Malawi24

Malawi24 All the latest Malawi news

 Bambo wa zaka 32, Masautso Chigwetsa ali mchitokosi cha Polisi ku Lilongwe pomuganizira kuti wapha m'chimwene wake, Cho...
21/08/2024



Bambo wa zaka 32, Masautso Chigwetsa ali mchitokosi cha Polisi ku Lilongwe pomuganizira kuti wapha m'chimwene wake, Chokonoka Chigwetsa wa zaka 34 atamukumbutsa ngongole.

Ofalitsa nkhani za polisi ku Lilongwe, a Hastings Chigalu akuti Loweluka sabata yatha, malemuwa adapita kunyumba kwa m'bale wawoyo kukakumbutsa ngongole yomwe m'chimwene wawoyo adabwereka.

Komatu izi akuti sizinakondweletse obweleka ngongoleyo ndipo kusamvana kudabuka zomwe zidapangitsa kuti awiriwa ayambe kumenyana.

Malingana ndi a Chigalu, ndewu ili mkati oganizilidwayu adatenga chikuni chomwe adamenyera nacho m'mutu m'chimwene wawoyoyu ndipo adagwa pansi ndi kukomoka.

A Chigalu ati malemuwa adathamangira nawo ku chipatala Cha Kamuzu Central komwe adamwalira.

Padakalipano, oganizilidwayu amutsegulira mlandu okupha.

Wolemba: Mac Donald Kaleso

  Mbali ya boma pano ikupereka nfundo zake zomaliza kuti bwalo lipeleke chigamulo pa mulanduwu, a Luka Golosi ndi a Davi...
21/08/2024




Mbali ya boma pano ikupereka nfundo zake zomaliza kuti bwalo lipeleke chigamulo pa mulanduwu, a Luka Golosi ndi a Davie Harry atapezeka olakwa pa milandu yonse yomwe ayivomera.

Mbali ya boma yatinso wolakwa wachiwiri, a Davie Harry ndikoyamba kupalamula mulanduwu pomwe a Luka Golosi, aka ndika chiwiri pomwe m'chaka cha 2019 anamagidwa ndi bwalo la ku Blantyre pa mulandu wakuba moopseza ndipo iwo anatuluka ku ndende ya Chichiri mu disembala m'chaka cha 2021.

Mbali ya boma yapempha bwaloli kuti lipeleke zilango zokhwima kwa anthuwa popeza anthuwa ndi zigandanga.

Wolemba: Ephraim Mkali Banda

  Pamene bwalo la milandu ku Mzimba likufuna kupitilira kumva mulandu wokhudza kuba moopseza komanso kuvulaza,  anthu al...
21/08/2024




Pamene bwalo la milandu ku Mzimba likufuna kupitilira kumva mulandu wokhudza kuba moopseza komanso kuvulaza, anthu ali pa nzere pomwe akufuna kulowa mkati.

Ndipo achitetezo akusecha wina aliyense yemwe akulowa mkati.

Wolemba: Ephraim Mkali Banda

21/08/2024




First Grade Magistrate Radson Gamariel wayamba waimitsa kaye kumvera mulanduwu omwe wabweretsa chikoka chachikulu kwa anthu.

Zambiri mukanemayu.

Wolemba: Ephraim Mkali Banda

  Mbali ya boma pa mulandu wa Luka Golosi ndi Davie Harry omwe akuwaganizira mulandu wokuba moopsedza ndi kuvulaza ikupi...
21/08/2024




Mbali ya boma pa mulandu wa Luka Golosi ndi Davie Harry omwe akuwaganizira mulandu wokuba moopsedza ndi kuvulaza ikupitilidza kuperekera ma umboni pa mulanduwu.

Pano mbali ya Boma yawonetsa katundu wina yemwe oimbidwa mulanduwa anagula, kuphatikazapo malata 47, ma felemu a ma zenera 4, ma matiresi awiri (2) a akulu akulu.

Mbali ya boma yaperekanso kubwaloli zotchinga ku nkhope (Face Mask) komanso ma foni anayi (4) omwe anthuwa anaphwanya ndi kukwilira ku manda aku kafoteka m'boma lomweli, komwe akutinso ndiko amagawanirana ndalama.

Oweruza mulandu First Grade Magistrate Radson Gamariel wati bwalo lalandira komanso kulemba zonsezo ngati ma umboni.

A Inspector Aubrey Maganga auza bwalori kuti a Luka Golosi anamangidwa m'boma la Balaka pomwe a Davie Harry anamangidwa ali m'boma la Mulanje.

A Bonface Zimba omwe anakhala masiku atatu asanadzuke ku chipatala chachikulu cha Mzuzu alinawo mubwaloli limodzi ndi anthu ena omwe anavulazidwa ndi anthuwo.

Wolemba: Ephraim Mkali Banda

  Pakadali pano bwalo la Mzimba Magistrate likupitilira kumva fundo zonse za  milandu yonse yomwe a Luka Golosi ndi a Da...
21/08/2024




Pakadali pano bwalo la Mzimba Magistrate likupitilira kumva fundo zonse za milandu yonse yomwe a Luka Golosi ndi a Davie Harry ayivomera.

Ndipo yemwe akutsogolera oyimira boma pa mulanduwu, a Inspector Aubrey Maganga kuchokera ku likulu la polisi chigawo cha kumpoto, pano aonetsa kubwaloli zikalata zakuchipatala zoonetsa momwe a Bonface Zomba anavulalira kamba ka kukhapidwa ndi anthu awiriwo.

