The Renowned political analysts in the country have advised the vice president Dr. Michael Usi to focus on his political career and clarify his stance, saying he cannot serve two masters at once.
The advice follows Usi's speech made at his area 12 residence in Lilongwe on Sunday that he remains loved and commands a large following within UTM.
Speaking to MIJ Online, Czar Kondowe, a renowned political analyst, emphasized that Usi needs to come out clearly and state which party he supports.
Kondowe warns that Usi's actions have potential of bringing confusion in UTM.
Another political analyst, George Phiri, echoed Kondowe's sentiments questioning basis of Usi's claim of having a huge following.
"Where is he taking them? It's unclear which party he is supporting," Phiri said.
Phiri criticized Usi's actions, saying they demonstrate lack of leadership skills and a tendency to create confusion
Meanwhile, The UTM has summoned Usi to appear to its disciplinary committee over his alleged conduct against the party’s constitution.
#mijnews #malawinews #malawi
-Alex Batison-
Video footage shows Usi entertaining some UTM followers through dance moves
#castelcupfinal
Umu ndi momwe zinalili pa bwalo la Bingu pomwe ochemelera timu ya Mighty Mukuru Wanderers amakuwa kuti 'timu ndiyomwei'.
Ochemelela ena omwe akuti ndi a FCB Nyasa Big Bullets amabweza kumati 'neba umu ndimomwe zimakomela tikamatenga zinthuzi'.
Wanderers yatenga Castel Cup itagonjetsa Mzuzu City Hammers chigoli chimodzi kwa duu
#malawinews #mijnews #malawi
-Malumbo Ngwira-
Political analyst Victor Chipofya has called on Member of Parliament for Mulanje Bale, Victor Musowa, to retract a statement he made during a political rally.
Speaking at a rally in Ndirande, Blantyre on Sunday, Musowa urged residents to chase anyone using the "Kwacha" slogan, associated with the Malawi Congress Party (MCP).
In an interview with MIJ Online, Chipofya described the remarks as "very unfortunate," stating that they have the potential to incite political violence.
When contacted, Musowa asked MIJ Online to call back, saying he was engaged with other important issues.
(Kanemayu akuwonetsa zina mwa zomwe Musowa anayankhula).
#malawinews #mijnews #malawi
-Thumbiko Nyirongo-
Nthambi yowona za nyengo yati Namondwe otchedwa Chido akuyembekezeka kubweletsa mvula m'madera ena a dziko lino kuyambira usiku uno mpaka mawa pa 16 December 2024.
Akatswiri azanyengo ku nthambi ati Namondweyu tsopano wafika m'dziko la Mozambique.
Ndipo nthambiyi yati, "Usiku uno ndi mawa pa 16 December, 2024 mvula ya mphamvu komanso mphepo ya mkuntho zikuyembekezeka ku m'mwera ndi M'madera ena amchigawo cha pakati kamba ka namondwe Chido".
Pakadali pano, anthu okhala m'madera akuchenjezedwa kukhala osamalitsa pa nthawiyi.
#malawinews #mijnews #malawi
-Aubrey Kalumpha-
Department of Climate Change and Meteorological Services
Mtsogoleri wa chipani cha UDF Atupele Muluzi watsutsa mphekesera zoti ali ku Dubai kochita zokambirana za mgwilizano ndi chipani cha MCP.
Mkuyankhula kwake iye wati, "Ndikufuna ndikudziwitseni ili ndi bodza, ine ndili m'Malawi mom'muno, sindinapite ku Dubai"
Mphekeserazi zikubwera pomwe mtsogoleri wa chipani cha MCP Lazarus Chakwera ali ku United Arab Emirates (Dubai) komwe wapitira ntchito za boma.
Koma Muluzi wati chikhalire mtsogoleri wa chipani cha UDF mmwezi wa October , sanachitepo zokambirana ndi chipani chilichonse za mgwilizano wa chisankho.
