13/08/2025
A Lawrence Chakakala Chaziya alemba mbiri mulamuliro wa demokalase
Wednesday, August 13th, 2025
Capital City, Lilongwe, Malawi 🇲🇼
Yemwe amayimira chipani cha Malawi Congress mdera lomwe bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) linakhazikitsa kumene la Chilobwe m'boma la Lilongwe ndiye katakwe wa zisankho zomwe dziko lino likhale nazo pa 16 Sepitembala chaka chino, chifukwa apita kunyumba ya malamuro ndi miyendo, zomwe ndi zoyamba chilandilireni ufulu wa demokalase mdziko muno.
Malinga ndi bungwe la MEC, a Chaziya a chipani cha MCP adali okhawo omwe anapereka zikalata zofuna kuyimira derali, ndipo bungwe la MEC litawunikira zikalata zawo, lapeza kuti a Chaziya akukwanira kudzapikisana nawo pa mpando wa phungu wa nyumba ya malamuro mdera la Chilobwe, komanso kuti ndi okhawo omwe anawonetsa chidwi kuti apikisane nawo pa udindowu mderali.
"Malinga ndi zomwe oyang'anira zisankho mdera la Chilobwe m'boma la Lilongwe apeza atawunikira mozama ndi mwa ukadaulo zikalata za a Lawrence Chaziya, anapeza kuti a Chaziya ndi oyenera kupikisana nawo pa mpando wa phungu mderali, ndipo potengera kuti pomwe timkatseka kulandira zikalatazi, a Chaziya adali munthu yekhayo yemwe anawonetsa chidwi kupikisana pa udindowu, oyendetsa zisankhoyu watsinikiza kuti iwo ndi phungu wa nyumba ya malamuro tsopano. Ifenso ngati bungwe loyendetsa zisankho tikutsindika kuti tsopano a Lawrence Chaziya, a chipani cha Malawi Congress, asankhidwa kukhala phungu wa nyumba ya Malamuro mdera la Chilobwe m'boma la Lilongwe" yatero mbali imodzi ya kalata yomwe bungwe la Malawi Electoral Commission latulutsa lachiwiri pa 12 Ogasiti, 2025, ndipo yasayinidwa ndi mkhala pampando wa bungweli, mai Annabel Mtalimanja.
Dera la Chilobwe lili ndi anthu okwana 58,395, omwe analembetsa mkaundula wa chisankho, ngakhale zipani zotsutsa zalephera kupeza anthu oti adzaziyimire pachisankho cha phungu.
Reported by Kondanani Chilimunthaka
©️ Copyright Power Global Media Limited. Company Limited by Guarantee (SC547426). All Rights Reserved