Nyika Daily News

  • Home
  • Nyika Daily News

Nyika Daily News Our aim is to feed the nation with timely and credible information that matters

16/06/2024

A President a SMC abwera ndi asilikali mkachisi

Mapemphero anaima kaye kwa mphindi makumi atatu pa Bangwe SDA Church mzinda wa Blantyre pamene kunabwera President wa South Malawi Conference Pastor Thomas ndi ma galimoto atatu odzadza ndi apolisi onyamula mifuti lero la Sabata.

Malinga ndi chikalata chomwe analembera mpingowu kubwera kwawo amabwera ndi cholinga chozathetsa mpingo. Ngakhale a khristu anawapempha k*ti audzidwe zifukwa zomwe ak*thetsera, iwo sanafotokoze pachifukwa ichi mpingo unawauza k*ti asabwere.

Kamba kak*ti a SMC anakakamira kubwera pogwiritsa ntchito mphamvu zawo ankhristu sanawapatse mpata oyankhula ndipo amangoimba nyimbo. Pastor Thomas omwe anabwera ndi Executive Secretary wa SMC a Smart Chimwaza anaganidza zobwerera kumapita ndi a police awo.

Akhristu sanafune zokangana ndi aliyense koma kumangoimba nyimbo ndipo panalibe kukangana kulikonse ndi a police ngakhale anthu oyandikira ochuluka amene anakhamukira panja pa kachisi podzidzimuka ndi mdipiti wa galimoto za apolisi anakuwidza galimoto zawo pamene anali kupita kwinaku akhristu akupitiridza kuimba nyimbo zawo mkachisi.

Atapita a president, mapemphero anapitiriranso monga mwa kupembedza kwa tsiku la Sabata.

19/10/2023

ZOMWE WACHITA MULUNGU KU BANGWE SDA UTATHA MSONKHANO WA MISASA [1-7 OCTOBER]

Anthu oposa 200 ku Bangwe SDA church ndi omwe abatizidwa potengera utumiki omwe YEHOVA MULUNGU wanena kupyolera mwa Atumiki ake mu msonkhano wa Misasa omwe udayamba pa 1 mpaka pa 7 october pa MUTU:'' ODALA ALI AKUZUNZIDWA'' chifukwa cha chilungamo . Ambiri mwa a KHRISTU wa sadakhalepo a SDA kotero tiyeni tiwayikize mmapemphero Abalewa k*ti asabwerere mbuyo komaso tiziyikize mmapemphero ife amene tinabatizidwa kale kuopa k*ti tingagwe .Ma utumiki onse a msonkhanowu mukawapeza pa Tsamba la ''Bangwe SDA Church'' kapena bwerani muzatenge pa Church Lasabata ndi space yosachepera 2GB [mwa ulere] MULUNGU adalitse Mpingo wa Seventh Day Adventist pa dziko lonse lapansi Amen.

16/10/2023
Stand up for the Champions !!!Malawi the Scorchers are the Champions of the 2023 Cosafa women's championship after beati...
15/10/2023

Stand up for the Champions !!!

Malawi the Scorchers are the Champions of the 2023 Cosafa women's championship after beating Zambia by 2 goal to one, in South Africa.

15/10/2023

CHIYAMBI CHA MACHILISO ATHU (INTRODUCTION)

Pali njira zambiri ZAMACHILISO Koma Pali njira imodzi yomwe Mulungu ak*tiuza k*t tichite yomwe ili Pa yakobo 5:15 (ndipo pemphero lachikhulupiliro lizachiza odwalayo.......) ndipo tisaiwale k*t chikhulupiliro chimayenda ndi ntchito popanda ntchito chikhulupiliro chikhala chakufa kotero ife tiyenera kuonesera ntchito za chikhulupiliro chathu k*t tichire

Tiyeni tione Pa Miyambo 14 :6, 17:1-14, yesaya 58:11 tiyenera kumvesesa bwino lomwe za chitetezo cha thupi lathu k*t tipewe komaso tichire ku matenda osiyanasiyana. K*t tichire ku matenda osiyanasiyanawa tiyenera ife kusiya choyambisacho kenako nkuyamba kuchita zoyenera zomwe tikambirane mma phunziro athu osatira.

