Uthenga wabwino ochokera kwa mulungu

Uthenga wabwino ochokera kwa mulungu cholinga cha page imeneyi ndikuphunzira uthenga Wa mulungu

19/04/2024

KODI MULUNGU WENIWENI DZINA LAKE NDINDANI?
(pemphani phunziro la Bible mwaulele ku inbox ndipo mudzauzidwa zoti muchite).

Usiku woti afa mawa lake, YESU KHRISTU,anayambitsa mwambo wokumbukira imfayake, Ndipo anauza ophunzira ake k*ti:"MUZICHI...
15/03/2024

Usiku woti afa mawa lake, YESU KHRISTU,
anayambitsa mwambo wokumbukira imfa
yake, Ndipo anauza ophunzira ake k*ti:

"MUZICHITA ZIMENEZI PONDIKUMBUKIRA"
Luke 22:19

Chaka chilichose, amboni Za Yehova
amachita mwambowu pachaka kamodzi.

Chakachino mwambowu uchitika Lamulungu
pa 24 march 2024 nthawi ya 6 koloko
madzulo.mwambowu udzakhala waulele
ndipo sipakhala chopereka chilichonse
mukuitanidwa nonsee!!! kumwambowu

LANDIRANI KAPEPALA KOSONYEZA MALO
OMWE MWAMBOWU UDZACHITIKIRE M'DERA LOMWE MULI
KUCHOKERA KWA WAMBONI ZA
YEHOVA ALIYESE YEMWE MULINAYE
PAFUPI .K*TI MUWONE ZAMBIRI PITANI PA
WEBSITE IYI 👉JW.ORG/NY

14/01/2024

Ndia ngati mukufuna kuphunzira Bible?.... inbox me........

Send a message to learn more

07/01/2024

SAMALANI NDI ULOSI WA DANIEL ⚠️

Vedio yothandiza kudziwa mfumu yakumpoto komanso yakumwera masiku ano

Kodi chipembedzo choona chilipo chimodzi chokha?Yesu anayambitsa chipembedzo choona chimodzi chokha, ndipo otsatira ake ...
24/12/2023

Kodi chipembedzo choona chilipo chimodzi chokha?

Yesu anayambitsa chipembedzo choona chimodzi chokha, ndipo otsatira ake anali m’chipembedzo chimenecho. Chipembedzocho chili ngati msewu womwe ukulowera ku moyo wosatha. Ponena za msewu umenewu, Yesu ananena k*ti: “Amene akuupeza ndi anthu owerengeka.” (Mateyu 7:14) Mulungu amavomereza anthu okhawo amene akumulambira mogwirizana ndi mfundo zochokera m’Mawu ake Baibulo, omwe ndi choonadi. Anthu onse omwe ndi olambira oona amakhulupirira zinthu zofanana.​—Werengani Yohane 4:23, 24; 14:6; Aefeso 4:4, 5.

Kodi Yesu ananena chiyani chokhudza Akhristu onyenga?

Yesu anachenjeza k*ti aneneri onyenga adzayamba kuphunzitsa zinthu zabodza pakati pa Akhristu. Pamaso chabe, aneneri onyenga amenewa amaoneka ngati amalambira Mulungu m’njira yoyenera. Komanso amanena k*ti zipembedzo zawo ndi zachikhristu. Komabe, munthu angathe kuwazindikira k*ti si Akhristu oona. Kodi angawazindikire bwanji? Angawazindikire chifukwa chak*ti ndi chipembedzo choona chokha chimene anthu ake ndi Akhristu enieni ndipo makhalidwe awo komanso zochita zawo zimakhala zabwino.​—Werengani Mateyu 7:13-23.

N’chiyani chingak*thandizeni k*ti mudziwe olambira oona?

Taonani zinthu zisanu zomwe ndi zizindikiro za olambira oona a Mulungu:

1. Olambira oona amalemekeza Baibulo monga Mawu a Mulungu. Iwo amayesetsa k*tsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo. Choncho chipembedzo choona chimasiyana ndi chipembedzo chimene chimayendera maganizo a anthu. (Mateyu 15:7-9) Komanso olambira oona samangophunzitsa chabe koma amayesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene amaphunzitsazo.​—Werengani Yohane 17:17; 2 Timoteyo 3:16, 17.

2. Otsatira a Yesu enieni amalemekeza dzina la Mulungu lak*ti Yehova. Yesu analemekeza dzina la Mulungu polidziwikitsa kwa anthu ena. Iye anathandiza anthu ena kudziwa Mulungu komanso anawaphunzitsa kupemphera k*ti dzina la Mulungu liyeretsedwe. (Mateyu 6:9) M’dera limene mukukhala, kodi ndi chipembedzo chiti chomwe chimauza anthu ena za dzina la Mulungu?​—Werengani Yohane 17:26; Aroma 10:13, 14.

3. Akhristu enieni amalalikira za Ufumu wa Mulungu. Mulungu anatumiza Yesu padziko lapansi k*ti adzalalikire uthenga wabwino wa Ufumu. Tsogolo la anthu likudalira pa Ufumu wa Mulungu wokha womwe udzabweretse madalitso ambiri. Yesu ankauza anthu za Ufumu umenewu mpaka pa tsiku la imfa yake. (Luka 4:43; 8:1; 23:42, 43) Iye ananenanso k*ti otsatira ake azilalikira za Ufumuwo. Ndiyeno kodi munthu wina atakupezani n’kumakuuzani za Ufumu wa Mulungu, mungaganize k*ti munthu ameneyu ndi wachipembedzo chiti?​—Werengani Mateyu 24:14.

4. Otsatira a Yesu sali mbali ya dziko loipali. Otsatira a Yesu mungawadziwe chifukwa chak*ti iwo salowerera nkhani zandale kapena mikangano imene imachitika m’madera amene iwo akukhala. (Yohane 17:16; 18:36) Komanso samatengera makhalidwe ndi maganizo oipa a m’dzikoli.​—Werengani Yakobo 4:4.

