Mizu online Broadcasting

  • Home
  • Mizu online Broadcasting

Mizu online Broadcasting Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Mizu online Broadcasting, .

*WELCOME TO MIZU ONLINE BROADCASTING *
CHOLINGA CHATHU:
-kudziwitsana zinthu zomwe zikuchitika mdera la Blantyre West ndimadera Ena ozungulira
-Kuika PA mbalambanda maganizo a mzika zakumudzi

"BULLETS YAPATSIDWA ZIGOLI ZITATU" - KATCHIKAMphunzitsi watimu ya Kumanda Stars, Innocent Katchika, wati wothandizira kw...
13/10/2024

"BULLETS YAPATSIDWA ZIGOLI ZITATU" - KATCHIKA

Mphunzitsi watimu ya Kumanda Stars, Innocent Katchika, wati wothandizira kwa oyimbira mmasewero omwe timuyi imakumana ndi FCB Nyasa Big Bullets wapereka zigoli zitatu kwa anzawowa zomwe sizimayenera kukhala zololedwa.

Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 22-1 pa bwalo la Kamuzu kuti atuluke mu chikho cha Castel Challenge Cup ndipo iye anaonetsa kusakhutira kwake ndi wothandizira oyimbirayu.

"Mukhonza kuona kuti oyimbira makamaka othandizira kwa oyimbira mmodzi wapereka zigoli zitatu kwa Bullets." Anatero Katchika.

Iye wati timu yake inagonja chifukwa anyamata ake anachita chabe mantha kuti amasewera ndi timu yaikulu ndipo wati mpikisanowu wawaphunzitsa zambiri zomwe agwiritse ntchito popita chitsogolo.

Pa zigolizi, khumi ndi chimodzi zinagoletsedwa mchigawo choyamba pomwe khumi ndi chimodzi zina zinalowa mchigawo chachiwiri.

Photo courtesy of Wa Ganyu

17/07/2024

M'boma la Neno mwabuka matenda achilendo omwe apha kale anthu atatu pofika dzuro pa 16 July, pomwe ena 20 onse ana awagoneka pa chipatala chachikulu cha Neno.

Mneneri wa chipatalachi a Caroline Banda atsimikiza izi, kuti matendawa akufanafana ndi a malungo koma simalungo poti palibe ampeza nawo pa anthu onse omwe awayeza kale.

Iwo ati zizindikiro zake ndi monga kutsegula m'mimba, kusanza, kuphwanya kwa mutu, kuphweteka m'mimba komanso kutentha thupi.

Padakali pano a Banda akuti akufufuzabe chomwe chayambitsa nthendayi.

Stay safe

12/07/2024

Shout out to my newest followers! Excited to have you onboard! Stanford Kamvazina, Dickson Matumbi, Edith Kagona, Austin Phiri

Kalata ya  UTM
12/07/2024

Kalata ya UTM

Trending ZathapoMneneri wa chipani cha UTM a Felix Njawala walengeza kuti atuluka mu mgwirizano wa Tonse.Iwo alengeza iz...
12/07/2024

Trending

Zathapo

Mneneri wa chipani cha UTM a Felix Njawala walengeza kuti atuluka mu mgwirizano wa Tonse.

Iwo alengeza izi pa msonkhano wa atolankhani omwe akuchititsa ku likulu la chipanichi mu mzinda wa Lilongwe.
Otsatira kwa Pulezidenti a Michael Usi saanapezeke nawo pa Mkumanowu ati kamba ka mantha.

07/07/2024

Kuli chi mfuu chachikuli pamene thupi la GVH Gwadani likufika kuchokela kunyumba yosungilamo zovuta.

Pamene anthu asonkhana kudikila thupi la malemu a Gulupu A Gwadani  nkhope zawo zamwetuliko chifukwa chasewero lomwe lik...
07/07/2024

Pamene anthu asonkhana kudikila thupi la malemu a Gulupu A Gwadani nkhope zawo zamwetuliko chifukwa chasewero lomwe likuchitika pakadali pano.
Monga mwa mwambo wa a mang'anja, anthu monga mafumu ena amachita sewero molingana ndi mmene mfumu yotisiyayo imachitila maka pozenga milandu.

Phungu opuma wa delari a Peter Kumpalume akuchita nawo seweroli.

Gulu la anthu ochuluka likusonkhana pa bwalo la Chikowa court  ndikhope zokugwa, pomwe akuyembekezela  mwambo wa Maliro ...
07/07/2024

Gulu la anthu ochuluka likusonkhana pa bwalo la Chikowa court ndikhope zokugwa, pomwe akuyembekezela mwambo wa Maliro a omwe anali a GVH Gwadani a mfumu yaikulu Kunthembwe.

A Gulupu A Gwadani adatisiya pa 5 July, 2024 pomwe adachita ngozi ya Galimoto.

26/09/2023

Kondwani Kachamba Ngwira writes

Achinyamata Ndimvereni.
Pompano Anzathu a Ndale aphweka chifukwa afuna vote yanu .Chilichonse mupemphe ayesesa kukupatsani

Achinyamata opusa , ogona awaseweresa chabe mpira ati ka trophy mdzina la MP ndikuwadukulila timagule . Uku ndikuganiza kofoooooila heavy .

Ndikukupemphani Dzukani and Demand Business Loans , Demand Processing machines , Demand Youth center , Demand irrigation equipment, Demand Technology.

Awuzeni bwana ife achinyamata ndalama zampirazo tipatseni matumba a feteleza tigawana.

Once mukawaphonya anthuwa simuzawaonanso mpaka 2030.
Ndimatewe aubongo kumakuseweresa mpira kumudzi nthawi ya campaign pamene Njala ili munyumba .

Dzuka wachinyamata . Siya kugona . Ask the Honourable member to establish Thumba la ngongole za ma business . Apempheni abwana akugulileni machine opangira ma cement block . mafuta ophikila , Soap , Bakery .
Ndalama Ali nazo . Nthawi yako ndiyomwei basi yoti nawenso usunthe

Izizi akwiya nane ndipo sandionera kukondwa koma mantha mwa ine mulibemo poti ndiziwa Amene ndimpembeza.

We have once produced a program on the same.. Let's open our eyes for the betterment of our communities
Thank you

Happy birthday to Innocent Malungah..Let's wish him good luck as he is exploring a new mile
05/06/2023

Happy birthday to Innocent Malungah..
Let's wish him good luck as he is exploring a new mile

Sharing is caring... Tell your friends to try their luck.
31/05/2023

Sharing is caring... Tell your friends to try their luck.

31/05/2023

Mulibwanji konse muli?

We have something good for you, coming your way....

Guess what?

Address


Telephone

+265888003392

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Mizu online Broadcasting posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Videos

Shortcuts

  • Address
  • Telephone
  • Alerts
  • Videos
  • Claim ownership or report listing
  • Want your business to be the top-listed Media Company?

Share