09/05/2022
Bwalo la First Grade Magistrate, Chimdima Phiri m’boma la Ntcheu, lakana kumasula pa belo anthu khumi omwe akuwaganizira kuti ndizigandanga zomwe zakhala zikutseka nseu wa M1 pa Kachipeya pafupi ndi Lizulu ndicholinga chobera oyendetsa galimoto.
Anthuwa akuyankha milandu inayi yomwe ndikuononga katundu, umbanda, umbava komanso kuika miyoyo ya anthu oyenda pa nseu pachiopsyezo, milandu yomwe onse akuikana choncho anapempha bwaloli liwapatse belo.
Koma oimila boma milandu a Samie Liwonde anatsutsa pempholi ponena kuti anthuwa akuyankha milandu yoopsya komanso kuwatulutsa akhoza kuthawa. Iwo anaonjezera kuti anthuwa akuyankhanso milandu yomweyi kubwalo la Senior Resident Magistrate m’bomalo.
Pakadali pano, a Phiri ayimitsa nkhaniyi mpaka pa 16 May, 2022 tsiku lomwe bwalo lidzayambe kuzenga mulandu anthuwa.