16/11/2023
FUNDO 15 ZOMWE A CHAKWERA ALENGEZA
1. Malawi yalandira ndalama zoposa 250 biliyoni kwacha kuchokera ku IMF
2. Mabugwe ochuluka omwe adasiya kuyika ndalama mu bajeti yathu abwelera tsopano ndipo ayika ndalama zaphwamwamu mu bajeti yathu.
3. Malawi yapeza ndalama zoposa 425 biliyoni kwacha zotukulira ntchito za ulimi ndi malonda kuchokera ku banki ya pa dziko lonse lapansi
4. Malawi yalandira ndalama zoposa 100 biliyoni kwacha zopita ku Bank zoti zithandizire amalonda poitanitsa katundu kuchokera kunja.
5. Ndalama zoposera 320 biliyoni kwacha zapezekanso zoti zithandizire kukozanso ndondomeko yakayendetsedwe ka chuma.
6. Mgwirizano wa mayiko a ku Ulaya (European Union) yapereka ndalama pafupifupi 110 biliyoni kwacha zoti tigwiritse ntchito pofewetsako mazuzo omwe angadze ndi kutsitsa mphavu kwa kwacha komwe kwachitika.
7. Banki yachitukuko muno mu Afirika yatsonyezamo mu bajeti yanthu ndalama zoposa 12 biliyoni kwacha.
8. Chakwera waletsa kuti pasapezekenso ogwiritsa ntchito ndalama zaboma popita kunja kwa dziko lino6 mpaka chaka cha chuma chino chidzathe mu Malichi chaka cha mawa.
9. Chakwera walamula kuti onse omwe anapita kunja kukagwira ntchito za boma koma pogwiritsa ntchito ndalama za boma, abwelere kuno kumudza ndipo asadikirenso kuti dzuwa lilowe ayi.
10. Chakwera wasiya zopitanso kunja mpaka chaka cha mawa mu April ndipo maulendo ake onse omwe iye amayenera kupita wawayimika kaye.
11. Ndalama zapadela zomwe nduna ndi akuluakulu a boma amapatsidwa zachepetsedwa ndi theka tsopano mpakana m'tsogolomo.
12. Nduna ya za chuma yalamulidwa kuti ikungenso ndondomeko zabwino zoti aphungu akambirane zothandizira a malonda ang'onoang'ono kuti apitilire kupeza phindu.
13. Nduna ya za chuma yalamulidwanso kuti pomwe aphungu akukambirana za bajeti panopa, akambiranenso zoowonjezera malipiro a iwo ogwira ntchito m'boma.
14. Chakwera walamulanso kuti msonkho omwe ogwira ntchito amapereka ku boma awuwunikirenso ndikuuchepetsako kuti malipiro a ogwira ntchito-wa akwere
15. Chakwera wanenetsa motemetsa nkhwangwa pamwala kuti asamve zoti mabungwe ogulitsa madzi m'dziko muno akweza mtengo wolipilira madzi.
Uku ndiye kumanganso Malawi komwe a chakwera akuchita.