27/12/2024
Kambani a Malawi pa wailesi ya Blantyre Synod okupatsirani Emmanuel Harry (07:20am - 08:00am)
Boma lati anthu pafupipafupi 1 million nyumba zawo zilumikizidwa magetsi kudzera mu ntchito yomwe ikutchedwa Ascent 2.
Nduna yoona za mphamvu ndi magetsi Ibrahim Matola yati ntchitoyi igwiridwa ndi thandizo la ndalama pafupipafupi 424 billion kwacha zomwe dziko la Malawi kudzera ku bungwe la ESCOM lalandira kudzera ku Bank yaikulu pa dziko lonse ya World Bank.
Poikirapo ndemanga mkulu wa bungwe la anthu ogula la Consumers Association of Malawi CAMA John Kapito wati ntchitoyi ithandiza anthu ochuluka kuti apeze magetsi mosabvuta.
Kapito wati ngakhale ili nkhani yabwino koma nkofunika kulingalira zowonjezera mphamvu magetsi m'dziko muno pofuna kuthana ndi bvuto lakuthimathima kwa magetsi.
Nkhaniyi mwailandira bwanji?
Tipatseni ndemanga yanu.
Imbani foni pa: 0885513399 kapena 0984425156
Tumizani uthenga wa m'manja ku: 0885205184