![Anthu okwiya amenya komanso kuvulaza mayi Mary Laini Kaude azaka 87 ochokera m'mudzi wa Matewere mdera la mfumu yayikul...](https://img5.medioq.com/105/005/1370207581050051.jpg)
05/01/2025
Anthu okwiya amenya komanso kuvulaza mayi Mary Laini Kaude azaka 87 ochokera m'mudzi wa Matewere mdera la mfumu yayikulu Juma m'boma la Mulanje powaganizira kuti akumanga mvula.
Malinga ndi malipoti anthu ena analowa m'nyumba ya mayiyu ndikuyamba kumumenya ndi cholinga chofuna kumukakamiza kuti amasule mvula.
Anthu ena oyandikira atamva phokoso la anthuwa anathamangira kunyumbayo komwe anawapulumutsa ndikuwatengela ku chipatala chaching'ono cha Namphungo ndipo anawatumiza kuchipatala chachikulu cha bomali komwe anawagoneka kwa masiku awiri akulandira thandizo.
Kutsatira izi bungwe la MANEPO lati ndilokhumudwa ndi nkhaza zomwe anthu achikulire akulandira m'dziko muno.
Kalata yomwe mkulu wa bungweli Andrew Kavala watulutsa yati m'chitidwewu ndikuphwanya ufulu wa anthu achikulire kotero apolisi akuyenera kuchita kafukufuku mwansanga ndikupeza anthu omwe achita izi kuti malamulo agwire ntchito.
Mbali ina ya Kalatayi yapemphanso boma kuteteza kuti likhazikitse ndondomeko za mbwino zomwe zidziteteza ufulu wa anthu achikulire maka a mmadera a kumidzi.
Wolemba Mathews Benard