29/07/2024
Timu ya mpira wa miyendo ya Mighty Mukuru Wanderers yatuluka mu mpikisano wa round of 16 FDH Bank Cup itagonja ndi team ya FCB Nyasa Big Bullets ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi (2-1) lero Lamulungu pa 28 July, 2024 pa bwalo la Kamuzu Stadium.
Zigoli ziwiri zochokera kwa Babatunde Adepoju zinali zokwanira kutsogoza timu ya FCB Nyasa Big Bullets mu chigawo choyamba ndipo mphunzitsi wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers anasintha osewera awiri kulowetsa Thierry Sama ndi Wisdom Mpingangira omwe anasinthana ndi Christopher Kumwembe komanso Clement Nyondo zomwe zinasintha kaseweredwa ka timuyi.
Mu chigawo chachiwiri timu ya Mighty Mukuru Wanderers inapitiliza kupanikiza kufikira pomwe inapeza chigoli chake kwa kudzera mwa Thierry Sama yemwe anagoletsa kutasala mphindi zokwana zisanu 86 koma chigolichi sichinali chokwanira kuti chipereke chipambano ku banja la nyerere.
Poyankhula ndi Mphunzitsi wamkulu wa FCB Nyasa Big Bullets Calisto Pasuwa, wati ndi wokondwa kuti osewera ake anagwiritsa ntchito zomwe anawauza komano mipata yomwe anaipeza m'katim'kati mwa masewerowa.
Ndipo Mphuzitsi wamkulu wa timu ya Mighty Mukuru Wanderers, Meck Mwase wavomeleza kugonja kwa timu yake ponena kuti sanasewele bwino ndipo zinawavuta kugwiritsa ntchito mipata yomwe anyamata ake anaipeza ndikumenyera pagolo.
Zatelemu Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yatuluka mu chikhochi, ndipo timu ya FCB Nyasa Big Bullets yazigulira malo a matimu asanu ndi atatu (8) pomwe akufuna kuteteza ukatswiri wa chikhochi kachitatu motsatana.
*Olemba:*
Aubrey Naluso
Powerful Global Media House
Blantyre - Malawi