndi mfuti pomwe amayesa mankhwala ake azisamba omwe amati amatete...
30/11/2024



Mkulu wina mdziko la Nigeria Ismail Usman wadziombera ndi mfuti pomwe amayesa mankhwala ake azisamba omwe amati amateteza munthu kuti asawomberedwe ndi mfuti.

Lipoti la nyumba youlutsa mawu ya DW lati, mkuluyu anazipaka mankhwala akewo ndipo anatenga mfuti ndikuziombera pomwe amaganiza kuti chipolopolo sichilowa poti iye wakhwima.

Koma chipolopolo sichidagonje ndi mankhwalawo ndipo chinalowa pa mimba ndipo pano mkuluyi ali mu ululu wazaoneni.

Apolisi aku Nigeria ati mkuluyu akangochira azengedwa mlandu wopezeka ndi mfuti mopanda chilolezo komanso mlandu wofuna kudzipha.

(Wolemba: Blessings Gondwe)

29/11/2024



Mphezi yapha anyamata anayi omwe amaphuzira pa sukulu ya Sekondale yoyendera ya Kaungwe ku Mponela m'boma la Dowa.

Ofalitsa nkhani za polisi ya Mponela, a Macpatson Msadala atsimikizira za ngoziyi ndipo ati omwalirawa ndi a Fatsani Chimkwamba a fomu 1, a Precious Singini a fomu 3, Alkangel Thomas fomu 1, ndi Amos Chapingasa wa fomu 1.

Mlangizi wa maphuziro m'dera la maphuziro la Kachulu, a George Mkambeni auza Times 360 Malawi kuti ngoziyi yachitika madzulo omwe ano pomwe kudelari kunabwera mvula yamphepo yomwe inabwera ndi Mphezi.

Iwo ati Anyamata khumi omwe amaphuzira pa sukuluyi amakhala nyumba imodzi koma mwangozi mpheziyi inawomba Anyamata asanu ndi mmodzi ndipo mwa asanuwo anayi amwaliliratu ndipo awiri awagoneka pa chipatala cha Mtengowanthenga komwe akulandira thandizo la mankhwala.

Wolemba Mphatso M'bang'ombe

MVULA YAMPHANVU IKUYEMBEKEZEKA KUGWA MADERA AKU MPOTO KUMATHERO ASABATAYINthambi yowona za nyengo yati madera am'chigawo...
29/11/2024

MVULA YAMPHANVU IKUYEMBEKEZEKA KUGWA MADERA AKU MPOTO KUMATHERO ASABATAYI

Nthambi yowona za nyengo yati madera am'chigawo chaku mpoto ayembekezere nyengo ya mphepo, yamitambo komanso mvula ya mabingu usiku uno ndi mawa m’mawa.

Malingana ndi nthambiyii nyengoyi ikuyembekezeka kupitilira mawa masana.

Nthambiyi ikuchenjeza anthu kukhala atcheru pofuna kuteteza moyo komanso katundu kamba koti nyengoyi ili ndi kuthekera kobweretsa chiopsezo cha mphezi, mphepo yamkutho komanso madzi osefukira.

28/11/2024



Anthu oposa 2.4 miliyoni ndi amene alembetsa mu kaundula wa mavoti mu gawo kachiwiri la kalembera.

Bungwe la Malawi Electoral Commission ndilo lalengeza izi ponena kuti kawuniwuni woyamba waonetsa kuti anthu onse amene alembetsa ndi okwana 2,422, 595.

Gawo lachiwiri lakalemberayu limene latha sabata yatha, limachitika m'maboma a Blantyre, Dowa, Kasungu, tawuni ya Luchenza, Mchinji, Nkhata Bay, Ntcheu, Rumphi, Thyolo komanso Zomba.

Pakadali pano gawo lachitatu la kalemberayu layamba lero.

Wolemba Isaac Salima

26/11/2024



Anthu atatu afa ku Nsanje, mphenzi zitawaomba malo osiyanasiyana Lamulungu kutsatira mvula ya mphepo yomwe inagwa m'bomali.

Times 360 Malawi yapeza kuti mayi wina kwa Nthondo m'dera la mfumu yayikulu Tengani komanso ana awiri kwa mfumu yayikulu Malemia afa atawombedwa ndi mphenzi.

Mkulu owona ngozi zogwa mwadzidzi ku khonsolo ya Nsanje a Daniel Mandala atsimikizira za izi.

"Talandiladi ma lipoti amenewa koma kwa mfumu yayikulu Malemia ndi munthu m'modzi yemwe wamwalira ndipo ena avulala," atero a Mandala.

Malinga ndi a Mandala, chiwelengero cha omwe avulala sichinadziwike kaye.

Wolemba: Innocent Kalikokha

SAD NEWSA hit and run driver has killed Sub Inspector Benson Mtota at Aret Police Roadblock along Lilongwe-Mchinji M12 R...
24/11/2024

SAD NEWS
A hit and run driver has killed Sub Inspector Benson Mtota at Aret Police Roadblock along Lilongwe-Mchinji M12 Road.

