Mibawa TV

Mibawa TV Malawi's Entertainment Channel.
(218)

 Bikers on a Mission has underscored the need for more support from the corporate world to students at Montfort School F...
15/12/2024



Bikers on a Mission has underscored the need for more support from the corporate world to students at Montfort School For the Blind in Chiradzulu which is currently in dire need of assistance to carry out it's operations.

The school is run with government support although it is not enough to carter for the current 48 learners with visual impairment needs.

The revelation comes as the group has made a donation of assorted items including soap, relish, salt, clothes, christian materials in braille and cash amounting to K130, 000 to the school earlier today.

One of the representative from Montfort School For the Blind Anne Chisasula said currently they are running the school with a budget of K400, 000 per month from government although the initial amount required for smooth operations is around K3 Million.

Pastor Joshua Lapken a representative of the Bikers on a Mission and Translators Network International has since pledged that they will continue to support the school in whatever way they can.

Reported by Bertha Chirwa.

 Unduna wa zamaphunziro wayamba waimitsa kaye maphunziro asukulu za pulaimare komanso sekondare mawa lolemba m'maboma om...
15/12/2024



Unduna wa zamaphunziro wayamba waimitsa kaye maphunziro asukulu za pulaimare komanso sekondare mawa lolemba m'maboma omwe akukhulupilira kuti akhonza kukhudzidwa ndi mvula yamphamvu kamba ka namondwe otchedwa Chido.

Kalata yomwe undunawu yatulutsa yati mabomawa ndi monga Machinga, Mangochi, Zomba, Phalombe, Mulanje, Thyolo, Chiradzulu, Nsanje, Chikwawa, Blantyre, Neno, Mwanza, Balaka, Ntcheu komanso Dedza.

"Izi zikuchitika pofuna kuteteza ophunzira komanso aphunzitsi m'mabomawa. Omwe ali kusukulu zogonera konko akhalebe komweko ndipo akuluakulu awo akupemphedwa kuonesetsa kuti aika ndondomeko zoyenera zotetezera ophunzirawa". Yatero kalatayi.

Olemba Bertha Chirwa.

 ULENDO WA PANTHERS  MU CHIKHO CHA CASTEL WATHERA PA NJIRA.Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yatulutsa timu ya Panthers Fc...
15/12/2024


ULENDO WA PANTHERS MU CHIKHO CHA CASTEL WATHERA PA NJIRA.

Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yatulutsa timu ya Panthers Fc mu chikho cha Castel Challenge mu ndime ya semifayinolo ndi zigoli zitatu kwa chilowere pa bwalo la Kamuzu.

Wanderers inapeza zigoli zake kudzera mwa Clement Nyondo, Blessings Singini komanso Gaddie Chirwa.

Panthers Fc imachokera mu mpikisano wa Chipiku Central Region Premier Division ndipo inatulutsa ma timu a Silver Strikers, Chitipa United komanso Civil Service United kuti ifike mu ndimeyi.

Zateremu Mighty Mukuru Wanderers yafika mundime yotsiliza ya chikhochi pamene ikuyembekezela kukumana ndi opambana pakati pa timu ya Mzuzu City Hammers komanso FCB Nyasa Big Bullets omwe asewere lachiwiri pa bwalo la Kamuzu.

Olemba Peter Nyasulu, Lilongwe

 FAM YALONJEZA ZOYIKA 1.2 BILLION KWACHA KU MASEWERO AMPIRA WAMIYENDO WA ACHISODZERABungwe loyang'anira masewero a mpira...
15/12/2024


FAM YALONJEZA ZOYIKA 1.2 BILLION KWACHA KU MASEWERO AMPIRA WAMIYENDO WA ACHISODZERA

Bungwe loyang'anira masewero a mpira wa miyendo m'dziko muno la Football Association of Malawi (FAM) lati lidzayika ndalama zokwana 1.2 billion kwacha ku masewero a mpira wa miyendo wa anyamata achisodzera mundondomeko yake yazachuma ya chaka cha mawa.

Wachiwiri kwa m'tsogoleri wa bungwe la FAM a Lameck Khonje anena izi pa mpikisano wolimbirana ukatswiri mu ndime yotsiliza ya chikho cha FCB katswiri under 20 womwe matimu am'zigawo zonse zitatu amapikisana ku Luwinga Youth Center mu mzinda wa Mzuzu.

