#Nkhani
Lolemba, moto waononga katundu wa ndalama za nkhani-nkhani pa golosale yomwe mwini wake ndi Abubakar Mwamadi m’boma la Mzimba.
Malingana ndi ofalitsa nkhani ku polisi ya Mzimba, Constable Maria Banda wati mwini wa malowa ataona motowu adadziwitsa apolisi omwe adathandizira kuitana gulu lothimitsa moto ku Raiply.
Koma Banda wati momwe gululi limafika pamalowa mkuti katundu ochuluka ataonongeka, komabe adakwanitsa kuthimitsa motowu koma katundu yemwe waonongeka ndi monga Malata, matress komaso simenti.
Pakadali pano, sizidadziwike kuti katundu waonongeka ndi wa ndalama zochuluka bwanji.
Kafukufuku ofuna kudziwa chomwe chidayambitsa motowu ulimkati.
#UmunthuFM
#liwulamzika
#Nkhani
Awa ndi ophunzira pa sukulu ya pulaimale ya Khuza m'dera la mfumu yaikulu Kaomba ku Kasungu.
Iwowa ayima m'mbali mwa msewu, pomwe padutse mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera pomwe akuyembekeza kuchititsa misonkhano yoyimaima m'bomali.
Wophunzirawa akuimba nyimbo zochemelera mtsogoleriyu kwinaku atanyamula uthenga opempha zosowa za pasukuluyi.
"Tikufuna ma desk, tikufuna transformer", uwu ndi wina mwa uthenga omwe wophunzirawa anyamula.
Mtsogoleri wadziko linoyu achititsa misonkhano yoimaima kwa Simlemba, Gogode, Kasungu boma komaso Chilowamatambe mwa ena.
#UmunthuFM
#liwulamzika
#Nkhani
#chakwerastopovernkk
Dr. Chakwera wafika pa town ya boma la Nkhotakota.
Mtsogoleriyu ayamba ndi kukumana ndi mafumu a m'bomali pa bwalo la masewero la Chigumula.
Akamaliza zokambilanazi, Dr Chakwera alankhula kwa anthu omwe asonkhana pa 4 ways pafupi ndi Simso filling station.
Malingana ndi kusintha kwa pologalamu, Dr. Chakwera analephera chipangitsa msonkhano pa msika wa Liwaladzi.
#UmunthuFM
#liwulanzika
#Nkhani
#chakwerastopovernkk
Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera akhale akufika pa nkhotakota boma komw akhale akulankhula ndi anthu omwe asonkhana pa misewu folo pafupi ndi malo ogulitsa mafuta a galimoto a Simso.
Dr Chakwera akhala akukumanaso ndi mafumu a m'bomali pa bwalo la Chigumula.
Iye akuchokera ku Dwangwa komwe analankhula kwa anthu omwe anasonkhana pa msikawu.
#UmunthuFM
#liwulanzika
#Nkhani
Mlembi wa mkulu wa chipani cha UTM, Patricia Kaliati akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu lero mu mzinda wa Lilongwe.
Ena mwa anthu otsatira chipanichi ayamba kale kusonkhana pa polisi ya Lilongwe kwinaku akuimba nyimbo zawo poyembekezera kuti akafike ku bwalo la milandu.
A Kaliati akhala akusungidwa mu chitokosi cha apolisi kuyambira lachinayi sabata yatha pomwe akuganiziridwa kuti anachita upo ofuna kupalamula mulandu waukulu (felony).
#UmunthuFM
#liwulanzika
#Nkhani
Awa ndi ana ochokera pa sukulu ya pulaimale ya Muuta, mdera la mfumu yaikulu Nthondo ku Ntchisi.
Iwowa anapatsa chidwi anthu ochuluka pa msankhono wosamalira zachilengedwe omwe a Lilongwe Wildlife Trust mogwilizana ndi African African Parks anakonza pa bwalo la zamasewero la sukuluyi.
Pomwe amayamba kuimba nyimboyi, anthu ena amaona ngati nyimboyi ndi ya uzimu maka potengera momwe wotsogolera kwayayi amaimbira.
Komatu ayi, nyimboyi si ya uzimu konse koma ndiyotamandira bungwe la African Parks lomwe limayendetsa nkhalango yotetezeka ya Nkhotakota yomwe yazungulira delari.
Bungwe la African Parks likulimbikitsa maphunziro m'maboma anayi komwe nkhalango ya Nkhotakota yazungulirako omwe ndi Kasungu, Ntchisi, Mzimba komaso Nkhotakota.
