Great Dominion Television

Great Dominion Television Great Dominion Television,
(4)

20/02/2024

GDTV NKHANI PA 20:00HRS ndi Chisomo Chingwalu

GDTV news Chipani cha DPP chamema nzika za dzikolino kuti zikhale tchelu powonetsetsa  zina mwa mfundo za ulamuliro wa d...
16/02/2024

GDTV news

Chipani cha DPP chamema nzika za dzikolino kuti zikhale tchelu powonetsetsa zina mwa mfundo za ulamuliro wa demokalase kuti aliyense kuphatikizapo adindo azitsatira ponena kuti demokalase yamdzikolino ili pachiopsyezo chachikulu ndipo anadzudzulanso boma la tonse pophwanya ma ufulu awathu angakhalenso atolankhani

Mtsogoleri waaphungu achipanichi mnyumba yamalamulo a Mary Navicha omwe pamodzi ndi akuluakulu ena achipanichi alankhula izi pamsonkhano waatolankhani omwe unachitikira ku golden peacock munzinda wa Lilongwe.

Iwo adzudzulanso Sipikala wanyumba yamalamulo a Catherine Gotani Hara kuti akuikira kumbuyo a Kondwani Nankhumwa kuti akhale mtsogoleri waaphungu otsutsa boma mnyumba yamalamulo ndicholinga choti mbali yotsutsa boma mnyumbayi ikhale yopanda mphavu.

Mwazina apepha boma kuti lithane ndimavuto a njala, kusayenda bwino kwa chuma, kulephera kupeleka ziphatso zaunzika komanso kukwera mtengo kwa ndalama zolipilira maphunziro

Ena mwa akuluakulu a DPP omwe ali pamsonkhanowu ndi Dr Clement Mwale, mlembi wamkulu wachipanichi, Dr George Chaponda, mkulu osungitsa mwambo mchipanichi mnyumba yamalamulo, a Jappie Mhango, a Chimwemwe Chipungu ndi a Christopher Mzomera Ngwira, gavanala wachipanichi kuchigawo chaku mpoto.

GDTV
Friday 16 February 2024
# Grevaxio Mota

Shout out to our newest followers! Excited to have you on board! Precious Diamond, Chifunilo Chintengo, Mercy Joshua, As...
14/02/2024

Shout out to our newest followers! Excited to have you on board! Precious Diamond, Chifunilo Chintengo, Mercy Joshua, Ash Gilinjala

Shout out to our newest followers! Excited to have you onboard! Rumbidzai Mpaya, Chifundo Matias, Catherine Chiwaya, Chr...
01/12/2023

Shout out to our newest followers! Excited to have you onboard! Rumbidzai Mpaya, Chifundo Matias, Catherine Chiwaya, Christopher Chimangeni, Godfrey Chifolo, Aja Man

Sitikweza mitengo ya Gas ndi zipangizo zophikila- 265 Energy yatero.Kampani ya 265 Energy yati ilibe malingaliro okweza ...
11/11/2023

Sitikweza mitengo ya Gas ndi zipangizo zophikila- 265 Energy yatero.

Kampani ya 265 Energy yati ilibe malingaliro okweza mitengo yazipangizo zophikila zogwilitsa ntchito gas ngakhale Bank ya Reserve yalengeza kuti ndalama ya dziko lino yatsika mphamvu ndi 44 kwacha pa 100 kwacha iliyonse.
Ofalitsa nkhani za 265 Energy Phillip White wati izi zatsatilanso ganizo la boma losakweza mitengo ya gas.
"Boma kudzera ku bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority -MERA- silinakweze mitengo ya gas ndi zipangizo zophikila zogwilitsa ntchito gas choncho ifenso sitikweza mitengo," atero a White muchikalata chomwe atulutsa.
A White ati izi zithandiza kuti anthu apeze mpumulo pamene akufinyika ndikusachita bwino pa magawo a zachuma mdziko muno.
A White anati, "tikudziwa anthu mdziko lino akudutsa munyengo zowawitsa pa nkhani za Chuma mchonchi ife [kampani ya 265 Energy] tiwonetsetsa kuti vutoli lisakhudze kwambiri anthu maka kugawo logwilitsa ntchito zipangizo zophikila gas."
Lachinayi sabata ino Bank ya Reserve inalengeza kuti ganizo lochepetsa mphamvu ya ndalama yadziko lino ladza potengera kusowa kwa ndalama yakunja (forex) ndi zina.

GDTV Exceptional Quality #

29/10/2023

KUMANGA LINGA

Kuphika moganizila chilengedwe nkotheka- Yatero kampani ya 265 EnergyKampani ya 265 Energy yati ndiyodzipeleka kupitiliz...
27/10/2023

Kuphika moganizila chilengedwe nkotheka- Yatero kampani ya 265 Energy

Kampani ya 265 Energy yati ndiyodzipeleka kupitiliza kuthandiza boma pantchito yolimbikitsa kaphikidwe kamakono ndi koganizila chilengedwe.
Ofalitsa nkhani za kampaniyi a Philip White auza GDTV kuti iyi ndi njira yokhayo yoonetsetsa kuti masomphenya achitukuko a Malawi 2063 akwanilitsidwa kumbali yosamalira za chilengedwe.
Iwo alankhula izi pamene kampaniyi imaonetsa kwa atolankhani zipangizo zophikila zamakono zomwe kampani yawo ibweletse pansika sabata yamawa.
"Zipangozo zimenezi zili ndi pophikila pawiri ndipo zili ndi chili chonse chofunikila pohikila gas," anafotokoza motero a White kwa atolankhani atafunsidwa.
Iwo anati, "kwambiri chomwe tikufuna ndikuonetsetsa kuti anthu akuphikila gas amene tikumutenga kwa opanga gas odziwika bwino ndipo alibe chiopsezo chili chonse pa anthu."
Kukhazikitsa kwa zophikila zatsopanozi kuchitika munzinda wa Blantyre lachisanu sabata yamawa.