While performing his duties at the roadblock, he was hit by an unregistered vehicle which was cruising from the direction of Njewa towards Kaunda Roundabout.

Mtota, aged 45, was from Villageheadman Khumbudza, Traditional Authority Kawinga in Machinga district.

MHSRIP

Breaking news: Moses Kunkuyu wagendedwa ku Ndirande, apolisi athila utsi okhetsa msoziKunali chipwirikiti mphindi zochep...
22/11/2024

Breaking news: Moses Kunkuyu wagendedwa ku Ndirande, apolisi athila utsi okhetsa msozi

Kunali chipwirikiti mphindi zochepa zapitazi ku Ndirande pamsika waukulu pomwe anthu agenda nduna yazofalitsa nkhani a Moses Kumkuyu.

Ndunayi inaganiza zodutsa kuno ndimdipiti wagalimoto ndipo itafika pamsika inatsika nkumayenda wapansi, koma mphuno salota, komwe kunatulukila miyala sikumadziwike zomwe zinapangitsa chipwirikiti mpaka apolisi kuponya utsi okhetsa msozi.

Anthu anafika poyatsa moto malaya a chipani cha MCP kwinaku akusangalala kuti Ndirande sidela lolichitila masewera.

Pakadali pano bata labwelera ngakhale ena akukhosomola, ena kutulukabe misonzi ndi zotsatila za utsiwo.

Wapha mwana wa zaka zitatu chifukwa chodutsa mmunda mwakeApolisi ku Chiradzulu amanga John Tebulo wazaka 43 pomuganizira...
21/11/2024

Wapha mwana wa zaka zitatu chifukwa chodutsa mmunda mwake

Apolisi ku Chiradzulu amanga John Tebulo wazaka 43 pomuganizira kuti wapha mwana wazaka zitatu kaamba kodutsa mmunda mwake.

Ofalitsankhani wapolisi ku Chiradzulu, Cosmas Kagulo, wati makolo a mwanayo analawilira kumunda kumusiya akugona kaamba koti mundawo unali pafupi.

Atadzuka, mwanayo anayamba kulondola makolo akewo ndipo anadutsira m'munda mwa Tebulo.

Izi sizinamusangalatse ndipo anatenga chikwanje ndikuyamba kukhapa mwanayo, yemwe anthu anathamangira naye kuchipatala koma mwatsoka, anali atamwalira.

Apolisi apulumutsanso woganiziridwayo kaamba koti anthu ammudzi anayamba kumumenya moti akulandira thandizo kuchipatala atavulala kwambiri.

Izi zachitika m'mudzi wa Likhomo, mfumu yaikulu Sandrack m'boma la Chiradzulu.

Olemba: Charles Pensulo

Nkhani za Uku ndi UkuMphezi yapha ng'ombe 34 mmudzi mwa Marimba Kwa T/A Simphasi ku Mchinji.Ng'ombezi zinali pamtengo ma...
20/11/2024

Nkhani za Uku ndi Uku
Mphezi yapha ng'ombe 34 mmudzi mwa Marimba Kwa T/A Simphasi ku Mchinji.

Ng'ombezi zinali pamtengo malingana ndimmodzi mwaomwe ng'ombe zake ziwili zafa nawo a Mickson Joseph.

(Luntha)

Nkhani za Uku ndi Uku!Rose Yasin wochokera mm'dera la Namaninga ku Mangochi wapereka chindapusa cha K20, 000 atapezeka o...
19/11/2024

Nkhani za Uku ndi Uku!

Rose Yasin wochokera mm'dera la Namaninga ku Mangochi wapereka chindapusa cha K20, 000 atapezeka olakwa kamba komuuza mwana wazaka 9 kuti azimuseweletsa kumaliseche.

Rose adavomera mlanduwo ponena kuti iye anali ndi nyere zoopsa nthawi imeneyo ndipo amukhululukire sazayambiranso.

Ndipo Oweluza agamula kuti chindapusacho chipite Kwa mwana yemwe amamukakamiza kuti achite za umvezo.

Moto waononga katundu pa sitolo ya Makolo Hardware yomwe ili pa Mzimba bomaMalingana ndiyemwe anaona izi zikuchitika Tow...
18/11/2024

Moto waononga katundu pa sitolo ya Makolo Hardware yomwe ili pa Mzimba boma

Malingana ndiyemwe anaona izi zikuchitika Towera Mhango wati anona nthambo za magetsi zikuthetheka kenako moto unayamba mkati mwa sitoloyi.

Izi zapangitsa kuti katundu monga zitsulo, cement mwazina kuti zipseretu.

Ozimitsa moto ochokera ku Raiply anafika katundu wambiri ataonongeka kale.

Khonsolo ya M'mbelwa ilibe makina ozimitsira moto.

Address

Lilongwe

Telephone

+265996303127

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Ntunda Osema News Online posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share