Bungweli likulipilira sukulu ana oposa 300 aku sekondale ndi sukulu za ukachenjede zosiyanasiyana pambali powonjezera komaso kukonzaso zipinda zophunzilira msukulu za m'mabomawa.
#UmunthuFM
#liwulanzika
#NewsUpdate
The Kasungu Lions Club has embarked on an initiative aimed at reinstating the solar powered pump at Khola health center's maternity wing in the district.
The president of the club Jones Banda told Umunthu FM on Saturday during an aerobic session at Kasungu stadium, that they are anticipating to raise 8 million Kwacha.
Banda adds the initiative is part of celebrating mothers day in style.
Meanwhile, National Initiative for Civic Education-NICE has partnered the club, and its Kasungu civic education officer Pilirani Chaguza says their mission is to instill active participation spirit among the citizenry despite utilizing the platform to sensitize the masses of the 16 September, 2025 general elections.
Among other partners include, NS gym and Hoho action Plus.
#UmunthuFM
#TheCitizenVoice
#msonkhanowadppkukasungu
Nkulu wa achinyamata mchipani cha DPP Norman Chisale wapeleka masiku atatu kwa mkulu wa apolisi mdziko lino a Merlyne Yolamu kuti apolisi amange anthu omwe anachitira chipongwe ndikuotcha galimoto za chipanichi ku Mbowe ku Lilongwe.
A Chisale ati chipani cha MCP chidapha masomphenya a sukulu zosula luso achinyamata za madera (Technical colleges) zomwe zasiya achinyamata pa dzuwa.
Naye gavanala wachipanichi mchigawo cha pakati a David Kambalame ati chipanichi mchamoyo mchigawo chapakati.
#UmunthuFM
#LiuLaNzika
#msonkhanowadppkukasungu
Wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha DPP mchigawo chapakati Alfred Gangata wati boma la MCP lakanika kukwanilitsa malonjezo omwe adalonjeza akulowa m'boma.
Gangata wati palibe chitukuko chomwe boma la MCP lapanga popeleka chitsanzo cha misewu yomwe ikuchitika mu mzinda wa Lilongwe kuti izi ndi mphatso ku chokera ku boma la China.
"Misewu yomwe ikumangidwa ku Lilongwe ndi thandizo kuchokera ku China ndipo anasainira ndi mtsogoleri wakale Professor Arthur Mutharika," watero Gangata.
Iye waonjezera kuti zinthu zisinthe mdziko lino yankho lake ndi Arthur Peter Mutharika kotero wapempha achinyamata kuti asatenge ndi ndalama zomwe ena akuwapasa pofuna kuwanyengelera kuti adzawavotele.
#UmunthuFM
#LiuLaNzika
#NKHANI
Chipani chotsutsa boma cha ma Democratic Progressive Party--DPP lero chikuchititsa msonkhano pa bwalo la zamasewero la sukulu ya pulaimale ya Chithiba ku Kasungu.
Mlendo wolemekezeka ku msonkhanowu ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanichi m'chigawo cha pakati Alfred Gangata.
Pamsonkhanowu pafikaso akuluakulu ena achipanichi monga nkulu wa achinyamata mchipanichi Norman Chisale komanso Charles Mchacha.
Aka ndikoyamba chipanichi kuchititsa msonkhano ku Kasungu chichititsileni msonkhano wawo waukulu.
#UmunthuFM
#LiuLaNzika
#Nkhani
#flamesvsBukinafaso
Umu ndi momwe chipinda chovalira osewera a timu ya Flames chikuonekera pomwe masewero awo ayandikira lero.
Timuyi isewera ndi dziko la Bukina Faso mu ndime yodzipezera malo ku mpikisano wa Africa Cup of Nations chaka cha mawa.
Masewerowa achitikira pa Stade de 24 Mars nthawi ya 9 koloko usiku uno mu mzinda wa Bamako m'dziko la Mali.
Flames idagonja 2:3 mmasewero ake oyamba pa Bingu Stadium pomwe imasewera ndi timu ya Burundi.
Pakadali pano, timuyi ilibe point iliyose mu gulu L.
Inu mukuona kuti masewero amenewa a Malawi ayembekezere zotsatira zotani?
#UmunthuFM
#liwulamzika
#Nkhani
#lakeofstarsnkhotakota
Sisandra and Ru ndiwomwe ali pa msanja pakadali pano ku Lake of Stars.
Onsewa ndi a mdziko la South Africa.
Sisandra akuimba pomwe Ru ndiyemwe akuika nyimbo.
#LOS