Muchithunzi: White (Kumanzere) kuima limodzi ndi akulu-akulu ena a 265 Energy.

GDTV Exceptional Quality #

25/10/2023

MORNING RISE

Jamaican Reggae sensation Everton Blender has hinted of fireworks as he is expected to headline a Jah Kings Reggae Jam F...
22/10/2023

Jamaican Reggae sensation Everton Blender has hinted of fireworks as he is expected to headline a Jah Kings Reggae Jam Festival in Lilongwe next weekend scheduled for Grand Business Park in Lilongwe.
Speaking on Saturday on arrival at Kamuzu international Airport, Blender promised to dishout undiluted reggae during the fest.
Another headliner for the event Luciano also known as the Jah Messenger, is expected to arrive in the country mid week.
Part of the proceeds during the event will go towards the construction of Kawale Nyambingi Tabernacle in Lilongwe.
Meanwhile, one of the priests for the temple has called upon Reggae fans and all to come out in large numbers to patronize the show and in turn help realise the fundraising dream.
Don Tarz, The Black Missionaries, Blasto, Chizmo Njuchi, Queen fire and others from Malawi are also expected to perform at the event which will be backed by the Tuff Lions International Band.

Ndalama za Jah Kings Reggae Jam Festival zimangidwila kachisi wa ma Ras- Atero akulu akulu a MwambowuZatsimikizika tsopa...
22/10/2023

Ndalama za Jah Kings Reggae Jam Festival zimangidwila kachisi wa ma Ras- Atero akulu akulu a Mwambowu

Zatsimikizika tsopano kuti zina mwa ndalama zomwe zipezeke pa mwambo wa mayimbidwe a Jah Kings Reggae Jam Festival omwe achitike loweluka likubwelari ku Grand Business Park ku Lilongwe zipita ku ntchito yomanga kachisi wa ma Rasta ku Kawale ku Lilongwe.
Wa nsembe wa pa Kachisiyi yemwenso ndi wa pampando wa Kawale Nyabingi Ras Fred Mwanamanga walankhula izi pa bwalo landege la Kamuzu pamene ma-Ras ndi ena okonda nyimbo za Reggae amakalandila oyimba wa mdziko la Jamaica Everton Blender yemwe ali mdziko muno kudzaimba ku mwambowu.
Ras Mwanamanga anati ndi osangalala kwambiri pozindikila kuti Mulungu amapeleka zinthu mu nyengo yake.
"Tilibe chomwe tinganene poona kuti abale athu aja abweladi moti aMalawi komwe muliko tipangeni support kuti mwina anzanufe tione kusintha kuti tikhale malo opemphelera choncho Mulengi akudalitseni nthawi zonse," anafotokoza choncho Ras Mwanamanga pamene amamema anthu kuti abwele mwaunyinji ku Mwambo wa za mayimbidwewu.
Polankhula kwa khwimbi la maRas komanso ena okonda Reggae omwe anakhamukila ku bwalo la ndege la Kamuzu, Blender analonjeza kudzaswa Reggae yosasungula ngati sobo.
Blender yemwe amaoneka wachimwemwe anayamikila Jah Kings kamba komuyitana kudzakhala nawo pa mwambo wamayimbidwewu.
Oyimba wina otchuka Luciano yemwe amadziwikanso ndi dzina loti Wamthenga wa Mulungu, Jah Messenger pachingelezi, akuyembekezeka kufika mdziko muno mkati mwasabatayi.
Oyimba ena akuno ku Malawi monga Don Tarz, Anne Matumbi, Queen Fire, Chizmo Njuchi, Blasto ndi ena adzayimba pa mwambowu omwe zing'wenyeng'wenye zake idzakwapule ndi Tuff Lions Band.

Olemba: Chisomo Chingwalu
GDTV Exceptional Quality #

Muchithunzimo:Blender kuima pamodzi ndi okonda nyimbo za Reggae omwe anamuchingamila pa Kamuzu Airport.

15/10/2023

MALAWI TO CELEBRATE WORLD TEACHERS' DAY IN MZUZU

All is set for a grand celebration of World Teachers' day, which will be commemorated in the City of Mzuzu on 18th October.

The day is celebrated every year on 5th October.

Speaking to GD TV, chairperson of the organizing committee of the celebration, Joseph Nkhata says they have selected four teachers from every district in Malawi to attend the commemorations at the Grand Palace Hotel in Mzuzu. The ceremony will start with a solidarity march from Mzuzu High Court to Grand Palace Hotel.
Two teachers are from the primary school section while the other two are from the secondary school section, one male and one female.

The best performing teachers from the districts will receive prizes including bicycles and cash.

Nkhata underscored the importance of celebrating the day. saying teachers are responsible for forging all professions including lawyers, doctors and journalists who are what they are today because of a teacher.

Last year, the commemorations were held at Mount Soche Hotel , while in 2021, activities marking the day took place at Crossroads Hotel in Lilongwe.

Blantyre

Address

P. O. Box 30544
Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Great Dominion Television posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Great Dominion Television:

Videos

Share


Other Broadcasting & media production in Lilongwe

Show All