5. Akhristu enieni amakondana kuchokera pansi pa mtima. Iwo amaphunzira m’Mawu a Mulungu k*ti ayenera kulemekeza anthu a mitundu yonse. Ngakhale k*ti zipembedzo zonyenga zakhala zikulowerera nkhondo mayiko osiyanasiyana akamamenyana, olambira oona amakana kuchita zimenezi. (Mika 4:1-3) M’malomwake, Akhristu oona amagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso chuma chawo k*ti athandize ena komanso kuwalimbikitsa.​—Werengani Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 4:20.

Kodi tsopano mwachidziwa chipembedzo choona?

Kodi ndi chipembedzo chiti chomwe mfundo zake zonse zimachokera m’Mawu a Mulungu, chimalemekeza dzina la Mulungu komanso chimalalikira zoti ndi Ufumu wa Mulungu wokha womwe ungabweretse madalitso kwa a anthu padziko lapansi? Kodi ndi gulu liti la anthu lomwe limakondana kuchokera pansi pa mtima komanso lomwe limakana kumenya nkhondo? Tikukhulupirira k*ti mwalidziwa tsopano.​—Werengani 1 Yohane 3:10-12.

17/12/2023

"Tate wa onse okhala ndi chikhulupiliro". 🙌🙌🙏

30/10/2023

Mulibwanji

SATANA ANAGWETSEDWA KUMWAMBA MU 1914 (mbali yachiwiri/yomaliza)........tikupitiriza.........👇mafumu omwe ankalamulira mm...
13/06/2023

SATANA ANAGWETSEDWA KUMWAMBA MU 1914 (mbali yachiwiri/yomaliza)
........tikupitiriza.........👇

mafumu omwe ankalamulira mmalo mwa mulungu ku yelusalemu anayamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Mulungu, choncho iye sanawalole k*ti apitirize kulamulira. Kenako Yerusalemu anawonongedwa m’chaka cha 607 B.C.E. Pamenepa ndi pomwe panayambira “nthawi zokwanira 7.”(2 Mafumu 25:1, 8-10; Ezekieli 21:25-27).Pamene Yesu ananena k*ti: “Anthu a mitundu ina adzapondaponda Yerusalemu, kufikira nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu inawo zitakwanira,” ankanena za “nthawi zokwanira 7” zimenezi. (Luka 21:24) “Nthawi zokwanira 7” zimenezi sizinathe Yesu ali padziko lapansi pano. Yehova analonjeza k*ti adzasankha Mfumu yatsopano kumapeto kwa “nthawi zokwanira 7.” Ulamuliro wa Mfumu yatsopano imeneyi ndi umene udzabweretse madalitso kwa anthu padziko lonse lapansi.—Luka 1:30-33.
Kodi “nthawi zokwanira 7” zimenezi ndi nthawi yaitali bwanji?: “Nthawi zokwanira 7” zinali zaka 2,520. Tikawerengetsera zaka 2,520 kuchokera m’chaka cha 607 B.C.E., zik*tifikitsa m’chaka cha 1914. Chaka chimenechi ndi chimene Yehova anasankha Yesu, yemwe ndi Mesiya kukhala Mfumu ya Ufumu wake wakumwamba.
Kodi tadziwa bwanji k*ti “nthawi zokwanira 7” ndi zaka 2,520? Baibulo limanena k*ti nthawi zitatu ndi hafu, ndi masiku 1,260. (Chivumbulutso 12:6, 14) Choncho “nthawi zitatu ndi hafu” kuwirikiza kawiri ndi masiku 2,520 zomwe ndi “nthawi zokwanira 7.” Koma masiku 2,520 amenewa ndi zaka 2,520 chifukwa Baibulo limanena k*ti ‘tsiku limodzi limaimira chaka chimodzi.’—Numeri 14:34; Ezekieli 4:6.
NDIKUKHULUPILIRA K*TI APA ALIYESE WAMVETSETSA ZOKHUDZA CHAKA CHA 1914.MWINA MUKUDABWA K*TI POPEZA YESU NDIMFUMU NDIPO ANALIPO KUYAMBIRA KALE "KODI UFUMU OMWE ANASANKHIDWA MU 1914 WU NDIUFUMU WANJI?.KHALANI TCHELU NKHANI YOTSATIRA IFOTOKOZA ZIMENEZI.

SATANA ANAGWETSEDWA MU 1914 (mbali yoyamba)Yesu atangokhala kumene mfumu Baibulo  limafotokoza k*ti kumwamba kubuka chin...
09/06/2023

SATANA ANAGWETSEDWA MU 1914 (mbali yoyamba)

