BEST Malawian Stories

BEST Malawian Stories M***A KUWERENGA NKHANI MONGA ; ZACHIKONDI, ZOSANGALATSA & ZOPHUNZITSA , INGOPANGANI LIKE PAGE YI

11/01/2022
10/20/2022

video muy peligroso que alguna vez escena

10/13/2022

Las niñas luchan

10/12/2022

Mejor vídeo del día

10/12/2022

Amazing video

10/04/2022

Vídeo de tendencia SUPERIOR

09/21/2022

Funniest hairstyle i have ever seen

09/21/2022

Things which are made fro bamboo

09/21/2022

World strangest bridge

08/03/2022

ALINAFE
Part 8
........
Nafe atakahala pheee anaganiza zowavomera ndikupita Nawo limodzi...
Atafika kunyumba Nafe analozeledwa chipinda chake choti azigona koma kaya ndi mwayi kaya Tsoka chipinda chakenso chinali Chomwe magona Jimmy, apo anangokhala ngati amukumbutsa tu nthawi yomwe anakhalako limodzi ndi jimmy ija 😂....
Nafe tsiku li anapangilidwa chili chonse ndithu monga mulendo.. Timasiku tinatha ndithu mpaka Week inakwanano Nafe akukhala mnyumba muja. Kunena zoona amakondedwamo ngati ndi mwana wanyumba momo ngakhale chakudya chake amadya chabwino, chomwe anangomupempha mchoti aziwathandiza ntchito zapakhomo komanso chomwe angafune aziwawuza ...................................Alinafe zakeno zinali bwino koma nanga komwe amachokera kunali bwanji ........ .........
Martha Anayambano kuona moyo kuvuta chifukwa chakuchoka kwa Nafe maka amasowa ocheza naye akakhala ali panyumba paja. Iyeyu tu amadana ndi Lucy komanso Charity, moti nthawi zambiri Martha amangokhalira kugona ndeno chifukwa cha izi zinayamba kumupatsa nthawi yochuluka yowerenga zomwe zinamusintha machitidwe ake aku sukulu kuyamba kumakhonza kwambiri kuposa kalasi yonse ........ Ndithudi kuonongeka kwa zina kumakhala kukonzekanso kwa zina,, Martha anali kokonzekera maeso ake a Standard 8 pomwe Lucy amakonzekera kulemba mayeso ake a form 2,...................
Zotsatira zamayeso zinayamba Kutuluka ndipo zoyamba zinali za Martha,,, Martha tu anachita bwino kwambiri pomwe anasankhilidwira ku Sukulu yogonera komko,,, patadutsanso week imodzi mayeso achina Lucy anatuluka ndipo zinali zonvetsa chisoni kuti Lucy analephera ... Apa nsanje inakula Chidani cha Lucy ndi martha chinakula zing'ono ng'ono amakhala ayambanapo ndipo Martha anafika pomasowa nazo mtendere koma Mai awo samayankhula kali konse kumangowayang'ana Basi............
Nthawi yoti Martha anyamuke inakwana ndipo chili chonse anagulilidwa ndikuperekezedwa Mwana ulendo wa Ku Sukulu kungowasiya azibale ali ndi nsanje .....
Kuchoka kwa Martha zambiri zinasintha pakhomo zinthu zinayamba Kuvuta maka ndalama amadalira kuti Bambo atumize inayamba kumavutano kufika ndipo zambiri zimasowekera pakhomo paja ...... Bambo ake a Lucy ataona zinthu zikuwavuta anaganiza zobwelera kaye kunyumba kuti mwina akapitidweko ka Mphepo koma atafika pakhomopo anapeze zambiri zitasokonekerapo .....
Bambo: Pakhomo payamba kuoneka chonchi bwanji ngati anthu anasamukapo bwanji Mpaka mwayamba Unve chonchi
Mai: Iiih Unve wake nde Uti ngati ndi masiku onse za lero lokha tu izi aliyense anachokapo tu lero nde ogwira ntchito anasowa tikonza zimenezi
Bambo: Owo Chabwino ndeno Alinafe wapita Kuti ?!
Mai: Ooh Alinafe anapita Kubanja tu
Bambo: Chani ?? Iwe unali uli kuti kumamuyang'anira mwana akupanga zimenezo sunandiimbire foni bwanji ?!
Mai: iiih Alinafe tu anatenga Mimba nditamufunsa anadana nazo anangonyamuka kumapita kwa Mamuna anampatsa Mimbayo
Bambo: Ndiperekeze komwe akukhalako ....
"Apatu mai anagwidwa njakata kusowano kuti awaperekeza kuti poti samaziwanso komwe kuli Nafe"....
Bambo: chete ameneyu bwanji mesa ndati undiperekeze komwe kuli mwana
