#PO_Nkhani_Yakumene
Uyoo uyoo! Mugwireni, nafe tatopa! Uwu ndi mkuwe wa anthu ochita malonda munsika wa Limbe.
Muli nkokenkoke, kukokana malaya kwamuthemuthe mumsika wa Limbe kamba kotu mavenda akutsutsana ndi ganizo la a city omwe akulanda katundu wa mavendawa.
Poyankhula ndi PO, Sanny mmodzi wa ophunzira pa MUBAS yemwe waona izi zikuchitika wati: "A city amalanda ma vendor katundu osiyanasiyana zimene zinazetsa nkangano."
Ma venda anagwira galimoto ya anthu a city-wo ndipo zatsimikidzika kuti oyendetsa galimotolo wafera pompo kutsatira kumenyedwa ndimavendawo.
"Lero tithane nawo! Nafenso Malawi tinaperekera matope nsika uno! Zinthu zavuta tonse" uku kunali kuyankhula Kwa Feston m'nyamata mmodzi oitanira ma minibus.
#Eye4Wadia. #FollowPolyObserverOnFacebookNow.
@Podcast
Ophunzira akhala akudzudzula mtsogoleri wa SRC, Gershom Nyirenda pokhuzana ndi zomwe wailesi ya MIJ yalemba kuti mtsogoleriyu akuti ChatGPT ndiyoipa.
Mverani zonse zomwe Gershom anauza wailesi ya MIJ kudzera mu interview iyi kuti mudziwe chilungamo chankhani yonse.
#PO_Zina_Ukamva
Nyamata wina yemwe amaphunzira pasukulu ino walira chokweza pamene chibwenzi chake chinazimitsa phone patsiku lake la birthday.
Mamunayu, panthawiyi anali atagula kale katundu wandalama zokwana K72,000 kuphatikizapo cake ndicholinga chofuna kubebetsa birthday yamkazi.
Koma tsoka likalimba umakuotcha ndi mkute wadzana, kamba koti mwini birthday yo analibe nazo zopangidwa spoil ndi mwamuna uyuyu.
Abwanawotu ndikuzimva kukonda kwawoko, kunali kuimba phone koyamba, lachiwiri, kachitatu iiih mpaka kachi 12, koma ata! Phone sizagwira.
Izitu zinapangitsa mkuluyi yemwe ali chaka chake chamaphunziro chachiwiri kulira chokweza makamaka akaganizira momwe anaipezera movutikira ndalamayi.
Pakadali pano cake ndizakudya zinazo zadyedwa kale ndima mesho. Ndipo sizikuziwika kuti tsogolo lachibwenzi chimenechi likhala lotani.
Nde zikumveka kuti khalangati mkazi-yu ali ndi njonda ina mkana wamupweteka nzakeyu.
Video ili mmusiyi ikufotokoza zambiri
#Eye4Wadia. #FollowPolyObserverOnFacebookNow.
PO EXCLUSIVE INTERVIEW - Live via OneStream Live #onestreamlive
With John Daka, a candidate for General Secretary - Live via https://onestream.live
#onestreamlive
PO EXCLUSIVE INTERVIEW - Live via OneStream Live #onestreamlive
WITH JOHN DAKA, A CANDIDATE FOR GENERAL SECRETARY - Live via https://onestream.live
#onestreamlive