Yesu atangokhala kumene mfumu Baibulo limafotokoza k*ti kumwamba kubuka chinkhondo chopsa pamene MIKAYELI yemwe ndi mtsogoleri wagulu lankhondo lakumwamba (k*tanthauza YESU) anamenyana ndi CHINJOKA (satana). Satanayo anagonja nkhondoyo kenako amponyera padziko lapansi pano limodzi ndi angelo ake .werengani chivumbulutso 12 :7-9. Ena mukudabwa k*ti kodi tikudziwa bwanji k*ti mikayeli ndi dzina lina ya Yesu?.werengani chivumbulutso 19:14,15.
popeza tafotokoza k*ti imeneyi ndintchito yoyamba yomwe yesu anagwira atangokhala kumene mfumu kumwamba ndiyeno KODI TINADZIWA BWANJI K*TI YESU ANAKHALADI MFUMU MU 1914??? (apa ndipomwe nkhani yathu yayambira werengani mofatsa)👇
Chaputala 4 cha buku la Danieli chinaneneratu k*ti Mulungu adzakhazikitsa Ufumu wake m’chaka cha 1914.
Ulosi: Yehova anachititsa Mfumu Nebukadinezara kulota maloto a zinthu zimene zinali kudzachitika m’tsogolo. Iye analota mtengo wautali umene unadulidwa ndipo chitsa chake sichinkaphukira mpaka panadutsa “nthawi zokwanira 7” chifukwa anali atachikulunga ndi zinthu zachitsulo. Kenako mtengowo unayambiranso kuphukira.—Danieli 4:1, 10-16.
Kodi ulosi umenewu uk*tanthauza chiyani?: Mtengowo ukuimira ulamuliro wa Mulungu. Kwa zaka zambiri, Yehova ankagwiritsira ntchito mafumu a ku Yerusalemu k*ti azitsogolera mtundu wa Isiraeli. (1 Mbiri 29:23) Koma mafumu amenewa anayamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Mulungu, choncho iye sanawalole k*ti apitirize kulamulira. Kenako Yerusalemu anawonongedwa m’chaka cha 607 B.C.E. Pamenepa ndi pomwe panayambira “nthawi zokwanira 7.”NDIYENO KODI NTHAWI ZOKWANIRA 7 ZIMATIFIKITSADI MU 1914?
mbali yachiwiri ikupitiriza kufotokoza
CHOONDE PANGANI LIKE PAGE INO, PANGANI TAG ,PANGANI INVITE KOMASO SHARE PAGE INO KWAMA FRIENDS ANU KOMASO KUGROUP ENA K*TI TONSE TIMVERE LIMODZI.ZIKOMO🙏🏾

⚠️ KUYAMBIRA MUCHAKA CHA 1914 ZINTHU ZINASINTHA KWAMBIRI PA DZIKO LAPANSI PANO.NKHONDO KOMASO MILILI ZINAONJEZEREKA KWAM...
06/06/2023

⚠️ KUYAMBIRA MUCHAKA CHA 1914 ZINTHU ZINASINTHA KWAMBIRI PA DZIKO LAPANSI PANO.NKHONDO KOMASO MILILI ZINAONJEZEREKA KWAMBIRI KUYAMBIRA MU CHAKACHI NDIPO ZINTHU ZIKUNGOYIPILA.ZOCHITIKA ZAMBIRI MUCHAKACHI ZIMASONYEZA K*TI INALI NTHAWI YA CHIYAMBI CHENI CHENI CHA MASIKU OTSIRIZA.AMBIRI MWAKHALA MUKUFUNSA KOMASO KUPEREKA MAGANIZO OSIYANA SIYANA KU INBOX PANKHANI YOKHUDZA CHAKA CHA 👉 1914.

1.kodi chikachi ndichomwedi satana anagwetsedwa kumwamba?

2.kodi m'baibulo muli ma vesi ofotokoza zokhudza chakachi?

3.Yesu khristu atangokhala kumene mfumu kumwaba ntchito yake yoyamba inali k*thamangitsa satana.ndiye kodi timadziwa bwanji k*ti yesu anakhaladi mfumu mu chakachi?
4.Nanga izi zitachitika kodi nchiyani chinachitikira dziko lapasi?

NKHANI YOTSATIRAYI IFOTOKOZA BWINO MAYANKHO,MAVESI KOMASO ZAMBIRI ZOKHUDZA CHAKACHI.

(CHOONDE PANGANI LIKE PAGE INO, PANGANI TAG ,PANGANI INVITE KOMASO SHARE PAGE INO KWAMA FRIENDS ANU KOMASO KUGROUP ENA K*TI TONSE TIMVERE LIMODZI.

SATANA ANATHAMANGITSIDWA KUMWAMBAMu 1914 kunali nkhondo kumwamba. Baibulo limati: “Ndipo kumwamba kunabuka nkhondo: Mika...
02/06/2023

SATANA ANATHAMANGITSIDWA KUMWAMBA

Mu 1914 kunali nkhondo kumwamba. Baibulo limati: “Ndipo kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo, koma sichinapambane, ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba. Choncho chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”
Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Baibulo limafotokoza k*ti: “Pa chifukwa chimenechi, kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko.” Angelo anasangalala chifukwa Satana komanso angelo oipa anathamangitsidwa kumwamba. Nanga bwanji za anthu padziko lapansi? Baibulo limati: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa k*ti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”​—Chivumbulutso 12:7-9, 12.
Satana ndi angelo ake oipa amasocheretsa anthu komanso kubweretsa mavuto padzikoli. Angelo oipawa ndi adani a Mulungu ndipo amadziwika ndi dzina lak*ti ziwanda.

30/03/2023

Munthu wina atatopa ndi mavuto anaganiza zozipha anakwera pa mwamba pa chinyumba yaitali stair number 4 ncholinga choti aziponye afe 😌 ali pomwepo atayangana pansi anaona munthu wopanda mikono akuvina, kuvinatu za ntchito zija, nde Ada wo anali odabwa, munthu alibe mikono yonse koma akuvina, chinsinsi chake nchotani k*ti azikhala osangalala chonchi? Pomwepo anachosa maganizo ofuna kuzipha aja, anaganiza zosika pansi k*t akamufunse. Atafika pansi anapeza nkulu uja dance ili nkati, Atafika pafupi kumufunsa k*t kod mbale ukuvina chachitika ndi chan k*t usangalale chonchi,
Anakhumudwatu atamva yankho la nzakeyo
Ati : " ase usaone ngat ndikuvina apa ndi zoti ndikumva kuyabwa ku nsana ku nde Ndikuvutika k*ti ndikanda bwanji 😢😭

ASE ATHU KUNJAKU ALI PA MAVUTO AKUULU KUPOSA AKOWO KMA SANAGANIZEKO ZOCHOSA MOYO, MOYO NDI OFUNIKA KWAMBIRI CHONDE OSACHOSA MOYO KOMANSO KUMAYAMIKA PA ZOCHEPA ULI NAZO KOZ ENA AKUZISOWA
Have a nice day 🌹💐

Send a message to learn more

Usiku woti afa mawa lake, YESU KHRISTU, anayambitsa mwambo wokumbukira infa yake, Ndipo anauza ophunzira ake k*ti:"MUZIC...
26/03/2023

Usiku woti afa mawa lake, YESU KHRISTU, anayambitsa mwambo wokumbukira infa yake, Ndipo anauza ophunzira ake k*ti:

"MUZICHITA ZIMENEZI PONDIKUMBUKIRA"
Luke 22:19

Chaka chilichose, Mboni Za Yehova zimachita mwambo wokumbukira infa ya KHRISTU umenewu ndipo umachitika kamodzi pa chaka.

