21/05/2023
CHINTONZO KOMASO KUTHILA MAPAWUDALA MUMIGOLO YAMADZI KWAPHA TSOGOLO LA BUSHIRI NKUWONONGESA NTCHITO ZA GOSHEN CITY
Mneneri wa a Prophet Shepherd Bushiri, Ephraim Nyondo wachenjeza a Malawi maka achinyamata omwe akumanyoza Prophet Shepherd Bushiri kuti asiye khalidwe loyipali kuwopa kutengelapo tsoka.
Nyondo wati Bushiri wakhala akuzunzika ndi nthenda ya mtima komaso kuthamanga kwamagazi kuchokela siku lomwe anachoka kudziko South Africa ndipo iwo amaganiza kuti anthu ena achipongwe anamudyesa poison ali muchitokosi cha police ku dzikolo pofuna kumupha koma zinakanika.
Nyondo watiso kulemba nkhani zoyipa ndinso zonyoza mneneriyu kukumamupangisa mneneriyu kukhala mwamantha, kudwaladwala, kubwelera mbuyo muntchito zake ndinso kusiya kutukula achinyamata.
Nayeso wachiwiri kwa mkulu wa GOSHEN City, Mr Kalonga ati Bushiri akhoza kulisintha dzikoli nkukhala dziko lolemelesesa kuposa dziko la South Africa ngati antolankhani a lokolo mumatsamba anchezo komaso achinyamata angasinthe kaganizidwe nkuyamba kumupasa ulemu.
Kalonga wati Bushiri ananyanyala nkusiya kulipilira fees achinyamata omwe anawatenga pa bursary yake kaamba kakunyozedwa ndipo izi zapangisa ophunzira onse 100 kusiyila panjira maphunziro awo.
Kalonga anapitiliza kunena kuti ntchito zomanga Goshen City zinayima kaamba koti anthu ena amathila ma pawuda mumigolo yamadzi ncholinga choti migoloyo iziwoneka ngati magazi, enanso amavala zovala ngati za Martse nkumakalira pakati pa usiku ngati mizukwa ku Goshen City zomwe zinapangisa ma contractor ndi anthu ogwira ntchito kunyanyala.
Nayeso Ephraim Nyondo wati zoophya zomwe ma contractor amakumana nazo ku Goshen City kuchokela kwa anthu achipongwe ndizinthu zobwelesa chitikuko mbuyo moti, Bushiri akuganiza zogulitsa mzindawo ndikumanga ma 5 Star Hotels mumizinda ikukuluikulu yadziko lino.
M'mawa wa lero Prophet Shepherd Bushiri anazunzika ndinthenda yakuthamanga kwamagazi zomwe zinamupangisa kuti achedwelepo kupita ku church.
MANA News Online