A Khonje anati kudzera mu chikhochi alimbikitsika kwambiri kuti masomphenya otukula masewero ampira wa miyendo kudzera mwa achinyamata achisodzera womwe bungweli lili nawo ndiwotheka.

Polankhulapo m'modzi mwa akulu akulu kuchokera ku banki ya FCB a Twikale Chirwa analonjeza zopitiriza kuthandiza bungwe la FAM komanso National Youth Football Association pamene pakadali pano m'gwirizano wawo ukutha zaka 15.

M'mawu ake yemwe anali m'lendo wolemekezeka pa mwambowu, a Monica Simwaka yemwenso ndi wachiwiri kwa mfumu ya mzinda wa Mzuzu anayamikira momwe anakonzela masewerowa posankha kuti ndime yotsiriza yikachitikire ku Mzuzu ati popeza mbali ina yathandizira kukweza ntchito za malonda mu mzindawu.

Timu ya kuchigawo cha kumpoto ndiyomwe yakhala akatswiri a chikhochi chaka chino pamasewero omwe anayamba lachisanu ndipo atha loweruka.

Wolemba Dismas Puluputu

 Nthambi yowona zanyengo yati usiku walero ndi mawa pa 16 December, 2024 mvula yamphamvu komanso mphepo ya mkuntho zikuy...
15/12/2024



Nthambi yowona zanyengo yati usiku walero ndi mawa pa 16 December, 2024 mvula yamphamvu komanso mphepo ya mkuntho zikuyembekezeka ku m'mwera ndi m'madera ena m'chigawo chapakati kamba ka namondwe otchedwa Chido.

Malingana ndi nthambiyi, chiyembekezo cha zotsatira za namondweyu kufika kuno ku Malawi chili pa 95%.

Pakadali pano, nthambiyo yati ikutsatira mwachidwi kayendedwe ka namondweyu.

Olemba Bertha Chirwa

Tikakumane ku Zomba lachisanu likubwelali pa lifetime park pafupi ndi mixed booze komanso BBQ. 💥💥💥💥 The Black Missionari...
15/12/2024

Tikakumane ku Zomba lachisanu likubwelali pa lifetime park pafupi ndi mixed booze komanso BBQ. 💥💥💥💥 The Black Missionaries siphweketsa.

 Bungwe la United Civil Servant Sacco lati  ndilokondwa kuti likukwanilitsa masophenya ake omwe linayika mu mchaka cha 2...
15/12/2024


Bungwe la United Civil Servant Sacco lati ndilokondwa kuti likukwanilitsa masophenya ake omwe linayika mu mchaka cha 2022 okuti pofika mchaka cha 2026 adzakhale ali ndi mamembala okwana 130,000.

Izi zadziwika pa mwambo wam'gonero omwe bungweli linakonzera ogwira ntchito ake ochokera m'zigawo zonse zadziko lino mumzinda wa mzuzu.

Polankhala ndi Mibawa Television mkulu wa bungweli a Francis Waliwa ati chikhazikitsireni masophenyawa akwanitsa kupeza ma membala okwana 85,000 kuchoka pa 43,000 zomwe zikupherezera kuti pofika mchaka cha 2026 adzakhala atakwanilitsa masophenya ako.

A Waliwa ati anthu omwe akulowa sacco ndiomwe apangitsa kuti bungweli likule.

"Chaka chino chokha takwanitsa kupeza ma membala atsopano okwana 17,000, chuma cha kampaniyi chafika pa 46 billion kuchoka pa 21 billion, phindu lomwe tapeza chaka chino ndilokwana 11.2 billion kuchoka pa 7 billion." Atero a Waliwa.

Pamwambowu munthu yemwe wagwira bwino ntchito kuposa anzake walandira photho ya galimoto ya mtundu wa honda fit.

Olemba: Lauryn Tembenu

14/12/2024


BOMA LILI NDI ZINTHU ZOYENERA KUKONZA

Komishoni imene pulezident Dr. Lazarus Chakwera anasankha kuti ifufuze zokhudza ngozi ya ndege yapereka m'ndandanda wa zinthu zimene likuti boma kudzera ku ziwalo zake monga asilikali, apolisi komanso oyang'anira za maulendo a ndege akuyenera kumatsatira.