Chakachino mwambowu uchitika Lachiwiri pa 4 april 2023 nthawi ya 6 koloko madzulo.mwambowu umakhala waulele ndipo sipakhala chopereka chilichonse mukuitanidwa nonsee!!! kumwambowu

LANDIRANI KAPEPALA KOSONYEZA MALO OMWE MWAMBOWU UDZACHITIKIRE KUCHOKERA KWA NZANU WAMBONI ZA YEHOVA ALIYESE YEMWE MULINAYE PAFUPI .K*TI MUONE ZAMBIRI PITANI PA WEBSITE IYI 👉JW.ORG/NY

20/02/2023

zikomo abale nonse!! .chifukwa mavuto ena tinasowa page pano.pano chilichonse chakonzedwa mauthenga ayamba kufika tsopano ,share, invite & follow page ino k*ti anzanu apinduleko.ZIKOMOO!!!.

Send a message to learn more

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRAMunthu akapanda k*tsatira lamulo linalake amakumana ndi mavuto. N’zimenenso zingachitike ngat...
11/12/2022

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA

Munthu akapanda k*tsatira lamulo linalake amakumana ndi mavuto. N’zimenenso zingachitike ngati mutapanda k*tsatira lamulo la m’Baibulo lak*ti: “Mukhale oyera mwa kupewa dama.”—1 Atesalonika 4:3.
Koma kodi munthu amene sangatsatire lamulo limeneli angakumane ndi mavuto otani? Baibulo limanena k*ti: “Amene amachita dama amachimwira thupi lake.” (1 Akorinto 6:18) Kodi zimenezi ndi zoona?
Kafukufuku amasonyeza k*ti achinyamata ambiri amene amayamba zogonana asanalowe m’banja amakumana ndi mavuto otsatirawa:
KUVUTIKA MAGANIZO. Amadziimba mlandu pambuyo pake.

KUSAKHULUPIRIRANA. Amayamba kudzifunsa k*ti, ‘Kodi amene ndagona nayeyu wagona ndi anthu angati?’

KUKHUMUDWA. Atsikana ambiri amafuna mnyamata amene angawateteze, osati kuwadyera masuku pamutu. Anyamata ambiri akagona ndi mtsikana sakopeka nayenso ndipo amayamba kumuona ngati wopanda ntchito.

Dziwani izi: Thupi lanu ndi lamtengo wapatali kwambiri. Choncho, mukagona ndi munthu musanalowe m’banja mumakhala k*ti mwadzitchipitsa.—Aroma 1:24.

Sonyezani k*ti ndinu olimba mtima ndipo mukhoza “kupewa dama.” (1 Atesalonika 4:3) Mukadzalowa m’banja mudzakhala ndi mwayi wogonana popanda kuda nkhawa kapena kudziimba mlandu ngati mmene zimakhalira ndi amene amagonana asanalowe m’banja.—Miyambo 7:22, 23; 1 Akorinto 7:3.

KODI ZAMOYO ZINACHITA KUSINTHA KUCHOKERA KUZINTHU ZINA?Baibulo limati: “Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma a...
15/11/2022

KODI ZAMOYO ZINACHITA KUSINTHA KUCHOKERA KUZINTHU ZINA?

Baibulo limati: “Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheberi 3:4) Kodi zimenezi n’zoona?
ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: Zinthu zonse zinangokhalako mwangozi.
1. Ngati ndi choncho, ndani amene kapena ndi chani chimene chinachititsa k*ti zinthu zikhaleko mwangozi?
2. Kodi ndi mfundo iti pa ziwirizi imene mukuona k*ti ndi yomveka? Yoti zinthu zinangokhalako zokha kapena yak*ti pali winawake amene anazilenga?
ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: Anthu anachokera ku nyama.
3. Ngati anthu anachokeradi ku nyama monga anyani, n’chifukwa chiyani amakhala anzeru kwambiri kuposa anyaniwo?
4. N’chifukwa chiyani zinthu zamoyo, ngakhale zing’onozing’ono kwambiri, ndi zogometsa kwabasi?
ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: Pali umboni wak*ti zamoyo zinachokera ku zinthu zina.
5. Kodi munthu amene amanena zimenezi anafufuzadi n’kupeza umboni?
6. Kodi si zoona k*ti ambiri amakhulupirira zoti zamoyo zinachokera ku zinthu zina chifukwa chak*ti anangomva kwa anthu ophunzira kwambiri?
“Tiyerekeze k*ti mukuyenda m’nkhalango ndipo mwaona nyumba yamatabwa yokongola kwambiri. Kodi mungaganize k*ti; ‘Palibe amene anaimanga koma mitengo imene inkagwera pamalowa yapanga nyumbayi’? Zimenezi n’zosamveka. Ndiye mukuona k*ti ndi nzeru kukhulupirira k*ti zinthu zinangokhalako mwangozi?”—Julia.

“Tiyerekeze k*ti munthu wina wakuuzani zoti makina pafakitale inayake yosindikiza mabuku anaphulika, inki n’k*tayikira m’makoma ndi kudenga ndipo inkiyo komanso mapepala zinapanga dikishonale yabwino zedi. Kodi mungakhulupirire zimenezi?”—Gwen.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUKHULUPILIRA K*TI KULI MULUNGU?

