24/10/2025
DPP NDI UTM APANGA MGWIRIZANO
Chipani Cha DPP chalowa mumgwirizano ndi chipani cha UTM ku nyumba ya malamuro pofuna kugwilira ntchito limodzi.
Zina mwamfundo za mgwirizanowu ndizakuti aphungu achipani cha DPP akavotere wachiwiri Kwa mtsogoleri wa chipani cha UTM a Dr Catherine Mzumara ngati wachiwiri Kwa spikira wa nyumba ya malamuro.
Mgwirizanowu omweso uli ndi aphungu onse amchigawo cha ku mpoto motsogozedwa ndi Hon Khumbo Kachale, ku UTM motsogozedwa ndi a Dr Patricia Kaliati pamene ku DPP motsogozedwa ndi a Hon Dr Ben Phiri.
Aphungu ambali ziwirizi akhalaso akupanga sapoti Hon Sameer Suleman ngati sipikara oyamba wanyumbayi komanso kugwilira limodzi ngati yokhazikisa ma bill osiyanasiyana.