16/01/2025
Bungwe la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) lapempha anthu kuti apewe kuchitila nkhanza anthu okalamba komanso anthu achialubino.
Bungweli lidakonza masewero ampira wa miyendo komanso ntchembele mbayi ndicholinga chofuna kufalitsa uthengawu ndipo mwambowu unachitika lachiwiri, pa 14 January 2025 pa bwalo la zamasewero la Mpondas CDSS m'boma la Mangochi
Polankhula ndi wailesi ino mkulu wa bungweli a Micheal Kaiyasa adati anagwilitsa ntchito masewerowa ngati njila imodzi yopelekela uthenga wawo umene umalunjika kunkhanza zimene anthuwa akukumana nazo.
A Kaiyatsa anati, anthu achikulire akuzuzidwa powaganizira kuti ndi afiti zomwe zikuzetsa nkhanza zosyanasyana monga kuthamangitsidwa kudera, kumenyedwa komanso kuphedwa kumene, zomwe zikubweletsa mantha pakati anthu achikulilewa.
Iwo adatinso miyoyo ya anthu achi alubino imakhala pachiopsezo maka mu chaka cha pamene chisankho chayandikira, pamene anthu ena amakhulupilira kuti mafupa awo amathandizira kuchitila zinthu zina zosyanasyana zamasenga ndipo izi zimayika miyoyo yawo pachiopsezo.
A Kayiyatsa adatinso mkofunika kuti anthu akhale ndi udindo kuti afalitse uthenga komanso poonetsetsa kuti anthu okalamba komanso achialubinono akukhala momasuka mdera mwawo.
Pothilirapo ndemanga sub-T/A Mambo adayamikila bungwe la CHRR chifukwa cha uthenga omwe adawabweretsera ponena kuti ndiofunika kwambiri mdera lawo.
Muchaka chapitachi anthu 18 achikulire aphedwa kamba kowaganizira kuti ndi afiti.
Timu yampira wa miyendo ya Mpondas United inagonjetsa team ya Kalonga Stars 4 kwa 2 kuzera kumapenate pamene mpila wa ntchembere mbaye timu ya Kalonga Sisters inagojetsa Mpondas United Sisters ndi mabasiketi 19 kwa 14.
Bungwe la CHRR lili pa ntchito yodziwitsa anthu za kuyipa kochitila nkhanza anthu achikulire komanso achialubino, mu project yotchedwa “ strength minority rights ‘’ ndipo ikugwira mothandizana ndi bungwe la CEDEP ndithandizo la ndalama kuchokera ku Royal Norwegian Embassy
By Brian Nkonde