Baibulo limati muzigwiritsa ntchito ‘luntha lanu la kuganiza.’ (Aroma 12:1) Izi zik*tanthauza k*ti musamangokhulupirira k*ti kuli Mulungu chifukwa . . .CHONGOTSANZIRA ENA (Kudera limene ndimakhala anthu ambiri ndi opemphera)

Koma inuyo panokha muyenera kupeza zifukwa zomveka zokuchititsani kukhulupirira k*ti kuli Mulungu.

ZOTI MUGANIZIRE : Ngakhale k*ti kwa nthawi yaitali asayansi akhala akuchita kafukufuku wokhudza nkhaniyi, sanapezebe mfundo zimene onse angagwirizane. Ngati asayansi, omwe amati ndi akatswiri, sakugwirizana chimodzi pa nkhaniyi, kodi mukuona k*ti n’chinthu chanzeru kumakhulupirira zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina?
K*TI MUDZIMVA ZAMBIRI PANGAN FOLLOW ,SHARE KOMANSO INVITE MA FRIENDS ANU PAGE YATHU INO.ZIKOMO🙏

ZIWANDA ZIMAPUSITSA ANTHU K*TI AKUFA ALIMOYOZiwanda zimayerekezera kukhala mizimu ya anthu amene anamwaliraSatana amagwi...
27/10/2022

ZIWANDA ZIMAPUSITSA ANTHU K*TI AKUFA ALIMOYO

Ziwanda zimayerekezera kukhala mizimu ya anthu amene anamwalira

Satana amagwiritsanso ntchito anthu olankhula ndi mizimu. Anthu amenewa amanena k*ti amalandira mauthenga ochokera kwa mizimu ya akufa ndipo anthu ambiri amakhulupirira zimenezi. Koma malinga ndi zimene taona m’Baibulo, zimenezi si zoona.​—Mlaliki 9:5, 6, 10.
Ndiyeno, kodi mauthenga amene amalandirawo amachokera k*ti? Ziwanda zimaonetsetsa munthu pa nthawi imene ali moyo n’kudziwa maonekedwe ake, kalankhulidwe kake, zimene akuchita komanso zimene akudziwa. Ndiyeno munthuyo akamwalira, zimayerekezera zimene ankachita komanso mmene ankalankhulira n’kumapereka mauthenga kwa anthu.​—1 Samueli 28:3-19.

Nkhani Zabodza

Satana amafalitsanso nkhani zabodza zokhudza anthu akufa. Nkhanizi zimachititsa anthu k*ti asamakhulupirire mfundo zoona za m’Baibulo.​—2 Timoteyo 4:4.

Anthu ena amaganiza k*ti aona anthu amene anamwalira alinso ndi moyo

Mu Africa muli nkhani zambirimbiri zofotokoza za anthu amene anaonekanso pambuyo poti amwalira. Anthuwo amakapezeka k*tali ndi kumene ankakhala ali moyo. Koma funso n’kumati: ‘Kodi zimenezi zikanakhala zoona, munthu woukayo akanapita dala k*tali kopanda achibale ake komanso anzake?’
N’k*theka k*ti anthu amangoona munthu wofanana ndi amene anamwalirayo. Mwachitsanzo, m’dziko lina bambo wina wachikulire ankangolondola Akhristu awiri amene ankalalikira. Bamboyo atafunsidwa, ananena k*ti ankaganiza k*ti m’modzi mwa Akhristuwo ndi mchimwene wake amene anamwalira zaka zingapo m’mbuyomo. Bamboyo anakakamira kwambiri m’baleyo n’kumanena k*ti ndi mchimwene wake basi. Ndiye kodi mukuganiza k*ti bamboyo atafika n anakanena zotani kwa anzake?
PANGANI FOLLOW👍 PAGE INO K*TI MUMVE ZAMBIRI.

KUKONGOLA KWENI KWENIBaibulo silinena k*ti kukongola kwa munthu ndi maonekedwe ake okha ayi, koma amafunikanso k*ti akha...
30/09/2022

KUKONGOLA KWENI KWENI

Baibulo silinena k*ti kukongola kwa munthu ndi maonekedwe ake okha ayi, koma amafunikanso k*ti akhale ndi khalidwe labwino losangalatsa Mulungu.—Miyambo 11:20, 22.Taganizirani za Abisalomu, mwana wa Mfumu Davide. Baibulo limati: “M’Isiraeli monse munalibe wina anthu anam’tama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pa mutu wake mwa iye munalibe chilema.” (2 Samueli 14:25) Koma mnyamatayu anali ndi nsanje yoopsa. Chifukwa chodzitukumula, anafuna kulanda ufumu kwa mfumu yodzozedwa ndi Yehova. Choncho, Baibulo limati Abisalomu anali munthu wosakhulupirika ndiponso woipa mtima kwambiri.Mfundo yofunika kuikumbukira ndi yak*ti: ‘Yehova amayesa mitima’ osati kukongola kwa munthu. (Miyambo 21:2) Choncho, ngakhale k*ti maonekedwe ndi ofunika, makhalidwe abwino ndi amene ali ofunika kwambiri. Ndipotu, makhalidwe auzimu ndi amene angakuchititseni k*ti mukhale munthu wosiririka kwambiri.

PANGANI LIKE👍 ,SHARE KOMASO INVITE PAGE INO KUMA GROUP KOMANSO KWAMA FRIENDS ANU K*TI MUMVE ZAMBIRI .ZIKOMOO🙏🙏🙏🙏

"NKHAWA!!!"Akatswiri azaumoyo  amanati: “Nthawi zambiri anthu akuluakulu ngakhaleso ana  amene akuvutika kwambiri ndi nk...
18/09/2022

"NKHAWA!!!"