Mai: kungoti Alinafe tu anachoka osanditsanzika nde ndinayesera kumusaka koma sindinamupeze
Bambo: iweyo ameneyo osaziwa komwe kuli mwana ukamusake pasathe masiku awiri mwana akhale atabwelera pakhomo apo ai iwenso uchoke pano .......... .......
Apatu mai Mutu unakula kusowa kuti akayambira pati kukamusaka Nafe pena kuganiza kuti akangopanga Report ku Police ngati kuti Nafe anachita kusowa koma akaganiza kuti akakawafunsa kuti anasowa liti nde azikatchula Kuti Miyezi yatha ndithu zikavutanso .... Masiku awiri omwe mai anapatsidwa Anatha chinangotsala ndichigamulo basi kuti kodi ziwathera bwanji......
Bambo: Wakanika kumusaka Alinafe nde chomwe ndingakuuze ndichoti tikugawana Ana iweyo ako ndi omwewa watsala nao apawa ineso ndiyang'anira Alianfe ndi Martha ndeno china mawa ndikunyamuka kubwelera Kuntchito .
Mai: komatu....
"Mai anasowanso Choti angayankhule pakamwa pataumiratu mau kukanika kutuluka ndipo Bambo anali atakwiya kwambiri".........
Kunja Kutacha bambo uja anakonzekadi ndikunyamuka koma osasiya kali konse pakhomo paja, apa mpamene mai aja anaziwadi kuti yalakwa akakhala Ana aja Lucy ekha ndamene amatha kuzindikira mene zikukhalira ndipo anayamba kulaka laka Alinafe akanakhala sanathamangitsidwe polingalira kuti sibwezi ali pamavuti chonchi .......
Bambo ake Lucy atachoka kunyumba Kuja anayesera kumusaka Alinafe koma Sanamupeze mpaka anabwelera komwe amagwilira ntchito koma chomwe anachita ndikuwauza anthu mene amaonekera Alinafe kuti amene angazamuone azawayimbire foni ndipo azapatsidwa chiona maso..... Umunthu ndi Umunthu ndipo Bambo ngakhale anali atakwiya koma anaganiza za ana Awo Lucy ndi Charity kotero sanafune kuti mpaka ana ake avutike kwambiri chifukwa chakulakwitsa kwa Mayawo ndipo anayamba kumatumiza thandizo mokwanira ngati kale lomwe ndipo zinthu zinayambako kuoneka kuti zikuyenda ..............................Alinafe kodi zinthu zinali zikumuyendera motani ...?
Alinafe moyo kwa iye unali uli bwino ndipo anthu omwe amakhala nawo samawapezeranso Vuto ndipo amamukonda ndichikondi chomwe kholo limapereka kwa Mwana wake .( mokumbutsana makolo omwe anayamba kukhala nawo alinafe wa sanali makolo ake a jimmy ngati mukumbukira bwino lomwe bambo aja anamuuza alinafe uja kuti ife tangolowamo kumene panthawi yomwe amakasaka jimmy zomwe zikutanthauza kuti anasamukawo anali makolo ake a jimmy ndipo awa anali atsopanomo mnyumbamo)........
CONT................... Mai omwe amakhala nawo alinafe aja poti amaziwa momwe zimayenera kukhalira kwa munthu oyembekezera anagulira tu alinafe zonse zomuyenereza ...........
Masiku anali akupita mothamanga Muja ndipo miyezi 9 ya Alinafe nde inakwana kunatsala ndikumangodikilira tsiku loti akachire basi..................
Unali Usiku pomwe matenda anamuyambikira Alinafe ndipo atawadziwitsa omwe amawatchula kuti Amai wo anadziwiratu kuti nthawi ija ndi imeneyo ndipo anakatenga Galimoto mkumutengera Alinafe kuchipitala Komwe anakafikira manja mwa anamwino .... Anapatsidwa thandizo loyenelera ndipo anamwinowo sanafune kumutalikira alinafe chifukwa anaziwa kuti ali pafupi kuchila.......... *ng'aaaaa !!! ng'aaaaaa !!! ng'aaaaa* ..... "Wow ayitaneni mayakewo" .....
Namwino: Mayi yandikirani mphatso yanu yafika mdzukulu wanu wabwera
"Mai anayenda mothamanga tu kuti akawone kuti alandira Mphatso yanji kuti ndiwa Mamuna kapena wamkazi"...............
Mwana nde wabadwa 😂 Alinafe pano ndi amayi koma kodi ndika Boy kapena Ka Girl tiyeni tiwatsatire mai wa Mu part 9 mo tikawone nawo mphatso yo 😂
Khalani pompo kudikira part yotsatirayo.... Love you All my Fanz ❤
Osaiwala kupanga
👍LIKE
✉COMMENT
🔁SHARE
💖💖💖💖💖💖
💻Hes Vh Dmn🖊

