Umfula online

Umfula online News updates

16/11/2024



Zokonzekera zonse za ndondomeko yogula feteleza wotsika mtengo wa chaka chino akutu zili mchimake pa malo ogulitsira a Namadidi pomwe tapenza kuti Matumba okwana 300 afika kale pamalopa.

Mmodzi mwa omwe akulongosola tchitoyi bambo Liwawa akuti pano chasala ndi makina a phone omwe azigwiritsa tchito pogulitsura fetelezayi omwe akuti padakali pano sadafike.

Alimi okwana 1 million ndiomwe akuyembekezeka kupindula ndi ndondomeko ya chaka chino dziko muno ngakhale pali nkhawa kuti ikhoza kukumana ndi zovuta.

15/11/2024



Malo olembetsera kalembera wa vote pa center ya Namadidi Trading sopano ayamba kuthandiza omwe alibe ziohatso komanso omwe akudiklira kuti ziphatso zituluke patadusa masiku 7 asakuwalora otero chiyambire.
yapeza kuti anthu omwe analibe zowayenerezazi amabwezeka ponena kuti makina a NRB anali asanabwere ndipo amawatumiza ku center ya Namadidi school ngakhale bungwe la MEC lidalengeza kuti malo onse olembetsera NRB izikhalapo.

Pofika lero anthu omwe ziphatso zawo zinasowa,kuonongeka kapena sizinatuluke ayamba kuthandizidwa kupatula omwe alibiletu chiphaso ndipo akumatumizidwa Ku malo ena a Namadidi school ati poti ndikomwe kuli Makina ojambulira cha Umzika.

Komatu izi zikususana ndi zomwe MEC idanena maka potsatira chigamulo cha Bwalo lalikulu. Ife ngati tikuuona kuti mmene ndondomeko yakalembera wa vote ikuyendera ili ndi kuthekera koti ambiri salembetsa maka kwaomwe alibe ziphatso za umzika.

Kusapezeka kwa makina ena ojambulira ndi Bungee la NRB malo ena akalembera kukhonza kuphwanya ufulu wa mzika zina zomwe zikufuna kutenga nawo gawo pachisankho.

11/11/2024



Vuto lakusowa kwa mafuta agalimoto lagundikanso mumzinda wa Zomba pomwe kuyambira dzulo wakhala opanda mafuta a Petrol. UmfulaOnline yayendera malo onse omwetsera mafuta komwe mwambiri mwa malowa muli mizere ya mafuta ngakhale kuti sizikuziwika kuti abwera liti mafutawo.

Polakhula ndi mmodzi mwa akabanza Patrick Kalele yemwe amachita kabanza kuchoka pa trading ya Namadidi kukafika ntown ya Zomba ati vutoli likusokoneza business yawo.
Iwo ati ogulitsa mafuta a black market akumakweza mtengo wamafutawa kuchoka pa k3000 kufika pa k10000 zomwe zodandaulitsa kwambiri.

Iwo adaonjezeranso kuti mafutawa akabwera mmalo oyenera, othira mafutawa akumafuna ndalama yapamwamba kuti athire mafuta ochulukirapo.
Kunena mwachilungamo vuto lakusowa kwa mafuta agalimoto lafika posautsa ndithu.

10/11/2024



Tchito yakalembera wa zisankho inayamba mochedwerako lero pa malo olembetsera a Namadidi Trading center kamba ka vuto la makina olembetsera. Modzi mwa omwe tidalakhula nawo anati angowalemba koma sadawalowetse mu system ndipo adati awayambira zonse zikatheka.

Tidayetsa kuti tilakhule ndi akuluakulu pamalopa koma sitidatero kamba kazovuta zina.

09/11/2024



Tchito yakalembera wa zisankho yayambika mgawo lachiwiri. malo angapo kuphatikiza center yayendera ma center angapo kuchangalume kuphatika center ya Namadidi.

Anthu ochepa chabe ndimwe ayamba kukalembetsa mamawa uno koma pali chiyembekezo kuti anthu ambiri kuchangalume atenga gawo patchitoyi.
Mmodzi mwa omwe atalakhula nawo ndi uMfula atiuza kuti amaoneka kuchedwa ndipo akakhala oyamba kulembetsa kalemberayu.

Padakali pano zonse zili mchimake ndipo kalembera aziyamba 6 koloko mamawa ndipo azitseka 5 koloko madzulo. Omwe alibe chiphatso cha uzika aku lpephedwa kutenga kalata ya kwa mfumu ndipo akathandizidwa.

06/11/2024

Changalume constituency Chipini ward Malo olembetsera kalembera wa mavote.

1.Kapako FP school
2.Matipa FP school
3.Chikungwa FP school
4.Kalira FP school
5.Masala FP school
6.Zobwe FP school
7.Kauzi Catholic ware House

Tiyeni tikalembetse!
Vote yanu, Ufulu wanu, kusakha kwanu, Mphavu zanu!

Abbas Adams

06/11/2024

Changalume constituency Namazi ward Registration Centers
1.Nthondwe Agriculture EPA
2.St Anthony FP school
3.Mwandama FP school
4.Dindi FP school
5.Linjizi FP school
6.Nambande FP school
7.Lithipe FP school
8.Mayera FP school
9.St Agnes FP school
10.Chingale FP school 11.Ndunde FP school
12.Gala JP school

Tiyeni Tikalembetse!
Vote yanu,Kusankha kwanu,mphavu yanu, Ufulu wanu!

Abbas Adams

06/11/2024

Good Morning?

The following list are registration centers established by MEC for Namilongo Ward (Changalume constituency).