Akatswiri azaumoyo amanati: “Nthawi zambiri anthu akuluakulu ngakhaleso ana amene akuvutika kwambiri ndi nkhawa. Zimenezi zili chonchi chifukwa moyo wa masiku ano umasinthasintha komanso ndi wosadalirika.” Zina mwa zinthu zimene zimachititsa k*ti anthu azikhala ndi nkhawa ndi monga:

1.k*tha kwa banja
2.kumwalira kwa munthu amene timamukonda
3.matenda aakulu
4.ngozi yaikulu
5.kuphwanya malamulo
5.kukhala wotanganidwa nthawi zonse
6.ngozi zachilengedwe kapena zochititsidwa ndi anthu
7.kupanikizika ndi zochitika za kuntchito kapena kusukulu
8.kusowa kwa ntchito komanso mavuto a zachuma

KUOPSA KWA NKHAWA!!⚠️

Nkhawa ingachititse k*ti munthu asamakhale ndi chilakolako chofuna kugonana. Choncho nkhawa kapena kupanikizika kwambiri kungachititse k*ti
"mwamuna azilephera kulowa kuchipinda komanso k*ti mkazi azisamba mosakhazikika"

Kodi izi zimachitika motani??
Nanga tingachepetse bwanji nkhawa?
PANGANI PANGANI LIKE👍 PAGE INO KOMASO IPANGENI SHARE OR INVITE KWAMA FRIENDS ANU K*TI MUDZIWE ZAMBIRI.ZIKOMO🙏

ANYAMATA KODI MUKUDZIWA??Ngati muli ndi chibwenzi, dzifunseni k*ti, ‘Kodi mtsikanayu ndimamukondadi?’ Ngati mumamukonda,...
14/09/2022

ANYAMATA KODI MUKUDZIWA??

Ngati muli ndi chibwenzi, dzifunseni k*ti, ‘Kodi mtsikanayu ndimamukondadi?’ Ngati mumamukonda, mungasonyeze zimenezi poyesetsa k*tsatira malamulo a Mulungu, popewa kukhala pamalo amene mukhoza kuyesedwa komanso pochita zinthu zosonyeza k*ti mumamuganizira.
Mukamachita zimenezi, mtsikanayo azikuonani ngati mmene Msulami ankaonera chibwenzi chake. Iye anati: “Wachikondi wanga ndi wanga, ndipo ine ndine wake.” (Nyimbo ya Solomo 2:16) Mwachidule tingati adzakukondani kwambiri.

Pangani share ndipo pangani like page ino k*ti muzimva zambiri 🙏🙏🙏

ATSIKANA KODI MUKUDZIWA??Anyamata ambiri amanena k*ti sangakwatire mtsikana amene anagonapo naye. Koma n’chifukwa chiyan...
09/09/2022

ATSIKANA KODI MUKUDZIWA??

Anyamata ambiri amanena k*ti sangakwatire mtsikana amene anagonapo naye. Koma n’chifukwa chiyani amanena zimenezi? Chifukwa chak*ti amafuna kukwatira mkazi woti sanagonepo ndi mwamuna.
Kodi zimenezi zikukudabwitsani mwinanso kukukhumudwitsani? Dziwani k*ti anthu opanga mafilimu komanso mapulogalamu a pa TV amachititsa achinyamata k*ti aziona ngati kugonana asanalowe m’banja n’kosangalatsa, kulibe vuto lililonse komanso ndi njira yosonyezera chikondi.
Koma musapusitsike. Dziwani k*ti munthu amene amakunyengererani k*ti mugone naye, ndi wodzikonda.—1 Akorinto 13:4, 5.

Pangani like page ino k*ti mumve zambiri 🙏🙏🙏🙏

27/08/2022

after world war 1,tikubwera ndi "imfa za ophunzira a yesu"
Plz pangani invite page ino kwa anzanu k*ti amvenawo
"TIKAFIKA 1K TIYAMBA KU POSTER MA VEDIO"
LETS SHARE!!!!!!🔥🔥🔥🔥

THE FIRST WORLD WAR 1(last part)📖Daniel 11:30a "Pak*ti zombo zaku Kitimu zizafika kuyambana naye, chifukwa chake adzaten...
19/08/2022

THE FIRST WORLD WAR 1(last part)

📖Daniel 11:30a "Pak*ti zombo zaku Kitimu zizafika kuyambana naye, chifukwa chake adzatenga mkhawa"
Munthawi ya Daniel Kitimu anali Cyprus(Kupro) koma munthawi yamkhondo yoyamba ya dziko lonse Cyprus anali kumbali ya Britain. Zombo za Kitimu munthawi ya nkhondo yapadziko yoyamba ndi sitima zonse za Britain zomwe zimakocheza magombe onse akumayiko akumadzulo kwa Ulaya.
Germany atapanga chiwembu chomiza sitima yotchedwa Lustania America inalemba makalata kupita kumaiko onse omwe amkatenga nawo mbali pankhondoyo k*ti aleke ndikukhala pansi akambirane. Germany anakana makamaka poona k*ti anali pafupi kupambana mkhondoyo, ndipo Germany anachenjeza USA k*ti akangoyelekeza kupanga masewera akaukiranso America. Apa America analemba kalata ina yomwe anayitchula k*ti "THE JOINT RESOLUTION" iyi inali yodziwitsa Germany k*ti America ikulowelera mkhondoyo pak*ti akupanga makani.

Pa April 6 1917 president wa ku America Woodrol William analengeza k*ti America yalowa nawo mumkhondoyo. Kulowelera kwa America kunapangitsa Germany kuchepa mphamvu, ndipo kumahambiliro a 1918 Germany anasakazidwa kwambiri

Pofika mu November 1918 Germany anaimika manja k*ti saikwanitsa ndipo Kaiser Welhelm 2 amathawa kupita kukabisala ku Netherland. Mmene imafika 11 koloko mmawa pa 11 mwezi wa 11 mu 1918 maiko onse anasaina pangano loleka mkhondoyo.