09/10/2023

Mmawa wabwino kwa nonse, Nyimbo ikhale yolembedwa ndi George Ewing Lee.

09 - Omba Lipenga

LIFT UP THE TRUMPET

1 Omba lipenga, limveke ponse;
Yesu adzabweranso!
Kondweranitu, yimbani nyimbo;
Yesu adzabweranso.

CHORUS:
Abweranso, abweranso, Yesu adzabweranso!

2 Lalikirani m’phiri ndi m’dambo;
Yesu adzabweranso!
Adzadza m’ulemerero wace;
Yesu adzabweranso.

3 Lalikirani m’zinyanja monse;
Yesu adzabweranso!
Lalikirani ponseponsepo;
Yesu adzabweranso.

4 Zibvomezi zimanena k*ti;
Yesu adzabweranso!
Namondwe ndi mafunde zinena;
Yesu adzabweranso.

5 Mitundu yakwiya tidziwatu;
Yesu adzabweranso!
Zizindikiro zakwanitsidwa;
Yesu adzabweranso.

02/10/2023

Mmawa wabwino kwa nonse. Ndadza ndi Nyimbo yolembedwa ndi William Howard Doane.

104. Mundimve, Yesu

COME, GREAT DELIVERER, COME

1. Mundimve, Yesu, ndikuliratu, ’Dzani kwa inetu.
Mu mtimanga ndilakalaka ’Nu, Yesu, idzanitu

CHORUS;
Ndinasoceratu k*tariko, k*tari ndi Atateyo
Tsopano, koma mndilandirenso, Yesu, idzanitu

2. Ndiribe malo mokhaliramo, ’Dzani kwa inetu.
Khalani nane m’mtima mwangamo, Yesu, Idzanitu

3. Njobvuta njira ndimayendamo, ’Dzani kwa inetu.
Ndione nkhope yanu, Mbuyanga, Yesu idzanitu.

4. Wolapa Mtima simunyozadi, ’Dzani kwa inetu.
Pemphero langa mumve lonseli, Yesu, idzanitu

28/09/2023

Facts about Bangwe SDA Church women and girls.

1. Always in long skirts and most times in chitenje (miniskirts are strictly not allowed)
2. Always cover their heads with hats or scarfs.
3. No Hair dressing and make up.
4. Always appreciate and maintain God given natural beauty and they are beautiful.

Come one day and worship with us. Amen.

28/09/2023

Tsiku lanu linali bwanji? Tiyeni tisanagone tiyimbe nyimbo iyi yolembedwa ndi Philp P Bliss.

34 - Pokhala Mtendere

WHEN PEACE LIKE A RIVER

1. Pokhala mtendere mu mtimangamu, Pamene ndisaukanso,
Pamene mabvuto ndi akurudi, Moyo wangawu ngwabwinotu.

CHORUS
Moyowu uli phee. Moyo wangawu ngwabwinotu.

2. Ngakhale Satana atizunza ’fe, Ciripo citonthozoco;
Cifundo ca Kristu anafera ’fe, Kundipatsa ’ne moyo wace.

3. Ucimo unapachikidwa pomwe, Pa mtanda wa Yesu Mbuye,
Macimo angawo anatherapo, Mbuye wanga ndiyamika ’Nu.

4. Ambuyathu tikhumba tsiku lija, Limene tidzaona ’Nu,
Lipenga limveke, tidzakondwatu, Pakukomana ndi Yesuyo.

Address


Telephone

+265993791186

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Nyika Daily News posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Videos

Shortcuts

  • Address
  • Telephone
  • Alerts
  • Videos
  • Claim ownership or report listing
  • Want your business to be the top-listed Media Company?

Share