04/01/2025
NKHANI PANG'ONO
Mu Chaka cha 2013 azibambo ena aku Kenya anathamangitsa kambuku mpaka kumugwira.
Ineso ndili ozizwa ngati mmene mwachitira inumu. Kodi zinakhala bwanji?
Kambukuyi wakhala akuba ziweto za anthu amenewa ndipo tsiku lina atabwera monga mwa chizolowezi kudzaba mbuzi , mzibambo wina anauza amzake ena atatu omwe adathamangitsa kambukuyi pa mtunda wosachepera 6km nkumugwira.
Dziwani kuti kambuku ndi nyama ya liwiro kwambiri ndipo imatha kuthamanga pa liwiro losachepera 100km/hr koma musaiwale kuti ku Kenya nakoso kuti anyamata odziwa kuthamanga ngati kuti ali ndi turbo V16 engine.
Atamugwira kambukuyi, azibambowa sadamuphe koma kukamusiya ku Kenya wildlife.
Zina ukamva!