Apatu mkhondo yoyamba yatha mfumu yakumpoto( Germany) yagonja, kodi mfumu yakumpoto imvomeredza kugonja kwake?
Nanga chinasatira ndichani after mkhondo k*tha? Tangopangan like👍 page ino
Ndili pano kukupasirani mbiri zankhondo zonse mpaka kufika pa mkhondo ikuchitikayi pakati pa Russia ndi Ukrain or china ndi Taiwan

THE WORLD WAR 1 PART 4Tisaiwale paja tikukambira chapter 11 cha buku la Daniel, ndipo pano tikuona mkhondo yoyamba ya dz...
11/08/2022

THE WORLD WAR 1 PART 4
Tisaiwale paja tikukambira chapter 11 cha buku la Daniel, ndipo pano tikuona mkhondo yoyamba ya dziko lonse lapansi.

Austria-Hungary anapita kukaiyamba mkhondo ku Serbia pa 28 July 1914 patangodusa mwezi umodzi after chiwembu chija. Podalira chithandizo chochokera ku Germany, Austria-Hungary anasimikidza mtima zothana ndi Serbia
Germany anali pambuyo k*thandiza Austria-Hungary monga mzake wamumgirizano wa Triple Alliance. Izi sizinakomele Russia ndipo anakailowa mkhondo kuyamba k*thandiza Serbia. Britain mdani wamkulu wa Germany anatumidza makalata kumaiko onse aku ulaya kuwachenjedza k*ti asalowelele nkhondoyo.

Germany ataona k*ti Russia wailowa mkhondo ak*thandiza Serbia, anaukira Russia ndipo anakalowa ku Russia kuyamba mkhondo kumeneko. Naye France ataona k*ti mzake Russia yemwe anali naye mumgwilizano wa Tiple Entent akuumbuzidwa ndi Germany, anakailowa mkondoyo k*thandiza Russia. Apatu tsopano ku Europe kwayamba kuyaka moyo.
Pambuyo pake Germany anafuna kumuonetsa zakuda France koma amafuna njira yachidule yokafikira ku Paris, Germany anaukira Belgium kufuna njira yopitira ku Paris. Britain ataona zamtopora wa Germany naye anakailowa mkhondoyo pa 4 August 1914. Mkhondo inavuta koopsa ndipo koma kumayambuliro amkhondoyo mzaka za 1914,1915,1916 Germany anali wamphamvu kwambiri ndipo mmene imafika mchaka cha 1916 Germany anali atalanda 3 quoter yama territories aadani awo

Mbali ya Germany imatchedwa ma Central Powers pamene mbali ya Britain ndi ena amkatchedwa ma Allies. Pa 9 April 1915 Italy anakailowa mkhondoyo koma mmalo molowa kumbali ya Germany analowa kumbali ya Britain k*thibula m'bale wake.
Kodi ndichifukwa chiyani Italy anasintha thabwa? Chifukwa chanthawi ndiloleni ndizaneneulendo wina,
Pa 7 May 1915 sitima yapamadzi ya Germany yotchedwa UH2o inakaphwasula sitima ina yonyamula anthu wamba yotchedwa Lustania ndipo panafa anthu ambiri. Mwa anthu omwe anafa pachiwembuchi anthu 128 zinali nzika zaku America kenako(NEXT.....)

PANGANI LIKE 👍 PAGE INO K*TI MUDZIMVA ZAMBIRI🙏

THE FIRST WORLD WAR PART 3Mkumano wachitika, khothi lalikulu lakhazikisidwa, Britain komanso Germany ndi maiko ena aku E...
03/08/2022

THE FIRST WORLD WAR PART 3

Mkumano wachitika, khothi lalikulu lakhazikisidwa, Britain komanso Germany ndi maiko ena aku Europ asainira pangano lantendere.

Koma Germany anayamba kuphanya pangano lopatilika atabwelera kwawo, mu 1899 Germany anayamba kupangisa training asilikali ochuluka, komanso anayamba kuonjedzera asilikali apanyanja komanso sitima zankhondo zapanyanja, uku kunali kufuna k*tenga ulamuliro wapanyanja. Panthawiyi Britain ndamene anali ndi sitima zochuluka pa nyanja zonse zamchere, Britain anali wamphamvu kwambiri padziko lonse lapansi.

Zochita za Germany zinayamba k*tutumutsa Britain ndimaiko ena aku Europ, ndipo mdani wakulu wa Germany (Britain) anayamba k*tutumuka naye Germany. Britain anaonjedzera asilikali pa nyanja komanso mlengalenga. Mu 1902 Britain anapanga military and politically alliance ndi dziko la France, ndipo ngwilizano wawo anautchula k*ti Entent Cordiale. Russia anazalowa mu mgwilizanowu mu 1907 ndipo unasintha dzina kukhala TRIPLE ENTENT.

Apatu tsopano ku Europe kunali koti kwavuta, kwabuka magulu awiri ankhondo. Kwinaku kuli TRIPLE ALLIANCE yamaiko a Germany, Austria-Hungary ndi Italy kwinakunso Britain, France ndi Russia apanga wawo mgwirizano otchedwa TRIPLE ENTENT. Maiko onse omwe anali pa udani anali atakonzeka koma amasowa k*ti amene ayambitse ndindani mkhondoyi.

📖Daniel 11:29 mngelo wa Mulungu anati, "panthawi yoikika mfumu yakumpoto (Germany) izabwera nizalowa kumwera koma nthawi yomalizirayi sikuzakhala monga poyamba paja".
Pa 28 June 1914 munthu wina yemwe anali kalonga waku Austria anaphedwa, munthuyi anali Archduck Francis Ferdinand ndipo chiwembuchi chinakomzedwa ndi gulu lina lotchedwa Black Hand Society ndipo gululi linali laku Serbia. Ndipo chiwembuchi chinakonzedwa ku Sarajevo ku Bosnia. Chigawengacho chinali Gabriel Prispi.