08/02/2022

ALINAFE
Part 7.............
Choyamba tipepese kamba kakuchedwa kwa nkhani vuto ndi magetsi amene anandsokoneza komano apa tiyeni tiwerenge part 7 ija zikomo......................Tsiku lina Mai ake a Martha analandira Mlendo emwe anali nzawo kwambiri nthawi imeneyo ali pa sukulu ndipo posafuna kuzionetsera nkhaza nzawo tsiku li Anakonza chakudya chomwe anthu onse anakhala pamodz mkumadya ndipo Ali mkati mokukudya Alinafe anafuna kusanza, anayesera kuzigwira koma zinakanika mpaka pomwe anadzuka mothamanga koma sanapitenso mtunda wautali koma kusanza basi.. Aliyense maso anali ali paiyeyu ndipo mai anachita manyazi pamaso panzawo ...............
Nafe atabwera kosanza sanapitilizenso kudya koma kukanhosamba mmanja mkulowa Kuchipinda kwake kumakagona....
Kunja kuatada Alendo aja atamaliza kucheza ananyamuka bwino lomwe ndikubwelera pambuyo...
Mai: Alinafe tabwera kuno
Nafe: ine a Mai
Mai: ungandiuze kuti chimachitika Ndi chani ??
Nafe: chakudya chinangondibwelera kukhosi komanso ndinayambira dzana kudwala sindikunva bwino
Mai: Owo tili tonse tu pano ngati ukuziwa kuti ndi Mimba Hoooo sindikuziwa .......
Zinaoneka modabwitsako pang'ono kuti Mai yu sanaluse kwambiri ndi mene Nafe amayembekezelera.. Ndipo Usiku wu sanamulore Nafe kuti aphike ndipo Mai wo anaphika Okha Ndipo onse anadya Ndikugona............
Kunja Kutacha Nafe anatsanzika mai aja kuti akufuna kupita kuchipatala ndipo anamulira kutero koma ngakhale Nafe amatsanzika zakuchipatala ulendo wu sunali opita kuchipatala koma kwawo kwa jimmy ndipi analimba mtima kuti kaya akawapeza makolo a jimmy akalongosola chili chonse ....... Nafe anayenda mpaka anafika Bwino lomwe ataoditsa anavomeredwa ndipo anatuluka mnyumba muja anali munthu wabambo...
Bambo: Tiaope ngati
Nafe: Ai osati kwambiri ndine Alinafe ndimafuna nzamuone Jimmy ndi nzanga waku School
Bambo: Ooh owo unayamba wabwerapo kunoko kuzachezanso ndi Jimmy yo ukunenayo
Nafe: Eya
Bambo: papita nthawi yaitali bwanji chibwelereni kuno
Nafe: patha Miyezi itatu
Bambo: Ooh Okay umakhala muno wo anasamuka ifenso tikungopanga Rent ndipo uno ndi mwezi wachiwiri
""Nafe anaoneka ozizidwa komanso wamantha kwambiri, maso kufiira kufuna kulira kusowa kuti apangeno chani ndipo bambo aja atamuona anaziwa kuti china chake pa mtsikanayu sichili bwino koma kumufunsa samaulura kali konse malo mwake anatsanzika ndikubwelera kwawo ndipo kwawo anangofikira kugona""
Bambo uja zinamukhudzabe ndimene anaonekera Nafe ngakhale sanafotokoze kali konse ndipo akazawo abambowa atabwera anawalongosolera mene zinalili nawonso mai ananva chisoni
Mai: nde simunamufunse kuti amakhala kuti ?
Bambo: Ai sinalingalirenso zimenezo....,............
Masiku anali akupita mpaka pomwe Nafe analowa Mwezi wa 5 chitengereni Mimba ndipo samaonekera mpaka mai aja amakanika kumuzindikira koma mayi yu anayamba kudabwa zambiri kuti Nafe akumakonda kumangogona, kuchipinda sakutulukanso mwachisawawa ndipo anaganiza zoitanitsa Book lakuchipatala la Alinafe ataona anapeza ma results analembeedwera Alinafe aja anakhala ndi chidwi kuti aoneso date lomwe anapitira kuchipatala anapeza kuti alino mwezi wa 5 apatu mai anafufuma ngati aphulike ndipo uwu unali mkwiyo oti sanaonetsepo .....
Mai: izi ndizomwe ndimakaikira ndinanena ine kuti Uhule wakowo mnyumba mwanga sindikufuna koyamba unakatenga foni nditakuphwanyira sunainve wati ukatengano mimba Hooo nde kuti ndkuphwanyeno iweyo uziwe kuti Moyo wako palibenso nde Usandiphulitse Ngozi ndichokere pakhomo panga pano upite kwa inake achimenecho
"Alinafe analibenso mwai oti angayankhule koma kumangolira,,, izo tu zinali zochepera koma mayi anapita panali alinafe ndikuyamba kumugaira makofi ndithu uku akumunena kuti Hule iwe choka Mnyumba mwanga uone kolowera"".............
Monse zimachitika izi mkuti Martha ndiazibale ake ali ku sukulu nde mai kunali kumuthira phunzi Nafe mpaka kutenga Zovala zake ndikumupinyera panja ndikumutulutsanso Nafe mkumuuza kuti ngatia achedwe kunyamuka ayatsanso Zovala zakezo sakufuna kumuonanso.....
Nafe ananyamuka ndi Zovala zake asakuziwa Kuti alowera kuti akaganiza zakumudzi kwawo anali oti sakudziwanso kuti kumudzi kwawo ndikuti.... Apati Nafe anayamba Kumangoziyendelera...
Martha Pobwera ku Sukulu anabwera ndi nsangala kwambiri maka mphatso yomwe anaikonza kuti akamuzizimutse Nayo Alinafe ndipo atasiya makope ake anangothamangira kuchipinda kwa Nafe koma azizwa kupeza kulibeko choonetsa kuti Nafe amakhalanso mnyumba, apatu Martha anagwidwa ndi Mantha ndipo atawafunsa mayake anangomuyankha Kuti Nafe wapita kubanja ....
"(Martha analira ngati kuti wanva kuti Nafe wamwalira uku akuziyankhulira kuti Nafe ndichifukwa chani osanditsanzika mene ndimakukondera muja ungachoke chonchi,,, martha anasweka mtima ndipo anakhala okhumudwa ngakhale chakudya anakana)"......,.......
Dzuwa linalowa ndipo kamdima kanayamba kugwa, Nafe anali akungoziyendera ngati munthu opanda umunthu osadziwa chomwe akupanga mpaka pomwe anaiwala zoti akuyenda munseu mpaka pomwe galimoto inachita kumuzemba kuopetsa kumugunda, mosakhalitsa Galimo ija inayima ndipo munatuluka munthu wabambo ndi Mai
Bambo: Ooh Make uyu ndi mtsikana ndimkamunena uja anabwera kunyumba uja
"Awatu anali bambo ndi akazawo akuja anapita Nafe kokamusaka Jimmy kuja"
Munthu wamai oziwa kukonda anamuimitsa Nafe uja ndikumunyengelera kuti awawuze Vuto ali nalo ndipo Nafe anakwanitsadi kumasuka ndikuwauza chili chonse apa tu Mai ananva Chisoni ndipo anakhala okhudzika
Mai: ndeno apa ukupita kuti ?!
Nafe: sindikuziwa koti ndingapite
Mai: Owo Tiye upite nane kunyumba ukagone kunyumba kwanga panopa kwada kuyenda munseu mu upangidwa chipongwe
"Nafe anakhala chete kusowa choti ayankhe uku akuzifunsa kuti kodi ndipite kapena ayi " .......
Kodi mukanakhala inuyo mukanatani ?????..............
Part 8 ..............🖊

