10/01/2026
M'malawi waphedwa ndi boyfriend pa Theba.
Mzimai mukumuwonayu waphedwa ndi boy friend wake ku Joni m'banda kucha wa lachiwiri pa 6 January.
Malipoti akuti anthuwa adali pa ubwezi ndipo nthawi zambili mkaziyu amakonda kupita komwe amakhala mamuna wakeyu ndipo padaliso nyumba zina pa malo omwe amakhala.
Ndiye akuti mkaziyu akapita ku Chimbudzi amatha 30 minutes ali mchimbudzi ndipo izi zidayamba kumamukayikitsa mamunayu mpaka adayamba kuganiza kuti mwina girl friend wakeyo akapita ku Chimbudzi amakanyengetsa ndi mabatchala omwe amakhala nawo moyandikana pa nyumba za rent.
Lero mawa kutacha mayiyu adachitaso chimodzimodzi kupita ku Chimbudzi ndipo adatha 30 minutes ali mchimbudzimo. Izi sizidakondweretse mamunayo mpaka adayamba kumumenya ndikumuvulaza ndipo anthu achifundo adatengera mayiyu ku chipatala komwe mkaziyu wamwalira.
Mumuna ndi mkaziyu onse ndi a Malawi ndipo izi zachitika ku South Africa.
Pakadali pano mamuna yemwe wapha bwezi lakeli wathawa.