20/12/2024
Kafukufuku wapeza kuti kwa Mfumu yaikulu Ndakwera m'boma la Chikwawa maukwati ndi mimba za ana achichepere ndi zochuluka kuposa madera ena a m'bomali.
Mwa chitsanzo, mu mwenzi wa November okha chaka chino, amayi 43 kuderali ndiwo anapezeka kuti ali ndi pakati ndipo mwa amayiwa 38 anali ana achichepere pomwe asanu okha anali amayi a msinkhu obereka.
Izitu zadziwika Lachisanu pa 20 December 2024 kwa Madrande Mfumu yaikulu Ndakwera m'bomali pomwe bungwe la zachipembedzo ndi chitukuko la CARD, limapereka maunthenga pa nkhani za ubereki ndi uchembere wabwino.
Malingana ndi nzika zina kumeneko, zauza Nyungwe FM kuti zikhalidwe zina zomwe makolo amakhulupirira ndi zomwe zikukolezera kuti asungwana adzitenga mimba akadali achichepere.
Bungwe la CARD ndi la Chikristu ndipo likugwira ntchito zake ndi cholinga cholimbikitsa nkhani za ubereki ndi uchembere wabwino pofuna kuchepetsa maukwati ndi mimba za ana achichepere kwa mafumu akulu Ndakwera ndi Ngabu.
Wolemba: Francis Mwale Jnr