Apa Germany analimbikitsa Austria-Hangary k*ti abwedzere chiwembuchi ndipo anamusimikizira k*ti azimuthandiza pachichonse.Kodi zinatha bwanji?(NEXT......)
PANGANI LIKE👍 PAGE INO K

Pangan like page ino
29/07/2022

Pangan like page ino

THE FIRST WORLD WAR Tikupitikiza kuona zankhondo yoyamba he dziko lonse lapansi, ndipo timuona k*ti zikugwilizana bwanji...
23/07/2022

THE FIRST WORLD WAR

Tikupitikiza kuona zankhondo yoyamba he dziko lonse lapansi, ndipo timuona k*ti zikugwilizana bwanji ndi ulosi wapa Daniel chapter 11,

Dzulo tinasiira poti Wilhelm 2 mwana wa Fredreck 3 anatenga ulamuliro wa dziko la Germany ( mfumu yakumpoto). Wilhelm 2 anali mfumu yamatuk*tuku ndipo anayamba zokuza ufumu wa Germany k*ti ufalikire padziko lonse lapansi. Germany anatenga maiko ena mu africa muno mkumawalamulira monga Tanzania ndi ena. Izi sizinakomere Otto Von Bizmack yemwe anali nduna yayikulu mdzikolo. Ndipo anazuzula Wilhelm 2 kamba kakuzikuza kwake, izi zinapangitsa Wilhem 2 kukakamidza Otto Von k*ti atule pansi udindo.

Mu 1890 Otto Von Buzmack anatula pansi udindo, ndipo izi zinapangitsa Wilhelm kulamulira mwantambasale, anayamba kupanga train asilikali ambiri mu Germany. Izi zinayamba kupeleka chiopsezo ku Britain yomwe inali super power on that time.

Sir Nicholas 2 mfumu yaku Russia inaitanisa mkumano okakhazikisa ntendere, ndipo mukumanowu unachitikira ku Netherlands mudzinda otchedwa Hague, meeting imeneyi unachitika pa 24 August 1898.

📖Daniel 11:27 limati "Mafumu onse awiri azakumbuka kuchita zoipa nadzanena bodza pagome limodzi". Awatu anali mafumu a Britain ndi Germany omwe onse anasainira pangano lantendere pa table limodzi ku meeting ya ku Hague. Ndipo maiko onse anagwilizana zokhazikitsa khothi lalikulu la dziko lonse lomwe liziona milandu yapakati pamaiko. Komanso anasankha Germany komanso Britain kukhala azitsogoleri.

📖Daniel 11:28 likupitiliza k*ti "ndipo mfumu yakumpoto (Germany) uzabwelera kudziko lake ndi chuma chambiri, ndi mtima wake uzatsutsana ndi chipangano chopatulika ndizachita chifuniro chaka".
Meeting itatha aliyense anabwelera kudziko lake, koma Germany poona chuma komanso mphamvu zomwe anali nazo sanasamalenso za pangano lantendere lomwe anasainira ku mkumano uja.Kodi Germany anatani?(NEXT...)
PANGAN 👍LIKE PAGE INO K*T MUDZIWE ZAMBIRI

18/07/2022

DANIEL CHAPTER 11

Nkhondo zonse zikuchitika pano zinakambidwa kale m'Baibulo kuyambira nkhondo ya dziko lonse yoyamba, yachiwiri, cold war mpaka nkhondo iyi ili mkati ya Russia ndi Ukrain.

Tsopano tiyeni tiyambe kusanthura chapter 11 cha buku la Daniel ndipo pamapeto ake muona k*ti nthawi yatha. Verse 1 mpaka 13 tikuona zamafumu a mmbuyo tisanafike mu 19 century koma ine ndiloleni ndiyambire verse 14.

THE FIRST WORLD WAR
Mzaka zamma 19 century maiko aku Europ anali ak*tukuka kwambiri, ndipo mayiko anali kupita patsogolo pa chuma, malutso azopangapanga, mphamvu yazachikhalidwe, ndi mphamvu pamaiko ena (colonism).

Mzaka zakumayambiliro Britain ndamene anali ndi mphamvu kuposa maiko onse, kenako Germany anazitolera naye. Mbaibulo pa 📖Daniel 11:14,15, Germany akukhala ufumu ya kumpoto ndipo Britain ndi ufumu wakumwera.

Pa 18 January 1871, Wilhelm 1 amakhala mfumu yaikulu ya Germany, ndipo anasankha Otto Von Bismark kukhala nduna yake yaikulu. Kenako pofuna k*teteza ufumu wawo anapanga mgwirizano ndi maiko monga Austria-Hungary komanso Russia koma pamapeto mgwilizanowu sunalimbe ndipo unatchedwa "loose alliance".
Kodi nchifukwa chiyani mgwilizanowu sunakhalitse?
Russia anali pa udani ndi Austria-Hungary, maikowa amakanganirana dera lina lomwe linali ku Poland. Ndipo zinali zovuta k*ti maiko omwe ali pamkangano then at same time apangenso mgwirizano. Russia anatulukamo mumgwilizano umenewo, kumbukirani k*ti munthawi imeneyi Sir Nicholas ndamene anali mfumu ku Russia.
Mu 1879 Germany ndi Austria-Hungary anabweleza kupanga mgwilizano, ndipo Italy anazapanga join mu 1882 that was Military and politically alliance. Mgwilizanowu anautchula k*ti Triple Alliance, unali uja oti attack in one attack in all.
Mu 1888 Wilhelm 1 anamwalira ndipo Frederick 3 anatenga ulamuliro mu Germany, koma naye analamulira masiku 99 okha naye mkumwalira. Kaiser Wilhelm 2 anatenga ulamuliro, koma Wilhelm 2 anali ozikonda komanso wamtopola(NEXT.....pangan like page ino k*t mudziwe zambir

Address

Mponda

Opening Hours

Tuesday 09:00 - 17:00
Thursday 09:00 - 17:00
Friday 09:00 - 17:00
Saturday 09:00 - 17:00

Telephone

+265992292897

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Uthenga wabwino ochokera kwa mulungu posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Contact The Business

Send a message to Uthenga wabwino ochokera kwa mulungu:

Videos

Share

Category