03/02/2023
*KASAKANIZA WA NKHANI*
🔹Gulu la mabungwe pansi pa Citizens for Justice and Equity lati lamwemwetera kwathunthu ndi ganizo la boma cloimitsa pa ntchito mkulu wa bungwe la Anti Corruption Bureau Martha Chizuma.
Kudzera pa msonkhano omwe guluri linachititsa lero ku Lilongwe, m'modzi mwa akuluakulu ake Fredrick Malata anati a Chizuma siofunika kuwaikira kumbuyo kaamba koti adapalamula mulandu kudzera pa macheza apa lamya omwe adachita ndi mkulu wina mu January chaka chatha.
"Komansotu a Chizuma ku ACB sizuyendako chifukwa pa zaka ziwiri chomwe akuchita sichuoneka", anatero a Malata.
Apa iwo ati mkofunika malamulo agwire ntchito pa zomwe a Chizuma adachita.
Dzulo, anthu mdziko muno anatutumuka zitadziwika kuti mkulu wa bungwe la ACB, Martha Chizuma waimitsidwa pa ntchito.
Magulu ambiri kuphatikizapo mphangala pankhani za malamulo zadzudzula was ganizoli ponena kuti lachitika modabwitsa.
🔹Nthambi ya polisi m'dziko muno yati anthu okwana 39 adzipha mwezi wa January okha
Wachiwiri kwa mneneri wa nthambiyi Harry Namwaza wati mwa anthuwa, 37 ndi amuna pomwe awiri anali akazi
Namwaza wati pa imfazi, wachichepere yemwe wadzipha anali ndi zaka 13 pomwe wachikulire anali ndi zaka 80
🔹Ku Zambia, aphungu avomeleza lamulo loletsa oyenda pansi kuoloka msewu atayika zomvera n'khutu kapena kulankhula pa lamya.
Munthu yemwe azipezeka akulakwira lamuloli, azilandira chilango chopeleka ndalama zokwana ($16, £12) zomwe ndizodutsa K 1000 ya dzikolo.
Mkulu yemwe amalankhulira bungwe loona zapa msewu Frederick Mubanga wati lamuloli ndilothandiza kuchepetsa ngozi zapa msewu.
Mubanga wati theka la ngozi zomwe zimachitika m'dzikolo zimakhudza anthu oyenda pansi omwe aphwanya malamulo apa msewu.
🔹Mtsogoleli wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wapempha nduna zomwe zalumbira lero kuti zigwire ntchito molimbika komanso motsata mfundo za mgwirizano wa Tonse
A Chakwera alonjeza kuti apitilira kuunikira momwe ndunazi zizigwirira ntchito yawo kuti dziko lino lichite bwino
Zina mwa nduna zomwe zalumbira dzulo ku Lilongwe ndi monga a Moses Kunkuyu, Ken Zikhale Ng'oma, Owen Chomanika komanso a Uchizi Mkandawire mwa ena
🔹 Gulu la alimi ena okhudzidwa munzinda wa Blantyre, apempha bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu la Anti-Corruption Bureau (ACB) kuti lifufuze mpheketsera zokhudza chinyengo zomwe akukayikira kuti zakhudza ntchito yogulitsa zipangizo za ulimi za AIP ku derali.
Alimi omwe ndi pafupifupi 46 ochokera ku dera la Somanje Makata m'boma la Blantyre, masana a lero anakhamukira ku maofesi a bungwe la ACB ku Blantyre, komwe apereka kalata yamadandaulo awo.
Polankhula, ena mwa alimiwa a Chavi Charles komanso a Swema Allan ati alimiwa akhala akubwezedwa ku malo ogulira feteleza powauza kuti mayina awo sakupezeka, zomwe ndizokumudwitsa kaamba koti analipira kale ndalama yokwana 30,000 kwacha ya zipangizo zi.
Alimi wa ati akuchita mantha kuti ngati sagula Feteleza-yu sakolola chakudya chokwanira.
Mau ake, mfumu yaikulu Somanje Makata komwe alimiwa akuchokera yavomereza kuti ikudziwa nkhawa za alimi wa koma kumbali ya mpheketsera za chinyengo mfumuyi yati vuto ndi ndondomeko yogulitsira zipangizozi popeza alimi ena sakupatsidwa ziphaso zotsimikiza kuti alipira ndalama ya zipangizozi.
Padakali pano akuluakulu a bungwe la ACB sanalankhulepo pa nkhaniyi.
100% UTM DH