14/01/2025
Alimi a fodya mdziko muno awalimbikitsa kuti adzigwilitsa ntchito dzigafa za moyo pa ntchito yawo pofuna kuthana ndi vuto la kusintha kwa nyengo.
Bungwe la atolankhani olemba nkhani zokhudza ulimi wa fodya mdziko muno la Media Network on To***co (MNT) ndilomwe lapereka pempholi.
Kalata yomwe wasainira ndi mtsogoleri wa bungweli Alfred Chauwa yati ulimi wa fodya ukukolezera kwambiri mchitidwe woononga mitengo mdziko muno ndipo alimi akuyenera kuyamba kugwilitsa ntchito dzigafa za mtunduwu.
A Chauwa alimbikitsanso alimiwa kuti abzale mitengo yochuluka m'malo onse omwe anadula mitengo ponena kuti izi zithandiza kwambiri pa ntchito yobwezeletsa chilengedwe mdziko muno.
Kudzera mu kalatayi a Chauwa ati bungweli likukhulupilira kuti mbewu ya fodya ikuthandiza kwambiri pobweretsa ndalama zakunja koma nkofunika kuti adindo akhazikitse njira zoyenera zotetezera malonda a mbewuyi ndi chilengedwe.
NewsOnline Kukupatsirani Nkhani Zamabungwe/Kampani/ Ndi Anthu ena