Nkhani Online

  • Home
  • Nkhani Online

Nkhani Online This is a Non-partizane media house where you can get the true and just coming in news
(1)

07/12/2025

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Sitifano Samison, Adamu Chikolowa

16/09/2025




Voting started at 6:15am at Kazengo Primary school in Mzimba Perekezi Constituency which is at Mzimba boma.

According to Malawi Electoral Commission officials, the delay came in because they were sorting transferred voters before letting people start polling, and ensuring that the machines are working perfectly.

They said the delay means the centre will also close at 4:15pm

However, voters who have turned out in large numbers are expressing hope that the exercise will be smooth.

Winston Nyasulu, 52, said he arrived at the site at around 5am, and expects to vote and go home to attend to other issues.

16/09/2025





Anthu ayamba kuvota pa Area 21 City Site Office polling station mu Constituency ya Masintha ku Lilongwe komwe anayamba kusinkhana m'ma 5 koloko kummawaku.

Anthu osachepera 100 anali atasonkhana ndi chidwi chodzaponya voti yawo.

"Ine ndikufuna ndivoteretu kuti ndikachite ntchito zina," a Mercy Kambilonje awuza .

(by Our Reporter—Lilongwe: 09/16/2025)

16/09/2025




Nkhwimbi la Anthu lochokera madera osiyanasiyana likufika pa malo oponyera voti a Kalema ku m'mwera kwa boma la Ntchisi.

Koma ngakhale izi zili chomwechi ntchitoyi yoponya voti sinayambe .

Yemwe akuyang'anira pa malopa a Charles Mkolola ati kuti ntchitoyi yachedwa Kamba koti makina omwe akuyenera kugwiritsa ntchitoyi sakutsekula

Iwo ati adziwitsa akuluakulu a bungwe la MEC za nkhaniyi kuti vutoli lithe.

28/06/2025



His Excellency The President of the Republic of Malawi Dr. Lazarus Chakwera in Nigeria

While here in Nigeria, I have been closely following the developments back home, and I strongly condemn the violence that marred recent demonstrations in the Capital.

The right of Malawians to protest peacefully is not only enshrined in the Constitution, but also a birthright. As such, both the violence and destruction of property that took place during these demonstrations are totally unacceptable and have no place in our democracy.

I have therefore directed all relevant state agencies to act swiftly and decisively to restore calm, as well as to investigate what happened and ensure that all those who violated the law are held accountable.

As President, I will be expecting a preliminary report on findings from both the Ministers of Homeland Security and Defense upon my return, which will form the basis of further actions we will take to ensure this does not happen again and that the 80 days between now and Election Day are peaceful and violence-free.

In the meantime, let us each remain vigilant against those who seek to use our right to protest as an occasion to perpetrate violence and lawlessness for political gain.

Let us not allow them to tear down the country we are working so hard to re-build.

28/02/2025



Malawi Chewa Heritage alembera kalata nduna yowona za maboma ang'ono a Richard Chimwendo Banda kuti asiye pansi udindo ngati nduna.

Malingana ndi mkumano omwe anali mnawona lero mu mzinda wa Lilongwe Wapampando wa Malawi Chewa Heritage Gogo Sosola ati mtundu wa achewa uli ndi mkwiyo ndi momwe akugwirila ntchito a Chimwendo Banda pa undunawo.

Gogo Sosola anati a Chimwendo Banda choyamba akulephela kuyanjanitsa Mafumu achewa mwachitsanzo akanika kuyanjanitsa kusavana komwe kuli pakati pa Chewa Heritage foundation komanso Malawi Chewa Heritage.

Iwo anatiso pali milandu ina yomwe ili kumabwalo amilandu yomwe sikumalizika zomwe zikusonyeza kuti a Chimwendo akanika ntchito yawo ngati nduna.

Iwo awonjezera kuti kalata yoyamba yomwe gulu la Malawi Chewa Heritage linalembera a Chimwendo sanayankhe.

Gogo Sosola ati pamkumanowu awapatsa a Chimwendo masiku 7 ndipo ati ngati satula pansi udindo achewa atulutsa mizimu kusonyeza kukwiya.

28/02/2025



Kuli chitetezo chokhwima ku mtaya wa Luchenza ku Thyolo komwe bungwe loona za milingo la MBS likutentha ufa omwe lidapeza ku kampani ya Rab Processors.

