27/12/2024
ya Bishop wamkulu wa mpingo wa Akatolika, Luke Thomas Msusa.
Thomas Luke Msusa, anabadwa pa 2nd February, mchaka cha 1962, m'mudzi mwa nyakwawa Iba, mfumu yaikulu Katuli, m'boma la Mangochi, ku Banja lomwe Bambo ake anali Shehe wamkulu wa chipembedzo cha chisilamu.
Thomas Luke Msusa, anayamba maphunziro ake pa sukulu ya mpingo wa Akatolika, pamene makolo ake anakanitsitsa kuti Mwana mwawo apite ku sukulu ya mpingo wa Akatolika, kamba koti anali wa chipembedzo cha chisilamu.
Koma Thomas Luke Msusa, anakakamira pa maphunziro ake, ndipo anachita chidwi ndi anzake pa sukulupo omwe anali a chipembedzo cha akatolika, ndipo makolo ake anakana kuti iye sanali mwana wawo kamba kokamira pa maphunziro ake, molimbikitsidwa ndi amalume ake.
Ndipo pang'ono pang'ono, Thomas Luke Msusa, anayamba kuonetsetsa chidwi chofuna kulowa mpingo wa Akatolika, koma anauzidwa kuti akatenge chilorezo kuchokera kwa makolo ake omwe anakanitsitsa.
koma molimbikitsidwa ndi amalume ake komanso Amsembe a mpingo wa Akatolika, Luke Thomas Msusa, mpaka anakapitiliza maphunziro ake ku Seninale, mpaka pomwe anavekedwa kukhala wamsembe wa mpingo wa Akatolika pa 3rd August, mchaka cha 1996 ndi Achi Bishop Alexandrio Assolari, omwe pa nthawi imeneyo anali Bishop wamkulu wa Dayosizi ya Mangochi.
Ndipo mwambo oyamba wa mapemphero anchititsa m'mudzi mwa kwawo kwa nyakwawa Iba, pomwe Bambo ake omwe Shehe wamkulu wa chipembedzo cha chisilamu, pamodzi ndi Abale ena ambiri amavomeleza kulowa mpingo wa Akatolika.
Thomas Luke Msusa, anabatiza yekha Bambo ake atamaliza maphunziro onse a chikhulupiliro cha mpingo wa Akatolika.
Pa 19th December, mchaka cha 2009, Luke Thomas Msusa, anasankhidwa mtsogoleri wa mpingo wa Akatolika pa Dziko lonse lapansi, Papa, kukhala Bishop wa Dayosizi ya Zomba.
Ndipo pa 21st November, mchaka cha 2013, Papa, Mkulu wa mpingo wa Akatolika pa Dziko lonse lapansi, anasankha Bishop Luke Thomas Msusa, kukhala Bishop wamkulu wa mpingo wa Akatolika m'dziko lonse la Malawi, komanso