16/06/2024
A President a SMC abwera ndi asilikali mkachisi
Mapemphero anaima kaye kwa mphindi makumi atatu pa Bangwe SDA Church mzinda wa Blantyre pamene kunabwera President wa South Malawi Conference Pastor Thomas ndi ma galimoto atatu odzadza ndi apolisi onyamula mifuti lero la Sabata.
Malinga ndi chikalata chomwe analembera mpingowu kubwera kwawo amabwera ndi cholinga chozathetsa mpingo. Ngakhale a khristu anawapempha k*ti audzidwe zifukwa zomwe ak*thetsera, iwo sanafotokoze pachifukwa ichi mpingo unawauza k*ti asabwere.
Kamba kak*ti a SMC anakakamira kubwera pogwiritsa ntchito mphamvu zawo ankhristu sanawapatse mpata oyankhula ndipo amangoimba nyimbo. Pastor Thomas omwe anabwera ndi Executive Secretary wa SMC a Smart Chimwaza anaganidza zobwerera kumapita ndi a police awo.
Akhristu sanafune zokangana ndi aliyense koma kumangoimba nyimbo ndipo panalibe kukangana kulikonse ndi a police ngakhale anthu oyandikira ochuluka amene anakhamukira panja pa kachisi podzidzimuka ndi mdipiti wa galimoto za apolisi anakuwidza galimoto zawo pamene anali kupita kwinaku akhristu akupitiridza kuimba nyimbo zawo mkachisi.
Atapita a president, mapemphero anapitiriranso monga mwa kupembedza kwa tsiku la Sabata.