
01/01/2025
Apolisi kwa Jenda m’boma la Mzimba amanga Emmanuel Phiri wa zaka 20 chifukwa chopezeka ndi njinga yamoto yomwe akuganiza kuti inabedwa m’boma la Kasungu.
M’neneri wa Polisi ya Jenda, MacFarlane Mseteka, watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti Phiri anamangidwa usiku wa pa 31 December 2024 ku Jeko Rest House kwa Jenda.
“Phiri adalephera kuyankha za njinga yamotoyo ponena kuti adabwereka kwa m'nzake ku Kasungu koma adakanika kulongosola zambiri za m'nzakeyo komanso za njingayo, zomwe zidapangitsa kuti apolisi amugwire,” adatero Mseteka.
Phiri amachokera m’mudzi mwa Chase, Mfumu Yayikulu Tengani m’boma la Mulanje, ndipo akaonekera kubwalo la milandu posachedwapa.
Wolemba: Georgy Dickson Mumba
,
!