07/30/2022

ALINAFE
Part 6.......
Foni ya Alinafe inaphwanyidwa zonvetsa chisoni zija ndipo Nafe analira kuzinva ngati wachikondi wake amuphera basi maka polingalira kuti mwai Ozalumikizananso ndi jimmy wathera pompo.....
Nde poti chisoni Cha wina ndi chimwemwe cha wina izi zinali chonchi chifukwa mene Amalira Nafe mkuti Lucy ndi Charity akuseka monyogodola muja,,, Mosakhalitsa Martha anatuluka panja Koma ali okwiya kwambiri..... Apat Martha anakatenga Chindodo ndikuyamba kukwapula Lucy ndi Charity chifukwa cha mkwiyo Omwe anali Nao ..... Apatu ndewu yapachibale inayambika ana kumenyana ndipo Martha anali yekha kumenyana ndei anthu awiri zinali zodabwitsa kuona Martha akulimba mpaka kuliza anthu awiri onse .... Izi tu zinakwiyitsa mai ndipo ndikupsa mtima anamumenya Martha koma zonsezi ngakhale mene zimachitika Nafe anali ali pompo koma sakanatha kulowelera chifukwa nde iye anali opalamula kale ....................
Mkangano utazizira aliyense anakhala chete kuchita kuti ziiii ngati kulibe anthu, koma Nafe sanawerengere zimenezo ndipo anachepetsa kukhumudwa kwake ndikukagwira ntchito zonse zapakhomo ndikukakhala ndi Martha Kuchipinda kwake kumacheza nkhani zawo ......
Martha: nafe koma umaziwa kuti iweyo uzakhala Olemera ?!
Nafe: hahahaha mmh Mah ukunena zoona iwe waona chani
Martha: ineyo ndimaona choncho ndipo usazandisiye ngakhale nyengo zizavute
Nafe: koma iwe usandiseketse tu komanso iweyotu ndimaona kuti uzakhala ndi tsogolo labwino ndiwe munthu oziwa kukonda
Martha: mmmh nafe ukunena zoona
Nafe: eya koma uziziwa kuti anthu amadana ndizabwino
Martha: Eya ndimaziwa,, ndimaonera pa iweyo koma sindingakutaye ....."Nafe ndi Martha tu Anacheza nkhani zawo ndipo awiri amasangalara kuiwalaso kuti anali pamkangano"............................
Masiku anayenda mothamanga mpaka pomwe mwezi unatha ndipo nthawi yotsegulira masukulu inakwana .. Ngakhale Alinafe anauzidwa kuti Term imeneyi asapite ku School kamba ka fees iyeyutu sizimamugwirabe ndipo atakhala pheee analingalira..."(Jimmy anagulira foni kuti tizilumikizana komano ndizomwe zinachitika zija kodi kuli jimmy ko amandiganizira ineyo kuti chani !? Koma Osalephera mene akutsegulilidwa Masukulumu jimmy akafika Kusukulu kuja kuti akandione nde zoti ndisapite siigwirayi ndingopitabe mwina ndikhonza kukakumana naye)"..... Apatu Nafe anapanga chiganizo chopitabe kusukulu kuja kuti kaya akakhala panja.....
Mai: Alinafe mesa mnakuuza kuti term ino fees palibe nde wavala uniform ukupita kuti ?!
Nafe: ndikupita ku Sukulu week yoyamba samabweza fees ndizasiya kupita akazayamba kubweza fees basi
"" Apatu mai Sanalimbane ndizambiri koma kumusiyadi kuti apite chifukwa anaziwa kuti sizingapitilire mpaka kale"...............
Nafe anayenda mwachangu kufika ku Sukulu ndikuyamba kumusaka jimmy koma osamuona chomwe amangonva iye ndi dzina la jimmy lo basi magulu awanthu akulikambirana ndipo iye zinamuimitsa mutu kuti kodi zikutanthauza chani zimenezo .. Atafufuza ndipamene amanva kuti zotsatira zamayeso a form 4 zinatuluka kale ndipo amene wakhonza bwino ndi Jimmy Apatu Nafe anamwetulira kunva kukoma mumtima kuti mamunake wachita bwino..... Oh izi zisandiiwalitse kusaka jimmy wanga"" anaziyankhulira choncho mumtima ndipo anapitiliza kumusaka koma sanamuone.. Kenako anakalowa Class ndikuphunzira kufika nthawi yoweruka kumapitanso kunyumba ............................
Nafe atagona usiku watsiku limeneli anaganiza zinthu zochulukirako mmutu mwake;,,,,,,,,,"' Ndifukwa chani mwezi mpaka watha ineyo osapanga Period !? paja ati zimatheka kudumpha mwezi Osapanga eti koma nde tsiku ndizapangero ndizapanga kwambiri.... Chabwino koma jimmy nde wandikwiyira mwina angoganiza kuti mnasiya zadala osamamuyankhula pa foni eti nde ndipange bwanj pamenepa kapena ndipite kwawo"" ......
Awatu anali maganizo omwe anayenda kwambiri mmutu mwa Nafe patsikuli mpaka anafika popanga chiganizo kuti apite kwa jimmy koma anaopa kuti akhonza kukapeza makolo a jimmy nde akasowa choyankha ........
Ma week awiri anadutsa Nafe akupitabe ku Sukulu ndipo week yachitatu yakeyo onse osapereka fees anabwezedwa ndipo nafe anakakhalano pakhomo kuvomeleza kuti Sukulu yalephelekadi....
Moyo okhala pakhomo nafe unafika pomukwana chifukwa nde samapatsidwa mwai Opuma kuangotumudwa Tsiku lonse koma anakapanga bwanj koposa kumangopilira.....
Mwezi winanso unadutsa mpamene Nafe amazazindikiranso kuti Sakupanga period anayamba kuziganizira ngati mwina ali ndu Vuto lina lake ndipo anapanga chiganizo chopita kuchipatala ndikukakumana ndi Doctor ndikuyezedwa.... Nthawi yazotsatira;
Doctor: kodi pakatipa unagonako ndi Mamuna ?
Nafe: Eya
Doctor: zikanakhala bwino mukanabwera nonse ndimamunayo komabe nokha tikuuzani,nkhani ndiyoti muli ndi Mimba chemwali
Nafe: Mwatiiiii Doctor mwati nd....
Doctor: Eya muli ndi mimba ..." Nafe sanayankhulenso kanthu koma kunyamuka kumapita.".........
Nafe anayamba kumaoneka moyo osasangala ngakhale Martha Amayesetsabe kumusangalatsa Nafe koma iye chimwemwe chinali naye kutali kwambiri kwa iye kunali kuzifunsa mafunso........."kodi ndekuti enawa sakhala ndi mimba or agone ndi mamunawa amatani koma ndichifukwa chani zabwera kwaineyo zimenezi ai zalakwika ndipange bwanji ine chikhala chodziwa ndikanangopanga naye kamodzi tu koma mpaka week yonse tikupanga aaah ine ndeeee"" ....... Osanama Alunafe anavutika ndimaganizo kwambiri ndipo amayesetsa kuzibisa kuti kwawo asamuzindikire mpaka muyezi itatu inadutsa mkulowaso wa 4............
Tsiku lina Mai ake a Martha analandira Mlendo emwe anali nzawo kwambiri nthawi imeneyo ali pa sukulu ndipo posafuna kuzionetsera nkhaza nzawo tsiku li Anakonza chakudya chomwe anthu onse anakhala pamodz mkumadya ndipo Ali mkati mokukudya ............................
Inu inu Abale mkati mokudya mo munachitikanso chani 😁😁😁
Zili tu mu Part yotsatirayi choncho musatalikire kuti tinvere limodzi zomwe zinachitikazo chachikulu osaiwala kupanga;
👍LIKE
✉COMMENT
🔁SHARE
BMS 💥
💻Hes Vh Dmn🖊 🤓

