17/01/2025
Bwalo la milandu ku Kasungu layimitsa mlandu okhudza wa polisi, a Patrick Makwale, yemwe anaombera ndi kuvulaza miyendo yonse iwiri ya a Precious Goliat Gowani a zaka 20 kuti uzapitiliranso pa 25 February chaka chino.
Lero, linali tsiku loyamba kuti bwaloli liyambe kumva mlanduwu ndipo mbali yodandaula ndiyomwe yaperekera ma umboni ake.
Malinga ndi a Goliat Gowani patsikuli, anali limodzi ndi anzawo kuseli kwa malo omwera mowa otchedwa "Blue and White" komwe amaphikako nsima ndipo woganiziridwayu, atafika adafunsa kuti mukutani, koma atayankha kuti amaphika nsima akuti woganiziridwayu analiza mfuti kukonzekera kuti aombere zomwe zinachititsa kuti ayambe kuthawa.
Apa woganiziridwayu akuti anaombera chipolopolo chimodzi chomwe chinaombera miyendo yonse iwiri ndi kuvulaza a Goliat Gowani.
Imodzi mwa mboni ku mbali ya wodandaula, omwe ndi mkulu wofufuza ku bungwe la Independent Complaints Commission (ICC), a Livison Gandaganda wati kafukufuku wawo anapeza kachiduswa ka chipolopolo pa malowa komanso anapeza kuti woganiziridwayu anaombera pa mtunda wa mamita a pakati pa 10 ndi 15.
Pa 25 February, bwaloli likuyembekezereka kudzapiliza kumva ma umboni ku mbali ya woganiziridwa.
Wolemba: Nelson Gonjani.