Olemba Patrick Njawala

14/12/2024


Komishoni imene pulezidenti Dr. Lazarus Chakwera anasankha kuti ifufuze za zimene zinachitika zokhudza ngozi ya ndege imene inatenga miyoyo ya anthu asanu ndi atatu kuphatikizapo wachiwiri kwa m'tsogoleri wa dziko lino yatulutsa zotsatirazi.

Ndege inali bwinobwino pamene inapita kukasiya malemu Chilima ndi onse amene anali mu ndege.

Komitiyi akuti yapezanso kuti ndegeyi amaikonza pafupipafupi kuti izigwira ntchito yake moyenera.

Akutinso oyendetsa ndege sanapeleke lipoti kuti ndege ili ndi vuto.

A komishoni akuti anapeza kuti malemu Colonel Sambalopa anali ndi ukadaulo wa ndege ndipo amaiziwa bwino ndege ya Dornier imene amayendetsa ndipo anakhonza mayeso amene amayenera kupanga pa ntchito yawo.

Akuti malemu Colonel Sambalopa anali atayendetsapo ndege munjira imeneyi m'mbuyomu.

Komitiyi akuti yapeza kuti oyendetsa ndege anakanika kupeza lipoti ya m'mene nyengo inaliri ku Mzuzu.

Akutinso oyendetsa sanatenge njira imene amayenera kutenga koma anatenga njira ina.

Pakusowa kwa ndege, komishoni yapeza kuti asilikali ankhondo anauzidwa nthawi yomweyo atangodziwa kuti ndege yasowa pasanapite nthawi.

A Pulezidenti akuti anauzidwa koyamba ndi mtsogoleri wa asilikali ankhondo pafoni.

Akuti lipoti yokuti ndege inali cha ku Usisya sunali oona ndipo unasokoneza kagwilidwe ka ntchito yoyang'ana ndegeyi.

Akuti nyengo sinali bwino ndipo izi zinapangitsa kuti anthu amene amasaka ndegeyi asamaone bwino.

Akuti a Polisi anapanga chiganizo choimitsa kusaka ndege ndi anthu chifukwa panali zifukwa zimene zimapangitsa ntchitoyi kuti izikanika ndipo mwazina zinthu zake zinali nyengo yozizila kwambiri, m'dima, kuchuluka kwa anthu wamba amene amasokoneza ntchitoyi komanso kuti panthawiyo samadziwa kuti azipita kukasaka ndege ndi anthuwa kuti.

Akuti a asilikali a MDF sanasiye kusaka ndegeyi mpaka itapezeka.

Lipoti likuti palibe umboni wakuti ndege inachita ngozi chifukwa inali ndi vuto.

Akuti kuuluka kwa ndege pansi sikukuonetsa kuti ndegeyi inali ndi vuto koma kuti oyendetsa amasaka mpata okuti auluke m'musi kuti azikwanitsa kuona kutsogolo bwino.

Olemba Patrick Njawala.

14/12/2024


MARY CHILIMA AKUTI KUNALIBE CHITETEZO POPITA KUMUDZI

Amene anali mkazi wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa kale wa dziko lino a Mary Chilima ati panalibe chitetezo chokwanira pamene ankapita ku Ntcheu kumene anakachita mwambo oika maliro a malemu Saulos Chilima.

Popereka zimene anthu amene anabwera kuzapereka umboni ananena, akuti mai Mary Chilima anauza komishoni kuti panali apolisi okwana khumi ndipo anthu anagenda galimoto zimene zimapelekeza maliro.

Lipoti likuti mai chilima akuti bokosi limene malemu chilima anagona linagendedwa mpaka kupindika pamalo pena ndi miyala.

Pakali pano wapampando wa komishoniyi a Justice Jabber Alide akupereka zotsatira za zofufuzazi

Olemba Patrick Njawala.

14/12/2024



Professor Nyengo Mkandawire wauza anthu amene abwera kuzamvera zotsatira kuti banja la kwa Chilima linapeza munthu amene anazaona ndi kuyeza thupi ndipo Dr. Tomoka ndi Dr. Kamiza ndi omwe anagwira ntchitoyo.

Matupi asanu anayedzedwa ku malo amodzi a Sunset.