07/30/2022

Hello,, People ndipepese lero kamba kakuchedwa kwa Nkhani, izitu zachiktika kamba kakuvuta kwamagetsi koma pompano tikhala tikukupatsiran part 6, Zikomo

07/29/2022

ALINAFE
Part 5..........
Nafe ananyamuka kuchoka kwa jimmy akungozinva kukoma akayang'ana samaonanso ngati kudziko ku kuli munthu wina hahahah koma paja ikakondwa kwambiri amakhala amalonda ali pafupi, apatu Nafe atayandikira kwawo anakumbukira mene anachokera ndipo nkhawa zija zinabweleranso mwakamodzi nafe anayenda mwamantha kuti zikamuthera bwanji tu koma atafika............ "Welcome back Nafe momwetulilidwa" awatu anali mau achimuna omwe anawanva nafe atangolowa mnyumba"......
Awa anali bambo awo achina Martha omwe nafe Amkangoganiza ngati anali bambo ake koma ndizomwe anauzidwa nafe ndi Martha kuti mai uja amanena Nafe mpamene anakumbukira kuti si bambo ake koma mosaonetsa kukhumudwa nafe anamwetulira ndikukawapatsa Moni...
.......
(Mokumbutsana Bambo wapakhomopo paja anapita dera lakutali kukagwira maganyu ndipo apa anali atabwera pakhomo kuti awone banja lake)............
Alinafe anayambako kukhala ngati mfulu tsiku li tu sanaphike koma kuphikilidwa or Kutumidwanso ai kungokhala basi zonse kumapanga Okha mai aja ndipo martha ataona izi anali okondwa mutsikuli naye nafe anasangalalabe kuona kuti ndimene anathawira muja bwezi ali pamavuto koma malo mwake wafikiranso pa mtendere.......
Atatha kudya chakudya chamazulo Martha anasamuka kuchipinda kwake kukalowa kwa Martha poziwa kuti palibenso omuletsa ......
Martha: Nafe ndikuganiza ngati ndiwawuze adad zomwe akupanga amai zija ine sizikumandisangalatsyi
Nafe: ukatero nde ulakwitsa kwambiri
Martha: ai adad apanga zoti amayi sazakuapangaso mkhanza
Nafe: eya koma zikhonza kusokoneza pakhomo pano mwina adad kuyambana ndi amai nde ndzosakhala Bho tu mmalo mwake amai wo mwina or adad apite akhala atasinthika
Martha: Chabwino tiyeni tigone mawa paja ku School
Nafe: eya tiyeni nazo
" Nafe anagona akungozinva kubhebha unali usiku wake wabwino maka akalingalira nthawi yabwino yomwe anali nayo ndi Jimmy" ,,,,
Kunja kutacha onse anakonzeka kumapita ku school koma kwa nafe amanyamuka ngati akupita ku School malo mwake umakhala straight wakwa jimmy ndipo akakumana Nafe samalora kungosiyana Osapanga kanthu. Eya zimakhala zokoma koma masikunso anathamanga kufika weekend ndio zinali zosatheka Nafe kuchokanso ngati akupita ku School mmalo mwake amangozinva kumusowa kwambiri jimmy.............
Masiku anali akupita mpaka pomwe term inatsendera kumapeto ndipo nthawi yoti achina Nafe atsekere nde inakwana... Kwa Nafe anali ndi nkhawa kuti akangotsekera amusowa kwambiri jimmy apano kunali kucheza kwawo komaliza chifukwa zinali zokaikitsa ngati nafe angamakayende kuti akumane ndi Jimmy...
Jimmy: Nafe nde zosamakayendazo sizikundinvekera bwino tu b nanga mpaka uzatsegulirenso??
Nafe: paja term yamawa ati sindibweranso ku School
Jimmy: ndichifukwa ndakubweretsera Mphatso iyi landira nafe
Nafe: iiiiiiih Jimmy wandigulira Foni