Ndipo zikalata zonse azipereka ku bwaloli ngati umboni pankhaniyi.

Bwalo likupitiliza kumva mulanduwu ndipo anthu adzaza m'bwaloli, pomwe ena alikunja.

Wolemba: Ephraim Mkali Banda

21/08/2024




Pamulandu wa chinayi, a
Luka Golosi akana kuti anaba ma foni okwana 195 pomwe 5 ndi mafoni a tachi kwa a Frank Samphwayi ndipo a Davie Harry avomera mulandu wa chinayiwu

Pano bwaloli lalemba kuti a Luka Golosi akana pomwe a Harry avomera milanduwu.

Wolemba: Ephraim Mkali Banda

21/08/2024




Panopa a Luka Golosi ndi Davie Harry avomeranso mulandu wa chitatu wakuba K21.2 million komanso kuvulaza a Bonface Zimba ndi chikwanje.

Bwalori pano lalemba mukaundula wake kuti a vomera.

Pakadali pano akuwawerengera mulandu wa chinayi.

Wolemba: Ephraim Mkali Banda

  A Luka Golosi ndi Davie Harry avomeranso  mulandu wachiwiri womwe ndi kuba zinthu zosiyanasiya ku nyumba kwa  a Ovala ...
21/08/2024




A Luka Golosi ndi Davie Harry avomeranso mulandu wachiwiri womwe ndi kuba zinthu zosiyanasiya ku nyumba kwa a Ovala Nkosi.

Ndipo Magistrate Gamalieli wati bwaloli lalemba kuti avomera milanduyo.

Pakadali pano akuwawerengera mulandu wa chitatu.

Wolemba: Ephraim Mkali Banda

21/08/2024




Mulandu wayamba tsopano ndipo woganizilidwawa a Luka Golosi ndi Davie Harry avomera mulandu oyamba atawawerengera.

Milandu yomwe avomera ndi kuba katundu komanso kuvulaza munthu.

Ndipo Magistrate Gamalieli wati bwaloli la lemba kuti avomera milanduyo.

Wolemba: Ephraim Mkali Banda

Nkhotakota Plane crash victims identified, survivor in stable conditionNkhotakota District Hospital has identified the t...
21/08/2024

Nkhotakota Plane crash victims identified, survivor in stable condition

Nkhotakota District Hospital has identified the three individuals involved in yesterday's plane crash. According to Dr Jacob Kafulafula, Director of Health and Social Services for Nkhotakota, Pilot Fungay Jonathan, a 50-year-old Zimbabwean national, and Frisco Westheim, a 29-year-old passenger, both perished in the accident.

Read More at: https://malawi24.com/2024/08/21/nkhotakota-plane-crash-victims-identified-survivor-in-stable-condition/

21/08/2024




Bwalo la Mzimba Magistrate lero liyamba kumva mulandu wa anthu atatu omwe akuwaganira kuti amaba komanso kuvulaza anthu m'bomali.

Mtolankhani wathu m'boma la Mzimba, Ephraim Mkali Banda akufotokoza zambiri za mulanduwu nkanema uyu.

Wolemba: Ephraim Mkali Banda

Mpinganjira boosts wife's project with K14mIn a heartwarming display of support and partnership, renowned businessman Th...
21/08/2024

Mpinganjira boosts wife's project with K14m

In a heartwarming display of support and partnership, renowned businessman Thomson Mpinganjira has injected K14 million into his wife's philanthropic project, 'Kuthandiza Omwe Alibe Kuthekera Kupita Patsogolo'. This significant contribution brings the total project funds to K30 million.

Read More at: https://malawi24.com/2024/08/21/mpinganjira-boosts-wifes-project-with-k14m/

Zimachitika!
20/08/2024

Zimachitika!

 Anthu okhala ku m'mwera kwa boma la Mzimba pano akuthamangira kutha maola nkhumi (10) opanda magetsi.A Fikani Nyirenda ...
20/08/2024



Anthu okhala ku m'mwera kwa boma la Mzimba pano akuthamangira kutha maola nkhumi (10) opanda magetsi.

A Fikani Nyirenda omwe ndi wa pampando wa anthu ochita malonda pa boma la Mzimba, ati anthu ambiri omwe amadalira magetsi lero sanachite malonda kamba ka vuto la magetsili.

Pakadali pano bungwe la ESCOM silinafotokoze chomwe chadzetsa vutoli.

Wolemba: Ephraim Mkali Banda

20/08/2024




Malipoti omwe tikutsatira mwachidwi akusonyeza kuti ndege yagwela m'nyanja ya Malawi m’dera la mfumu yaikulu Mwadzama m'boma la Nkhotakota.

Zikumveka kuti ndegeyi inanyamula anthu atatu ndipo m'modzi mwa anthuwa yemwe ndi wachizungu amupulumutsa ndipo athamangira naye kuchipatala.

Tikhala tikukupatsirani zambiri zokhudza nkhaniyi.

Wolemba: Archangel Nzangaya

Address


Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Malawi24 posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Malawi24:

Videos

Shortcuts

  • Address
  • Alerts
  • Contact The Business
  • Videos
  • Claim ownership or report listing
  • Want your business to be the top-listed Media Company?

Share