1.Namadidi Trading center
2. Namilongo FP school
3. Nkanda FP school
4.Namadidi FP school
5.Msamba FP school
6.Nswaswa FP school
7.Katete FP school
8.Mbeza FP school
9.Changalume Barracks FP school

Let's Go and register!
Vote yanu Kusakha kwanu, mphavu yanu, ufulu wanu!

Abbas Adams

05/11/2024

Kwasala masiku ochepa kuti (4days)to go kuti tikayambe kulembetsa nkawundula wa zisankho. Tiyeni tikalembetse mwa unyinji kwathuko zikayamba.

Mukakalembetsa ndeuti
Muzakhala ndi mwayi ozavoteta wakumtima kwanu,
Vote Yanu,mphavu yanu,kusakha kwanu

Tiyeniii!

05/11/2024

UTHENGA WAPADERA!

Bungwe la Malawi Electro Commission (MEC) layamba kalembera wake wa chisakho cha mchaka cha 2025 pa 16 September dziko muno.

Amalawi azanga ndikukupephani kuti kalembera akayamba kwanuko, tiyeni tikalembetse mwaunyinji kuti tizakhale ndi mwayi ovota.

ZOYENERA POKALEMBETSA
1.Mukhale kuti ndinu Mzika ya Malawi kapena mwakhala dziko muno kwa zaka 7.

2.Mukhale ndi chiphatso Cha uzika/ Chipepera chodikira kuti chaumzika chituluke ndipo ngati mulibe zonsezi ,pitani mutatenga kalata ya kwa mfumu ndipo aNRB alikonko akakuthandizani

3.Mukhale kuti muli ndi zaka 18 kapena muzakwanitsa zaka 18 pomazafika tsiku lovota pa 16 September 2025

NB osavala zovala za makaka achipani chilichonse ayi. Pewani ziwawa pa malo olembesera.

Vote yanu, Mphavu yanu, kusakha kwanu Ufulu wanu.!
Mukalembetsa Lero ndekuti muzakhala ndi mphavu komanso ufulu osankha wakumtima kwanu.........OSAPHWEKETSA!

Abbas Adams ( shadow councillor Namilongo ward/changalume).

27/10/2024




"Not stupid" ndi nyimbo imene anthu omwe adasokhana Ku bwalo la Civol Ku Lilongwe amudandaula nayo Burning Spear.
Nyimboyi kwambiri imakamba za ulamuliro wa nkhanza, kuzuzula adindo osalemekeza ma ufulu a anthu komanso ku kukanika kukwanitsa malonjenzo.

Ngakhale anthu amakuwa kuti akufuna nyimbo katswiriyu ayimbe nyimboyi koma katalangweyi sanayelekeze.
(They told us things will be better,they told things will be cheaper) pena imatero nyimboyo.
Padakali pano anthu omwe anali Ku phwando la mayimbidweli akuti Spear wasiya mwendo mmalere ndipo akuganiza kuti Ku State house kuja mwina kapena.......Nanga ndichani?

25/10/2024


Pomwe wina Ali Ku ndende,

President wa dziko la Malawi Dr Lazorous Chakwera ndi mphavu zomwe alinazo wakhazikitsa committee yapadera yoti ifufuze kulekelera komwe kunachitika pa ngozi yomwe idapha Wachiwiri wadziko lino Dr Saulos Chilima ndi anthu ena 8 pa 10 June 2024 Ku chikangawa.

Committee yi isogozedwa ndi Justice Jabbar Alide. Ena mwa omwe Ali mu committee ndi Brigadier Mituka ( Retired), senior Chief Makwangwa, nkulu wa CIDED Silvester Namiwa Monsignor Patrick Thawale kungotchula ochepa.

Tikupstsirani zambiri

22/10/2024



Ntchito yolemba mzika nkaundula wa zisankho yayamba lero dziko muno mmadera omwe MEC idalengeza kuti iyamba.
Zomwe tapeza, anthu ochepa chabe ndiwo akutuluka kukachita kalemberayi.

Izi zikuchitika pomwe mabungwe ena komaso zipani zosusa zikuti sidzikukondwa ndi ndondomeko ya kalemerayi.

 Mwambo okumbukira achinyamata pa dziko lonse la pansi (International youth day) wachitika lero pa bwalo la sukulu ya Ns...
17/10/2024



Mwambo okumbukira achinyamata pa dziko lonse la pansi (International youth day) wachitika lero pa bwalo la sukulu ya Nsondole kwa TA Kuntumanji M'boma la Zomba.

Mwambowu omwe udasokhanitsa achinyamata osiyanasiyana udachitika pa mutu oti "Wachinyamata ndi njira zamakono pachitukuko chokhazikika". Pamwambowu padaliso mabungwe osiyanasiyana monga ANAPA, Hope Project Namibia,Emanuel international, spakle Foundation komanso YONECO mwa ena.

Achinyamata ochokera Madeira osiyanasiyana awonetsa zithu zosiyana siyana zomwe zambiri mwa izo ndi zamakono komanso tchito za Maluso amanja. Mmawu ake wa wa pampando wa achinyamata m boma la Zomba M***a Sanudi adathokonza mabungwe omwe anathandizira mwambowu kuti utheke komanso kulimbikitsa achinyamata kuti azikhala oganiza mwakuya panjira zamakono za Digital kuti zikoli litukuke.

Mafumu, Makhansala, phungu wadera la Zomba Nsondole DYO ndi ena mwa omwe analemekeza mwambowu.
Tsiku lokumbukira achinyamata limachitika pa 12 August pa dziko lonse la pansi chaka chilichonse.


Olemba: Abbas Euza Adams

Address


Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Umfula online posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share