"Nafe anakondwa moposa chifukwa anaziwa kuti kulumikzina ndi jimmy sikunathe malo mwake azikacheza pa foni"
Jimmy: ndikufuna ndzikutumizilira ndalama pa Foni upitikize School kwanuko akakufunsa uzangowauza kuti wapempha apbinzitsi ako akunvetsetsa kuti uzikaphunzira kaye ulele
Nafe: ndisaname jimmy ine nde ndikunva kukoma kwambiri kaya mamuna iwe ndizakutani ine 😂
" kuna zoona Nafe anakondwadi koopsa kuja.... Anacheza ndi Jimmy motsanzika kuti pozawonananso ndipotsegulira achina nafe".................
Moyo waku Holiday unayambika ngakhale panali patanhodutsa masiku atatu koma Nafe anali atamusoweratu Jimmy ngakhale amacheza pa foni daily koma foni imakhala mobisidwa kuti kwao asaionei..........Bambo aja atacheza mokwanira ndi Banja lake anatsanzika kuti abwelere kokazisaka ndipo atangonyamuka mai matsinya anabwelera pankhope yake kutuma kosaleka Kuja mpaka nafe amakagona tsiku ili ana otopa kwambiri.......... Kunja kutacha nafe chifukwa chakutopa komanso kugona mochedwa pochezetsana ndiwachikondi wake zinamuapanhitsa kuti achedwe kudzuka ndipo mai anachilowa kuchipinda komko kuti akamudzutse nafe ayambe kugwira ntchito anadabwa chakumutu kwa Nafe kuli foni ndipo anaitenga ndikuyamba kuona ma SMS onse... Atamaliza anamudzutsa nafe ngati Zaulemu tu........
Mai: Ei nthawi zino kugonabe wajaila eti dzuka apa ukuyambe kugwira ntchito
Nafe: chabwino amai ndikudzuka .......
Nafe atadzuka anafuna aone kaye kuti jimmy watumiza mauthenga oti chani chifukwa anangogona foni ili mmanja koma ataisaka samaiona kuti ili pati kenako sanafune kuchedwa anangoti ayang'anabe iye mkupita kumakagwira kaye ntchito....... Atagwira gwira ndikumaliza anakalowa kuchipindw kwake ndikuyang'ana foni koma anagwidwa ndi mantha asakuona kuti ili potani koma zinali zoti palibe akanamufunsa chifukwa zoti ali ndi foni amadziwa ekha ................
Tsiku lonse linatha kunja kutadano mpamene mai anaitana Alinafe ....
Mai: Iwe ichi ndi chani
Nafe: foni amai
Mai: waitenga kuti ?
Nafe: ndiyanzanga anandi.....
Mai: Choka apa "nafe ndimakukonda" amenewonso ndimauthenga anzanko yo ?!
"Nafe anasowa choyankha ndipo anali ndi mantha kuti zimuthera bwanji"""
Mai: Zauhule mnyumba mwanga muno Ai......"(Meme amayankhula Chomchi uku anali akumenyetsa foni ija pamsi ndipo inanyenyeka zoti panalibenso kutolera kanthu koma mtima sunawaphwere pompo koma kuitemga kukaiyatsanso,,,,, Apatu Nafe anali kuzinva ngati amuphera wachikondi wake kuganizano kuti jimmy nde azalumikizana bwanji Osanama Nafe analira ....paja kulira kwa wina ndi chimwemwe cha wina ,, panthawi yomwe nafe amalira Lucy tu ndi Charity iwo kunali kuseka uku akuimba wina amphwanyira foni,, panthawi Martha analibe choyankhula koma anali odzadzidwa ndi mkwiyo maka zomwe zimachitikazo zitafika pomukwana anangotuluka panja ndikutenga chindodo chachikulu bwino ndikulowa nacho mnyumba........ ..... .........
Hahahahahha kodi Martha ndodo yo amafuna apange nayo Chani hahahah 😂 Okay tiyeni tione mu Part yotsatirayo kuti zinathamo bwanji.....
Osaiwala kupanga
👍LIKE
✉ COMMENT
🔁 SHARE
💻 Hes 🖊