Kuli apolisi omwe akuonetsetsa kuti pasapezeke otenga ufawo.

Anthu azinga mtayawo pomwe akuonelera kutentha matani 25 a ufa, ena akumveka akusilira "mukutaya zoona".

Thyolo

 Zadziwika tsopano kuti mtengo ogulitsira ndalama zakunja "dollar" watsika pa msika osavomelezeka ku Lilongwe.Dollar ya ...
28/02/2025



Zadziwika tsopano kuti mtengo ogulitsira ndalama zakunja "dollar" watsika pa msika osavomelezeka ku Lilongwe.

Dollar ya America yomwe imagulitsidwa pakati pa 4300 kwacha ndi 4700 kwacha tsopano Ili pakati pa 3,500 kwacha ndi 3,800 kwacha.

M'neneri wa banki yaikulu m'dziko muno a Boston Maliketi Banda wati izi zili chomwechi kamba ka njira zina zomwe boma likukhazikitsa powonetsetsa kuti anthu ena omwe akumangokweza ndalamayi opanda chifukwa uthe.

28/02/2025



Apolisi ku Lilongwe dzulo amanga mayi ndi abambo awiri ochita bizinesi ya Taxi powaganizira kuti amafuna kubera K6 million nzika ina ya mdziko la Zambia.

M'neneri wa polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, watsimikiza za nkhaniyi pofotokoza kuti anthuwa adanyamula munthuyo kuchokera ku Mchinji kubwera ku Lilongwe, pomwe ankafuna kutsika anthuwa adakhoma zitseko zonse za galimoto lawo.

Malingana ndi a Chigalu, anthu omwe awanjatawa ndi a Davie Kaunda azaka, 34, a Habib Foster azaka 26 ndi a Charity Kathumba omwe ndi azaka 26.

28/02/2025



Apolisi akupitirira kuthira utsi okhetsa msonzi ku Ndirande, pomwe zikuoneka kuti bata likuvuta kupezeka.

Anthu ena amafuna azichita zionetsero zosonyeza kusakondwa ndi kukwera kwa mitengo ya katundu.

Ngakhale akuthira utsiwu, anthu akupitirira kusonkhana magulumagulu kuti ayende ulendo wa ndawala.

Pakadali pano, apolisi atseka msewu otulukira pa sukulu ya Blantyre Girls pochokera kwa Chinsewu, ndipo akuthirabe utsiwu.

28/02/2025



Heavy rains accompanied by strong winds have rendered scores of villagers in Traditional Authority Wasambo and Sub T/A Mwinuka in Karonga destitute as roofs of their houses have been blown off.

District Disaster Risk Management Officer, Humprey Magalasi said that an assessment is being conducted to determine extent of the damage caused.

Magalasi added that apart from people's houses, the strong winds have also blown off roofs of several schools in the two areas.

26/02/2025



Asilikali a MDF amenya ndi kuvulaza ogwira ntchito ku nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka mdziko muno pa malo ochitira chipikisheni a Khwawa ku Rumphi powaganizira kuti anathandizira nzika za maiko ena kudutsa.

Anthu ena ati asilikaliwa poyamba anaombera galimoto yomwe amayiganizira kuti yinanyamula nzika za maiko ena mdera la Chitimba kenako anapita pa malo ochitira chipikisheniwa kukatenga ogwira ntchito ku nthambi yoona za anthu olowa ndikuturuka mdziko muno.

Iwo ati asilikaliwa anawatenga anthuwa nkuwayika ku boot kwa galimoto lawo la mtundu wa X- trail ndikupita nawo ku malo omwe anaombera galimoto lija, nkuwaponya mumatope, kuwamenya komanso kuwalanda lamya zawo zam'manja ndi ndalama.

Nduna yoona za chitetezo cha m'dziko, a Ezekiel Ching'oma, yati yalandira nkhaniyi ndipo ikhazikitsa kafukufuku kuti apeze chenicheni chomwe chinachitika.

Padakali pano, nthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka m'dziko muno yatseka malo ochitira chipikisheni a Khwawa ku Rumphi

Address


Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Nkhani Online posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Nkhani Online:

  • Want your business to be the top-listed Media Company?

Share