"komanso ndikufuna ndikuwuzeni kuti pamene ndinabwelera pa mpando wa mtsogoleri wa chipani, palibe tsiku limene ndinakhala pansi kukambilana ndi chipani chinachilichonse za mgwilizano". watero Atupele.
Zambiri mu kanema ali mmusiyu
#malawinews #mijnews #malawi
-Aubrey Kalumpha-
Madera ena a mu nzinda wa Blantyre akulandira mvula ya mphamvu ndi yamabingu.
Mbali ya komwe muli nyengo ili bwanji?
#malawinews #mijnews #malawi
#Vote for Bwande in the 2024 MBC EOY Awards. Details in poster.
Aphungu a chipani cha Democratic Progressive Party anyanyala zokambirana za Nyumba ya Malamulo.
#mijnews #malawinews #malawi
-Robert Mbetewa-
#tnmsuperleague
Akuluakulu oyendetsa masewero pakati pa Civil Service ndi FCB Nyasa Big Bullets agwirizana kuti masewerowa apitilire ngakhale Mvula yochuluka ikupitilirabe munzinda wa Lilongwe.
Anthuwa agwirizana kuti akape madzi omwe ali pa bwaloli.
HT: Civil 0-1 Bullets
#CDEDI_Demos_Update
Gulu la achinyamata omwe anyamula zida zosiyanasiyana akupitilira kuthamangitsa aliyense yemwe akumukayikira kuti ali mgulu la ochita ziwonetsero. Kanemayu akuwonetsa momwe gulu la anyamata azitho likuyendera. Mkulu wa bungwe la CDEDI Sylvester Namiwa sanawoneke pa malowa.
#malawinews #mijnews #malawi
-Precious Katema-
Nthambi yowona za ngozi zogwa mwadzidzidzi (DODMA) yati kugwiritsa ntchito sitima ya pa mtunda zikuthandiza kunyamula chimanga chochuluka komanso kupulumutsa ndalama kusiyana ndi kugwiritsa galimoto.
Izi zadza pamene nthambiyi ikutumiza chimanga china mchigawo chakummwera kudzera pa sitima ya pa mtunda kuchokera ku Kanengo chokwana 4000 metric tonnes.
Poyankhula ndi MIJ Online Fyawupi Mwafongo mmodzi mwa akuluakulu a DODMA wati kugwiritsa ntchito galimoto akumatha kugwilitsa ntchito ndalama pafupifupi 1.5 million kwacha koma pa njanji akugwiritsa ntchito ndalama zokwana 800 thousand kwacha.
Mwafongo wati iwo apitiliza kuthandiza mabanja onse omwe ali pavuto la njala omwe ndi 5.7 million.
Ndipo mmau ake Cosmas Pelekani mmodzi mwa akuluakulu aku NFRA wati anali ndi chimanga chokwana 83 thousand metric tonnes ndipo 16 thousand metric tonnes yapita kale ku DODMA kuti athandize anthu omwe akukhudzidwa ndi njala.
#mijnews #malawi #malawinews
-Malumbo Ngwira-
#TNMSUPERLEAGUE
Oyimbila masewero pabwalo la Civo motsogozedwa ndi Mwai Msungama atuluka pabwalori ndi chitetezo kamba koti ochemelera a timu ya Silver Strikers ena analusa kwambiri ndi ziganizo zina.
Ena mwa ochemelera a Silver Strikers anaoneka atatenga mabotolo uku akulunjika kwa Msungama ndi anzake.
Koma mwai achitetezo ndi thandizo la osewera ena a Silver Strikers omwe anayesetsa kuti izi zisachitike.
Ochemelera a Silver Strikers analutsa Misheck Selemani atapatsidwa red card pamene nthawi inali kumapeto.
Masewerowa Silver Strikers yagonjetsa MAFCO 6-1.
#mijfm #mijonline #malawi
-Malumbo Ngwira-