07/28/2022

ALINAFE
Part 4 .....
Ngakhale kunja kunali kukuda Alinafe sizimamukhudza chomwe amangosamala iye ndiza jimmy
Koma mosakhalitsa anasiyana,, naye Nafe anayenda changu kukafika ndipo atafika kwawo kunali kuyankhulidwa.........
Mai: nthawi yobwera munthu pakhomo ino ? Pakhomo pano pakukwana eti ingosamuka upeze banja lako uzibwera nthawi yomwe ufune
Nafe: Pepan kungoo......
Mai: Pepan ndekuti chani ?? Nde umati ataphike ndi ndani nthaw zino kapena umafuna uzapeze akapolo ako atakuphikira eti,,,,, Kuli ma Poto ukukuziwa ngati njala ikupweteka ukaphika..........
Atayankhula chonchi Alinafe sanayankhulenso kalikonse mmalo mwake anakangolowa Kuchipinda kwake Ndikumakagona, mosakhalitsa Martha naye analowa Komko...
Martha: Nafe Ukugona sudya ??
Nafe: Eya ndili Okhuta Dear Osadandaula Ndadya ku School ku nzanga anabweretsa zakudya
Martha: Ai ukundinamiza ukufuna kungondinyengelera iwe dzuka chonde ukaphike ndikakudikira
Nafe: mmh Zoona tu koma ndili okhuta kwambiri or ndikaphike sindikwanitsa kudya
Kukana kwa Nafe kuphika izi zinamukwiyitsa martha ndipo ananyanyala kuyamba kulira zomwe zinapangitsa Nafe kunva chisoni koma zinali zomuvutabe kuti angakaphike maka mau opweteka omwe anayankhulidwawo ..... Mwachoncho anagona ............
Miyezi inali ikupita masikunso mkumatha ndipo mthawi yoti A form 4 alembe mayeso inakwana ndipo ama Class enawa anapatsidwa Holiday...
Kwa nthawi yomwe Nafe anali pakhomo nthawi ya Holiday anangosandukano ngati kapolo kuchita kukhumba atangotsegulira kuti nthawi ina azikhala ali ku School komaso akalingalira kumusowa Jimmy zimamupweteka kwambiri... Kenako tsiku lina ali khale kuchipinda kwake anaitanidwa
Mai: Alinafe !!!!
Nafe: Weeee Mah.......
Mai: Ukutan ?!
Nafe: ndimalemba zina zake zaku School
Mai: Okay komano School ikuoneka kuti ivuta maka Fees siipezekanso nde term inoyi ikatha basi School yonso yathera pompo
Nafe: Ahm ahm (Mosakhalitsa Nafe anayamba kugwetsa misonzi kusowa choti angayankhe kenako anakalowanso nyumba)
Izitu zinalo zifukwa zokwanira kumukhazika Nafe Okhumudwa ndi chakudya chomwe samachinva kukoma,, Umoyo wa Nafe unasinthiratu ndipo maganizo anamuchulukiliratu kwanthawi yochepa anachita Kuonda Nafe ......
Mayeso anamalizidwa ndipo achina Nafe anabwelera Ku school ndipo tsiku li atangofika anali ndi chikhulupiliro kuti Jimmy ali komko kumudikira iyeyu nde naye Nafe sanachedwe koma kuyamba kumusaka Jimmy.... Mosakhalitsa anangoti Maso Phaaaaaa,, apa tu aliyense kunali kuyenda mwachangu ndikukumbatirana kwaka nthawi uku akauuzana monong'ona kuti ndakusowa.........
Jimmy: Nafe ndakusowa koma
Nafe: ineso kwambiri ndipo tsiku ndi tsiku ndimaganizira iweyo mamunanga
Jimmy: ukumaganiza kwambiri koma eti Nafe
Nafe: iiiih Jimmy sungazinvetse koma ngakhale ili nkhani yaitali komanso ngakhale ndinayamba kukubisira kale kale osamakuuza leroli ndikuuza chili chonse
"Nafe anayambapo kufotokoza chili chonse mene amakhalira kwawo komanso zokhudza kusiya kwake kwa School Chifukwa cha Fees" ...... Mene amamaliza izi kuyankhula Naye Jimmy nkhope yake inaoneka yokhumudwa ndipo poyankhula panachita kumusowa poyambira..
Jimmy: Okay nafe ndanva Ndizosakhala bwino koma ndili ndi Plan ineyo ndipeza njira ndipo School yako itheka wanva Osadandaula ndimakukonda
Nafe: zikomo kwambiri Jimmy koma nde upanga motani ?
Jimmy: koma nafe Nthawi ikutha tu umayenera ukalowe Class
Nafe: Inayi ndikufuna kungokhala ndiweyo lero sindkulowa Class ine....... Ali mkati mocheza ananva Belu kulira ndipo uku kunali kuitana Ophunzira kuti akakhale pa Assembly zomwe zinasonyeza kuti pali uthenga wapadera mosakhalitsa ophunzira onse anakhamukira komweko ndipo aliyense anali tcheru kuti anva Chani...
