18/05/2024
Timveni Online yalemba:
ZACHIKUNJA IFE AYI- MAGU
Mfumu ya zinyau, Tay Grin walira chokweza pomwe akulu-akulu a sukulu ya ukchenjede ya Malawi Assemblies of God (MAGU) aletsa kwatswiri wa mayimbidweyu kukayimba ku sukuluyi ati popeza nyimbo zake zimalimbikitsa chikhalidwe cha gule.
Malingana ndi wachiwiri kwa phunzitsi wa mkulu wa sukulu ya MAGU, nyimbo zaTay Grin sizigwirizana ndi maziko a chikhiristu omwe sukuluyi imalimbikitsa.
Grin amayembekezera kukayimba pa sukuluyi pa mwambo olonga Mr & Miss Magu.
Polemba pa tsamba lake la mchezo la Facebook, Tay Grin wati ndi odabwa kuti sukuluyi, yomwe ndi ya mpingo, ikulimbikitsa tsankho ndikusalana pa chikhalidwe pomwe imayenera kukhala patsogolo kulimbikitsa umodzi.
Iye wati ili ndi phunziro ku dziko kuti likambirane zakufunika kolimbikitsa ndi kulemekeza chikhalidwe cha dziko lino.
Mwambo olonga Mr & Miss Magu ukuyembekezeka kuchitika lero Loweluka ndipo oyimba monga Pop Young, Keli Devine komanso Zonke Too Fresh akuyembekezera kukayimba pa mwambowu.