28/12/2024
MWAGWIRA CHIYANI MMANJA MWANU.....
Mkulu wina yemwe ankadusa munjira ina anapeza mzimai atavula nsapato zake, kwinaku akumangila nsalu yake molimba, miyala yake itatu ili poteropo...
Mkuluyo anali odabwa ndizomwe amachita mai yo ndipo anamufunsa:
🤷‍♂️"KODI MAYI CHIKUCHITIKA NDI CHIYANI"?
Mzimai uja mosasamala kwambiri anati,
🙅‍♀️"ohoooo!!! Kodi k*tero simukuziwa k*t nyumba yapatsogoloyo pali agalu olusa, ineyo apapa k*tero ndamangila kale nsalu yanga, nsapato zangaz zikhala manja, lero agalu amenewa adziwanso, ndikakawandikira, nkangowagenda kenako ndikathamange chiliwiro basi ndiduse"...
Mkulu uja anamuyang'ana mzimai uja ndipo anamuuza k*t;
🤔"MAI INU MULI NDI TSOKA, NDIPONSO MWINA MUTU WANU SUKUGWIRA, MIYALA MWATENGAYI, MUTAKHALA MWAMUPHONYA GALUYO, MUNGATHAMANGISANE NAYE? MMENE GALU AMATHANGILA MUNGACHITE NAYE MPIKISANO"?
...
Mzimai anangot zyoliii ndipo mkulu uja analowa pakatchire nafuna NDODO yabwino yamphamvu namupasa mai uja, ndipo anamuuza k*t avale nsapato zake...
Anamutsimikizira k*t choyamba akhulupire k*t MTENGO WAMUPATSAWO UMUTHANDIZA, CHIFUKWA KAKHULUPIRIRA, SANGAUTAYE ANGAKHALE AGALU ATACHITA UKALI CHOTANI, AZADUTSA MOSAVUTA CHIFUKWA SAZAFIKA NAYE PAFUPI..
Mzimai anadutsa mosavuta, agalu ankangochita ukali osafika naye pafupi.....
M'bale kunja kuno kuli agalu, kulimbana nawo wekha, popanda chilichonse Mmanja mwako, sungapambane...KODI MWAGWIRA CHIYANI MMANJA MWANU?
Okondedwa k*tero satana pa inu nokha simungapange nae mpikitsano, satana ali ndi mphamvu, ndipo ndiiye akulamula dziko la pansi YOHANE 14 VS 30 .
Anthu lero atenga miyala nkuika mmanja, ati kufuna kulimbana ndi mkuru wa dziko lapansi, Miyala imene itatitaika tizasowa chozitetedzera, tikudalira nyanga, ziwanda pofuna kulimbana ndi mkuru wadziko lapansi... l MUkatenga miyala nkuika manja mwanu kuchekera, k*tsilika nyumba k*tsilika business, nkumat Mukulimbana nae, nkumati mwathana nae ndiye mwasaka njira yolakwika, chifukwa simukudziwa k*t komwe mwakatenga zimenezo ndi kwa bambo wake wa iyeyo satana, akupasani bwanji zogonjesera ufumu wake, chabwino nanga zitakhala k*t zomwe akupasanizo zatha ntchito, mungalimbe polimbana ndi mfiti inu?..
YOHANE 14 VS 6...YESU anati, INE NDINE NJIRA CHOONADI NDI MOYO, PALIBE MUNTHU ADZA KWA ATATE KOMA MWAINE...
Okondedwa ndi Yesu yekha ndiye Njira yabwino yogonjesera oipa... Tengani Yesu akhale NDODO yanu..akhale mumtimamo
Mkulu uja anamuuza mai uja k*t choyamba akuyenera kukhulupira k*t ndodo ija imuthandiza ndipo izamuthandizad pamavuto sangaitaye, ifenso tiyen tikhulupirire Yesu yemwe ali mumitima yathu ndipo tikatero angakhale zitavuta sitingakagwadenso kwa milungu yakunja, sik*t pamene uli ndi Yesu agalu samachita ukali ai, sik*t satana asiya kulimbana nawe ai, sik*t mayesero alekeka ai..., koma baibulo lik*ti Mulungu sazalola k*t tizayesedwe moposera msinkhu wathu, azaonesesa k*t waika adani onse kunsi kwamapaz athu, EXODUS 14 VS 14 azatigwirira nkhondo tili chete..
Tiyeni tisanyengeke ndi nkhalidwe wina uliwonse odza ndi mphamvu ya oipayo, angakhale zitakoma chotani, mutalemera chotani koma kumbukiran k*t slogan ya satana ndi KUPHA..KUBA .. NDI KUONONGA...CHISANGALALO CHILICHONSE POPANDA JESUS IS EQUAL TO GAHENA....
AMBUYE AKUDALITSENI NDIPO MUKHALE NDI TSIKU LABWINO ..