Mr kasiya (Mphunzitsi): Uthenga Wachisoni Mmodzi mwa aziphunzitsife waitisiya nde ndi dongosolo lomwe likhale pa mwambo onse kuti uthe ndiwautaliko nde munkhala ndi week ya Holiday muzabwerenso Lolemba linalo zikomo.. Anayankhula Choncho Mphuzitsiyo akuoneka okhumudwa ... Atabalalika Ophunzira aja aliyense kumaona Kolowera naye Jimmy ndi Nafe nawo analowera kwawo komwe anakakhala ndkumachezetsana atagula zokudya zao ukukumadyetsananso zachikondi zija .............
Kunena zoona Nafe amanva kukoma akakhala ndi Jimmy pafupi amayiwaladi Zambiri ....
Nafe: jimmy ndaganiza Mofatsa Kunyumba Za Holiday yi sindikanena ubwino wakenso sangaziwe kali konse nde Daily ndizinyamuka ngati ndikubwera Ku School tizikumana Daily ndikufuna ndizingokhala ndiweyo
Jimmy: Oooh yah ndazikonda nde malo mwake mawalo tikakumana ndikutenga ukaziwe kunyumba
Nafe: kwanu ai sindizizamasuka
Jimmy: Ai anthu onse kumakhala kulibe tizakakhala awiri wiri Momasukanso
Nafe: chabwino ndizatero
Jimmy: Eya ndipo osangoti mawa Lokhaliyi koma week yonsei akuapatsani Holiday yi uzingobwera straight kunyumba tizakhala ngati banja basi......."""hahahahaha !!, onse anaseka""..........
Awiriwa anacheza mpaka chakumadzulo kenako anasiyana onse ndikumapita kwawo.... Usiku watsikuli Nafe unamutalikira kuona kuchedwa kuti Kuche koma mopilira momo kunachadi ndipo Nafe anakonzeka bwino lomwe ngati akupita ku School koma akuti azinyamuka......
Mai: Ukupita kuti
Nafe: Ku School
Mai: mesa Lucy ndinamutumira kuti akuuze kuti lero usapite ku School ndikufuna ndikutume
Nafe: Sanandiuze tu ine ndipo....
Mai: Chokaaa ukupangira Dala iwe koma ndakuuza apa ndikusamba Kaye
"Nafe anachita kuziona ngati dziko lamuthera atabalalikiratu ndizosemphana ndizomwe amayembekezera kuzifunsa kuti kuona kuchedwa konse kuja amaonera kuchedwera zimenezi"
Mtima unamuwawa kwambiri ndipo anakanika kupilira mpaka anaganiza zongothawa basi ndipo mpaka anachoka mwakachetechetedi Mai osaziwa anangodabwa ziii munthu kulibe .....................
Nafe Anakumana Ndi Jimmy monga mene anagwiliziranirana kenako anatengana ndikumapita kwawo kwa Jimmy....
Jimmy: lero nyumba ndiyathu timasuke ngati Banja lero ndidye zophika akazanga
(Hahahhaahhahahahaha) onse anasekelera mosakhalitsa jimmy anamuza nafe kuti athandizane kuphika zakudya,,,,, atamaliza anakhala ndithu onse ndikudya limodzi monga Banja........ Nkhani zawo zinali pakamwa uku akumenyana mwachikondi mpaka kumagwirananso mwakamodzi onse anakhala chete ngati kwagwa chivomerezi ndipo panthawi mkuti aliyense akuyang'ana mmaso mwanzake ndipo mosachedwa zodyana milomo zinayambika Nafe anakumbukira tsiku lake loyamba lija anapangaso ndi jimmy lija anazinva kukoma kwambiri ndipo anakanika kuti amusiye Jimmy ndipo samkaziwa kuti kwinako zimapitilira bwanji komano anafuna atazilawa mene zimakhalira mosakhalutsa Nafe anayamba kumuchotsa zovala Jimmy naye Jimmy sanachedwe koma kuchotsa Zovala Nafe ..........ziiiiiiii 😁😁😁 game inaseweredwa mbambande Mpaka Nafe anachita kuzinva ngati ali dziko lina...
Nafe: Jimmy sindkwanitsa ine ineyo jimmy ndineyo wako Jimmy chita nane chonde
"hahahahha Nafe anayamba kuyankhula ngati wapenga nkhani zovuta kulumikizika kuti akufuna kunena chani"..........
Linali tsiku lokoma kwa Nafe ndipo amkachita kuona kuluza kuti asiyane ndi jimmy koma poti kunja nthawi imapita ndipo anayenera kubwelera mmbuyo kenako jimmy anamuperekeza Nafe ndikumupatsa ndalama yoti azigwiritsa ntchito..........
Nafe atafika kwawo nanji machokedwe anali ochita kuthawa ,,,, hahahahahaha zinaliko ukuuuu tiyeni tione mu Part yotsatirayo ..
👍Like
✉Comment
🔁Share
💻 Hes 🖊

Address

Los Angeles, CA

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when BEST Malawian Stories posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Videos

Share