Njinga ya moto ya mtundu wa SanLG yapsya pomwe amayiotchelera pa msika wa Chayamba turn off m'tawuni ya Kasungu.
Tatha Banda wazaka 22 yemwe amayendetsa njingayo wati anabwereka njingayi kuti akasiyire bambo ake kwa Chulu kuchoka nawo kwa Chilowamatambe koma iye amakhala koma pobwelera ndipomwe njingayo inaduka malo ena.
Atangoyamba kuotchelera, moto unaphulika ndi kugwira njinga yonse koma mwa mwayi palibe yemwe wavulala.
Nawo ochelerawo ati akuganiza kuti chomwe chinayambitsa moto ndi chifukwa chakuti sanachotse pulagi.
Wolemba Samson Baza
#KCRnkhani
#Bwenzilanupachitukuko
Mverani KCR pa 107.6Mhz kapena pa utatavu Kudzera pa 👇🏾
https://live.netradio.pro/listen/kcr/radio.mp3
Mvula ikugwa koma anthu akadali pa mfolo kwa Ofesi, T/A Kawamba, kufuna kuponya voti pa chisankho chachipulula cha MCP kummwera chakumadzulo kwa boma la Kasungu.
Anthu ochokera m'madera (areas) 215 a m'mawodi a Lusa ndi Misozi ndiwo akuvota pofuna kupeza yemwe adzayimire chipanichi pa chisankho chapatatu ngati khansala komanso phungu wanyumba ya malamulo.
Anthu 18 akupikisana pa udindo wa khansala pomwe 6 pa udindo wa phungu wanyumba ya malamulo.
Pakadali pano kuvota kuli mkati ndipo kanema ali mmusiyi akuonetsa momwe ziliri.
Wolemba Samson Baza
#KCRnkhani
#Bwenzilanupachitukuko
Mverani KCR pa 107.6Mhz kapena pa utatavu kudzera pa 👇🏾
https://live.netradio.pro/listen/kcr/radio.mp3
Mtsogoleri wadziko lino Dr. Lazarus Chakwera wafika m'boma la Kasungu komwe akhale akuyendera zitukuko zosiyanasiyana komanso kulimbikitsa anthu kuti akalembetse m'kaundula wa chisankho cha chaka cha mawa.
Dr. Chakwera akuyembekezeka kuchititsa misonkhano yoima-ima m'madera a Gogode, Simulemba, Wimbe, Chilowamatambe komanso pa Kasungu pa Boma.
Pomwe amadutsa pafupi ndi sukulu ya pulaimale ya Khuza m'dera la mfumu ya ndondo Kaomba, ophunzira apemphako mtsogoleriyu zinthu zingapo.
Ophunzirawa ati akufuna boma liyike transformer ya magetsi m'deralo komanso abweretse mipando yokhalira ophunzira (Desks) pa sukulupo, mwazina.
Wolemba Tadala Hudson Njelesa
#KCRnkhani
#Bwenzilanupachitukuko
Mverani KCR pa 107.6MHz kapena pa utatavu kudzera pa 👇🏾
https://live.netradio.pro/listen/kcr/radio.mp3
Kuli kanthu kokanthula mchala pa bwalo la chithiba m'boma la Kasungu komwe kuli msonkhano wa Democratic Progressive Party DPP.
#KCRnkhani
#Bwenzilanupaçhitukuko
Mverani KCR pa 107.6MHz.
Amayi ena anasokhana madzulo a lachinayi, kuyimba nyimbo zodandaula ndi zomwe mtsikana wina yemwe akuti zaka zake zitha kukhala pakati pa 18 ndi 20 wachita m'dera la mfumu yayikulu Wimbe m'boma la Kasungu.
Amayiwa ati akuganizira mtsikanayo kuti ndiye anabadwitsa ndi kutaya khanda lomwe lakhala likuzungulira m'masamba a mchezo masiku awiri apitawa litapezeka mbali imodzi agalu atadya pa mjigo wina m'deralo.
Amayiwa ati mtsikanayu anali ndi pa thupi, koma sizikudziwika komwe wakachilira ndipo dzulo anathamangira naye ku chipatala chaching'ono cha Wimbe, komwe anakalandira thandizo la mankhwala, adotolo atapeza kuti sakupeza bwino kaamba kobadwitsa khandalo.
M'nyimbo zomwe amayiwa amayimba, mwazina amati: “ Wapha mwana wosalakwa azimayi tikulira, anthu ena akusalakudya kusowa mwana, koma iwe wapha mwana."
Wachiwiri kwa mneneri a apolisi m'bomali a Miracle Hauli wati ndi zoona kuti amanga mtsikanayu koma pakadali pano akufufuzabe chenicheni cha nkhaniyi.
Wolemba Topson Banda
#KCRnkhani
#Bwenzilanupachitukuko
Mverani KCR pa 107.6MHz kapena pa utatavu kudzera pa 👇🏾
https://r114.netradio.pro:2000/main
Mfumu ya ndodo Kapelura ya m'boma la Kasungu yatsimikiza kuti Njovu zochoka mu nkhalango yotetezeka ya Nkhotakota zinafika m'dera lawo la chinayi lapitali.
Iyo yati njovuzi zitafika m'mudzi wa Mtambalika zinadzetsa chidwi chachikulu kwa anthu a m'deralo kamba koti ambiri mwa iwo kunali koyamba kuona nyamazi.
Mfumuyi yati anthuwa anayamba kugenda komanso kuthamangitsa njovuzi zomwe zapangitsa kuti munthu wina avulazidwe ndi imodzi mwa Njovuzi.
'Anthu ali mkati mozilondora, Njovu ina inagunda munthu ndipo mwamwayi wake anagwera mu dzenje lomwe linali pafupi zomwe zinapangitsa kuti isamuone pomwe imafuna imuponde'
'Komanso ndauzidwa kuti dimba la munthu ku dera lomwe Njovuzi zinali lasakazidwa', Mfumuyi inatsimikiza motero
Pakali pano wovulazidwayi anagonekedwa pa chipatala chachikulu cha boma la Kasungu.
Pomwe timafuna timve kuchoka kwa wofalitsa nkhani za umoyo pa pa chipatalachi a Catherine Yoweli anati tiwapatse nthawi kuti afufuze kaye.
Mpungwepungwe wa pakati pa anthu ndi Njovu m'boma la Kasungu ukumka namachulukirabe pomwe anthu angapo atayapo kale miyoyo, kuvulazidwa komanso mbewu zawo kusakazidwa.
Wolemba: Vincent Madalitso Chauma (13-10-23)
Kanema: njovu zomwe zinafika m'mudzi wa Mtambalika
#KCRNKHANI
#BwenziLanuPaChitukuko
Mverani KCR pa 89.0 MHz kapena pa utatavu kudzera pa 👇🏾
http://r114.netradio.pro:2000/main