Mizwanya FM Radio

  • Home
  • Mizwanya FM Radio

Mizwanya FM Radio Mizwanya FM is a community radio station located in a small rural community, Yasini within Chiradzulu District to the Southern Part of Malawi.
(1)

03/06/2024

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Binwell Kandodo, Maye Ntuana, Iqra Adan, Innocent Kachingwe, Aubrey Chisemphere Mbuna, Jonah Bandazi, Sean Joseph, Blessings Makoza Juniour, Austin Chikhusa, Cidreck Mwamadi, Kennedy Kaledzera, Phillip Stephano, Damiano Thengo, Phillip Kazembe, Albert M Banda, Laiton Dougalas, Enock WA Chilungamo Jrd, Aubrey Liwambano, Rhodah Panganani, Manuel Mpulula, Mikeas Crement Tomas, Samuel Khomela, Madah Chawango, Iveness Shaibu, E Pedro Kun Chrispin, Frank Gnazio, Iqbal Ibrahim Mussah, Dumba LLoyde, Nelson Chavula, Said Dickson, Victor Manyozo, Lington Chimutu, Tonny Montana, Taibu Mayeso, Lameck Josephy, Magrit Simeon, Kelvin Folley

22/08/2023

Dr Michael Usi zikuonetsa kuti alowa muchipani cha Malawi Congress Party mwachinsinsi ndipo izi zakwiyitsa akuluakulu ena achipani cha UTM.

10/06/2023

Kusayenda bwino kwa zinthu mdziko muno kaamba ka kusowa kwa utsogoleri wabwino, kwapangitsa a Malawi ambiri kukhala mu umphawi komanso kukumana ndi mavuto otsamwitsa pa umoyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

Pofuna kuthana ndi mavuto amene amalawi ambiri akukumana nawo, anthu ambiri ayamba kuwonetsa chidwi chofuna kuzapikitsana nawo mma udindo osiyanasiyana pazitsankho zomwe zizachitike mchaka cha 2025.

Pongolani Mustafa yemwenso ndi mmodzi mwa anthu omwe ali ndi chidwi chofuna kuzapikitsana nawo pa mpando wa phungu wa nyumba ya malamulo ku chigawo chakummawa m’boma la Machinga, wati atsogoleri ambiri akhala akumangolonjeza zinthu zosiyanasiyana kwa a Malawi koma osakwaniritsa malonjezo awo.

Mwazina a Mustafa ati iwo khumbo lawo ndikuzawonetsetsa kuti moyo wa munthu ukulandira zomwe ukufuna mu nthawi yake.

Anthu ambiri mdziko muno ali mu mavuto azaoneni monga umphawi, kusowa kwa ntchito, chakudya, kusowekera kwa chitetezo, ntchito za malonda sizikuyenda bwino, ndalama zikupezeka kwa anthu ochepa ndi zina zambiri zomwe zikusowekera utsogoleri wabwino wa masomphenya.

>>>team_mizwanyafm

08/05/2023
Association of Malawians living in Zambia (AMZA) in collaboration with Malawi High Commission in Lusaka - Zambia donated...
08/05/2023

Association of Malawians living in Zambia (AMZA) in collaboration with Malawi High Commission in Lusaka - Zambia donated assorted relief items worth over 10 million kwacha to the survivors of tropical Cyclone Freddy in Mulanje and Phalombe districts.

Craig Chongwe chairperson for AMZA has confirmed that the development will change the lives of the victims in the areas of senior chiefs Mkanda and Namasoko and more than two thousand people have benefited from the aid. However police officers who were also affected by the cyclone at Muloza boarder in Mulanje are among the beneficiaries.

AMZA donated similar items worth 13 million kwacha on their first trip and the relief conceded are blankets, heavy duty pots, clothes, shoes, maize flour, Matemba, Gerry cans, sanitary pads, bathing soap etc and these were given to Katuma, Misimisi,Tamani, and Police Officers in Muloza, Mulanje.

>>>team_mizwanyafm

Anthu omwe akukhala pa malo osungirapo okhuzidwa ndi Namondwe otchedwa Freddy pa Sukulu ya Lauderdale komanso mzika zokh...
02/04/2023

Anthu omwe akukhala pa malo osungirapo okhuzidwa ndi Namondwe otchedwa Freddy pa Sukulu ya Lauderdale komanso mzika zokhala midzi yozungulira gulupu Chipoka mfumu yaikulu Mabuka ku Mulanje adandaula kamba ka dyera la mafumu ena amene akumapezeka pa malowa tsiku ndi tsiku.

Mizwanya FM yapeza kuti mafumu okwana asanu ndi mmodzi omwe ndi a Masanga, Mukhwera, Chipoka, Muthiwa, Mwangala, Mugonya mosogozedwa ndi a Mphwera akumakhala pa malowa tsiku lirilonse ndipo thandizo likafika akumatenga mwanseri kukasiya ku nyumba zawo.

Polankhula ndi ena mwa okhuzidwawa ati zinthu monga mafuta, mkaka, ufa ndizina sizikumaoneka bwino zikabwera ndipo akumatha masiku ochuluka asanadye ndiwo zoika mafuta. Mwazina iwo akupempha amabungwe ndi ena akufuna kwabwino kuti akabweretsa thandizo azigawa okha kwa mawanja omwe ali pamalopo.

Chiwerengero cha anthu okhuzidwa omwe ali pa Sukulu ya Lauderdale ndi pafupipafupi 1,391.

>>>team_mizwanyafm

31/03/2023

Mavuto omwe ali m'malo osungiramo anthu okhuzidwa ndi Namondwe wa Freddy mmadera ambiri m'dziko muno akupitirirabe kamba koti zokudya zimene akumadya sizakasinthasintha ndipo ena mwa okhuzidwawa ndi a ulumali osiyanasiyana komanso ena amadwala matenda omwe amayambisidwa ndi kachilombo ka HIV.

Kafukufuku amene Mizwanya FM yapeza waonetsa kuti m'malo ambiri mukumapita ndiwo za ntundu wa Soya pieces opandanso ndiwo zina.

Ena mwa anthuwa kuchokera Madera onse omwe akhuzidwa mdziko lino la Malawi adandaula kuti pakumasowekera upangiri wabwino kuchokera kwa azaumoyo kamba koti ena mwa anthuwa amamwa mankhwala omwe amathandizira kubwezeretsa chitetezo mthupi ndipo ena akumavutika kudya kamba ka ulumali.

Mwazina iwo ati akanakonda kuti aboma komanso amabungwe ndi anthu ena akufuna kwabwino azitumiza zokudya zokwanira m'malo onse ndipo zizikhala zakasinthasintha zimene zikhonza kuthandizira matupi awo kuti azikhala athanzi.

Maboma omwe anakhuzidwa ndi Namondweyi ndi monga Chikwawa, Mulanje, Phalombe, Chiradzulu, Zomba, Machinga, ndi Madera amchigawo chapakati, kumpoto mwa ena.

>>>team_mizwanyafm

Address

Yasini

Telephone

+265881784516

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mizwanya FM Radio posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Mizwanya FM Radio:

Shortcuts

  • Address
  • Telephone
  • Alerts
  • Contact The Business
  • Claim ownership or report listing
  • Want your business to be the top-listed Media Company?

Share