Thupi la malemu Abdul Lapken sanalipime potengera malamulo a chipembezo cha Chisilamu amene amafunika kuti thupi liikidwe m'manda pasanadutse nthawi yaitali.

Zithunzi zimene zinajambulidwa akuti sizinali zabwino ndiponso sizinathandize ngati m'mene zimayenerera pothandiza kuti anthu opima awone m'meme malo a imfa analili.

Pali malipoti osiyanasiyana kutengera kuti kodi analetsa kujambula ndani?.

Akuti chifukwa chopima matupiwa kunali kufuna kupeza ngati mabala amagwirizana ndi ngozi.

Dr Kamiza akuti panalibe mgwirizano kuti kodi ndani amene amayenera kupima matupiwa komanso pamayenera kukhala ndondomeko yotani.

Akuti matupi ena anapezeka atatsukidwa kale zinthu zimene amayenera kudikira anthu opima ndipo ati mabala pa matupi ena anali atasokedwa.

A MDF akuti anapangitsa okonza matupi a asilikali kuti awakonze mwachangu ndi cholinga choti akapange mwambo wa maliro.

Iwo atinso matupi onse anaonetsa kuti anthu anafa chifukwa cha ngozi ya ndege
ndipo onse anali ndi mabala amene mkati mwake munali mafuta a ndege.

Akuti panalibe umboni okuti anthu anaphedwa ndi chinthu china ngati mfuti kapena zilombo pa nthawi imene matupiwa anali asanapezeke.

Iwo atinso mafuta a ndege anapezeka m'mabala a anthu omwalira.

Dr. Kamiza akuti sakuganiza kuti oyendetsa ndege analedzera.

Kupeleka kwa maumboni amene analandira kukupitilira.

Wolemba Patrick Njawala.

14/12/2024


MAUMBONI AMBIRI OKHUDZA NDEGE ANALI OSADALILIRIKA

Ma lipoti akuti maumboni ambiri amene anthu amene anafunsidwa zokhudza ndege anali osadalilirika.

Ripoti likuti izi zili chonchi chifukwa nthawi imene anthu ambiri amati anaona kapena kumva za ngoziyi, nyengo sinali bwino.

Corled Nkosi amene anapeleka umboni akuti anamva ndi kuona ndege ikuuluka cha mmusi mwina mamita 10 kapena 14 kuchokera pansi. Nkosi akuti ndegeyi matayala ake anali atatuluka ngati m'mene zimakhalalira ndege ikamafuna kutera.

Anthu ena amene anafunsidwa akuti anamva chiphokoso koma anaganiza kuti mwina ndi mabomba ophulitsira miyala popeza mbali ina ya Nthungwa kuli malo okumbirako miyala.

A Manda amene amayang'anira pa nkhalango ya RAIPLY akuti anamva phokoso ndipo iwo amaganiza kuti inali generator yaikulu ya pamalopo itaphulika.
Anakayang'ana ndipo ataona kuti generator ili bwino anaganiza kuti mwina ndi bomba lophulitsira miyala yaikulu.

Wolemba nkhani Patrick Njawala.

14/12/2024


ZIMATHEKA NDEGE YA DORNIER KUGWA OSAYAKA

M'modzi mwa anthu amene anakapereka umboni ku komishoni yofufuza za ngozi imene inatenga moyo wa a Chilima ndi ena asanu ndi anayi akuti anauza komishoniyi kuti ndi zotheka ndege kugwa koma osaphulika.

Umboni umene anapeleka mmodzi mwa asilikali akuti ati pali nthawi ina ndege ya Dornier inagwa koma sinayake.

Msilikaliyu akuti anati izi zitha kukhala choncho chifukwa ndegeyi mapiko ake amakhala cha m'mwamba ndipo ngati mapiko amene mumakhala ma thanki a mafuta samenya pansi zitha kutheka ndege osayaka.

Olemba Patrick Njawala.

Address

Blantyre

Opening Hours

Monday 09:00 - 17:00
Tuesday 09:00 - 17:00
Wednesday 09:00 - 17:00
Thursday 09:00 - 17:00
Friday 09:00 - 17:00
Saturday 09:00 - 17:00
Sunday 09:00 - 17:00

Telephone

00265999844266

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mibawa TV posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Mibawa TV:

Videos

Share

Nearby media companies